Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 March tsamba 7
  • Imfa ya Yesu Inathandiza Kuti Akufa Adzaukitsidwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Imfa ya Yesu Inathandiza Kuti Akufa Adzaukitsidwe
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Ngakhale Tilira, Sitili Opanda Chiyembekezo
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Njira Yokhayo Yothetsera Imfa
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Achibale Anu Ndi Anzanu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 March tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Imfa ya Yesu Inathandiza Kuti Akufa Adzaukitsidwe

Banja komanso achibale akulira chifukwa cha mtsikana amene wamwalira, mlongo amene waferedwa akuganizira za kuukitsidwa kwa akufa

Pamwambo wa Chikumbutso, timakhala ndi mwayi woganizira madalitso amene tidzapeze mtsogolo chifukwa cha dipo. Ena mwa madalitso amenewa ndi kuuka kwa akufa. Yehova sankafuna kuti anthu azifa. N’chifukwa chake anthufe zimatipweteka kwambiri wachibale kapena mnzathu akamwalira. (1 Akor. 15:26) Yesu anamva chisoni kwambiri ataona ophunzira ake akulira chifukwa cha imfa ya Lazaro. (Yoh. 11:33-35) Yesu amachita zinthu mofanana ndi Atate wake. Choncho sitingakayikire kuti Yehova nayenso zimam’pweteka akamationa tikulira chifukwa cha imfa ya wachibale kapena mnzathu. (Yoh. 14:7) Yehova akufunitsitsa kudzaukitsa atumiki ake amene anamwalira. Ifenso tiziyembekezera mwachidwi kuti akufa adzauka.—Yobu 14:14, 15.

Yehova ndi wadongosolo ndipo m’pomveka kunena kuti adzachita zinthu mwadongosolo poukitsa akufa. (1 Akor. 14:33, 40) N’kutheka kuti pa nthawiyo tizidzakhala ndi mwambo wolandira anthu oukitsidwa. Kodi timaganizira za kuuka kwa akufa makamaka pa nthawi yomwe wachibale kapena mnzathu wamwalira? (2 Akor. 4:17, 18) Kodi timathokoza Yehova chifukwa chopereka dipo komanso chifukwa chotidziwitsa kuti akufa adzauka?—Akol. 3:15.

  • Kodi ndi achibale kapena anzanu ati amene mumafunitsitsa kudzaonana nawonso?

  • Kodi ndi anthu ati otchulidwa m’Baibulo amene mumafunitsitsa kudzacheza nawo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena