NYIMBO 133
Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata
Losindikizidwa
1. Anyamata ndi atsikanafe
Ndife ofunika kwa Mulungu.
Tikamam’tumikira mwakhama
Azitidalitsa nthawi zonse.
2. Timasonyeza chikondi chathu
Tikamalemekeza makolo.
Anthu ndi M’lungu amatikonda
Ndipo timayandikira M’lungu.
3. Tizikumbukira M’lungu wathu.
Tikonde choonadi kwambiri.
Tikakhulupirika kwa iye
Tizisangalatsa mtima wake.
(Onaninso Sal. 71:17; Maliro 3:27; Aef. 6:1-3.)