Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 10/15 tsamba 32
  • Kulera Ana a Khalidwe labwino—Kodi Kudakali Kotheka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulera Ana a Khalidwe labwino—Kodi Kudakali Kotheka?
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 10/15 tsamba 32

Kulera Ana a Khalidwe labwino​—Kodi Kudakali Kotheka?

“TSOPANO tikukhala m’chitaganya chocholoŵana kwambiri, m’chikhalidwe chosanganikana kwambiri, mmene mulibe malamulo ogwirizana a khalidwe labwino,” akutero Robert Glossop wa pa Vanier Institute for the Family ku Ottawa, Canada. Chotsatirapo chake nchiyani? Lipoti la m’nyuzipepala ya The Toronto Star likuti: “Ana otenga mimba, achinyamata achiwawa ndi achinyamata odzipha okha onse akuwonjezeka.”

Vutolo silili mu North America mokha. Bill Damon, mkulu wa Center for Human Development pa Brown University ku Rhode Island, U.S.A., wafufuza mavutowa ku Britain ndi maiko ena a ku Ulaya, limodzinso ndi ku Australia, Israel, ndi Japan. Akutchula za kulephera kwa matchalitchi, masukulu, ndi mabungwe ena kuti apereke chitsogozo kwa achinyamata. Chikhalidwe chathu, iye amakhulupirira motero, “sichikudziŵa chilichonse ponena za zimene ana amafunikira kuti akhale ndi umunthu ndi mikhalidwe yabwino.” Pogwira mawu akatswiri a zakulera ana amene amaphunzitsa kuti “chilango chingawononge thanzi ndi ubwino wa ana,” Damon akunena kuti imeneyi ndiyo “njira yopangira ana kukhala odzigangira ndi osamva.”

Kodi achinyamata amakono amafunikira chiyani? Nthaŵi zonse amafunikira malangizo achikondi amene amawongolera maganizo ndi mtima. Achinyamata osiyanasiyana amafunikira mitundu yosiyanasiyana ya chilango. Ngati chilango chasonkhezeredwa ndi chikondi, nthaŵi zambiri chingaperekedwe mwa kukambitsirana. Ndiye chifukwa chake pa Miyambo 8:33 timauzidwa ‘kumva mwambo.’ Komatu ena “sangalangizidwe ndi mawu.” Kwa iwo, chilango choyenera pa kusamvera, choperekedwa moyenerera, chingafunikire. (Miyambo 17:10; 23:13, 14; 29:19) Poyamikira zimenezi, Baibulo silikuloleza kukwapula mokwiya kapena kumenya mopambanitsa, zimene zingachititse mikwingwirima kapena kuvulaza mwana. (Miyambo 16:32) M’malo mwake, mwana ayenera kudziŵa bwino chifukwa chake akuwongoleredwa ndi kuona kuti nchifukwa chakuti kholo lili kumbali yake.​—Yerekezerani ndi Ahebri 12:6, 11.

Uphungu wa m’Baibulo wogwira ntchito ndi wabwinowu ukufotokozedwa m’buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena