PHUNZIRO 5
Kuwerenga Molondola
1 Timoteyo 4:13
MFUNDO YAIKULU: Muziwerenga momveka bwino komanso mosalakwitsa.
MMENE MUNGACHITIRE:
Muzikonzekera bwino. Muzidzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani mawu amenewa analembedwa? Muziwerenga magulu a mawu osati kumangotchula liwu ndi liwu. Muzipewa kuwonjezera mawu, kudumpha mawu kapena kusemphanitsa mawu. Muzitsatira zizindikiro zonse za m’kalembedwe.
Muzitchula mawu alionse molondola. Ngati simukudziwa katchulidwe kabwino ka mawu, muyenera kufufuza, kumvetsera nkhani zojambulidwa kapena kufunsa anzanu omwe amadziwa bwino.
Muzilankhula momveka bwino. Kuti mawu anu azituluka bwino muyenera kukweza bwino mutu komanso kutsegula pakamwa mokwanira. Muzitchula mawu alionse momveka bwino.