NYIMBO 78
Kuphunzitsa Mawu a Mulungu
Losindikizidwa
1. Tikamaphunzitsa anthu
Timasangalala.
Timapeza madalitso
Ochuluka ndithu.
Timatsanziratu Yesu
Pophunzitsa ena
Ndiponso timawathandiza
Kukonda Mulungu.
2. Pamene tikuphunzitsa
Tichite zabwino,
Anthu onse aziona
Kuwala kwa M’lungu.
Timafufuza mwakhama
Mawu a Mulungu.
Pouza ena uthengawu
Timadziphunzitsa.
3. M’lungu watipatsa zoti
Tiziphunzitsira
Ndipo tikamamupempha
Adzatithandiza.
Timakonda mawu ake
Omwe ndi oona.
Tizikonda anthu omwe
Timawaphunzitsawo.
(Onaninso Sal. 119:97; 2 Tim. 4:2; Tito 2:7; 1 Yoh. 5:14.)