Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
DECEMBER 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 9-11
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 10:6
Simoni, wofufuta zikopa: Munthu wofufuta zikopa ankagwiritsa ntchito laimu pochotsa ubweya kapenanso mafuta pa zikopa za nyama. Kenako ankapaka mowa pachikopapo kuti chisalale ndipo akatero ankatha kuchigwiritsa ntchito popanga zinthu zosiyanasiyana. Pogwira ntchitoyi pankakhala fungo loipa moti pankafunika kuti pakhale madzi ambiri. N’kutheka kuti n’chifukwa chake Simoni ankakhala m’mbali mwa nyanja, mwina chakumapeto kwa mzinda wa Yopa. Malinga ndi Chilamulo cha Mose, munthu amene ankagwira nyama yakufa ankaonedwa kukhala wodetsedwa. (Lev. 5:2; 11:39) Choncho Ayuda ambiri ankasala anthu ofufuta zikopa moti sankafuna ngakhale kukagona kunyumba kwawo. Buku lina lotchedwa Talmud linanena kuti ntchito yofufuta zikopa inali yotsika poyerekezera ndi ntchito yochotsa ndowe. Komabe Petulo sanalole kuti tsankho limulepheretse kukakhala kunyumba kwa Simoni. Zimene anachitazi zinachititsa kuti asavutike kulandira utumiki umene anapatsidwa wopita kunyumba kwa munthu wina wachikunja. Akatswiri ena amati mawu Achigiriki omwe anawamasulira kuti “wofufuta zikopa,” (byr·seusʹ) linali dzina la bambo ake a Simoni.
DECEMBER 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 12-14
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 13:9
Saulo, wotchedwanso Paulo: Kungochokera pa nthawi imeneyi, Saulo anayamba kutchulidwa kuti Paulo. Mtumwiyu anabadwira m’banja lachiheberi lomwe linali nzika za Roma. (Mac. 22:27, 28; Afil. 3:5) Choncho n’zoonekeratu kuti kungochokera ali mwana, iye ankadziwika ndi dzina lachiheberi lakuti Saulo komanso lachiroma lakuti Paulo. Sizinali zachilendo pa nthawiyo, makamaka kwa Ayuda amene ankakhala kunja kwa Isiraeli, kuti munthu azidziwika ndi mayina awiri. (Mac. 12:12; 13:1) Zikuoneka kuti ena mwa abale ake a Paulo anali ndi mayina achiroma komanso achigiriki. (Aroma 16:7, 21) Monga mtumwi “wotumidwa kwa mitundu ina” Paulo ankafunika kukalengeza uthenga wabwino kwa anthu a mitundu ina. (Aroma 11:13) Choncho iye anaganiza zogwiritsa ntchito dzina lake lachiroma chifukwa ankaona kuti likhala lovomerezeka kwa anthu ambiri. (Mac. 9:15; Agal. 2:7, 8) Anthu ena amanena kuti n’kutheka kuti Paulo anasankha kugwiritsa ntchito dzinali pofuna kulemekeza Serigio Paulo. Koma zimenezi si zomveka chifukwa iye anapitirizabe kugwiritsa ntchito dzinali atachoka ku Kupuro. Pomwe ena amanena kuti Paulo sankafuna kugwiritsa ntchito dzina lachiheberi chifukwa katchulidwe ka dzinali m’chigiriki kankamveka mofanana ndi liwu lina lachigiriki lomwe linkanena za munthu (kapena nyama) amene amayenda moyerekedwa kapena modzimva.
Paulo: M’Malemba Achigiriki, dzina lakuti Pauʹlos, lomwe m’chilatini ndi Paulus, limatanthauza “Chaching’ono; Chochepa.” Dzinali limapezeka maulendo 157 ponena za Paulo ndipo malo amodzi limanena za bwanamkubwa wa Kupuro dzina lake Serigio Paulo.—Mac. 13:7.
DECEMBER 17-23
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 15-16
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 16:37
ndife Aroma: Kapena kuti nzika za Roma. Zikuoneka kuti nayenso Sila anali nzika ya Roma. Malamulo a Aroma ankanena kuti nzika zake ziyenera kuweruzidwa bwinobwino komanso munthu sankayenera kupatsidwa chilango pagulu mlandu wake usanaweruzidwe. Kukhala nzika ya Roma kunkapatsa munthu maufulu ena apadera komanso ankatha kuchitiridwa zinthu m’njira yapadera kulikonse kumene angapite mu ufumu wa Roma. Nzika ya Roma inkayenera kumatsatira malamulo achiroma, osati malamulo a kudera limene akukhala. Akamaimbidwa mlandu, iye ankakhala ndi mwayi wosankha kuweruzidwa ndi khoti lam’deralo. Komabe akafuna, iye ankatha kupempha kuti akufuna kukaweruzidwa ndi khoti lachiroma. Ngati wapalamula mlandu waukulu kwambiri, iye ankakhalabe ndi ufulu wochita apilo kwa Kaisara. Mtumwi Paulo analalikira kwambiri m’chigawo chomwe chinkalamuliridwa ndi ufumu wa Roma. M’Baibulo muli malo atatu omwe Paulo anagwiritsa ntchito ufulu wake monga nzika ya Roma podziteteza. Ulendo woyamba kunali ku Filipi pamene anauza woweruza milandu wa m’derali kuti waphwanya ufulu wake pomukwapula.
DECEMBER 24-30
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 17-18
“Muzitsanzira Mtumwi Paulo pa Nkhani Yolalikira Komanso Kuphunzitsa”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 17:2, 3
anakambirana: Sikuti Paulo ankangowauza uthenga wabwino. Iye ankafotokoza komanso kupereka umboni wochokera m’Malemba, omwe ndi Malemba ouziridwa achiheberi. Iye ankachita zambiri osati kungowerenga Malemba. Ankakambirana nawo komanso kufotokoza mfundo zogwirizana ndi anthu amene ankawalalikira. Mawu achigiriki akuti di·a·leʹgo·mai angatanthauze “kukambirana, kuyankhulana kapena kucheza.” Choncho mawu omwe anagwiritsidwa ntchito pavesili amatanthauza kuyankhulana ndi anthu. Mawu achigiriki amenewa anagwiritsidwanso ntchito pa Mac. 17:17; 18:4, 19; 19:8, 9; 20:7, 9.
kusonyeza umboni wolembedwa: M’chigiriki, mawu ake enieni amatanthauza “kuika pambali.” Zimenezi zikusonyeza kuti Paulo ankayerekezera mosamala kwambiri maulosi a Mesiya omwe analembedwa m’Malemba Achiheberi ndi zimene zinachitika pamoyo wa Yesu n’kuwasonyeza anthu mmene Yesu anakwaniritsira maulosiwo.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 17:17
pamsika: Msika umenewu unali kumpoto chakum’mwera kwa tauni ya Atene (m’Chigiriki, a·go·raʹ) ndipo unali waukulu maekala 12 kapena kuposa. Msika unkagwira ntchito zambiri osati kokha ngati malo ogula komanso kugulitsa zinthu. Unali paphata pa zamalonda, zandale komanso zachikhalidwe. Anthu a ku Atene ankakonda kukumana malo amodzi kumisika n’kumakambirana zinthu zosiyanasiyana.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 17:22, 23
Kwa Mulungu Wosadziwika: Mawu achigiriki akuti A·gnoʹstoi the·oiʹ anali ena mwa mawu omwe analembedwa pa guwa lansembe lina ku Atene. Anthu a ku Atene ankalambira milungu yosiyanasiyana ndipo ankamanga akachisi komanso maguwa ansembe ambirimbiri ngakhalenso kwa milungu yomwe sankatha kuiona monga mulungu wa kutchuka, wa kudzichepetsa, wa mphamvu, wa chilimbikitso komanso wa chisoni. Chifukwa chakuti anthuwa ankaopa kukhumudwitsa mulungu wina chifukwa chomuiwala, anamanga guwa lansembe “Kwa Mulungu Wosadziwika.” Pomanga guwa limeneli, anthuwo ankaona kuti akusangalatsa mulungu wina yemwe sankamudziwa. Paulo anagwiritsa ntchito guwa lansembe limeneli ngati njira yoyambira kukambirana ndi anthuwo za Mulungu woona, yemwe tinganene kuti kufikira pa nthawiyo anthuwo anali asanamudziwebe.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 18:21
Yehova akalola: Mawu amenewa amasonyeza kufunika koika zofuna za Yehova pamalo oyamba tikamachita zinthu kapena tikamakonza mapulani athu. Mtumwi Paulo ankazindikira mfundo imeneyi. (1 Akor. 4:19; 16:7; Aheb. 6:3) Nayenso mtumwi Yakobo anauza Akhristu anzake kuti: “Yehova akalola, tikhala ndi moyo, ndi kuchita zakutizakuti.” (Yak. 4:15) Mawu amenewa sayenera kumangonenedwa ndi pakamwa basi. Munthu amene wanena kuti “Yehova akalola,” ayenera kuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Yehovayo. Sikuti nthawi zonse timayenera kuyankhula mawuwa. Nthawi zambiri mawu amenewa timawanena mumtima.