Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya October 2018
OCTOBER 1-7
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 9-10
“Yesu Amasamalira Nkhosa Zake”
nwtsty zithunzi ndi mavidiyo
Khola la nkhosa
Khola la nkhosa linali malo omwe ankamangidwa kuti aziteteza nkhosa kwa akuba komanso zilombo zolusa. Abusa ankasunga nkhosa zawo m’makola amenewa usiku. Kale, makola a nkhosa ankakhala opanda denga ndipo ankakhala ooneka mosiyanasiyana. Nthawi zambiri ankamangidwa ndi miyala ndipo ankakhala ndi khomo limodzi. (Num. 32:16; 1 Sam. 24:3; Zef. 2:6) Yohane ananena kuti m’busa ankalowa m’khola “kudzera pakhomo” pomwe pankakhala “mlonda.” (Yoh. 10:1, 3) Pankakhalanso makola a mudzi wonse. M’makola amenewa munkatha kusungidwa nkhosa za anthu angapo ndipo mlonda ankayang’anira nkhosazo usiku wonse. Kukacha m’mawa, mlondayo ankatsegulira abusa kuti atenge nkhosa zawo. Abusawo ankaitana nkhosa zawo ndipo nkhosazo zinkazindikira mawu a m’busa wawo n’kumutsatira. (Yoh. 10:3-5) Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha zimene zinkachitikazi pofotokoza mmene ankasamalirira ophunzira ake.—Yoh. 10:7-14.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 10:16
kuzibweretsa: Kapena kuti “kutsogolera.” Mawu achigiriki akuti aʹgo omwe anagwiritsidwa ntchito palembali angamasuliridwe kuti “kubweretsa” kapena “kutsogolera” malingana ndi nkhani yake. Mumpukutu wina wachigiriki womwe unalembedwa cha m’ma 200 C.E. muli mawu achigiriki ofanana ndi amenewa (sy·naʹgo) omwe m’malo ambiri anawamasulira kuti “kusonkhanitsa.” Yesu yemwe ndi M’busa Wabwino amasonkhanitsa, kutsogolera, kuteteza komanso kudyetsa nkhosa zake za m’nkhola ili (zomwenso zimatchulidwa kuti “kagulu ka nkhosa” pa Luka 12:32) komanso nkhosa zina. Nkhosa zimenezi zimakhala gulu limodzi ndipo zimayang’aniridwa ndi m’busa mmodzi. Mfundo imeneyi ikutithandiza kumvetsa mgwirizano umene otsatira a Yesu amakhala nawo.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 9:38
anamugwadira: Kapena kuti “kuweramira; kupereka ulemu.” Mawu achigiriki akuti pro·sky·neʹo akagwiritsidwa ntchito potanthauza kulemekeza mulungu, nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “kulambira.” (Mat. 4:10; Luka 4:8) Choncho palembali, munthu amene poyamba anali wosaona uja anazindikira kuti Yesu anatumidwa ndi Mulungu ndipo anamugwadira. Sanachite zimenezi chifukwa choti ankamuona ngati Mulungu, koma ankangomulemekeza podziwa kuti Yesu ndi “Mwana wa munthu” komanso Mesiya yemwe Mulungu anamupatsa mphamvu. (Yoh. 9:35) Zimene anachitazi, zikufanana ndi zomwe anthu ena otchulidwa m’Malemba Achiheberi ankachita. Iwo ankawerama akakumana ndi aneneri, mafumu kapena anthu ena otumidwa ndi Mulungu. (1 Sam. 25:23, 24; 2 Sam. 14:4-7; 1 Maf. 1:16; 2 Maf. 4:36, 37) Malemba ambiri amasonyeza kuti anthu ankagwadira Yesu pothokoza kuti Mulungu wawathandiza kapena kuwachitira zinazake.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 10:22
chikondwerero cha kupereka kachisi kwa Mulungu: Dzina lachiheberi la chikondwererochi ndi Hanukkah (chanuk·kahʹ). Dzinali limatanthauza “kupereka kapena kutsegulira.” Chikondwererochi chinkachitika kwa masiku 8, kuyambira pa tsiku la 25 la mwezi wa Kisilevi, nyengo yozizira itangotsala pang’ono. (onani sdg mutu 19) Chikondwererochi chinkachitika pokumbukira mwambo woperekanso kachisi wa ku Yerusalemu womwe unachitika mu 165 B.C.E. Mfumu ya ku Siriya dzina lake Antiyokasi wa nambala 4 kapena kuti Epifanasi, ananyoza Yehova Mulungu wa Ayuda poipitsa kachisi. Mwachitsanzo, iye anamanga guwa lake pamwamba paguwa la nsembe lomwe Ayuda ankaperekapo nsembe zopsereza. Pa tsiku la 25 la mwezi wa Kisilevi m’chaka cha 168 B.C.E., Antiyokasi anapereka nsembe ya nkhumba paguwa ndipo kenako anawaza msuzi wa nkhumbayo m’kachisi monsemo pofuna kudetseratu kachisiyo. Iye anawotcha mageti apakachisi, kugumula zipinda za ansembe komanso anatenga guwa la nsembe la golide, tebulo la mkate wachionetsero ndiponso choikapo nyale chagolide. Kenako anapereka kachisi wa Yehovayu kwa mulungu wachikunja dzina lake Zeu wa ku Olympus. Patatha zaka ziwiri, Yuda Makabeo analanda mzinda wa Yerusalemu komanso kachisi. Atayeretsa kachisiyo anamuperekanso kwa Mulungu pa tsiku la 25 la mwezi wa Kisilevi mu 165 B.C.E. Pamenepo n’kuti patadutsa zaka zitatu kuchokera pamene Antiyokasi anadetsa kachisi popereka nsembe kwa Zeu. Kuchokera nthawi imeneyo anthu anayambiranso kupereka nsembe kwa Yehova. Baibulo silisonyeza kuti Yehova anapereka mphamvu kwa Yuda Makabeo kuti alande Yerusalemu n’kukonzanso kachisi. Yehova anagwiritsapo ntchito anthu a mitundu ina monga Koresi wa ku Perisiya kuti akwaniritse cholinga chake. (Yes. 45:1) Choncho n’zomveka kunena kuti Yehova akanatha kugwiritsira ntchito m’modzi mwa anthu ake pokwaniritsa cholinga chake. Malemba amasonyeza kuti kachisi ankayenera kupitirizabe kugwira ntchito n’cholinga choti maulosi okhudza Mesiya, utumiki wake komanso nsembe yomwe anapereka akwaniritsidwe. Komanso, ansembe achilevi ankayenera kupitirizabe kupereka nsembe pakachisi kufikira pamene Mesiya anapereka nsembe yoposa zonse, popereka moyo wake m’malo mwa anthu onse. (Dan. 9:27; Yoh. 2:17; Aheb. 9:11-14) Otsatira a Khristu sanalamulidwe kuti azichita chikondwerero chopereka kachisi kwa Mulungu. (Akol. 2:16, 17) Komabe palibe pamene pamasonyeza kuti Yesu analetsa otsatira ake kuchita chikondwererochi.
OCTOBER 8-14
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 11-12
“Muzitsanzira Yesu pa Nkhani Yochitira Ena Chifundo”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 11:24, 25
Ndikudziwa kuti adzauka: Malita ankaganiza kuti Yesu ankanena za kuukitsidwa kwa akufa kwam’tsogolo patsiku lomaliza. Chikhulupiriro cha Malita pa nkhaniyi chinali chochititsa chidwi kwambiri. Tikutero chifukwa atsogoleri ena achipembedzo pa nthawiyo otchedwa Asaduki, sankakhulupirira zoti akufa adzaukitsidwa. Iwo ankachita zimenezi ngakhale kuti Malemba ankafotokoza momveka bwino kuti akufa adzauka. (Dan. 12:13; Maliko 12:18) Pomwe Afarisi ankakhulupirira kuti mzimu wa munthu suufa. Malita ankadziwa kuti Yesu ankalalikira kuti akufa adzauka komanso anamuonapo ataukitsa anthu. Koma anali asanaonepo ataukitsa munthu amene anakhala m’manda nthawi yaitali ngati mmene zinalili ndi Lazaro.
Ine ndine kuuka ndi moyo: Imfa ya Yesu inapereka mwayi woti anthu amene anamwalira adzakhalenso ndi moyo. Yesu ataukitsidwa, Yehova anamupatsa mphamvu zoti adzaukitse akufa komanso kupereka moyo wosatha. Pa Chivumbulutso 1:18, Yesu ananena kuti iyeyo ndi “wamoyo” komanso kuti ali ndi “makiyi a imfa ndi a Manda.” Choncho Yesu amapereka chiyembekezo kwa anthu amoyo komanso akufa. Iye analonjeza kuti adzatsegula manda n’kuukitsa akufa kuti akalamulire naye limodzi kumwamba ndipo ena adzakhale padziko lapansi n’kumalamuliridwa ndi Ufumu wakumwamba.—Yoh. 5:28, 29; 2 Pet. 3:13.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 11:33-35
kulira: Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “kulira,” nthawi zambiri amatanthauza kulira kotulutsa mawu. Mawuwa ndi amenenso anagwiritsidwa ntchito ponena za Yesu pamene ankalosera za kuwonongedwa kwa Yerusalemu.—Luka 19:41.
anadzuma . . . ndi kumva chisoni: Kugwiritsa ntchito mawu awiriwa pavesili kumasonyeza mmene Yesu ankamvera mumtima mwake pa nthawiyi. Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “kudzuma” (em·bri·maʹo·mai) ndi mawu amene amasonyeza kumva kupweteka kwambiri mumtima. Vesili limasonyeza kuti Yesu anakhudzidwa kwambiri moti anadzuma. Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “kumva chisoni” (ta·rasʹso) kwenikweni amatanthauza kuwinduka. Katswiri wina ananena kuti mawuwa amatanthauza “kusokonezeka kwambiri kochokera mumtima kumene kumachititsa kuti munthu amve ululu woopsa.” Mawu omwewa ndi amenenso anagwiritsidwa ntchito pa Yoh. 13:21 pofotokoza mmene Yesu anamvera atazindikira kuti Yudasi akufuna kumupereka.
povutika mumtima: Mawu achigiriki akuti pneuʹma omwe anagwiritsidwa ntchito pavesili amatanthauza mphamvu yochokera mumtima imene imapangitsa munthu kuchita kapena kulankhula m’njira inayake.
anagwetsa misozi: Mawu achigiriki omwe anagwiritsidwa ntchito pamenepa (da·kryʹo) amatanthauza misozi ndipo ndi omwe anagwiritsidwanso ntchito pamalemba monga Luka 7:38; Mac. 20:19, 31; Aheb. 5:7; Chiv. 7:17; 21:4. Mawuwa amatsindika kwambiri mfundo yakuti Yesu anagwetsa misozi osati analira motulutsa mawu. M’Malemba Achigiriki, mawu achigirikiwa amapezeka pavesi lokhali ndipo ndi osiyana ndi amene anagwiritsidwa ntchito pa Yoh. 11:33, pomwe pamafotokoza kuti Mariya komanso Ayuda ena ankalira. Yesu ankadziwa kuti aukitsa Lazaro koma anakhudzidwa mtima ataona anzake apamtima akulirira m’bale wawo. Zimenezi zinamumvetsa chisoni kwambiri moti nayenso anagwetsa misozi pagulu. Nkhani imeneyi imatithandiza kudziwa kuti Yesu amakhudzidwa mtima kwambiri akamationa tikulira chifukwa choti abale athu amwalira.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 11:49
mkulu wa ansembe: Pa nthawi imene Aisiraeli ankadzilamulira okha, mkulu wa ansembe ankakhala pa udindowu kwa moyo wake wonse. (Numeri 35:25) Koma pa nthawi imene Aisiraeli ankalamulidwa ndi Aroma, mkulu wa ansembe ankasankhidwa ndi olamulira achiroma ndipo ankathanso kumuchotsa pa udindowu. Kayafa yemwe anasankhidwa ndi Aroma, anali wodziwa kulankhula ndipo anakhala paudindowu kwa nthawi yaitali kuposa anthu amene anasinthana nawo. Iye anaikidwa paudindowu cha m’ma 18 C.E. ndipo anakhalabe mkulu wa ansembe mpaka cha m’ma 36 C.E. Pamene Yohane analemba kuti Kayafa anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, chomwe ndi chaka cha 33 C.E., ankatanthauza kuti Kayafa ndi amene anali mkulu wa ansembe pa nthawi yosaiwalika imene Yesu anaphedwa.—Onani sgd mutu 16, kuti muone pamalo pamene payenera kuti panali nyumba ya Kayafa.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 12:42
olamulira: Pamenepa mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “olamulira” ayenera kuti amanena za oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda la Sanihedirini. Mawu amenewa amapezekanso pa Yoh. 3:1 ndipo amanena za Nikodemo yemwe anali mmodzi wa oweruza a khotili.
angawachotse musunagoge: Mawu achigiriki akuti a·po·sy·naʹgo·gos amapezeka pa malo awiri okha m’Baibulo. Malo ake ndi pa Yoh. 12:42 ndi pa Yoh. 16:2. Munthu amene wachotsedwa m’sunagoge ankasalidwa komanso ankaonedwa ngati wosafunika. Zimenezi zinkachititsa kuti Ayuda amene achotsedwa asamathandizidwe ndi ena ndipo ankakumana ndi mavuto azachuma. Masunagoge ankagwiritsidwa ntchito ngati masukulu, ndipo nthawi zina ankagwiritsidwa ntchito ngati makhoti ang’onoang’ono komwe munthu ankatha kuweruzidwa kuti akwapulidwe kapena kuchotsedwa musunagoge.
OCTOBER 15-21
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 13-14
“Ndakupatsani Chitsanzo”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 13:5
kusambitsa mapazi a ophunzira: Kale ku Isiraeli anthu ankavala masandasi. Masandasiwa ankangokhala ndi chapansi ndi zingwe, ndipo munthu amene wayenda mtunda wautali, mapazi ake ankatuwa ndi fumbi kapenanso kuda ndi matope. Chimenechi n’chifukwa chake munthu asanalowe m’nyumba ankafunika avule masandasi ake ndipo ngati mwininyumba ali wodziwa kuchereza, ankasambitsa mapazi a alendo ake. M’Baibulo muli zitsanzo zingapo zofotokoza mwambo umenewu. (Gen. 18:4, 5; 24:32; 1 Sam. 25:41; Luka 7:37, 38, 44) Pamene Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake, anagwiritsa ntchito mwambo umenewu pofuna kuwaphunzitsa kukhala odzichepetsa komanso kuti azitumikirana.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 13:12-14
muyenera: kapena kuti “ndi udindo wanu.” Mawu achigiriki amene anagwiritsidwa ntchito pamenepa kawirikawiri ankagwiritsidwa ntchito pankhani zandalama, makamaka ngati wina wakongola zinthu kapenanso ngati wakongoza wina zinthu. (Mat. 18:28, 30, 34; Luka 16:5, 7) Pa lembali komanso m’malo ena, mawuwa awagwiritsa ntchito m’njira yakuti munthuyo ali ndi udindo kapena kuti akuyenera kuchita zinazake.—Yobu 3:16; 4:11; 3 Yoh. 8.
Munthu Wamkulu Koposa Onse Anasonyeza Kudzichepetsa
Pamene Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake, anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kudzichepetsa. Kunena zoona Mkhristu aliyense ayenera kupewa kumadziona kuti ndi wofunika kwambiri n’kumangoyembekezera kuti ena azimuchitira zinthu. Sayeneranso kufuna udindo n’cholinga choti atchuke kapenanso kuti ena azimulemekeza. M’malomwake ayenera kutengera chitsanzo cha Yesu yemwe “sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Choncho otsatira a Yesu ayenera kukhala okonzeka kugwira ntchito zotsika pothandiza abale awo.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 14:6
Ine ndine njira, choonadi ndi moyo: Yesu ndi njira chifukwa anthu ayenera kudzera mwa iye kuti mapemphero awo akafike kwa Mulungu. Iyenso ndi “njira” chifukwa anathandiza kuti anthu onse agwirizanenso ndi Mulungu. (Yoh. 16:23; Aroma 5:8) Yesu ndi choonadi chifukwa ankalankhula komanso ankachita zinthu mogwirizana ndi choonadi. Anakwaniritsanso maulosi omwe malemba ananeneratu ndipo zimenezi zimasonyeza kuti anali ndi udindo wapadera pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. (Yoh. 1:14; Chiv. 19:10) Maulosi amenewa anakhala “‘inde’ [kapena kuti anakwaniritsidwa] kudzera mwa iye.” (2 Akor. 1:20) Yesu ndi moyo chifukwa dipo limene anapereka linathandiza kuti anthu adzapeze “moyo weniweniwo” kapena kuti “moyo wosatha.” (1 Tim. 6:12, 19; Aef. 1:7; 1 Yoh. 1:7) Iye adzakhalanso “moyo” kwa anthu mamiliyoni ambiri omwe adzaukitsidwe n’kukhala m’paradaiso padziko lapansili kwamuyaya.—Yoh. 5:28, 29.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 14:12
ntchito zazikulu kuposa zimenezi: Yesu sankanena kuti ophunzira ake adzachita zozizwitsa zambiri kuposa zimene iyeyo anachita. Koma m’malomwake ankadziwa kuti ophunzira akewo adzagwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu kuposa mmene iyeyo anachitira. Ophunzira ake akanalalikira dera lalikulu kwambiri, kwa anthu ambiri komanso kwa nthawi yaitali. Mawu a Yesuwa akusonyeza kuti ankafuna kuti ophunzira ake adzapitirize ntchito imene anayambitsayo.
OCTOBER 22-28
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 15-17
“Simuli Mbali ya Dzikoli”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 15:19
dziko: Palembali, mawu achigiriki akuti koʹsmos amatanthauza anthu onse omwe ali padzikoli, kupatulapo atumiki a Mulungu. Amenewa ndi anthu osalungama omwe ndi otalikirana ndi Mulungu. Yohane ndi wolemba Uthenga Wabwino yekhayo amene anagwira mawu a Yesu onena kuti otsatira ake sali mbali ya dziko. Mfundo imeneyi inatchulidwanso maulendo awiri m’pemphero limene Yesu anapempherera atumwi ake.—Yoh. 17:14, 16.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 15:21
chifukwa cha dzina langa: M’Baibulo, mawu akuti “dzina” amaimira munthuyo, mbiri yake komanso mmene anthu amamuonera. Ponena za Yesu, dzina lake likuimiranso mphamvu komanso udindo umene Atate wake anamupatsa. (Mat. 28:18; Afil. 2:9, 10; Aheb. 1:3, 4) Palembali Yesu anafotokoza chimene chimachititsa kuti anthu a m’dzikoli azidana ndi otsatira ake. Ananena kuti anthuwo amadana nawo chifukwa sadziwa amene anamutuma. Kudziwa Mulungu kukanawathandiza kumvetsa zimene dzina la Yesu linkaimira. (Mac. 4:12) Iwo akanadziwa udindo wa Yesu monga wolamulira wosankhidwa ndi Mulungu, Mfumu ya mafumu, yemwe anthu onse ayenera kumuweramira kuti adzapeze moyo wosatha.—Yoh. 17:3; Chiv. 19:11-16; yerekezeraninso ndi Sal. 2:7-12.
it-1 516
Kulimba Mtima
Akhristu ayenera kuchita zinthu molimba mtima kuti asatengere makhalidwe komanso zochita za anthu a m’dzikoli omwe ali paudani ndi Yehova Mulungu. Kulimba mtima kungawathandizenso kuti apitirize kukhala okhulupirika kwa iye ngakhale anthu ena akamawatsutsa. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.” (Yoh. 16:33) Yesu sanatengere zochita za anthu a m’dzikoli mpang’ono pomwe. Chitsanzo chake chabwino pa nkhani yogonjetsa dziko komanso madalitso amene anabwera chifukwa cha kukhulupirika kwake, zingatithandize kuchita zinthu molimba mtima kuti tisadetsedwe ndi dzikoli.—Yoh. 17:16.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 17:21-23
amodzi: Kapena kuti “ogwirizana.” Yesu anapempherera otsatira ake kuti akhale “amodzi” kuti azigwira ntchito mogwirizana monga mmene iyeyo ndi Atate wake alili “amodzi.” Zimenezi zikusonyeza kuti ayenera kuchita zinthu mogwirizana kwambiri ali ndi maganizo amodzi. (Yoh. 17:22) Pa 1 Akor. 3:6-9, Paulo anasonyeza mmene mgwirizano umenewu umakhalira pakati pa Akhristu akamagwira ntchito limodzi ndi anzawo komanso Mulungu.—Onani 1 Akor. 3:8.
akhale mu umodzi weniweni: Kapena kuti “akhale ogwirizana kwambiri.” M’vesili, Yesu anasonyeza kuti pali mgwirizano pakati pa kukhala ogwirizana ndi kukondedwa ndi Yehova. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene lemba la Akol. 3:14 limanena, lomwe limati: “Chikondi . . . chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” Mgwirizano umenewu ndi wapadera kwambiri. Zimenezi sizikutanthauza kuti anthuwo amakhala ndi makhalidwe, luso komanso zokonda zofanana. Koma zikutanthauza kuti otsatira a Yesu amakhala ogwirizana pa zimene amachita, amakhulupirira komanso zimene amaphunzitsa.—Aroma 15:5, 6; 1 Akor. 1:10; Aef. 4:3; Afil. 1:27.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 17:24
musanayale maziko a dziko: Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “musanayale maziko a dziko,” anamasuliridwa pa Aheb. 11:11 kuti “kubereka” ndipo amanena za kubereka “ana.” Zikuoneka kuti palembali mawu akuti ‘kuyala maziko a dziko,’ akunena za nthawi imene Adamu ndi Hava anayamba kubereka ana. Pamene Yesu ananena mawuwa ankanena za Abele yemwe anali munthu woyambirira woyenera kupulumutsidwa komanso amene dzina lake linali loyamba kulembedwa “mumpukutu wa moyo kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” (Luka 11:50, 51; Chiv. 17:8) Zimene Yesu ananena m’pempheroli zimasonyezanso kuti kuyambira kale kwambiri, Adamu ndi Hava asanayambe kubereka ana, Mulungu ankakonda kwambiri Mwana wake wobadwa yekha.
OCTOBER 29–NOVEMBER 4
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 18-19
“Yesu Anachitira Umboni Choonadi”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 18:37
kudzachitira umboni: Malinga ndi mmene mawuwa anawagwiritsira ntchito m’Malemba Achigiriki, mawu akuti “kuchitira umboni” (mar·ty·reʹo) komanso akuti “umboni” (mar·ty·riʹa; marʹtys) amatanthauza zambiri. Mawu awiri onsewa angatanthauze kuuza ena zimene ukudziwa komanso “kulengeza, kutsimikizira kapenanso kunena zabwino za chinachake.” Yesu ankachitira umboni ndiponso kulengeza choonadi chomwe ankachidziwa bwino ndipo zochita zake zinkasonyeza kuti maulosi komanso malonjezo a Atate wake ndi oona ndiponso olondola. (2 Akor. 1:20) Malemba ananeneratu mwatsatanetsatane za cholinga cha Mulungu chokhudza Ufumu komanso wolamulira wake yemwe ndi Mesiya. Zimene zinachitika pa moyo wa Yesu mpaka pamene anapereka moyo wake nsembe, zinakwaniritsa maulosi onse okhudza iyeyo kuphatikizapo zinthu zina za m’Chilamulo. (Akol. 2:16, 17; Aheb. 10:1) Choncho tinganene kuti zolankhula komanso zochita zake zimasonyeza kuti Yesu ‘ankachitira umboni choonadi.’
choonadi: Sikuti Yesu ankangonena za zinthu zolondola komanso zoona basi, koma ankanena za choonadi chokhudza cholinga cha Yehova. Mbali yaikulu ya cholinga cha Mulungu inali yoti Yesu, yemwe ndi “mwana wa Davide,” adzakhala Mkulu wa Ansembe komanso Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 1:1) Yesu anafotokoza kuti cholinga chachikulu chimene anabwerera padziko lapansi chinali kudzachitira umboni za Ufumu wa Mulungu. Angelo analengeza uthenga wofanana ndi umenewu Yesu asanabadwe komanso atabadwa ku Betelehemu wa ku Yudeya, mzinda umene Davide anabadwira.—Luka 1:32, 33; 2:10-14.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 18:38a
Choonadi n’chiyani? Zikuoneka kuti funso la Pilato linkanena za zinthu zolondola komanso zoona basi, osati “choonadi” chomwe Yesu anali atangochinena kumene. (Yoh. 18:37) Zikanakhala kuti Pilato anafunsa funsoli kuti adziwe yankho lake, Yesu akanamuyankha. Koma zikuoneka kuti Pilato sankafuna kuti ayankhidwe funsoli ndipo analifunsa monyoza ngati akunena kuti, “Choonadi ndiye chiyani? Padzikoli pangapezekenso choonadi!” Komanso Pilato sanayembekezere kuti Yesu amuyankhe moti anangonyamuka n’kupita kukakumana ndi Ayuda omwe anali panja.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 19:30
kupereka mzimu wake: Kapena kuti “kutsirizika, kusiya kupuma.” Mawu akuti “mzimu” (m’Chigiriki, pneuʹma) omwe ali palembali angatanthauze “kupuma” kapena “mphamvu yomwe imachititsa kuti munthu akhale ndi moyo.” Mfundo imeneyi ndi yoona chifukwa pamalemba ena omwe amakamba nkhani yomweyi, anagwiritsa ntchito mawu achigiriki akuti ek·pneʹo (omwe amamasuliridwa kuti “kupuma”) pa Maliko 15:37 komanso pa Luka 23:46 (pomwe anawamasulira kuti “kutsirizika”). Anthu ena amanena kuti mawu achigiriki omwe anawamasulira palembali kuti “kupereka” amatanthauza kuti Yesu anasiya kudzilimbitsa kuti akhalebe ndi moyo, popeza zinthu zonse zinali zitakwaniritsidwa. Iye “anakhuthula moyo wake mu imfa” mofunitsitsa kwambiri.—Yes. 53:12; Yoh. 10:11.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 19:31
Sabata la tsiku limeneli linali lalikulu: Tsiku la 15 la mwezi wa Nisani, linkabwera pambuyo pa Pasika ndipo nthawi zonse linkakhala tsiku la sabata mosasamala kanthu kuti ndi tsiku lanji pa mlungu. (Lev. 23:5-7) Ndiye Sabata lapaderali likafika pa tsiku lasabata (lomwe ndi tsiku la 7 pa mlungu wa Ayuda, womwe unkayamba Lachisanu dzuwa likangolowa mpaka Loweruka dzuwa likamalowa), linkakhala Sabata “lalikulu.” Tsiku lasabata ngati limeneli linatsatana ndi tsiku limene Yesu anafa, lomwe linali Lachisanu. Kungochokera mu 29 mpaka mu 35 C.E., chaka chokhacho chimene tsiku la Nisani 14 linali Lachisanu chinali cha 33 C.E. Umboni umenewu ukusonyeza kuti Yesu ayenera kuti anafa pa Nisani 14 mu 33 C.E.