Nyimbo 95
“Talawani Ndipo Muone Kuti Yehova Ndi Wabwino”
Losindikizidwa
1. Kutumikira Mulungu
Kumatisangalatsadi.
Ntchito n’njambiri yolalikira
Timaipezera nthawi.
(KOLASI)
M’lungu akuti: ‘Talawani,
Inetu ndi wabwino’
Timapindula tikachita
Zonse zomwe tingathe.
2. Mtumiki wanthawi zonse
M’lungu amamudalitsa.
Amalandira zosowa zake
Amakhala wokhutira.
(KOLASI)
M’lungu akuti: ‘Talawani,
Inetu ndi wabwino’
Timapindula tikachita
Zonse zomwe tingathe.
(Onaninso Maliko 14:8; Luka 21:2; 1 Tim. 1:12; 6:6.)