NYIMBO 38
Adzakulimbitsa
Losindikizidwa
1. Panali chifukwa chimene Mulungu
Anakupatsira choonadi.
Anaona mtima wofuna kuchita
Zabwino zomusangalatsadi.
Unalonjeza kum’tumikira
Ndipo iye anakuthandiza.
(KOLASI)
Ndi magazi a Yesu
Anakuwombola.
Ndiwe wa Mulungu,
Adzakulimbitsa.
Adzakutsogolera
Ndi mzimu woyera.
Adzakuteteza,
Adzakulimbitsa.
2. Mulungu anapereka Mwana wake,
Amafuna zizikuyendera.
Ngati mwana wake anakupatsadi
Sangalephere kukulimbitsa.
Chikondi chako sangaiwale
Ndipo sangasiye anthu ake.
(KOLASI)
Ndi magazi a Yesu
Anakuwombola.
Ndiwe wa Mulungu,
Adzakulimbitsa.
Adzakutsogolera
Ndi mzimu woyera.
Adzakuteteza,
Adzakulimbitsa.
(Onaninso Aroma 8:32; 14:8, 9; Aheb. 6:10; 1 Pet. 2:9.)