Nyimbo 149
Tikukuthokozani Chifukwa cha Dipo
Lero tabweratu,
kwa inu Yehova,
Chifukwa munatisonyezadi
chikondi.
Munapereka Mwana,
wanu woyamba.
Monga nsembe yoposa ina
iliyonse.
(KOLASI)
Anafera anthu onse.
Kuti tidzapulumuke.
Tikuthokoza ndi mtima wonse,
Inu M’lungu.
Mofunitsitsa Yesu
anapereka.
Nsembe ya dipo moti
tikusangalala.
Asanabwere
kudzatipulumutsa.
Sitinkayembekezera,
moyo wosatha.
(KOLASI)
Anafera anthu onse.
Kuti tidzapulumuke.
Tikuthokoza ndi mtima wonse,
Inu M’lungu.
(Onaninso Aheb. 9:13, 14; 1 Pet. 1:18, 19.)