Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr20 March tsamba 1-3
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2020

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2020
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
  • Timitu
  • MARCH 2-8
  • MARCH 16-22
  • MARCH 23-29
  • MARCH 30–​APRIL 5
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
mwbr20 March tsamba 1-3

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2020

MARCH 2-8

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 22-23

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 853 ¶5-6

Kudziwiratu Zam’tsogolo, Kulemberatu Zam’tsogolo

Mulungu amachita kusankha zinthu zomwe akufuna kudziwiratu. Mphamvu zomwe Mulungu ali nazo zotha kudziwiratu zinthu zam’tsogolo ziyenera kukhala zogwirizana ndi mfundo zake zolungama komanso zimene amanena kudzera m’Mawu ake. Mosiyana kwambiri ndi zimene anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu analemberatu chilichonse chomwe chidzachitike, Malemba angapo amasonyeza kuti Mulungu ankayamba wafufuza kaye zomwe zikuchitika asanasankhe zoti achite.

Mwachitsanzo, pa Genesis 11:5-8, Baibulo limafotokoza kuti Mulungu anapita kukaona mmene zinthu zinalili ku Babele. Ataona zomwe zinkachitika kumeneko, anaganiza zolepheretsa cholinga cholakwika chomwe anthuwo anali nacho. Anthu a ku Sodomu ndi Gomora atayamba kuchita zinthu zoipa, Yehova anauza Abulahamu kuti akufuna kukafufuza za nkhaniyi (pogwiritsa ntchito mngelo). Anamuuza kuti: “Nditsikirako kuti ndikaone ngati akuchitadi monga mwa kudandaula kumene ndamva ndiponso ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho. Ndikufuna ndidziwe zimenezi.” (Ge 18:20-22; 19:1) Posonyeza kuti ankamudziwa bwino Abulahamu, Yehova ananena kuti “ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu.” Koma pamene Abulahamu ankafuna kupereka nsembe mwana wake Isaki, Yehova anati: “Tsopano ndadziwa kuti ndiwe woopa Mulungu, pakuti sunakane kupereka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.”—Ge 18:19; 22:11, 12; yerekezerani ndi Ne 9:7, 8; Aga 4:9.

it-1 604 ¶5

Kodi zinatheka bwanji kuti Mulungu aziona Abulahamu ngati munthu wolungama Khristu asanapereke moyo wake?

Nayenso Abulahamu chifukwa cha chikhulupiriro komanso zochita zake, “anaonedwa ngati wolungama.” (Aroma 4:20-22) Komabe zimenezi sizikusonyeza kuti Abulahamu ndi anthu ena okhulupirika omwe anakhalako Chikhristu chisanayambe anali olungamadi kapena kuti opanda tchimo lililonse. Koma chifukwa chosonyeza chikhulupiriro pa zomwe Mulungu analonjeza pa nkhani yokhudza “mbewu,” komanso chifukwa chotsatira malamulo a Mulungu, Mulunguyo anawaona kuti anali olungama ndipo zimenezi ndi zosiyana ndi anthu ambiri m’dzikoli omwe amaonedwa kuti ndi osalungama. (Gen. 3:15; Sal. 119:2, 3) Mokoma mtima, Yehova anaona Abulahamu ndi anthu ena okhulupirikawo monga anthu opanda cholakwa. Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi anthu a m’dzikoli omwe ndi otalikirana ndi Mulungu. (Sal 32:1, 2; Aef. 2:12) Choncho chifukwa cha chikhulupiriro cha anthuwa, Mulungu ankawakonda kwambiri ndipo anawadalitsa. Mulungu anachita zimenezi popanda kuphwanya mfundo zake zolungama. (Sal 36:10) Ngakhale zili chonchi, anthuwa ankazindikira kuti akufunika kupulumutsidwa ku uchimo ndipo ankayembekezera nthawi imene Mulungu adzawapulumutse.—Sal 49:7-9; Aheb. 9:26.

MARCH 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 25-26

it-1 1242

Yakobo

Esau anali wosiyana kwambiri ndi Yakobo. Esau ankakondedwa kwambiri ndi bambo ake. Iye anali wovuta, ankakonda kuyenda m’tchire komanso anali wodziwa kusaka. Pomwe Yakobo yemwe anali wofatsa, ankakondedwa ndi mayi ake ndipo Baibulo limanena kuti Yakobo ‘anali munthu wosalakwa (m’chiheberi, tam) ndipo ankakhala nthawi yambiri m’mahema.’ Yakobo ankaweta nkhosa ndipo anali wodalirika pogwira ntchito za pakhomo. (Ge 25:27, 28) Mawu achiheberi akuti tam, ankagwiritsidwa ntchito ponena za munthu amene Mulungu ankasangalala naye. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti: “Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi aliyense wopanda cholakwa.” Ponena za munthu wopanda cholakwa, Yehova anati: “Tsogolo la munthu ameneyu ndi lamtendere.” (Miy 29:10; Sl 37:37) Baibulo limanenanso za Yobu yemwe anali wokhulupirika kuti “munthu wopanda cholakwa [m’chiheberi, tam], wowongoka mtima.”​—Yob 1:1, 8; 2:3.

it-1 835

Mwana Woyamba Kubadwa

Kuyambira kale kwambiri, mwana woyamba kubadwa ankakhala ndi udindo waukulu kwambiri m’banja ndipo ndi amene ankapatsidwa udindo woyang’anira banja lonse bambo ake akamwalira. Ankapatsidwanso magawo awiri a chuma cha bambo ake. (De 21:17) Baibulo limanena kuti Rubeni anakhala pansi pafupi ndi Yosefe ndipo abale ake enawo anakhala aliyense malinga ndi msinkhu wake, kuyambira wamkulu kukamalizira wamng’ono. (Ge 43:33) Koma si nthawi zonse pamene Baibulo likamatchula za ana aamuna limayamba ndi mwana woyamba kubadwa. Nthawi zambiri mwana wokhulupirika ndi amene ankatchulidwa koyambirira.​—Ge 6:10; 1Mb 1:28; yerekezerani ndi Ge 11:26, 32; 12:4.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 245 ¶6

Bodza

Ngakhale kuti Baibulo limatsutsa za kunena mabodza oipa, zimenezi sizikutanthauza kuti munthu amafunika kuulula chilichonse kwa anthu amene sakuyenerera kudziwa zoona. Yesu anati: “Musamapatse agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zanu, kuopera kuti zingapondeponde ngalezo kenako n’kutembenuka ndi kukukhadzulani.” (Mt 7:6) Ichi n’chifukwa chake nthawi zina Yesu sankauza anthu zinthu zonse kapena sankapereka yankho lachindunji ku mafunso awo chifukwa kuchita zimenezi kukanabweretsa mavuto ambiri. (Mt 15:1-6; 21:23-27; Yoh 7:3-10) Ndi mmenenso zinalili ndi Abulahamu, Isaki, Rahabi komanso Elisa. Atafunsidwa zinthu zinazake ndi anthu osakhulupirira Yehova, sanapereke yankho lachindunji kapena kufotokoza zonse zimene anthuwo ankafuna.​—Ge 12:10-19; chaputala 20; 26:1-10; Yos 2:1-6; Yak 2:25; 2Mf 6:11-23.

MARCH 23-29

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 27-28

it-1 341 ¶6

Madalitso

Kalelo, nthawi zambiri bambo ankadalitsa ana ake aamuna akangotsala pang’ono kumwalira. Anthu ankaona kuti zimenezi zinali zofunika kwambiri. Ichi n’chifukwa chake nthawi ina Isaki anadalitsa Yakobo ngakhale ankaganiza kuti akudalitsa Esau mwana wake woyamba. Isaki anapereka madalitso kwa Yakobo m’malo mwa Esau ndipo popeza Isaki anali atakalamba kwambiri moti sankaona, n’zosakayikitsa kuti anapempha Yehova kuti achite zimenezi. (Ge 27:1-4, 23-29; 28:1, 6; Ahe 11:20; 12:16, 17) Kenako, Isaki anatsimikiziranso Yakobo kuti adzadalitsidwa ndipo anamuonjezeranso madalitso ena. (Ge 28:1-4) Komanso atangotsala pang’ono kumwalira, Yakobo anayamba ndi kudalitsa ana awiri a Yosefe, kenako anadalitsa ana ake. (Ge 48:9, 20; 49:1-28; Ahe 11:21) Nayenso Mose atangotsala pang’ono kumwalira, anadalitsa mtundu wonse wa Isiraeli. (De 33:1) Pa nthawi zonsezi, madalitso amene anthuwo analandira ankalosera zam’tsogolo. Nthawi zina munthu akamapereka madalitso ankaika dzanja lake pamutu pa munthu amene akumudalitsayo.​—Ge 48:13, 14.

MARCH 30–​APRIL 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 29-30

“Yakobo Anakwatira”

it-2 341 ¶3

Banja

Chikondwerero cha Ukwati. Ngakhale kuti pochita ukwati sankachita mwambo ulionse wapadera, zikuoneka kuti Aisiraeli ankasangalala kwambiri pa tsiku la ukwati. Mwachitsanzo, mkazi adakali kwawo ankafunika kuchita zinthu zosiyanasiyana. Choyamba, ankayenera kusamba komanso kudzola mafuta onunkhira. (Yerekezerani ndi Ru 3:3; Eze 23:40.) Nthawi zina, mothandizidwa ndi mnzake, mkwatibwi ankavala nsalu yapachifuwa komanso mkanjo woyera womwe unkakongoletsedwa ndi zinthu zosiyanasiyana malinga ndi m’mene mtsikanayo ankapezera ndalama. (Yer 2:32; Chv 19:7, 8; Sl 45:13, 14) Nthawi zinanso ankatha kuvala zodzikongoletsera zosiyanasiyana. (Yes 49:18; 61:10; Chv 21:2) Akatero ankadziphimba ndi nsalu yopyapyala yofanana ndi velo yomwe inkayambira kumutu mpaka kumiyendo. (Yes 3:19, 23) Zimenezi zikutithandiza kumvetsa chifukwa chake Labani anakwanitsa kupusitsa Yakobo pomupatsa Leya m’malo mwa Rakele. (Ge 29:23, 25) Pamene Rabeka ankakumana ndi Isaki, anaphimba kumutu. (Ge 24:65) Kuchita zimenezi kunkasonyeza kuti mkwatibwi akugonjera mkwati, yemwe anali ngati mutu wake.​—1Ak 11:5, 10.

it-1 50

Kutenga Ana Ngati Ako

Rakele ndi Leya ankaona ana omwe akapolo awo anabereka ngati ana awo enieni. (Ge 30:3-8, 12, 13, 24) Ana amenewa analandira cholowa mofanana ndi ana ena onse omwe Yakobo anabereka ndi akazi ake awiriwa. Ana amenewanso, bambo awo anali Yakobo ndipo popeza akapolowa anali a Rakele ndi Leya, tingati zinali zomveka kuti Rakele ndi Leya aziwaona ngati ana awo enieni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena