Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 30 tsamba 186-tsamba 189 ndime 4
  • Kusonyeza Chidwi mwa Munthu Winayo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusonyeza Chidwi mwa Munthu Winayo
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Sonyezani Chikondwerero Chaumwini mwa Ena
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Yesetsani Kuwafika Pamtima Anthu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 30 tsamba 186-tsamba 189 ndime 4

PHUNZIRO 30

Kusonyeza Chidwi mwa Munthu Winayo

Kodi muyenera kuchita motani?

Sonyezani kuti mumasamala za maganizo a ena ndi miyoyo yawo.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Ndi njira imodzi yotengera chitsanzo cha Yehova pa kusonyeza chikondi, ndipo kumatithandiza kufika munthu pamtima.

POUZAKO ena za choonadi cha m’Baibulo, tisangowapatsa uthenga wokhawo basi. Tizikopanso mitima yawo. Njira imodzi yochitira zimenezo ndiyo kusonyeza omverawo chidwi chenicheni chochokera pansi pa mtima. Chidwi choterocho tingachisonyeze m’njira zosiyanasiyana.

Ganizirani Malingaliro a Omvera Anu. Mtumwi Paulo anaganizira za mikhalidwe ya omvera ake ndi kalingaliridwe kawo. Iye anafotokoza kuti: “Kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo; kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo. Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena. Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.” (1 Akor. 9:20-23) Kodi ifenso lero tingakhale bwanji “zonse kwa anthu onse”?

Ngati mwakhala ndi mwayi wopenyerera ena, ngakhale kwa nthaŵi yochepa chabe musanalankhule nawo, mungayambe kuzindikira zimene amakonda ndi mikhalidwe ya moyo wawo. Kodi mungadziŵe ntchito imene amagwira? Kodi pali zizindikiro zosonyeza chipembedzo chawo? Kodi mukuonapo chilichonse chosonyeza mkhalidwe wa banja lawo? Malinga ndi zimene mungaone, kodi mungasinthe ulaliki wanu kuti ukhale wosangalatsa kwa omvera anu?

Kuti ulaliki wanu ukhale wosangalatsa kwambiri muyenera kuganiziratu kuti anthu a m’gawo lanu mukawafikira motani. M’madera ena, anthuwo angaphatikizepo aja ochokera kumayiko ena. Ngati anthu oterowo alimo m’gawo lanu, kodi mwapeza njira yogwira mtima yowalalikira nayo? Popeza kuti ndi chifuniro cha Mulungu kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi,” khalani ndi cholinga cholalikira uthenga wa Ufumu m’njira yosangalatsa kwa onse amene mungakumane nawo.—1 Tim. 2:4.

Mvetserani Mosamala. Ngakhale kuti Yehova amadziŵa zonse, amamvetserabe ena akamalankhula. Mneneri Mikaya analandira masomphenya mmene anaona Yehova akulimbikitsa angelo kuti alankhule maganizo awo pankhani inayake imene anali kukambirana. Kenako Mulungu analola mmodzi wa angelowo kuchita malinga ndi maganizo amene mngeloyo anapereka. (1 Maf. 22:19-22) Pamene Abrahamu anasonyeza nkhaŵa yake pa chiweruzo cha Sodomu, Yehova mwachisomo anamulola kuti alankhule maganizo ake. (Gen. 18:23-33) Pankhani ya kumvetsera, kodi tingatengere motani chitsanzo cha Yehova pamene tili mu utumiki wa kumunda?

Limbikitsani ena kulankhula maganizo awo. Funsani funso loyenerera, ndipo perekani mpata wokwanira kuti ayankhe. Mvetserani mosamala. Kutchera khutu kwanu kudzawalimbikitsa kulankhula momasuka. Ngati yankho lawo livumbula kanthu kena koonetsa zinthu zimene amakonda, funsanibe mosamala kuti mumve zambiri. Musawafunse mafunso ambiri ngati kuti mukuwafufuza, m’malo mwake onetsani kuti mungofuna kudziŵana nawo bwino. Yamikirani maganizo awo, ngati mungatero moona mtima. Ngakhale kuti simukuvomereza maganizo awo, athokozenibe mwachikondi polankhula zimene amakhulupirira.—Akol. 4:6.

Komabe, tisamale kuti chidwi chathu kwa anthu chisapitirire malire. Kudera nkhaŵa anthu ena si chilolezo chakuti tiloŵerere nkhani za eni. (1 Pet. 4:15) Posonyeza chidwi chathu chokomera mtima munthu wamkazi kapena wamwamuna, tisamale kuti asaone ngati kuti tili ndi zolinga zina. Popeza chimene anthu angachione kukhala chidwi choyenerera chimasiyana m’madera osinayanasiyana, ngakhalenso kwa anthu osiyanasiyana, m’pofunika kulingalira mosamala.—Luka 6:31.

Kukonzekera kumathandiza kukhala womvetsera wabwino. Ngati uthenga wathu tikuudziŵa bwino lomwe, timakhazika mtima pansi ndipo timamvetsera kwa ena mwachibadwa. Zimenezi zimawathandiza kukhazika mtima pansi ndipo amatha kulankhula nafe momasukirapo.

Mwa kumvetsera ena akamalankhula timawapatsa ulemu. (Aroma 12:10) Timaonetsa kuti timalemekeza maganizo awo ndi kalingaliridwe kawo. Kungawapangitsenso kumvetsera kwambiri zimene tinganene. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amatilangiza kukhala ‘otchera khutu [mofulumira, NW], ndi odekha polankhula.’—Yak. 1:19.

Thandizani Ena Kupita Patsogolo. Kudera nkhaŵa ena kudzatithandiza kuganizirabe aja osonyeza chidwi ndi kuwafikiranso kuti tikakambirane nawo mfundo za m’Baibulo zimene zingakwaniritse bwino zosoŵa zawo. Poganizira za ulendo wotsatira, kumbukirani zimene munazindikira ponena za iwo pamaulendo apita. Konzekerani mfundo za nkhani imene imawakhudza. Unikani phindu lenileni la nkhaniyo, ndipo athandizeni kuona mmene angapindulire ndi zimene akuphunzira.—Yes. 48:17.

Ngati womvera wanu atchula mavuto amene ali nawo, uoneni kukhala mpata wapadera wakuti mum’gaŵire uthenga wabwino. Tengerani chitsanzo cha Yesu, amene nthaŵi zonse anali wokonzeka kulimbikitsa anthu opsinjika mtima. (Marko 6:31-34) Kanizani maganizo ofuna kupereka yankho la mwamsanga kapena kupereka langizo longofuna kum’kondweretsa. Zimenezo zingachititse munthuyo kuona kuti mulibe chidwi chenicheni. M’malo mwake, sonyezani kuti mukumvetsa mkhalidwe wakewo. (1 Pet. 3:8) Fufuzani m’zofalitsa zophunzirira Baibulo, ndipo fotokozani mfundo zolimbikitsa kuti muthandize munthuyo kuthana ndi vuto lakelo. Ndiponso nkhaŵa yanu pom’konda womvera wanu iyenera kukuletsani kuulula zinsinsi zimene angakuuzeni, kupatula ngati pali chifukwa chomveka chochitira zimenezo.—Miy. 25:9.

Tiyenera kusonyeza chidwi makamaka kwa aja amene timaphunzira nawo Baibulo. Ganizirani mosamala zosoŵa za wophunzira wanu komanso kum’pempherera, ndipo pokonzekera phunziro, ganizirani zosoŵazo. Khalani mukumadzifunsa kuti, ‘Kodi tsopano ayenera kuchitanji kuti apitebe patsogolo?’ Mwachikondi, thandizani wophunzirayo kumvetsa zimene Baibulo limanena pankhaniyo, komanso zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Nthaŵi zina, kungofotokozera munthu mfundo kungakhale kosakwanira. Mungafunikire kusonyeza wophunzirayo mmene angagwiritsire ntchito mfundo ya m’Baibulo. Mungachite zimenezo mwa kuchita naye limodzi kanthu kena kosonyeza mmene mfundoyo imathandizira.—Yoh. 13:1-15.

M’pofunika kuchita mosamala komanso molingalira bwino pothandiza ena kuti ayambe kuyendera miyezo ya Yehova pamiyoyo yawo. Anthu amakula mosiyanasiyana ndipo amakhala ndi maluso osiyanasiyana; amapitanso patsogolo pamlingo wosiyanasiyana. Pachifukwa chimenecho, tisayembekezere zambiri kwa iwo. (Afil. 4:5) Musawapanikize kuti asinthe miyoyo yawo nthaŵi yomweyo. Lolani kuti Mawu a Mulungu ndi mzimu wake uwakhudze mtima ndi kuwalimbikitsa kuchitapo kanthu. Yehova amafuna kuti anthu am’tumikire mwaufulu, osati mowaumiriza. (Sal. 110:3) Peŵani kupereka maganizo anuanu pankhani zaumwini zimene ayenera kugamula okha; ndipo ngati ena akupemphani kuti muperekepo maganizo anu, samalani kuti musawagamulire zochita.—Agal. 6:5.

Athandizeni pa Zosoŵa Zawo. Ngakhale kuti Yesu ankadera nkhaŵa kwambiri moyo wauzimu wa omvera ake, anali wozindikiranso zosoŵa zawo zina. (Mat. 15:32) Ngakhale tili osoŵa, zilipo njira zambiri zimene tingathandizire ena.

Kukhala ndi chidwi mwa ena kudzatithandizanso kuganizira ena. Mwachitsanzo, ngati kunja sikunache bwino ndipo zikukhala zovuta kwa womvera wanu pamene mwakhalapo, sunthirani pa malo ena amene aliko bwino, kapena konzani zoti mudzapitirize kukambiranako nthaŵi ina. Ngati mwafika nthaŵi yosayenerera, pemphani kuti mufikenso nthaŵi ina. Ngati munthu woyandikana naye makomo kapena wokondweretsedwa ndi uthenga wathu wadwala kapena ali kuchipatala, sonyezani kum’dera nkhaŵa mwa kum’tumizira khadi kapena kakalata kapenanso kukamuona. Ngati n’koyenera, mungam’tengereko kachakudya kapena kum’sonyeza chifundo mwa njira ina.

Pamene ophunzira Baibulo akupita patsogolo, angayambe kusungulumwa chifukwa alibenso nthaŵi yambiri yocheza ndi mabwenzi awo akale. Khalani mabwenzi awo. Zichezani nawoni pambuyo pa phunziro la Baibulo ndi nthaŵi zina. Alimbikitseni kupeza mabwenzi abwino. (Miy. 13:20) Athandizeni kuti azifika pamisonkhano yachikristu. Khalani nawoni pamisonkhanoyo, ndipo athandizeni kusamalira ana awo kotero kuti onse apindule mokwanira ndi msonkhano.

Sonyezani Chidwi Chochokera Pansi pa Mtima. Kusonyeza chidwi mwa anthu, si mwambo wochita kukumbukira, koma ndi mtima wa munthu. Ukulu wa chidwi chathu mwa anthu ena umaoneka m’njira zosiyanasiyana. Umaoneka ndi mmene timamvetsera ena ndi zimene timanena. Umaonekanso mwa chifundo ndi kuganizirana kumene timasonyeza ena. Ngakhale popanda kuchita kapena kunena kanthu, chidwicho chimaonekabe mwa khalidwe lathu ndi maonekedwe a nkhope yathu. Ngati timasamaladi za anthu ena, sangalephere kuona zimenezo.

Chifukwa chachikulu chosonyezera chidwi mwa ena n’chakuti timakhala tikutsanzira chikondi ndi chifundo cha Atate wathu wakumwamba. Zimenezo zimakopera omvera athu kwa Yehova ndi ku uthenga umene iye watipatsa kuti tiufalitse. Choncho, pamene tikulalikira uthenga wabwino, tiyesetse kuti “munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.”—Afil. 2:4.

MMENE MUNGASONYEZERE CHIDWI CHENICHENI

  • Tcherani khutu pamene munthu wina akulankhula. M’yamikireni chifukwa chopereka maganizo ake. Funsani mafunso kuti mumvetse bwino kalingaliridwe kake.

  • Mutatha kukambirana naye, ganizirani za munthuyo. Muchezereninso mwamsanga.

  • Mufotokozereni mfundo za m’Baibulo zokhudza zosoŵa zake.

  • M’thandizeni kuchita zinthu zina. Ganizirani zosoŵa zake za panopo ndi za m’tsogolo.

ZOCHITA: (1) Msonkhano wa mpingo usanayambe, sonyezani chidwi mwa munthu wina amene wafikapo. Musangonena “muli bwanji” basi. Yesetsani kum’dziŵa bwino munthuyo. Musonyezeni kuti mumasamala. Chikhale chizoloŵezi chanu nthaŵi zonse. (2) Pamene muli mu utumiki wa kumunda, sonyezani chidwi mwa munthu amene mukumana naye. Musangopereka ulaliki wokha ayi. Dziŵanani nayeni munthuyo. Nenani ndi kuchita zinthu malinga ndi zimene mwadziŵa za munthuyo. Nthaŵi zonse funafunani mipata yochita zimenezo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena