Nyimbo 109
Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova!
Losindikizidwa
1. Tamandani Yesu
Mfumu yodzozedwayo.
Yokonda choonadi
Komanso chilungamo.
Popereka ulemu
Ku dzina la M’lungu,
Ulamuliro wake
Adzalengezatu.
(KOLASI)
Tamandani Yesu!
Wodzozedwa wa M’lungu.
Anakhazikitsidwa
Pampando monga Mfumu!
2. Tamandani Yesu
Yemwe anatifera.
Anapereka dipo.
Ndithu n’ngodzichepetsa.
Mkwatibwi wake pano
Akudikirira.
Ukwati n’ngwakumwamba
Udzatidalitsa.
(KOLASI)
Tamandani Yesu!
Wodzozedwa wa M’lungu.
Anakhazikitsidwa
Pampando monga Mfumu!
(Onaninso Sal. 2:6; 45:3; Chiv. 19:8.)