Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
FEBRUARY 25–MARCH 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 9-11
“Fanizo la Mtengo wa Maolivi”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 1260 ¶2
Nsanje
Kudzipereka Kosayenera. Munthu akhoza kukhala wodzipereka ndi mtima wonse pochita zinazake n’kupezeka kuti akuchita zosayenera komanso sakusangalatsa Mulungu. Umu ndi mmene zinalili ndi Ayuda a m’nthawi ya Atumwi. Iwo ankaganiza kuti akhoza kukhala olungama ngati atamatsatira kwambiri Chilamulo cha Mose. Koma Paulo anasonyeza kuti kudzipereka kwawo kunali kosayenera chifukwa sankadziwa zinthu zolondola. Choncho sanalandire chilungamo chenicheni chochokera kwa Mulungu. Iwo ankafunika kuti azindikire zolakwa zawo, n’kutembenukira kwa Mulungu kudzera mwa Khristu kuti alandire chilungamo komanso ufulu n’kumasuka ku Chilamulo. (Aroma 10:1-10) Saulo wa ku Tariso anali wodzipereka kwambiri ku Chiyuda mpaka anafika ‘pozunza kwambiri mpingo wa Mulungu ndi kupitirizabe kuuwononga.’ Iye ankatsatira kwambiri Chilamulo n’kumadziona monga ‘wopanda chifukwa chomunenezera.’ (Agal. 1:13, 14; Afil. 3:6) Komatu kumeneku kunali kudzipereka kosayenera. Komabe iye anali ndi mtima wabwino ndipo Yehova anamusonyeza kukoma mtima kwakukulu kudzera mwa Khristu pomuthandiza kuti ayambe kumulambira m’njira yoyenera.—1 Tim. 1:12, 13.