Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jr mutu 2 tsamba 14-31
  • Kutumikira Mulungu “M’masiku Otsiriza”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutumikira Mulungu “M’masiku Otsiriza”
  • Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MMENE ZINTHU ZINALILI M’NTHAWI YA YEREMIYA
  • ZINTHU ZINASINTHA KU YUDA
  • ‘ULEMBEMO MAWU ONSE’
  • UFUMU WA BABULO UNAKULA MPHAMVU
  • KUTHA KWA UFUMU
  • ANAPITIRIZA KUTUMIKIRA PAKATI PA AYUDA OTSALA
  • Yeremiya—Mneneri Wachilendo wa Ziweruzo za Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Mumasankha Anthu Otani Kuti Akhale Anzanu?
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • “Ndaika Mawu Anga M’kamwa Mwako”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Kodi Tsiku Lililonse Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
Onani Zambiri
Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
jr mutu 2 tsamba 14-31

Mutu 2

Kutumikira Mulungu “M’masiku Otsiriza”

1, 2. (a) Kodi Yeremiya anaona masomphenya otani, omwe anasonyeza mfundo yaikulu ya uthenga wake waulosi? (b) N’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi uthenga wa Yeremiya?

MULUNGU anafunsa Yeremiya, yemwe anali wachinyamata komanso anali atangomusankha kumene kukhala mneneri, kuti: “Ukuona chiyani?” Iye anayankha kuti: “Ndikuona mphika wakukamwa kwakukulu umene uli pamoto, ndipo motowo aupemerera kuti uyake kwambiri. Mphikawo wafulatira kumpoto.” Masomphenya amenewa, omwe Yeremiya anaona kumayambiriro kwenikweni kwa utumiki wake, anasonyezeratu mtundu wa uthenga umene iye azidzalengeza. (Werengani Yeremiya 1:13-16.) Iye anaona mphika wophiphiritsa uli pamoto, ndipo motowo anaupemerera kuti uyake kwambiri. Apa Yehova analosera kuti mavuto oopsa kwambiri adzagwera dziko la Yuda chifukwa choti anthu ake anapitirizabe kukhala osakhulupirika. Iye anayerekezera zimenezi ndi madzi owira okhuthulidwa kuchokera mumphika uja. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani kamwa ya mphikawo inayang’ana kum’mwera? Zimenezi zinkatanthauza kuti mavuto adzachokera kumpoto, kapena kuti Ababulo adzagonjetsa dzikolo kuchokera kumpoto. Ndipo ndi mmenedi zinachitikira. Pa zaka zimene Yeremiya anali mneneri, iye anaona ndi maso ake mavuto otsatizanatsatizana, omwe ankakhala ngati akuchokera mumphika wowira wophiphiritsa uja, akukhuthulidwa padziko la Yuda, ndipo zimenezi zinafika pachimake pamene Yerusalemu anawonongedwa.

2 N’zoona kuti masiku ano mzinda wa Babulo kulibe. Komabe muli ndi zifukwa zabwino zochitira chidwi ndi uthenga waulosi wa Yeremiya. N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti mukukhala “m’masiku otsiriza” ndipo anthu ambiri akunena kuti iwo ndi Akhristu. Komabe iwowo pamodzi ndi matchalitchi awo, sakondweretsa Mulungu. (Yer. 23:20) Mosiyana ndi anthu amenewa, inuyo pamodzi ndi Mboni zinzanu mukutsanzira Yeremiya polalikira uthenga, osati wachiweruzo wokha, komanso wopatsa chiyembekezo.

Chithunzi patsamba 14

3. (a) Kodi nkhani za m’buku la m’Baibulo la Yeremiya zinasanjidwa motani? (b) Kodi cholinga cha Mutu 2 wa buku lino n’chiyani?

3 Zikuoneka kuti chakumapeto kwa utumiki wake monga mneneri, Yeremiya anapempha mlembi wake kuti alembe buku lotchedwa Yeremiya. Iye sankalemba zinthuzo pa nthawi yomwe zinkachitika. (Yer. 25:1-3; 36:1, 4, 32) Komanso buku la Yeremiya silinalembedwe motsatira ndondomeko ya mmene zinthuzo zinachitikira. M’malomwake, Yeremiya anasanja nkhani zambiri za m’bukuli mogwirizana ndi mitu yake. Choncho, zingakuthandizeni kwambiri ngati mutadziwa zinthu zina zimene zinkachitika pa nthawi imene mabuku a Yeremiya ndi Maliro ankalembedwa, komanso ndondomeko imene zinthuzo zinkachitikira. Mwachitsanzo, mungaone tchati chimene chili patsamba 19. Mungamvetse bwino zimene Yeremiya ankanena kapena kuchita ngati mutadziwa yemwe anali mfumu ya Yuda pa nthawiyo. Nthawi zina mungamvetse bwino nkhani za m’bukuli ngati mutadziwa zimene zinkachitika ku Yuda kapena m’madera ozungulira dzikolo. Zimenezi zikuthandizani kuti mupindule kwambiri ndi uthenga wa Mulungu wopita kwa anthu ake, umene anaulengeza kudzera mwa Yeremiya.

MMENE ZINTHU ZINALILI M’NTHAWI YA YEREMIYA

4-6. Kodi zinthu zinkawayendera bwanji anthu a Mulungu kutatsala zaka zambiri ndithu kuti Yehova asankhe Yeremiya kukhala mneneri wake?

4 Yeremiya anali mneneri pa nthawi imene kunali mavuto ambiri chifukwa chakuti zinthu zinkasinthasintha m’dziko la Yuda. Pa nthawiyo, panali mpikisano waukulu pakati pa Asuri, Ababulo ndi Aiguputo chifukwa ankalimbirana ulamuliro. Komanso zaka pafupifupi 93 Yeremiya asanayambe utumiki wake monga mneneri, Asuri anagonjetsa ufumu wakumpoto wa mafuko 10 wa Isiraeli, ndipo anatenga anthu ambiri n’kupita nawo ku ukapolo. Pa nthawiyo, Yehova anateteza Yerusalemu pamodzi ndi Hezekiya, yemwe anali mfumu yokhulupirika, kuti asawonongedwe ndi Asuri. Mungakumbukire kuti Mulungu anapha mozizwitsa asilikali a Asuri okwana 185,000. (2 Maf. 19:32-36) Mfumu Hezekiya anali ndi ana angapo ndipo mmodzi wa iwo anali Manase. N’kutheka kuti Yeremiya anabadwa mkati mwa ulamuliro wa zaka 55 wa Manase, ndipo pa nthawiyo, dziko la Yuda linkalamuliridwa ndi Asuri.—2 Mbiri 33:10, 11.

5 Yeremiya analemba mabuku a 1 ndi 2 Mafumu, ndipo timawerenga m’mabukuwa kuti Manase anamanganso malo okwezeka amene bambo ake anawononga. Manase anamanga maguwa a nsembe a Baala ndiponso maguwa a nsembe a magulu akumwamba. Iye anafika pomanga maguwa amenewa m’kachisi weniweni wa Yehova. Komanso Manase anakhetsa magazi ochuluka zedi a anthu osalakwa, moti mpaka anapereka mwana wake wamwamuna nsembe yopsereza kwa mulungu wonyenga. Mwachidule tingati “iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova.” Chifukwa cha zoipa zonsezi, Mulungu ananena kuti Yerusalemu ndi Yuda akumana ndi tsoka, ngati limene linagwera Samariya ndi Isiraeli. (2 Maf. 21:1-6, 12-16) Manase atamwalira, mwana wake Amoni anayamba kulamulira, ndipo anapitiriza kulambira mafano mofanana ndi bambo ake. Koma posakhalitsa zinthu zinasintha. Amoni atangolamulira kwa zaka ziwiri zokha, anaphedwa. Kenako mwana wake Yosiya anayamba kulamulira m’chaka cha 659 B.C.E., ali ndi zaka 8 zokha.

6 Mu ulamuliro wa zaka 31 wa Yosiya, Ababulo anayamba kukhala ndi mphamvu kwambiri kuposa Asuri. Apa Yosiya anapezerapo mwayi wochotsa dziko la Yuda mu ulamuliro wa dziko lina kuti likhale loima palokha. Mosiyana ndi bambo ake komanso agogo ake, Yosiya anatumikira Yehova mokhulupirika ndipo anasintha zinthu kwambiri pa nkhani ya kulambira. (2 Maf. 21:19–22:2) Mwachitsanzo, m’chaka cha 12 cha ulamuliro wake, iye anawononga ndi kuchotsa malo okwezeka, mizati yopatulika ndiponso mafano onse a milungu yonyenga m’dera lonse la ufumu wake, ndipo kenako analamula kuti kachisi wa Yehova akonzedwenso. (Werengani 2 Mbiri 34:1-8.) N’zochititsa chidwi kuti Mulungu anauza Yeremiya kuti akhale mneneri wake m’chaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya (647 B.C.E.).

Kodi inuyo mukanamva bwanji mukanakhala mneneri m’nthawi ya Yeremiya?

7, 8. (a) Kodi ulamuliro wa Mfumu Yosiya unali wosiyana bwanji ndi wa agogo ake a Manase komanso wa bambo ake a Amoni? (b) Kodi Yosiya anali munthu wotani? (Onani bokosi patsamba 20.)

7 Ntchito yokonzanso kachisi ili mkati, m’chaka cha 18 cha ulamuliro wabwino wa Mfumu Yosiya, mkulu wa ansembe anapeza “buku la chilamulo.” Ndiyeno mfumuyo inauza mlembi wake kuti awerenge bukulo pamaso pake mokweza. Kenako Yosiya anazindikira kuti anthu ake anali olakwa kwambiri, ndipo anapempha malangizo kwa Yehova kudzera mwa Hulida, mneneri wamkazi. Komanso mfumuyo inalimbikitsa anthu ake kuti azimvera malamulo a Mulungu. Hulida anauza Yosiya kuti Yehova adzabweretsa “tsoka” kwa Ayuda chifukwa cha kusakhulupirika kwawo. Komabe, chifukwa choti Yosiya ankakonda kulambira koona, Yehova ananena kuti tsoka limenelo silibwera m’nthawi yake.—2 Maf. 22:8, 14-20.

Tchati patsamba 19

8 Mfumu Yosiya anapitirizabe ntchito yake yoyeretsa dzikolo pochotsa chilichonse chogwirizana ndi kulambira mafano. Iye anagwira ntchito imeneyi mwakhama kwambiri, moti mpaka anakafika kudera limene poyamba linali la ufumu wakumpoto wa Isiraeli. Kumeneko iye anagwetsa ndi kuwononga malo okwezeka a ku Beteli ndiponso guwa la nsembe. Kenako iye anakonza zoti pachitike chikondwerero chachikulu kwambiri cha Pasika. (2 Maf. 23:4-25) Yeremiya ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi zimene Yosiya ankachita. Komabe zinali zovuta kuti anthuwo amvere uthenga wa Mulungu n’kusiya makhalidwe awo oipa. Manase ndi Amoni anali ataphunzitsa anthuwo khalidwe lonyansa lolambira mafano, choncho iwo sankakonda kulambira koona. Ngakhale kuti Yosiya anasintha zinthu zambiri, Mulungu anachititsa Yeremiya kuuza Ayuda kuti milungu yawo inali yochuluka mofanana ndi mizinda yawo. Ndipo Ayuda anzake a mneneriyu anali ngati mkazi wosakhulupirika chifukwa anasiya Yehova n’kuyamba kuchita uhule ndi milungu yachilendo. Yeremiya ananena kuti: “Chinthu chochititsa manyazi mwachimangira maguwa ansembe, anthu inu. Mwachimangira maguwa ansembe ochuluka mofanana ndi misewu ya mu Yerusalemu. Mwamanga maguwa ansembe kuti muzifukizira Baala nsembe zautsi.”—Werengani Yeremiya 11:1-3, 13.

9. Kodi m’mayiko ozungulira dziko la Yuda munkachitika zotani pa zaka zomaliza za ulamuliro wa Yosiya?

9 Ngakhale kuti Yeremiya anapereka mauthenga ambiri otere, Ayuda sanasinthe, ndipo mayiko oyandikana nawo anapitiriza kulimbana kuti azilamulira mayiko ena m’chigawo chimenechi. Mu 632 B.C.E., asilikali a Ababulo ndi a Amedi, mogwirizana anagonjetsa mzinda wa Nineve, umene unali likulu la dziko la Asuri. Patapita zaka zitatu, Farao Neko wa ku Iguputo anatenga asilikali ake n’kulowera nawo kumpoto kukathandiza Asuri amene ankagonja pa nkhondoyo. Pa zifukwa zimene Baibulo silinanene, Yosiya anapita ku Megido kuti akabweze asilikali a ku Iguputo, koma anavulazidwa kwambiri n’kufa. (2 Mbiri 35:20-24) Kodi imfa yomvetsa chisoniyi inasintha bwanji zinthu pa ndale komanso pa nkhani ya chipembedzo m’dziko la Yuda? Ndipo kodi Yeremiya anakumana ndi mavuto atsopano otani?

ZINTHU ZINASINTHA KU YUDA

10. (a) Kodi mmene zinthu zinalili Yosiya atamwalira zikufanana bwanji ndi mmene zilili masiku ano? (b) Kodi kuona mmene Yeremiya ankachitira zinthu kungakuthandizeni bwanji?

10 N’zodziwikiratu kuti Yeremiya anamva chisoni kwambiri atamva kuti Yosiya wamwalira. Chifukwa cha chisoni chimenechi, iye anaimbira mfumuyi nyimbo za maliro. (2 Mbiri 35:25) Yosiya anamwalira pa nthawi imene zinthu zinali kale zovuta, ndipo anthu mu Yuda ankakhala mwamantha chifukwa cha nkhondo zimene zinkachitika m’mayiko ozungulira. Mayiko atatu amphamvu omwe anali Iguputo, Asuri ndi Babulo ankalimbana koopsa chifukwa dziko lililonse linkafuna kuti lizilamulira derali. Ndipo Yosiya atamwalira zinthu zinasinthanso mu Yuda pa nkhani ya kulambira. Izi zili choncho chifukwa Yosiya atamwalira, ulamuliro umene sunkatsutsa ntchito ya Yeremiya unathera pomwepo, ndipo ulamuliro wankhanza unayamba. Masiku anonso abale athu ambiri aona kusintha kotereku. Poyamba iwo ankalambira Mulungu mwaufulu, koma kenako zinthu zinasintha n’kuyamba kuzunzidwa komanso kuletsedwa kulambira. Inunso zimenezi zingathe kukuchitikirani nthawi ina iliyonse. Kodi tingatani zimenezi zitatichitikira? Kodi tingafunike kuchita chiyani kuti tipitirize kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika? Poganizira mafunso amenewa, tilimbikitsidwa tikaona mavuto amene Yeremiya anakumana nawo ndi zimene anachita pothana nawo.

YOSIYA ANALI MFUMU YOMALIZA PA MAFUMU ABWINO A YUDA

Chithunzi patsamba 20

Yosiya anakhala mfumu ya Yuda ali ndi zaka 8 zokha, bambo ake a Amoni atamwalira. Pamene anali ndi zaka 15, iye anayamba kufunafuna Mulungu ndi ‘kuyenda m’njira zonse za Davide kholo lake.’ Atafika zaka 19, anayamba kuyeretsa Yuda ndi Isiraeli pophwanya mafano ndi kugumula malo onse amene ankagwiritsidwa ntchito pa kulambira konyenga. Ali ndi zaka 25, anayamba ntchito yokonzanso kachisi wa Yehova.—2 Maf. 21:19–22:2; 2 Mbiri 34:2-8.

Ntchito yokonzanso kachisiyo ili mkati, panapezeka buku la Chilamulo. Mwina bukuli linali loyambirira lenileni limene linalembedwa ndi Mose ndipo linawerengedwa pamaso pa Yosiya. Atamva uthenga wake, Yosiya anadzichepetsa ndipo anang’amba zovala zake komanso analira. Kenako Yosiya anakonza zoti bukulo liwerengedwe pamaso pa ansembe, Alevi ndi anthu ake onse, aang’ono ndi aakulu omwe. Nkhaniyi imapitiriza kuti, mfumuyo inachita pangano pamaso pa Yehova “kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo ake . . . ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse.” Kenako Yosiya anapitiriza mwakhama kwambiri ntchito yothetseratu kulambira konyenga. Komanso mfumuyo inachitira Yehova mwambo wa Pasika waukulu kwambiri, ndipo mwambo ngati umenewu unali usanachitikepo kuchokera m’masiku a Samueli.—2 Mbiri 34:14–35:19.

11. Kodi chinachitika n’chiyani mu Yuda, Yosiya atamwalira?

11 Anthu a ku Yuda analonga ufumu Yehoahazi ku Yerusalemu, kulowa m’malo mwa bambo ake Yosiya. Yehoahazi, amenenso ankadziwika ndi dzina lakuti Salumu, anangolamulira kwa miyezi itatu yokha. Izi zili choncho chifukwa pamene Farao Neko ankabwerera kum’mwera atagonjetsa Ababulo, anachotsa mfumu yatsopanoyi pampando n’kuitenga kupita nayo ku Iguputo. Izi zitachitika, Yeremiya ananena kuti Yehoahazi “sadzabwereranso kwawo.” (Yer. 22:10-12; 2 Mbiri 36:1-4) Zitatero, Neko analonga ufumu Yehoyakimu, mwana winanso wa Yosiya kuti alowe m’malo mwa Yehoahazi. Koma Yehoyakimu sanatengere chitsanzo chabwino cha bambo ake ndipo ankalambira mafano m’malo mopitiriza kusintha zinthu ngati mmene bambo ake ankachitira.—Werengani 2 Mafumu 23:36, 37.

12, 13. (a) Kodi kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yehoyakimu, zinthu zinali bwanji pa nkhani ya kulambira? (b) Kodi atsogoleri achipembedzo achiyuda anamuchitira chiyani Yeremiya?

12 Kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yehoyakimu, Yehova anauza Yeremiya kuti apite kukachisi ndi kukadzudzula Ayuda mosapita m’mbali chifukwa cha zoipa zimene ankachita. Ayudawo ankaganiza kuti kachisi wa Yehova ali ndi mphamvu inayake yapadera yoti ingawateteze. Komabe, ngati iwo akanapitiriza ‘kuba, kupha, kuchita chigololo, kulumbira monama, kufukiza nsembe zautsi kwa Baala ndi kutsatira milungu ina,’ Yehova akanasiya kugwiritsa ntchito kachisiyo. Iye akanasiyanso anthu achinyengo amene ankalambira m’kachisi ameneyu, ngati mmene anasiyira chihema cha ku Silo m’masiku a Mkulu wa Ansembe Eli. Ndipo dziko la Yuda ‘likanawonongedwa’ n’kukhala bwinja lokhalokha. (Yer. 7:1-15, 34; 26:1-6)a Pamenepatu Yeremiya anafunika kulimba mtima kuti alengeze uthenga umenewo. N’kutheka kuti iye ankalengeza uthengawu pagulu, pamaso pa anthu olemekezeka komanso otchuka. Abale ndi alongo ena masiku ano amaona kuti amafunika kulimba mtima kuti akwanitse kuchita ulaliki wa mumsewu mwinanso kuti alalikire anthu olemera kapena otchuka. Komabe, mfundo imene tiyenera kukumbukira nthawi zonse ndi iyi: Mulungu sadzasiya kutithandiza ngati mmene anathandizira Yeremiya.—Aheb. 10:39; 13:6.

Chithunzi patsamba 22

13 Poganizira mmene zinthu zinalili ku Yuda pa nkhani ya ndale ndiponso kulambira, kodi atsogoleri achipembedzo anachita chiyani atamva uthenga wa Yeremiya? Mneneriyu akutiuza yekha zimene zinachitika, kuti: “Ansembe, aneneri ndi anthu onse [anandigwira] ndi kunena kuti: ‘Ukufa basi.’” Iwo anakwiya kwambiri ndipo anati: “Munthu uyu akuyenera chiweruzo cha imfa.” (Werengani Yeremiya 26:8-11.) Komabe, adani a Yeremiyawa sanapambane chifukwa Yehova anateteza mneneri wakeyu. Ndipo ngakhale kuti adani akewo anali ambiri moti akanatha kumugonjetsa mosavuta, Yeremiya sanachite mantha. Inunso simuyenera kuchita mantha anthu akamakutsutsani.

Kodi mungasiyanitse bwanji mmene zinthu zinalili mu ulamuliro wa Manase, Amoni ndi Yosiya? Kodi mukuphunzira chiyani mukaona mmene Yeremiya anagwirira ntchito yovuta imene anapatsidwa?

‘ULEMBEMO MAWU ONSE’

14, 15. (a) Kodi Yeremiya ndi mlembi wake Baruki anayamba kugwira ntchito yotani m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu? (b) Kodi Yehoyakimu anali munthu wotani? (Onani bokosi patsamba 25.)

14 M’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu, Yehova anauza Yeremiya kuti alembe mawu onse amene iye anamuuza kuyambira m’masiku a Yosiya. Choncho Yeremiya anauza mlembi wake Baruki kuti azilemba mawu onse amene Mulungu anakhala akuuza Yeremiyayo kwa zaka 23. Mauthenga ake achiweruzo anali okhudza mafumu ndi maulamuliro pafupifupi 20. Kenako Yeremiya anauza Baruki kuti akawerenge mokweza mpukutu umenewu m’nyumba ya Yehova. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Yehova anafotokoza kuti: “Mwina anthu a m’nyumba ya Yuda adzamva za masoka onse amene ndikufuna kuwagwetsera ndipo aliyense abwerera ndi kusiya njira yake yoipa. Akatero, ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndi machimo awo.”—Yer. 25:1-3; 36:1-3.

15 Koma nduna ya panyumba ya mfumu itawerenga mpukutuwo pamaso pa Mfumu Yehoyakimu, mfumuyo inaung’amba n’kuuponya pamoto. Kenako inalamula anthu kuti akagwire Yeremiya ndi Baruki n’kuwabweretsa pamaso pake, “koma Yehova anawabisa.” (Werengani Yeremiya 36:21-26.) Popeza kuti Yehoyakimu anali ndi mtima woipa kwambiri, Yehova ananena kudzera mwa mneneri wake kuti Yehoyakimuyo “adzaikidwa m’manda ngati mmene amaikira bulu wamphongo.” Mulungu anapitiriza kunena za Yehoyakimu kuti anthu “adzamukoka kudutsa naye pazipata za Yerusalemu ndi kukamutaya kunja.” (Yer. 22:13-19) Kodi mukuganiza kuti Yeremiya ankangokokomeza pofotokoza ulosi wochititsa manthawo?

16. Kodi Yeremiya ankalengeza uthenga wosangalatsa woti chiyani?

16 Ngakhale kuti Yeremiya analengeza mauthenga achiweruzowa, iye sikuti ankangolosera zinthu zoipa zokhazokha koma ankalengezanso uthenga wopatsa chiyembekezo. Mwachitsanzo, iye analengeza kuti Yehova adzalanditsa Aisiraeli ena m’manja mwa adani, n’kuwabwezera kudziko lawo kumene azidzakhala motetezeka. Iye analengezanso kuti Mulungu adzachita “pangano latsopano” ndi anthu ake, “lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,” ndiponso kuti adzalemba chilamulo chake m’mitima yawo. Mulungu adzawakhululukira zolakwa zawo ndipo sadzakumbukiranso machimo awo. Iye analoseranso kuti mbadwa ya Davide “idzaweruza mwachilungamo m’dzikoli.” (Yer. 31:7-9; 32:37-41; 33:15) Ena mwa maulosi amenewa anali oti adzakwaniritsidwa patapita zaka zingapo, ndipo ena patapita zaka zambiri. Enanso akutikhudza ifeyo masiku ano ndipo amatipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. Koma tikabwerera m’nthawi ya Yeremiya, adani a Yuda anali akumenyanabe n’cholinga choti azilamulira deralo.—Werengani Yeremiya 31:31, 33, 34; Aheberi 8:7-9; 10:14-18.

UFUMU WA BABULO UNAKULA MPHAMVU

17, 18. M’zaka zomaliza za ulamuliro wa Yehoyakimu ndi Zedekiya, kodi ku Yuda kunkachitika mavuto otani oyambitsidwa ndi mayiko ena?

17 M’chaka cha 625 B.C.E., Ababulo anamenyana ndi Aiguputo pa nkhondo yoopsa kwambiri imene inachitikira ku Karikemisi, pafupi ndi mtsinje wa Firate, pa mtunda wa makilomita 600 kumpoto kwa Yerusalemu. Pa nkhondoyo, Mfumu Nebukadinezara anagonjetsa asilikali a Farao Neko, ndipo analanda deralo m’manja mwa Aiguputo. (Yer. 46:2) Kenako Nebukadinezara anayamba kulamulira dziko la Yuda, ndipo Yehoyakimu anakakamizika kukhala mtumiki wake. Koma patapita zaka zitatu, Yehoyakimu anagalukira ulamuliro wa Ababulo. (2 Maf. 24:1, 2) Nebukadinezara ataona zimenezi, anatenga asilikali ake n’kulowa m’dziko la Yuda m’chaka cha 618 B.C.E., ndipo anazungulira mzinda wa Yerusalemu. Mungathe kuona m’maganizo mwanu kuti imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri, ngakhale kwa Yeremiya mneneri wa Mulungu. Zikuoneka kuti Yehoyakimu anaphedwa pa nthawi imeneyi.b Ndiyeno mwana wake, Yehoyakini, analowa m’malo mwake, koma iye anadzipereka m’manja mwa Ababulo patangopita miyezi itatu yokha atakhala mfumu ku Yuda. Nebukadinezara anatenga chuma chonse cha mu Yerusalemu pamodzi ndi Mfumu Yehoyakini komanso anthu onse a m’banja lachifumu ndiponso mabanja a anthu olemekezeka mu Yuda. Anatenganso amuna amphamvu ndi amisiri, n’kupita ndi anthu onsewa ku ukapolo. Pa gulu la anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolowo panalinso Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya.—2 Maf. 24:10-16; Dan. 1:1-7.

18 Ndiyeno Nebukadinezara anaika Zedekiya, mwana wina wa Yosiya, kukhala mfumu ya Yuda. Iye anali mfumu yomaliza pa mafumu apadziko lapansi a m’banja la Davide. Koma ulamuliro wake unatha pamene Yerusalemu anawonongedwa pamodzi ndi kachisi wake mu 607 B.C.E. (2 Maf. 24:17) Zedekiya analamulira kwa zaka 11, ndipo pa zaka zonsezo, m’dziko la Yuda munali mavuto akuluakulu azandale ndiponso mavuto ena osiyanasiyana. Choncho, Yeremiya anafunika kukhulupirira kwambiri Mulungu amene anamutuma kuti akhale mneneri.

YEHOYAKIMU, MFUMU IMENE INAPHA MNENERI WA YEHOVA

Chithunzi patsamba 25

Yehoyakimu anali ndi zaka 25 pamene anakhala mfumu ku Yuda, ndipo analamulira kwa zaka pafupifupi 11. Lemba la 2 Mbiri 36:5-8, lomwe limafotokoza mwachidule zimene Yehoyakimu anachita, limanena kuti sikuti iye anangochita zoipa zokha ayi, koma anachitanso zinthu “zonyansa.” Ngakhale kuti Yehoyakimu anachenjezedwa ndi Yeremiya, iye sanamvere, ndipo ankalamulira mopanda chilungamo, ankalanda anthu katundu wawo komanso ankapha anthu. Mwachitsanzo, pamene mneneri Uliya anauza Mfumu Yehoyakimu uthenga wofanana ndi wa Yeremiya, mfumuyo inamupha. Koma zikuoneka kuti nayonso mfumuyi inaphedwa pa nthawi imene Ababulo anazungulira mzinda wa Yerusalemu.—Yer. 22:17-19; 26:20-23.

19. Kodi anthu amene Yeremiya ankawalalikira anachita chiyani atamva uthenga wake, ndipo n’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi zimenezi?

19 Taganizirani mmene Yeremiya ankamvera pa nthawi imeneyi. Kungoyambira m’masiku a Yosiya, Yeremiya anaona mavuto ambiri azandale komanso kulowa pansi kwambiri kwa moyo wauzimu wa anthu a Mulungu. Ndipotu iye ankadziwa kuti zinthu zipitiriza kuipiraipira chifukwa anthu a mumzinda umene iye ankakhala anamuuza kuti: “Usanenere m’dzina la Yehova, ngati ukufuna kuti tisakuphe.” (Yer. 11:21) Ayudawo sanamvere Yeremiya ngakhale kuti anaona maulosi amene iye analosera akukwaniritsidwa. Iwo anamuuza kuti: “Ife sitimvera mawu amene watiuza m’dzina la Yehova.” (Yer. 44:16) Ngakhale zinali choncho, moyo wa anthuwo unali pa ngozi, ngati mmene zilili masiku ano. Uthenga umene timalengeza ndi wochokera kwa Yehova, mofanana ndi uthenga umene Yeremiya ankalengeza. Choncho, kuona mmene Yehova anatetezera mneneri wake mpaka kudzafika nthawi imene Yerusalemu anawonongedwa, kungakuthandizeni kuti mupitirize kuchita utumiki wanu kwa Mulungu mwakhama kwambiri.

Kodi tingaphunzire chiyani tikaona mmene Yeremiya ankachitira zinthu mu ulamuliro wa Yehoyakimu? Kodi Yeremiya ananena ulosi wapadera uti umene ukufika m’nthawi yathu ino?

KUTHA KWA UFUMU

20. N’chifukwa chiyani nthawi ya ulamuliro wa Zedekiya inali yovuta kwambiri kwa Yeremiya? (Onani bokosi patsamba 29.)

20 Mwina nthawi yovutitsitsa kwambiri pa nthawi yonse imene Yeremiya anali mneneri, inali nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Zedekiya. Mofanana ndi mafumu ambiri a Yuda amene analipo iye asanayambe kulamulira, Zedekiya “anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.” (Yer. 52:1, 2) Iye anali pansi pa ulamuliro wa Ababulo, ndipo Nebukadinezara anamulumbiritsa m’dzina la Yehova kuti adzapitiriza kugonjera mfumu ya ku Babulo. Ngakhale kuti Zedekiya anachita zimenezi, patapita nthawi iye anagalukira Ababulo. Pa nthawi imeneyi, adani a Yeremiya ankamukakamiza kwambiri kuti agwirizane ndi mfumu yogalukirayo.—2 Mbiri 36:13; Ezek. 17:12, 13.

21-23. (a) Kodi m’dziko la Yuda munali magulu awiri ati otsutsana pa nthawi ya ulamuliro wa Zedekiya? (b) Kodi anthu anamuchitira chiyani Yeremiya chifukwa cha uthenga wake, ndipo n’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi nkhani imeneyi?

21 Zikuoneka kuti Zedekiya atangoyamba kumene kulamulira, amithenga ochokera kwa mafumu a ku Edomu, Mowabu, Amoni, Turo ndi ku Sidoni anafika ku Yerusalemu. Mwina cholinga chawo chinali choti anyengerere Zedekiya kuti alowe nawo mumgwirizano wofuna kulimbana ndi Nebukadinezara. Koma Yeremiya analimbikitsa Zedekiya kuti agonjere Ababulo. Pofuna kutsindika mfundo imeneyi, Yeremiya anapereka magoli kwa amithengawo. Magoliwo ankaimira mfundo yakuti mayiko awo nawonso akuyenera kutumikira Ababulo. (Yer. 27:1-3, 14)c Anthu sanasangalale ndi zimene Yeremiya anachitazo, ndipo Hananiya anachititsa kuti ntchito ya Yeremiya yolengeza uthenga wa Mulungu ikhale yovuta kwambiri. Hananiya anali mneneri wonyenga, ndipo ananena motsimikiza pamaso pa anthu m’dzina la Mulungu kuti goli la Ababulo lidzathyoledwa. Koma kudzera mwa Yeremiya, Yehova anauza Hananiya mneneri wonyengayo, kuti amwalira chaka chisanathe, ndipo zinachitikadi.—Yer. 28:1-3, 16, 17.

22 Tsopano anthu a m’dziko la Yuda anagawanika pawiri. Panali gulu la anthu amene ankafuna kuti mfumu yawo izigonjera Ababulo, ndipo gulu lina linkafuna kuti mfumuyo igalukire Ababulowo. Mu 609 B.C.E., Zedekiya anagalukiradi popempha asilikali a ku Iguputo kuti amuthandize kulimbana ndi Ababulo. Zimenezi zinachititsa kuti ntchito ya Yeremiya ikhale yovuta chifukwa anthu ambiri anayamba kukhala ndi mtima wokonda kwambiri dziko lawo, ndipo ankagwirizana ndi zogalukira Ababulo osati zimene Yeremiya ankalengeza. (Yer. 52:3; Ezek. 17:15) Kenako Nebukadinezara ndi asilikali ake anabwerera ku Yuda kuti akathane ndi anthu ogalukirawo, ndipo anagonjetsa mizinda yonse ya ku Yuda komanso anazungulira mzinda wa Yerusalemu kachiwiri. Pa nthawi yovutayi, Yeremiya anauza Zedekiya ndi anthu ake kuti mzinda wa Yerusalemu uwonongedwa ndi Ababulo. Iye ananenanso kuti anthu onse amene adzakhalebe mumzindawo adzafa, koma amene adzatuluke mumzindawo n’kupita kwa Akasidi, adzapulumuka.—Werengani Yeremiya 21:8-10; 52:4.

23 Akalonga a ku Yuda anayamba kunena kuti Yeremiya anali kazitape yemwe ankagwirizana ndi Ababulo. Iye atawauza zoona, akalongawo anam’menya ndi kumutsekera m’ndende. (Yer. 37:13-15) Komabe zimenezi sizinachititse Yeremiya kufewetsa uthenga wa Yehova. Motero akalongawo ananyengerera Zedekiya kuti Yeremiya aphedwe. Iwo anatenga mneneriyo n’kumuponyera m’chitsime chakuya chomwe munalibe madzi, koma munali matope okhaokha. Yeremiya akanafera m’chitsimechi akanapanda kupulumutsidwa ndi Ebedi-meleki, munthu wochokera ku Itiyopiya yemwe ankatumikira m’nyumba ya mfumu. (Yer. 38:4-13) M’nthawi yathu ino, anthu a Yehova ambirimbiri akumanapo ndi mavuto oopsa kwambiri ngati amenewa chifukwa chokana kulowerera ndale kapena nkhondo potsatira chikumbumtima chawo. Choncho, n’zoonekeratu kuti chitsanzo cha Yeremiya chingakuthandizeni kuti mukhale olimba komanso kuti muthe kupirira mavuto amene mungakumane nawo.

ZEDEKIYA, MFUMU YOMALIZA YA KU YUDA

Chithunzi patsamba 29

Zedekiya anali wolamulira wamantha, komanso wosachedwa kusintha maganizo ake n’kutengera maganizo a ena. Iye ankangoyendera maganizo a akalonga ake ndipo ankachita zinthu zambiri mwamantha. Ababulo atazungulira mzinda wa Yerusalemu komaliza, Zedekiya anakafunsira malangizo a Mulungu kwa Yeremiya. Komabe Zedekiya sanatsatire malangizowo atauzidwa kuti agonjere Ababulo, ndipo iye anaika m’ndende Yeremiya chifukwa anamuuza uthenga umene sunamusangalatse. (Yer. 21:1-9; 32:1-5) Ngakhale zinali choncho, mfumuyo inapitiriza kufunsira malangizo kwa Yeremiya, koma inkachita zimenezi mobisa poopa kukhumudwitsa akalonga a ku Yuda. Akalongawo atapempha kuti Yeremiya aphedwe, Zedekiya anayankha mwamantha kuti: “Iye ali m’manja mwanu. Palibe chimene ine mfumu ndingachite motsutsana nanu.” Yeremiya anapulumuka pa chiwembucho, ndipo kenako mfumuyo inakafunsanso malangizo kwa iye. Pa nthawiyi, Zedekiya anavomereza pamaso pa Yeremiya kuti ankaopa kuti akamvera Mulungu, anthu akhoza kumukhaulitsa.—Yer. 37:15-17; 38:4, 5, 14-19, 24-26.

Komabe, Zedekiya “sanadzichepetse pamaso pa mneneri Yeremiya . . . , ndipo anapitiriza kuumitsa khosi lake ndi mtima wake kuti asabwerere kwa Yehova.”—2 Mbiri 36:12, 13; Ezek. 21:25.

24. Fotokozani zimene zinachitika mu 607 B.C.E.

24 Mu 607 B.C.E., Ababulo anaboola mpanda wa Yerusalemu n’kulowa mumzindawo ndipo anaulanda. Asilikali a Nebukadinezara anatentha kachisi wa Yehova, anagwetsa mpanda wa mzindawo ndiponso anapha akuluakulu a ku Yuda. Ndiyeno Zedekiya anayamba kuthawa, koma Ababulo anam’gwira n’kumupereka kwa Nebukadinezara. Ana aamuna a Zedekiya anaphedwa iye akuona, ndipo kenako Nebukadinezara anavulaza Zedekiyayo m’maso n’kumuchititsa khungu. Atatero, anam’manga n’kupita naye ku Babulo. (Yer. 39:1-7) Apa ulosi umene Yeremiya ananena wokhudza Yuda ndi Yerusalemu unakwaniritsidwa. Koma m’malo mosangalala, mneneri wa Mulunguyu analira chifukwa cha tsoka limene linagwera anthu ake. Tikhoza kuwerenga mawu ake achisoni m’buku la m’Baibulo la Maliro. Tikamawerenga buku limeneli, tingakhudzidwe mtima kwambiri.

ANAPITIRIZA KUTUMIKIRA PAKATI PA AYUDA OTSALA

25, 26. (a) Yerusalemu atawonongedwa, kodi panachitika zinthu zotani? (b) Kodi Yerusalemu atawonongedwa, anthu a m’nthawi ya Yeremiya anachita chiyani atamva uthenga umene iye ankawauza?

25 Pamene zinthu zoopsazi zinkachitika, kodi zinthu zinkamuyendera bwanji Yeremiya? Akalonga a ku Yerusalemu anamuika m’ndende, koma Ababulo amene anagonjetsa mzindawo anamukomera mtima, moti anamutulutsa. Patapita nthawi, Yeremiya anapezeka pa gulu la Ayuda ena amene anagwidwa kuti apititsidwe ku ukapolo, koma kenako iye anamasulidwa. Mulungu ndi yemwe anachititsa zimenezi chifukwa panali ntchito yambiri yoti mneneriyu achite, monga kulalikira pakati pa anthu amene anatsala mu Yuda. Kenako Nebukadinezara anasankha Gedaliya kuti akhale bwanamkubwa wolamulira dziko limene anagonjetsalo, ndipo analonjeza Ayuda omwe anatsala kuti adzakhala mwamtendere ngati angapitirize kutumikira mfumu ya ku Babuloyo. Koma Ayuda ena, omwe sankasangalala ndi ulamulirowo, anapha Gedaliya. (Yer. 39:13, 14; 40:1-7; 41:2) Komabe Yeremiya analimbikitsa Ayuda amene anatsalawo kuti apitirize kukhala m’dzikolo ndipo asaope mfumu ya ku Babulo. Koma anthu omwe ankawatsogolera anayamba kunena kuti Yeremiya akunama ndipo iwo anathawira ku Iguputo. Popita kumeneko, iwo anatenga Yeremiya ndi Baruki mochita kuwakakamiza. Komabe, Yeremiya analosera kuti Nebukadinezara adzalowa m’dziko la Iguputo n’kuligonjetsa, ndipo Ayuda amene anathawira kumeneko adzakumana ndi tsoka.—Yer. 42:9-11; 43:1-11; 44:11-13.

26 Kachiwirinso, Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya anasankha kusamvera mneneri woona wa Mulunguyo. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Iwo ananena kuti: “Kuyambira pamene tinasiya kupereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa ‘mfumukazi yakumwamba,’ chilichonse chikutisowa, ndipo tawonongeka chifukwa cha lupanga ndi njala yaikulu.” (Yer. 44:16, 18) Mawu amenewa akungosonyeza kuti moyo wauzimu wa anthu a m’nthawi ya Yeremiyawo unafika poipa kwambiri. Mosiyana ndi zimenezi, n’zolimbikitsa kuona kuti munthu wopanda ungwiro angathe kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale atakhala pakati pa anthu osakhulupirika.

27. Kodi tikudziwa zotani zokhudza Yeremiya pa zaka zomalizira za moyo wake monga mneneri?

27 Nkhani yomaliza imene Yeremiya analemba, inachitika mu 580 B.C.E. Nkhani yake inali yokhudza Yehoyakini yemwe anamasulidwa m’ndende ndi Evili-merodaki, amene analowa m’malo mwa Nebukadinezara. (Yer. 52:31-34) Pa nthawiyi, Yeremiya ayenera kuti anali ndi zaka pafupifupi 90. Koma tilibe umboni wotsimikizirika wonena za mmene mneneriyu anafera. Zikuoneka kuti iye anakhala ku Iguputo pa zaka zomaliza za moyo wake ndipo anamwalirira komweko ali wokhulupirika, atatumikira Yehova mwapadera kwa zaka pafupifupi 67. Iye anatumikira Mulungu pa zaka zimene anthu ankalimbikitsa kulambira koona, komanso pa zaka zina zambiri pamene anthu ankalambira milungu yonyenga chifukwa cha ampatuko amene anali ponseponse. Komabe, iye anapeza anthu ena oopa Mulungu, omwe anamvetsera uthenga wake, ngakhale kuti anthu ambiri anakana, ndipo anafika pomuchitira nkhanza. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yeremiya analephera pa ntchito yake? Ayi. Chakumayambiriro kwenikweni kwa utumiki wake, Yehova anamuuza kuti: “Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzapambana, pakuti . . . ‘Ine ndili ndi iwe.’” (Yer. 1:19) Masiku ano, ntchito yathu monga Mboni za Yehova ndi yofanana ndi ya Yeremiya. Choncho tingayembekezere kuti anthu akamva uthenga wathu, adzachita zofanana ndi zimene anthu a m’nthawi ya Yeremiya anachita. (Werengani Mateyu 10:16-22.) Ndiyeno, kodi tingaphunzire zotani kwa Yeremiya, ndipo utumiki wathu tiyenera kuuona motani? Tiyeni tione mayankho a mafunso amenewa.

Kodi n’chiyani chinachitikira Zedekiya ndi anthu ake amene anakana kumvera uthenga wa Yeremiya? Kodi munganene chiyani za Yeremiya?

a Kufanana kwa lemba la Yeremiya 7:1-15 ndi la Yeremiya 26:1-6, kwachititsa anthu ena kuganiza kuti malembawa akufotokoza nkhani imodzi.

b Lemba la Danieli 1:1, 2 limanena kuti m’chaka chachitatu cha ulamuliro wa Yehoyakimu, mfumuyi inaperekedwa m’manja mwa Nebukadinezara, ndipo zikuoneka kuti chimenechi chinali chaka chachitatu cha ulamuliro wa Yehoyakimu pansi pa Ababulo. Zimenezi zingatanthauze kuti mfumuyi inamwalira pa nthawi imene asilikali a Babulo anazungulira mzinda wa Yerusalemu n’kuugonjetsa. Palibe umboni wa m’Baibulo wotsimikizira mfundo imene Josephus analemba yakuti Nebukadinezara anapha Yehoyakimu, ndipo mtembo wake sanauike m’manda koma anauponya kunja kwa mpanda wa Yerusalemu.—Yer. 22:18, 19; 36:30.

c Mwina anthu amene ankakopera Baibulo analakwitsa polemba dzina lakuti Yehoyakimu pa Yeremiya 27:1. Izi zili choncho chifukwa vesi 3 ndi 12 limatchula dzina la Zedekiya.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena