NYIMBO 81
Moyo wa Mpainiya
Losindikizidwa
1. Tsiku likayamba, tulo tikukoma
Timadzuka kupita
Kolalikira uthenga
Ndipo Mulungu amatitsogolera.
Timasangalala
Anthu akamatimvetsera.
(KOLASI)
Tinasankha
Kutumikira Yehova.
Timachita zofuna zake.
Tipitilizabe kulalikiraku.
Tikatero timasonyeza
Chikondi.
2. Pofika madzulo timatopa ndithu
Komabe timapeza
Chimwemwe potumikira.
Yehova Mulungu amatidalitsa.
Nthawi zonse
Timamuthokoza potithandiza.
(KOLASI)
Tinasankha
Kutumikira Yehova.
Timachita zofuna zake.
Tipitilizabe kulalikiraku.
Tikatero timasonyeza
Chikondi.
(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 92:2; Aroma 14:8.)