Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 2 tsamba 5
  • Kulankhula Mokambirana ndi Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula Mokambirana ndi Anthu
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula ndi Mtima Wonse
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kulankhula Mwachibadwa
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kulankhula Motsimikiza
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 2 tsamba 5

PHUNZIRO 2

Kulankhula Mokambirana ndi Anthu

Lemba

2 Akorinto 2:17

MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula mwachibadwa komanso kuchokera mumtima kuti anthu adziwe mmene nkhaniyo ikukukhudzirani komanso kuti mumawaganizira.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzikonzekera mokwanira ndipo muzipemphera. Muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni n’cholinga choti muziganizira kwambiri za uthenga wanu osati za inuyo. Muziganizira kwambiri mfundo zikuluzikulu zimene mukufuna kuuza anthu. Muzifotokoza mfundozo m’mawu anuanu osati kumangotchula ndendende mmene zilili pa autilaini.

    Mfundo yothandiza

    Mukamawerenga Baibulo kapena buku lina muziidziwiratu bwino nkhaniyo n’cholinga choti musamadodome. Ngati mawu amene mukuwerengawo ndi a munthu winawake, muziwawerenga mosonyeza mmene munthuyo ankamvera koma musachite zimenezi mokokomeza.

  • Muzilankhula kuchokera mumtima. Muziganizira mmene uthengawo ungathandizire anthu amene mukulankhula nawo. Muziganizira kwambiri za anthuwo. Mukatero, nkhope yanu, thupi lanu ndiponso mawu anu zidzasonyeza kuti mumawaganizira ndipo ndinu anzawo.

    Mfundo yothandiza

    Koma apa sitikutanthauza kuti muzichita zinthu motayirira. Muyenera kulankhula ndi anthu mwaulemu, kugwiritsa ntchito mawu omveka komanso kutsatira malamulo achilankhulo.

  • Muziyang’ana anthu. Ngati n’zololeka kudera limene mukukhala, muziyang’ana anthu m’njira yoti maso anu aziphana. Pokamba nkhani, muziyang’ana munthu mmodzi pa nthawi imodzi, osati kumangomwazamwaza maso kuti muone gulu lonse nthawi imodzi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena