Nyimbo 95
Chipatso cha Ubwino
1. Yehova ndiye Mfumu yamuyaya,
Ubwino chifundo mkhalidwe wake.
Anatumiza Mwana Kristu Yesu
Kuti asonyeze anthu kulapa.
2. Anthu athandizidwa ndi ubwino
Kumasulidwa kuchoka m’Babulo.
Mulungu atipatsa kuunika,
Kupatula chabwino ku choipa.
3. Ubwino wa M’lungu tiutsanzire;
Chipatso cha mzimu tichikulitse.
Tikhale aufulu m’chilungamo,
Kudalira M’lungu ndi Kristu Yesu.
4. Kukula mu’bwino tidzachitanji?
Kuphunzira kupemphera ndi ntchito.
Osaleka kusonkhana n’abale
Tidzakhala okhoza mu ubwino.