Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr19 April tsamba 1-2
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya April 2019

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya April 2019
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
  • Timitu
  • APRIL 1-7
  • APRIL 22-28
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
mwbr19 April tsamba 1-2

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

APRIL 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 7-9

“Kusakhala Pabanja ndi Mphatso”

w96 10/15 12-13 ¶14

Munthu Amene Sali Pabanja Amatumikira Yehova Popanda Chosokoneza

14 Sitinganene kuti Mkhristu amene sali pabanja ‘akuchita bwino’ kuposa amene ali pabanja ngati Mkhristuyo amangokhalira kuchita zinthu zodzisangalatsa. Tikutero chifukwa iye sali pabanja “chifukwa cha ufumu,” koma chifukwa cha zofuna zake. (Mateyu 19:12) M’bale kapena mlongo amene sali pabanja ayenera “kumadera nkhawa zinthu za Ambuye” kapena kuganizira kwambiri zinthu “zokondweretsa ambuye,” ndipo nthawi zonse ayenera kutumikira Ambuye popanda chosokoneza. Zimenezi zikutanthauza kuti sayenera kulola chilichonse kumusokoneza potumikira Yehova komanso Yesu Khristu. Mkhristu amene sali pabanja akamachita zimenezi, m’pamene angasonyeze kuti ‘akuchita bwino’ kwambiri kuposa amene ali pabanja.

APRIL 22-28

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 14-16

“Mulungu Adzakhala ‘Zinthu Zonse kwa Aliyense’”

w98 7/1 21 ¶10

“Imfa nayonso, . . . idzawonongedwa”

10 Mawu akuti “mapeto” akunena zimene zidzachitike Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu ukamadzatha. Pa nthawiyo Yesu modzichepetsa, adzabwezera Ufumu kwa Atate wake. (Chivumbulutso 20:4) Nthawi imeneyo, cholinga cha Mulungu chofuna “kusonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu,” chidzakhala chitakwaniritsidwa. (Aefeso 1:9, 10) Komabe, zimenezi zisanachitike, Khristu adzayamba kaye wawononga “maboma onse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse” zomwe zimatsutsana ndi zimene Mulungu amafuna. Komabe, palinso zinthu zina zomwe zidzachitike pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo. (Chivumbulutso 16:16; 19:11-21) Mwachitsanzo Paulo anati: “[Khristu] ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:25, 26) Choncho imfa komanso mavuto onse amene amabwera chifukwa cha uchimo wa Adamu, zidzachotsedwa. Kenako Mulungu adzaukitsa anthu onse omwe ali “m’manda achikumbutso.”​—Yohane 5:28.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 1197-1198

Thupi Lomwe Silingawonongeke

Odzozedwa omwe amaukitsidwa kuti akakhale kumwamba limodzi ndi Yesu, sikuti amangopatsidwa moyo wauzimu wamuyaya koma amapatsidwa moyo womwe sungawonongeke komanso womwe sungafe. Chifukwa chakuti odzozedwawa anasonyeza kuti ndi okhulupirika komanso anafa ndi matupi omwe amatha kuwonongeka, pa 1 Akorinto 15:42-54 Paulo anasonyeza kuti pa nthawiyi adzapatsidwa matupi auzimu omwe sangawonongeke. Choncho mawu akuti moyo umene sungafe, akusonyeza kuti adzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Pomwe mawu akuti moyo womwe sungathe kuwonongeka akunena za matupi amene Mulungu adzawapatse omwe sangawole kapena kutha. Zikuoneka kuti Mulungu adzawapatsa mphamvu zoti asamadalire chilichonse kuti akhale ndi moyo ngati mmene zilili ndi anthufe komanso angelo. Umenewu ndi umboni wakuti Mulungu amawakhulupirira kwambiri. Ngakhale kuti anthu amenewa adzakhala ndi moyo womwe sungathe kuwonongeka, adzapitirizabe kulamuliridwa ndi Mulungu. Mofanana ndi mtsogoleri wawo Yesu Khristu, iwo adzapitirizabe kumvera komanso kutsatira zimene Atate wawo amafuna.​—1 Akor. 15:23-28.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena