CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 17-21
Yesetsani Kukhala Mwamtendere ndi Ena
Sikuti zimangochitika zokha kuti anthu a Yehova azikhala mwamtendere. Iwo akhoza kusemphana maganizo ndipo nthawi zina zimakhala zovuta kuti asakwiyirane. Koma malangizo a m’Baibulo amawathandiza kwambiri kuti akhazikitsenso mtendere.
Akhristu akasemphana maganizo amayesetsa kukhala mwamtendere ndipo . . .
amakhala odekha
amayesetsa kuti adziwe nkhani yonse asanachite chilichonse
amasonyeza chikondi pokhululukira munthu amene wawalakwira