Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr19 March tsamba 1
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2019

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2019
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
  • Timitu
  • MARCH 4-10
  • MARCH 11-17
  • MARCH 18-24
  • MARCH 25-31
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
mwbr19 March tsamba 1

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

MARCH 4-10

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 12-14

“Mmene Tingasonyezere Chikondi Chachikhristu”

it-1 55

Chikondi

Mkhristu aliyense mumpingo ayenera kukonda abale [m’Chigiriki, phi·la·del·phiʹa kutanthauza “kukonda m’bale wako”]. (Aroma 12:10; Aheb. 13:1; onaninso 1 Pet. 3:8.) Choncho, anthu onse mumpingo ayenera kumakondana komanso kumagwirizana kwambiri ngati anthu apachibale. Ngakhale zitakhala kuti abale ndi alongo amasonyezana kale chikondi chimenechi, ayenera kuchita zimenezo mowonjezereka.​—1 Ates. 4:9, 10.

Mawu achigiriki akuti phi·loʹstor·gos, omwe amatanthauza “chikondi chenicheni,” amanena za munthu yemwe amagwirizana kwambiri ndi mnzake. Mawuwa anapangidwa kuchokera ku mawu akuti sterʹgo, omwe amakonda kugwiritsidwa ntchito ponena za chi­kondi chachibadwa chomwe anthu apachibale amasonyezana. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti azisonyezana chikondi chimenechi. (Aroma 12:10) Paulo anasonyezanso kuti m’masiku otsiriza anthu adzakhala “osakonda achibale awo” (m’Chigiriki aʹstor·goi) ndipo anthu amenewa ndi oyenerera imfa.​—2 Tim. 3:3; Aroma 1:31, 32.

MARCH 11-17

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 15-16

“Muzidalira Yehova Kuti Akulimbikitseni Komanso Kukuthandizani Kupirira”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

w89 12/1 24 ¶3

Mungadziwe Bwanji Ngati “Chikondi Chanu Chilidi Chenicheni”?

Zinali zoyenera kuti Akhristu a mitundu ina athandize Akhristu achiyuda omwe anali pamavuto. Anthu amenewa anamva uthenga wabwino kuchokera kwa Akhristu a ku Yerusalemu, choncho zinali ngati anali nawo “ngongole.” Poganizira mfundo imeneyi, Paulo anati: “Ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti anthu a mitundu inawo ayeneranso kutumikira oyera amenewa mwa kuwapatsa zinthu zofunika pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.”—Aroma 15:27.

it-1 858 ¶5

Kudziwiratu Zam’tsogolo, Kusankhiratu

Mesiya, kapena kuti Khristu, anali Mbewu yolonjezedwa yomwe ikanadzathandiza kuti Mulungu adalitse anthu olungama ochokera m’mitundu yonse. (Agal. 3:8, 14) “Mbewu” imeneyi inatchulidwa koyamba Adamu ndi Hava atangochimwa, koma Abele asanabadwe. (Gen. 3:15) Kuchokera nthawi imeneyi, panadutsa zaka 4,000 kuti Mulungu athandize anthu kudziwa kuti “mbewu” yomwe inatchulidwa mu “chinsinsi chopatulika” chimenechi ndi Mesiya. Choncho tingati chinsinsichi ‘chinakhala chobisika kuyambira nthawi zakale.’​—Aroma 16:25-27; Aef. 1:8-10; 3:4-11.

MARCH 18-24

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 1-3

“Kodi Ndinu Munthu Wakuthupi Kapena Munthu Wauzimu?”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 1193 ¶1

Nzeru

Anthu omwe ankadziona ngati anzeru, anakana mwayi womwe Mulungu anapereka kudzera mwa Khristu ndipo ankaona nkhani imeneyi ngati chinthu chopusa. Olamulira komanso oweruza awo, omwe ankaoneka ozindikira, anafika ‘popachika Ambuye waulemerero.’ (1 Akor. 1:18; 2:7, 8) Zimenezi zinachitika chifukwa Mulungu ankafuna kusonyeza kuti nzeru za anthu a m’dzikoli ndi zopusa ndipo anawachititsa manyazi pogwiritsa ntchito zimene ankaona kuti ndi “chinthu chopusa cha Mulungu.” Anagwiritsanso ntchito anthu ooneka ngati ‘opusa, ofooka komanso onyozeka’ kuti akwaniritse cholinga chake. (1 Akor. 1:19-28) Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Korinto kuti amene amatsatira “nzeru ya nthawi ino [komanso] ya olamulira a nthawi ino” adzawonongedwa. Chimenechi n’chifukwa chake mu uthenga wake sankalimbikitsa anthu kufufuza nzeru zam’dzikoli. (1 Akor. 2:6, 13) Iye anachenjeza Akhristu a ku Kolose kuti asamale kuti wina asawagwire ngati nyama pogwiritsa ntchito “nzeru za anthu [m’Chigiriki, phi·lo·so·phiʹas, kutanthauza kukonda kwambiri nzeru] ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.”​—Akol. 2:8; yerekezerani ndi vesi 20-23.

MARCH 25-31

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 4-6

“Chofufumitsa Chaching’ono Chimafufumitsa Mtanda Wonse”

it-2 230

Chofufumitsa

Nayenso mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito fanizo lomweli pamene ankauza Akhristu a ku Korinto kuti achotse munthu wina yemwe ankachita chiwerewere. Iye anati: “Kodi simukudziwa kuti chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa mtanda wonse? Chotsani chofufumitsa chakalecho, kuti mukhale mtanda watsopano, popeza ndinu opanda chofufumitsa.” Kenako anawafotokozera chimene ankatanthauza ponena za “chofufumitsa.” Anati: “Chotero tiyeni tichite chikondwererochi, osati ndi chofufumitsa chakale, kapena chofufumitsa choimira zoipa ndi uchimo, koma ndi mikate yopanda chofufumitsa yoimira kuona mtima ndi choonadi.” (1 Akor. 5:6-8) Apa Paulo ankanena zimene zinkachitika pa Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa, chomwe chinkayamba Pasika akangotha. Mofanana ndi mmene chofufumitsa chinkachititsira kuti mtanda wonse ufufume, Yehova akanaona kuti mpingo wonsewo ndi wodetsedwa akanapanda kuchotsa munthu wachiwerewereyo. Kuti zimenezi zisachitike, Akhristuwa ankafunika kuchotsa “chofufumitsa” mumpingomo, mofanana ndi mmene Aisiraeli ankachitira akamachotsa chofufumitsa chilichonse m’nyumba zawo pa nthawi ya chikondwerero chija.

it-2 869-870

Satana

Kodi mawu akuti “mupereke munthu ameneyu kwa Satana kuti thupilo liwonongedwe” amatanthauza chiyani?

Pamene ankauza akulu a mpingo wa ku Korinto kuti apereke chilango kwa munthu wina woipa, yemwe ankachita chiwerewere ndi mkazi wa bambo ake, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mupereke munthu ameneyu kwa Satana kuti thupilo liwonongedwe.” (1 Akor. 5:5) Iye ankawauza kuti achotse munthuyo mumpingo ndipo mpingo wonse unkafunika kusiyiratu kucheza naye. (1 Akor. 5:13) Kumupereka kwa Satana kukanachititsa kuti asakhalenso mumpingo ndipo akanakhala mbali ya Satana yemwe ndi mulungu komanso wolamulira wa dzikoli. Mofanana ndi mmene “chofufumitsa chaching’ono” chinkafufumitsira “mtanda” wonse wa mkate, munthu wachiwerewereyu yemwe tingati ndi “thupi,” kapena kuti munthu wakuthupi, akanadetsa mpingo wonse. Choncho kumuchotsa mumpingo kukanakhala ngati kuwononga “thupi” lomwe linali pakati pawo. (1 Akor. 5:6, 7) Mofanana ndi munthu ameneyu, Paulo anapereka Hemenayo ndi Alekizanda kwa Satana chifukwa anakankhira kumbali chikhulupiriro ndi chikumbumtima choyera, moti chikhulupiriro chawo chinasweka ngati ngalawa.​—1 Tim. 1:20.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 211

Lamulo

Chilamulo cha Angelo. Angelo, omwe ndi apamwamba kuposa anthu, amamvera chilamulo cha Mulungu. (Aheb. 1:7, 14; Sal. 104:4) Pa nthawi ina, Yehova anapereka lamulo komanso kuletsa Satana, yemwe ndi mdani wake, kuti asachite zinazake. (Yobu 1:12; 2:6) Komanso pamene Mikayeli mkulu wa angelo ankakangana ndi Mdyerekezi, anasonyeza kuti amazindikira udindo wa Yehova monga Woweruza Wamkulu. Iye anauza Mdyerekezi kuti: “Yehova akudzudzule.” (Yuda 9; yerekezerani ndi Zek. 3:2.) Baibulo limasonyezanso kuti Yehova anapatsa Yesu udindo woyang’anira angelo onse. (Aheb. 1:6; 1 Pet. 3:22; Mat. 13:41; 25:31; Afil. 2:9-11) Choncho, Yesu ndi amene anatumiza mngelo kwa Yohane. (Chiv. 1:1) Koma pa 1 Akorinto 6:3, mtumwi Paulo anauza abale ake a Khristu kuti nawonso adzaweruza angelo. Izi zili choncho chifukwa nawonso adzagwira nawo ntchito yopereka chiweruzo kwa angelo oipa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena