Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
DECEMBER 2-8
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 7-9
“Khamu Lalikulu la Anthu Likudalitsidwa ndi Yehova”
it-1 997 ¶1
Khamu Lalikulu
Zimenezi zikubweretsa funso lakuti: Ngati “khamu lalikulu” lidzapulumuke n’kukhala padziko lapansili, n’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti iwo ‘aimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa’? (Chiv. 7:9) Nthawi zina Baibulo likamanena kuti anthu ‘aimirira’ pamaso pa munthu winawake, limakhala likutanthauza kuti munthuyo amakondwera nawo. (Sal. 5:5; Miy. 22:29; Luka 1:19) Chimenechi n’chifukwa chake chaputala 6 cha buku la Chivumbulutso chimanena kuti “mafumu a dziko lapansi, nduna, akuluakulu a asilikali, olemera, amphamvu, kapolo aliyense ndi mfulu aliyense” anabisala kuti asaonekere pamaso pa ‘iye amene wakhala pampando wachifumu, ndiponso kuti abisike ku mkwiyo wa Mwanawankhosa, chifukwa tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika, ndipo ndani angaimirire pamaso pawo?’ (Chiv. 6:15-17; yerekezerani ndi Luka 21:36.) Choncho apa n’zoonekeratu kuti “khamu lalikulu” ndi anthu omwe adzapulumuke mkwiyo umenewu ndipo adzakhala ngati ‘aimirira’ pamaso pa Mulungu komanso Mwanawankhosa chifukwa iwo adzakhala akusangalala nawo.
it-2 1127 ¶4
Chisautso
Patadutsa zaka pafupifupi 30 kuchokera pamene Yerusalemu anawonongedwa, mtumwi Yohane ananena za khamu lalikulu la anthu ochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse komanso mtundu uliwonse kuti: “Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:13, 14) Mfundo yakuti khamu lalikululi latuluka “m’chisautso chachikulu” ikusonyeza kuti anthuwa adzakhala oti apulumuka chisautsochi. Mfundoyi ikuonekeranso bwino palemba la Machitidwe 7:9, 10, pomwe pamati: “Mulungu anali [ndi Yosefe], ndipo anamulanditsa m’masautso ake onse.” Mawu akuti Yosefe analanditsidwa m’masautso ake onse, sakungotanthauza kuti Mulungu anamuthandiza kuti apirire, komanso kuti anamupulumutsa m’masautso ake onse.
it-1 996-997
Khamu Lalikulu
Kodi Tingalidziwe Bwanji? Chinthu chomwe chingatithandize kudziwa khamu lalikulu chafotokozedwa bwino m’Chivumbulutso chaputala 7 komanso m’malemba ena a m’Baibulo omwe amanena za nkhaniyi. Lemba la Chivumbulutso 7:15-17, limanena kuti Mulungu ‘adzawatambasulira hema wake,’ n’kuwatsogolera “ku akasupe a madzi a moyo” ndipo “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.” Pa Chivumbulutso 21:2-4, timapezanso nkhani yofanana ndi imeneyi. Lembali limati: ‘Chihema cha Mulungu chidzakhala pakati pa anthu,’ ‘adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo,’ ndipo ‘imfa sidzakhalaponso.’ Masomphenya amenewa amasonyeza kuti anthuwa sadzapita kumwamba chifukwa ngati zitatero ndiye kuti akhoza kudzasemphana ndi ‘Yerusalemu Watsopano yemwe adzatsike kuchokera kumwamba’ n’kubwera padziko lapansi pomwe padzakhale khamu lalikululi.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 12
Abadoni
Kodi Abadoni, “mngelo wa phompho” ndi ndani?
Malinga ndi Chivumbulutso 9:11, “Abadoni” ndi dzina la “mngelo wa phompho.” M’Chigiriki dzinali limadziwikanso kuti Apoliyoni ndipo limatanthauza “Wowononga.” M’zaka za m’ma 1800, anthu ankanena kuti Apoliyoni ankaimira Vasipashani, Muhamadi ngakhalenso Napoliyoni ndipo ankaona kuti mngelo wotchulidwa pavesili ndi “mngelo woipa.” Komabe mfundo yofunika kuiganizira ndi yakuti, pa Chivumbulutso 20:1-3, mngelo yemwe ali ndi “kiyi wa paphompho” ndi wabwino ndipo ndi mngelo wa Mulungu. Tikutero chifukwa mngeloyu ndi amene adzamange Satana ndi kumuponya kuphompho. Ponena za lemba la Chivumbulutso 9:11, buku lina limati: “Abadoni si mngelo wa Satana koma wa Mulungu ndipo Mulunguyo amamugwiritsa ntchito popereka chiweruzo.”—The Interpreter’s Bible.
M’Malemba Achiheberi omwe taona aja, zikuonekeratu kuti mawu akuti ʼavad·dohnʹ ndi ofanana ndi akuti Sheol komanso imfa. Pa Chivumbulutso 1:18, Yesu ananena kuti: “Ndili ndi moyo kwamuyaya, ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi a Manda.” Lemba la Luka 8:31 limasonyeza kuti Yesu ali ndi mphamvu zoponyera ziwanda kuphompho. Lemba la Aheberi 2:14 limasonyeza kuti iye ali ndi mphamvu zowonongera Satana. Lembali limanenanso kuti Yesu anakhala wamagazi ndi mnofu n’cholinga choti “kudzera mu imfa yake, awononge Mdyerekezi, amene ali ndi njira yobweretsera imfa.” Lemba la Chivumbulutso 19:11-16 limasonyeza kuti Yesu anasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale Wowononga.
DECEMBER 9-15
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 10-12
“Mboni Ziwiri Zinaphedwa Koma Zinakhalanso ndi Moyo”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 880-881
Mpukutu, Kutambasula
Tanthauzo Lophiphiritsira. M’Baibulo pali malo angapo omwe mawu akuti “mpukutu” amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsira. Mneneri Ezekieli komanso Zekariya anaona mpukutu wolembedwa mbali zonse. Popeza nthawi zambiri mpukutu unkalembedwa mbali imodzi, zimene aneneriwa anaona zikusonyeza kuti uthenga wachiweruzo umene unali mumpukutu wolembedwa mbali zonsewo unali wamphamvu kwambiri. (Ezek. 2:9–3:3; Zek. 5:1-4) M’masomphenya a m’buku la Chivumbulutso, wokhala pampando wachifumu anagwira m’dzanja lake lamanja mpukutu wokhala ndi zidindo 7 zomatira. Zidindozi zinachititsa kuti uthenga wa mumpukutuwo ukhale wachinsinsi kufikira Mwanawankhosa wa Mulungu atazichotsa. (Chiv. 5:1, 12; 6:1, 12-14) Kenako m’masomphenya omwewo Yohane anapatsidwa mpukutu uja n’kuuzidwa kuti audye. Mpukutuwo unkatsekemera mkamwa mwake koma unamupweteketsa m’mimba. Popeza mpukutuwo unali wotambasula ndipo unalibe chidindo chomatira, zikuoneka kuti uthenga wake unali woti anthu akhoza kuumva. Uthengawo unali wotsekemera kwa Yohane chifukwa sanavutike kuumva koma unali wopweteka m’mimba chifukwa ankafunikabe kulosera uthenga wovutawu mogwirizana ndi mmene anauzidwira. (Chiv. 10:1-11) Ezekieli anaonanso masomphenya ofanana ndi amenewa, omwe anapatsidwa mpukutu womwe unali ndi “nyimbo zoimba polira, mawu odandaula ndi mawu olira.”—Ezek. 2:10.
it-2 187 ¶7-9
Zowawa Zapobereka
M’masomphenya a m’buku la Chivumbulutso, mtumwi Yohane anaona mkazi wakumwamba akulira “pomva ululu chifukwa cha zowawa za pobereka.” Mkaziyu anabereka “mwana wamwamuna, mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.” Ngakhale chinjoka chinayesetsa kuti chidye mwanayo, mwanayo “anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.” (Chiv. 12:1, 2, 4-6) Popeza mwanayo anatengedwa ndi Mulungu, zikusonyeza kuti iye anamuvomereza kukhala mwana wake monga mmene anthu ankachitira kale. Pa nthawiyo mwana akangobadwa ankamutenga n’kupita naye kwa bambo ake omwe ankamulandira posonyeza kuti akuvomereza kuti ndi wawo. Choncho ngati Mulungu anamuvomereza mwanayu ndiye kuti “mkaziyo” ndi “mkazi” wa Mulungu yemwe ndi “Yerusalemu wam’mwamba,” amene ndi “mayi” wa Khristu komanso abale ake odzozedwa.—Agal. 4:26; Aheb. 2:11, 12, 17.
Popeza kuti “mkazi” wa Mulungu wakumwamba ndi wangwiro, ndiye kuti sangamve zowawa pobereka. Choncho zowawa za poberekazi ndi zophiphiritsira, zikungosonyeza kuti “mkaziyu” anazindikira kuti watsala pang’ono kubereka mwana.—Chiv. 12:2.
Kodi ndi ndani amene ali “mwana wamwamuna, mnyamata,” yemwe “adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo?” Lemba la Salimo 2:6-9 linaneneratu kuti ameneyu ndi Mfumu komanso Mesiya. Koma Yohane anaona masomphenyawa patadutsa zaka zambiri Khristu atabwera padzikoli, kufa, n’kuukitsidwa. Choncho masomphenyawa ayenera ankatanthauza kubadwa kwa Ufumu wa Mesiya womwe Mfumu yake ndi Yesu Khristu yemwe ataukitsidwa anapita kumwamba ndipo “anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu. Kuyambira pamenepo, akuyembekezera kufikira pamene adani ake adzaikidwe monga chopondapo mapazi ake.”—Aheb. 10:12, 13; Sal. 110:1; Chiv. 12:10.
DECEMBER 23-29
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 17-19
“Nkhondo ya Mulungu Idzathetsa Nkhondo Zonse”
it-1 1146 ¶1
Hatchi
Mtumwi Yohane m’masomphenya ophiphiritsira, anaona Yesu Khristu ali muulemerero wake ndipo anakwera hatchi yoyera. Pambuyo pake pankabwera gulu lankhondo ndipo onse anakweranso mahatchi oyera. Yohane anauzidwa kuti masomphenyawa ankaimira nkhondo yolungama imene Khristu adzamenye polimbana ndi adani ake. Iye adzamenya nkhondoyi m’malo mwa Yehova Mulungu yemwe ndi Atate wake. (Chiv. 19:11, 14) M’chaputala 6, Yohane anaona masomphenya osonyeza Yesu atakwera pahatchi yake monga mfumu ndipo kumbuyo kwake kunkabwera mahatchi ena ndi okwerapo ake.—Chiv. 6:2-8.
DECEMBER 30–JANUARY 5
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 20-22
“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 249 ¶2
Moyo
Adamu akanamvera lamulo limene Mulungu anamupatsa, sakanafa. (Gen. 2:17) Choncho m’tsogolomu, mdani womalizira yemwe ndi imfa akadzawonongedwa, anthu onse omvera adzakhala angwiro ndipo adzakhala ndi moyo mpaka kalekale. (1 Akor. 15:26) Imfayi idzathetsedwa kumapeto kwa ulamuliro wa Khristu womwe buku la Chivumbulutso limanena kuti udzakhala wazaka 1,000. Chaputala 20 chimafotokoza kuti anthu omwe adzakhale mafumu ndi ansembe limodzi ndi Khristu “anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000.” Koma “akufa enawo sanakhalenso ndi moyo kufikira zitatha zaka 1,000.” Akufa amenewa ndi amene adzakhale ndi moyo kumapeto kwa zaka 1,000, Satana asanamasulidwe kuchokera kuphompho kuti awayese. Zaka 1,000 zikamadzafika kumapeto, anthu onse omwe adzakhale padziko lapansi adzakhala angwiro mofanana ndi mmene Adamu ndi Hava analili asanachimwe. Pa nthawiyo anthu azidzachita zinthu mosalakwitsa chilichonse. Choncho anthu amene adzakhalebe okhulupirika pambuyo poti Satana wamasulidwa kuphompho n’kuwayesa, adzasangalala kukhala ndi moyo wangwiro kwamuyaya.—Chiv. 20:4-10.
it-2 189-190
Nyanja Yamoto
Mawu amenewa amapezeka m’buku la Chivumbulutso lokha ndipo ndi ophiphiritsira. Baibulo limapereka tanthauzo la mawu amenewa. Limati: “Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”—Chiv. 20:14; 21:8.
Tanthauzo lophiphiritsali limaonekera bwino m’mavesi enanso a m’buku la Chivumbulutso. Mwachitsanzo mavesi ena amanena kuti imfa idzaponyedwanso m’nyanja yamotoyi. (Chiv. 19:20; 20:14) Apatu n’zoonekeratu kuti imfa siingawotchedwe ndi moto. Komanso Baibulo limanena kuti Mdyerekezi yemwe ndi cholengedwa chauzimu, nayenso adzaponyedwa m’nyanja imeneyi. Popeza iye ndi mzimu, sangapse ndi moto.—Chiv. 20:10; yerekezerani ndi Eks. 3:2 ndi Ower. 13:20.
Popeza nyanja yamoto ikuimira “imfa yachiwiri” komanso chifukwa chakuti lemba la Chivumbulutso 20:14 limanena kuti “imfa ndi Manda” zidzaponyedwa m’nyanjayi, n’zoonekeratu kuti nyanja imeneyi siikutanthauza imfa imene inabwera chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu (Aroma 5:12), komanso siikutanthauza Manda a anthu onse (Sheol). Choncho nyanja imeneyi ikuimira imfa ya mtundu wina. Tikutero chifukwa chinthu chomwe chaponyedwa m’nyanjayi chimawonongekeratu. Izi n’zosiyana ndi zimene Baibulo limafotokoza ponena za imfa yomwe inabwera chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu komanso Manda a anthu onse (Sheol), omwe Baibulo limanena kuti adzapereka akufa amene anali mmenemo. (Chiv. 20:13) Tinganene kuti anthu omwe sadzapezeka “m’buku la moyo” komanso anthu osalapa omwe adzapitirize kutsutsa ulamuliro wa Mulungu, adzaponyedwa m’nyanja yamoto kutanthauza kuti adzawonongedwa kotheratu, yomwe ndi imfa yachiwiri.—Chiv. 20:15.