NYIMBO 28
Tikhale pa Ubwenzi Ndi Yehova
Losindikizidwa
1. Ndani angakhale
bwenzi lanu M’lungu?
Ndani mungam’khulupirire,
angakhale mnzanu?
Ndi onse amene
amakudziwani,
Amakukhulupirirani,
amakukondani.
2. Ndani angakhale
bwenzi lanu M’lungu?
Ndani angafike kumpando
wanu wachifumu?
Ndi onse amene
Amakumverani,
Olemekeza dzina lanu,
Okulambirani.
3. Timakuuzani
Zamumtima mwathu.
Mumakhala nafe pafupi
Mumatithandiza.
Tikufunitsitsa
Kukhala anzanu
Ndipo palibe bwenzi
Lomwe lingakuposeni.
(Onaninso Sal. 139:1; 1 Pet. 5:6, 7.)