Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 70-tsamba 74
  • Chikumbutso (Mgonero wa Ambuye)

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikumbutso (Mgonero wa Ambuye)
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuchita Chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mgonero wa Ambuye Tiziukumbukira Motani?
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 70-tsamba 74

Chikumbutso (Mgonero wa Ambuye)

Tanthauzo: Chakudya chokumbukira imfa ya Yesu Kristu; chifukwa chake chikutchedwa chikumbutso cha imfa yake, imfa imene inakhala ndi ziyambukiro zazikulu kwambiri kuposa ya munthu wina aliyense. Chimenechi ndicho chochitika chokha chimene Ambuye Yesu Kristu analamula ophunzira ake kuchikumbukira. Chimatchedwanso Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, kapena Mgonero wa Ambuye.—1 Akor. 11:20.

Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la Chikumbutso?

Kwa ophunzira ake okhulupirika Yesu anati: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Polembera ziŵalo zauzimu za mpingo wa obadwa ndi mzimu Wachikristu, mtumwi Paulo anawonjezera kuti: “Nthaŵi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.” (1 Akor. 11:26) Chotero, Chikumbutso chimasonyeza mwapadera kufunika kwa imfa ya Yesu Kristu m’kuchitidwa kwa chifuno cha Yehova. Chimagogomezera tanthauzo la imfa yansembe ya Yesu makamaka mu unansi wa pangano latsopano ndi njira imene imfa yake imayambukirira awo amene adzakhala oloŵa nyumba limodzi naye mu Ufumu wakumwamba.—Yoh. 14:2, 3; Aheb. 9:15.

Chikumbutso chirinso chokumbutsa kuti imfa ya Yesu ndi mmene inakwaniritsidwira, mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu monga momwe kwasonyezedwera pa Genesis 3:15 ndi pambuyo pake, inatumikira kulemekeza dzina la Yehova. Mwa kusunga umphumphu kwa Yehova kufikira pa imfa yake, Yesu anatsimikizira kuti tchimo la Adamu silinali chifukwa cha cholakwa chirichonse m’kulinganizidwa kwa munthu ndi Mlengi koma kuti kuli kotheka kwa munthu kusunga kudzipereka kwaumulungu kwangwiro ngakhale pansi pa chipsinjo chachikulu, ndipo motero Yesu analemekeza Yehova Mulungu monga Mlengi ndi Mfumu Yachilengedwe chonse. Kuwonjezera apa, Yehova anali atalinganiza kuti imfa ya Yesu ikakhala nsembe yangwiro yaumunthu yofunika kuwombolera ana a Adamu, ndipo motero kutheketsa mabiliyoni ambiri amene akasonyeza chikhulupiriro kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wa padziko lapansi, mokwaniritsa chifuno choyambirira cha Yehova ndi kusonyeza chikondi chake chachikulu kaamba ka anthu.—Yoh. 3:16; Gen. 1:28.

Ha ndikatundu wothodwetsa chotani nanga amene anali pa Yesu pausiku wake womaliza padziko lapansi monga munthu! Iye anadziŵa zimene Atate wake wakumwamba anamlinganizira, koma anadziŵanso kuti akafunikira kusonyeza kukhulupirika pansi pa chiyeso. Ngati akadalephera, ndimtonzo wokulira chotani nanga umene kumeneku kukanatanthauza kwa Atate wake ndipo kukanakhala kutayikiridwa chotani nanga kwa anthu! Chifukwa cha zonse zimene zikanakwaniritsidwa kupyolera mwa imfa yake, kunali koyenera koposa kuti Yesu analangiza kuti ikumbukiridwe.

Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la mkate ndi vinyo zogwiritsiridwa ntchito pa Chikumbutso?

Ponena za mkate wopanda chotupitsa umene Yesu anapereka kwa atumwi ake poyambitsa Chikumbutso, iye anati: “Thupi langa ndi iri.” (Marko 14:22) Mkate umenewo unaphiphiritsira thupi lake lanyama lopanda uchimo. Akapereka limeneli kaamba ka ziyembekezo za moyo wamtsogolo wa anthu, ndipo pa chochitika chimenechi chisamaliro chapadera chikuperekedwa pa ziyembekezo za moyo zimene limatheketsera awo amene akasankhidwa kukhala ndi phande limodzi ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba.

Popereka vinyo kwa atumwi ake okhulupirika, Yesu anati: “Ichi ndimwazi wanga wachipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri.” (Marko 14:24) Vinyo ameneyo anaphiphiritsira mwazi wa moyo wa iyemwini. Kupyolera mwa mwazi wake wokhetsedwa, chikhululukiro cha machimo chikakhala chotheka kwa awo omkhulupirira. Pa chochitika chimenechi Yesu anali kugogomezera kuyeretsedwa ku uchimo kumene kukapangitsa kukhala kotheka kwa oloŵa nyumba anzake oyembekezeredwa. Mawu ake amasonyezanso kuti kupyolera mwa mwazi umenewo pangano latsopano pakati pa Yehova Mulungu ndi mpingo Wachikristu wa odzozedwa ndi mzimu likachititsidwa kugwira ntchito.

Wonaninso tsamba 280-282, pamutu wakuti “Misa.”

Kodi ndani amene ayenera kudya mkate ndi vinyo?

Kodi ndani amene anadya pamene Yesu anayambitsa Mgonero wa Ambuye mwamsanga iye asanafe? Otsatira okhulupirika khumi ndi mmodzi kwa amene Yesu anati: ‘Ndikuchita pangano ndi inu, monga momwedi Atate wanga wachita pangano ndi ine, laufumu.’ (Luka 22:29, NW) Iwo onse anali anthu amene akaitanidwa kukalamulira limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba. (Yoh. 14:2, 3) Onse amene amadya mkate ndi kumwa vinyo lerolino ayeneranso kukhala anthu amene Kristu wawaloŵetsa mu ‘pangano laufumu.’

Kodi pali angati amene amadya? Yesu ananena kuti “kagulu ka nkhosa” kokha kakalandira Ufumu wakumwamba monga mphotho yawo. (Luka 12:32) Chiŵerengero chokwanira chikakhala 144 000. (Chiv. 14:1-3) Kagulu kameneko kanayamba kusankhidwa mu 33 C.E. Moyenerera, pakakhala chiŵerengero chaching’ono chokha cha akudya tsopano.

Kodi Yohane 6:53, 54 amasonyeza kuti ndiawo okha amene amadya amene adzapeza moyo wosatha?

Yoh. 6:53, 54: “Yesu anati kwa iwo, Indetu, Indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.”

Mwachiwonekere kudya kumeneku ndi kumwa kukayenera kuchitidwa mophiphiritsira; ngati sikunali motero wakudyayo akakhala akuswa lamulo la Mulungu. (Gen. 9:4; Mac. 15:28, 29) Komabe, kuyenera kudziŵika kuti mawu a Yesu pa Yohane 6:53, 54 sananenedwe panthaŵi ya kukhazikitsidwa kwa Mgonero wa Ambuye. Palibe aliyense wa amene anamumva amene anali kudziŵa za kuchitidwa kwa phwandolo ndi mkate ndi vinyo zogwiritsiridwa ntchito kuimira thupi ndi mwazi wa Kristu. Kakonzedwe kameneko sikanayambidwe kufikira pafupifupi chaka chimodzi pambuyo pake, ndipo mawu a Yohane osimba za Mgonero wa Ambuye samayamba kufikira pambuyo pa machaputala oposa asanu ndi aŵiri (m’Yohane 14) mu Uthenga Wabwino wokhala ndi dzina lake.

Pamenepa, kodi ndimotani, mmene munthu ‘angadyere thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa vinyo wake’ mwanjira yophiphiritsira ngati kusali mwakudya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso? Tamverani kuti Yesu ananena kuti awo akudya ndi kumwa mwanjirayo akakhala nawo “moyo wosatha.” Poyambirira, m’vesi 40, polongosola zimene anthu ayenera kuchita kuti akhale nawo moyo wosatha, kodi anati nchiyani chimene chinali chifuniro cha Atate ŵake? Kuti “yense wakuyang’ana Mwana, ndi kukhulupirira iye, akhale nawo moyo wosatha.” Pamenepa, moyenerera, ‘kudya thupi lake ndi kumwa mwazi wake’ m’lingaliro lophiphiritsira kumachitidwa mwa kusonyeza chikhulupiriro m’mphamvu yowombola ya thupi la Yesu ndi mwazi wake zimene anapereka m’nsembe. Kusonyezedwa kwa chikhulupiriro kumeneku kuli kofunika kwa onse amene adzapeza moyo wopanda mapeto kaya m’miyamba limodzi ndi Kristu kapena m’Paradaiso wapadziko lapansi.

Kodi Chikumbutso chiyenera kusungidwa mwa kaŵirikaŵiri motani, ndipo liti?

Yesu sanafotokoze mwachindunji kuti chikachitidwa kaŵirikaŵiri motani. Iye anangoti: ‘Chitani ichi pondikumbukira.’ (Luka 22:19) Paulo anati: “Pakuti nthaŵi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye” (1 Akor. 11:26) “Nthaŵi zonse” satofunikira kutanthauza nthaŵi zambiri m’chaka; angatanthauze kamodzi pachaka kwanyengo yazaka zambiri. Ngati inu mukumbukira chochitika chofunika, monga ngati tsiku lachaka ndi chaka laukwati, kapena ngati dziko lichita phwando la chochitika chofunika m’mbiri yake, kodi chimachitidwa kaŵirikaŵiri motani? Kamodzi pachaka padeti lofananalo la chaka. Zimenezi zikakhalanso zogwirizana ndi chenicheni chakuti Mgonero wa Ambuye unakhazikitsidwa padeti la Paskha Yachiyuda, phwando lachaka ndi chaka limene silinafunikirenso kusungidwa ndi Ayuda amene anakhala Akristu.

Mboni za Yehova zimasunga Chikumbutso pambuyo pa kuloŵa kwadzuŵa pa Nisani 14, mogwirizana ndi kuŵerenga kwa kalendala Yachiyuda imene inali yofala m’zaka za zana loyamba. Tsiku Lachiyuda limayamba pa kuloŵa kwadzuŵa ndipo limapitirira kufikira kuloŵa kwadzuŵa kwatsiku lotsatira. Chotero Yesu anafa patsiku limodzimodzilo lakalendala Yachiyuda limene anayambitsa Chikumbutso. Chiyambi cha mwezi wa Nisani chinali kuloŵa kwadzuŵa pambuyo pa mwezi wam’mwamba watsopano pafupifupi ndi nyengo ya kufanana kwa masana ndi usiku umene unawonekera m’Yerusalemu. Deti la Chikumbutso limakhalako masiku 14 pambuyo pa tsikulo. (Motero deti la Chikumbutso silingayenderane ndi la Paskha yosungidwa ndi Ayuda amakono. Chifukwa ninji? Kuyambika kwa miyezi yawo yakalendala kwalinganizidwa kuti kuyenderane ndi mwezi watsopano wowonekera m’mlengalenga, osati mwezi watsopano wowonekera m’Yerusalemu, umene ungakhaleko maora 18 mpaka 30 pambuyo pake. Ndiponso, Ayuda ambiri lerolino amasunga Paskha pa Nisani 15, osati pa 14 monga momwe anachitira Yesu mogwirizana ndi zimene zinafotokozedwa m’Chilamulo cha Mose.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena