Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr19 January tsamba 1-3
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya January 2019

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya January 2019
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
  • Timitu
  • JANUARY 7-13
  • JANUARY 14-20
  • JANUARY 21-27
  • JANUARY 28–​FEBRUARY 3
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
mwbr19 January tsamba 1-3

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

JANUARY 7-13

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 21-22

“Chifuniro cha Yehova Chichitike”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 22:16

kusamba kuti uchotse machimo ako mwa kuitana pa dzina lake: Kapena “kusamba kuti uchotse machimo ako ndi kuitana pa dzina lake.” Machimo a munthu amachotsedwa osati chifukwa cha madzi a ubatizo koma chifukwa choitanira pa dzina la Yesu. Machimowo angachotsedwe ngati atamakhulupirira Yesu komanso kuchita ntchito zosonyeza kuti amamukhulupirira.​—Mac. 10:43; Yak. 2:14, 18.

JANUARY 14-20

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 23-24

“Anaimbidwa Mlandu Wosokoneza Anthu Komanso Kuukira Boma”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 23:6

ine ndine Mfarisi: Ena mwa anthu amene ankamvetsera Paulo, ankamudziwa bwino. (Mac. 22:5) Iwo ayenera anaganiza kuti pamene iye ankadzinena kuti ndi mwana wa Afarisi, ankafuna kusonyeza kuti nayenso anali Mfarisi. Iwo ankaona kuti Paulo akunena zoona chifukwa Afarisi omwe anali m’Khoti Lalikulu la Ayuda ankadziwa kuti anachita kusintha n’kukhala Mkhristu wodzipereka kwambiri. Komabe, zimene Paulo ananena pa nthawiyi zoti anali Mfarisi zingakhalenso ndi tanthauzo lina. Iye anadzitchula kuti anali Mfarisi osati Msaduki chifukwa chakuti ankakhulupirira zofanana ndi Afarisi pa nkhani ya kuukitsidwa kwa akufa. Pamenepa tingati anayambitsa nkhani imene Afarisi omwe anali pamalowo ankaidziwa bwino. Ankaona kuti kuyambitsa nkhaniyi kukanachititsa kuti anthu ena, omwe anali m’khotili, akhale kumbali yake ndipo zimenezi zinachitikadi. (Mac. 23:7-9) Mawu a Paulo amenewa opezeka pa Mac. 23:6, amafanana ndi amene anagwiritsa ntchito podziteteza pamene ankalankhulana ndi Mfumu Agiripa. (Mac. 26:5) Ndiponso pamene anali ku Roma, pomwe ankalemba kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Filipi, ananenanso kuti anali Mfarisi. (Afil. 3:5) Pa Mac. 15:5, pamafotokozanso za Akhristu ena omwe poyamba anali Afarisi.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 24:24

Durusila: Anali wamng’ono pa ana atatu aakazi a Herode wotchulidwa pa Mac. 12:1, amene ndi Herode Agiripa Woyamba. Iye anabadwa cha m’ma 38 C.E. ndipo anali mlongo wake wa Agiripa Wachiwiri komanso mng’ono wake wa Berenike. Bwanamkubwa Felike anali mwamuna wake wachiwiri. Mwamuna wake woyamba anali mfumu ya Asiriya dzina lake Azizus wa ku Emesa. Durusila anathetsa banja lake n’kukwatiwa ndi Felike cha m’ma 54 C.E., ndipo zikuoneka kuti pa nthawiyi anali ndi zaka 16 zokha. N’kutheka kuti Durusila analipo pamene Paulo ankalankhula ndi Felike “za chilungamo, za kudziletsa, ndi za chiweruzo chimene chikudzacho.” (Mac. 24:25) Pamene Felike anapereka udindo wake monga bwanamkubwa kwa Fesito, iye anasiya Paulo m’ndende n’cholinga choti “Ayuda azimukonda.” Ena amaganiza kuti anachita zimenezi pofuna kusangalatsa mkazi wake wachitsikanayu, yemwe anali Myuda.​—Mac. 24:27.

JANUARY 21-27

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 25-26

“Paulo Anapempha Kukaonekera kwa Kaisara Ndipo Kenako Analalikira Mfumu Herode Agiripa”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 26:14

nyama imene ikuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosera: Chisonga chotosera inali ndodo yosongoka yomwe ankatosera nyama ikamalowera kolakwika. (Ower. 3:31) Mawu akuti “nyama imene ikuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosera” unali mwambi wachigiriki. Mwambiwu umanena za ng’ombe yomwe ikuchita makani n’kumamenya chotosera, zomwe zingachititse kuti ivulale kwambiri. Saulo ankachita zofanana ndi zimenezi asanakhale Mkhristu. Pamene ankalimbana ndi otsatira a Yesu, omwe Yehova Mulungu ankawateteza, Paulo ankangodzipweteka yekha. (Yerekezerani ndi Mac. 5:38, 39; 1 Tim. 1:13, 14.) Pa Mlal. 12:11, “zisonga zobayira” zimatchulidwa mophiphiritsa, kutanthauza mawu a munthu wanzeru omwe amathandiza munthu wina kumvera malangizo.

nwt matanthauzo a mawu ena

Chisonga chotosera. Inali ndodo yaitali yosongoka yomwe alimi ankagwiritsa ntchito pobweza nyama yomwe ikulowera kolakwika. Zisonga zotosera zimayerekezedwa ndi mawu a munthu wanzeru omwe amathandiza munthu wina kumvera malangizo. “Kuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosera” ndi mawu omwe anachokera pa zimene ng’ombe yamakani imachita ikamamenya chotosera, zomwe zingachititse kuti ivulale kwambiri.​—Mac. 26:14; Ower. 3:31.

JANUARY 28–​FEBRUARY 3

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 27-28

“Paulo Anapita ku Roma”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 27:9

kusala kudya kwa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo: Kapena kuti “kusala kudya.” Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “kusala kudya” amanena za lamulo la kusala kudya lomwe linali m’Chilamulo cha Mose. Kusala kudyaku kunkachitika chaka ndi chaka pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, lomwenso linkatchulidwa kuti Yom Kippur (m’Chiheberi, yohm hak·kip·pu·rimʹ, kutanthauza “tsiku lophimba machimo”). (Lev. 16:29-31; 23:26-32; Num. 29:7) Mawu akuti “muzidzisautsa” omwe ankawagwiritsa ntchito ponena za Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, angatanthauzenso kusala chakudya ndiponso kudzimana zinthu zina. (Lev. 16:29, mawu a m’munsi.) Kugwiritsidwa ntchito kwa mawu akuti “kusala kudya” pa Mac. 27:9, kumasonyeza kuti chinthu chachikulu chimene anthu ankachita posonyeza kudzimana pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo chinali kusala kudya. Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo linkakhala kumapeto kwa mwezi wa September kapena kumayambiriro kwa October.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 28:11

Ana . . . a Zeu: Malinga ndi zimene Agiriki komanso Aroma akale ankakhulupirira, “Ana . . . a Zeu” (m’Chigiriki, Di·oʹskou·roi) anali Kasitolo ndi Polakisi ndipo anali ana amapasa a mulungu wotchedwa Zeu (Jupita) omwe anabereka ndi mkazi wake wa ku Sparta, dzina lake Leda. Anthu ankatenga ana a Zeu ngati milungu yoteteza anthu oyenda maulendo apanyanja. Mfundo imeneyi yonena za chizindikiro chomwe chinali kutsogolo kwa ngalawa yomwe Paulo anakwera ndi umboni wakuti nkhaniyi inalembedwa ndi munthu wina yemwe anaona ndi maso zochitikazi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena