Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr20 April tsamba 1-3
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
  • Timitu
  • APRIL 13-19
  • APRIL 20-26
  • APRIL 27–​MAY 3
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
mwbr20 April tsamba 1-3

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

APRIL 13-19

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 31

“Yakobo ndi Labani Anachita Pangano Lamtendere”

it-1 883 ¶1

Galeeda

Yakobo ndi Labani atathetsa kusamvana kwawo anapanga pangano lamtendere. Kenako Yakobo anaimika mwala wachikumbutso ndipo anauza “abale ake” kuti atenge miyala n’kuiika mwadongosolo kuti ikhale ngati tebulo lomwe anadyerapo chakudya cha pangano. Labani anatchula mulu wa miyalawo kuti “Yegara-sahaduta” lomwe linali dzina la Chiaramu, koma Yakobo anautchula kuti Galeeda limene ndi dzina lomwelo m’Chiheberi. Kenako Labani anati: “Mulu [m’Chiheberi gal] wa miyalawu ndi mboni [m’Chiheberi ʽedh] yathu lero pakati pa ine ndi iwe.” (Ge 31:44-48) Mulu wa miyalawu komanso mwala wachikumbutsowo zinali ngati mboni kwa anthu odutsa. Mogwirizana ndi vesi 49, zinthu zimenezi zinali ngati “Nsanja ya Mlonda [m’Chiheberi mits·pahʹ],” yomwe inkasonyeza kuti Yakobo ndi Labani anagwirizana kuti mabanja awo azikhala mwamtendere. (Ge 31:50-53) M’kupita kwa nthawi, anthu anayamba kugwiritsa ntchito miyala ngati mboni akagwirizana kuchita zinazake.​—Yos 4:4-7; 24:25-27.

it-2 1172

Nsanja ya Mlonda

Yakobo anauza anthu kuti aunjike mulu wamiyala ndipo anautchula kuti “Galeeda” (kutanthauza “Mulu wa Umboni”) komanso “Nsanja ya Mlonda.” Kenako Labani anati: “Yehova aziyang’anira iwe ndi ine tikasiyana pano.” (Ge 31:45-49) Mulu wa miyalawu unali ngati mboni m’njira yakuti Yehova ankaona zonse zomwe Yakobo ndi Labani ankachita pokwaniritsa pangano lawo lamtendere.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 1087-1088

Aterafi

Akatswiri ofukula zinthu zakale ku Mesopotamiya komanso madera ena ozungulira, anapeza umboni wosonyeza kuti munthu amene anali ndi aterafi ndi amene ankakhala woyenerera kulandira cholowa. Pamwala wina womwe unapezeka ku Nuzi panalembedwa kuti ngati mkamwini anali ndi aterafi, zinali zotheka kupita kukhoti n’kukanena kuti ali ndi ufulu wolandira cholowa cha apongozi ake. (Ancient Near Eastern Texts, lokonzedwanso ndi J. Pritchard, 1974, tsa. 219, 220, komanso mawu a m’munsi 51) N’kutheka kuti Rakele ankaganiza kuti sikulakwa kutenga aterafiwo chifukwa bambo ake sankachitira chilungamo mwamuna wake Yakobo. (Yerekezerani ndi Ge 31:14-16.) Umboni wina woti anthu ankaona kuti aterafi ndi ofunika pa nkhani yolandira cholowa ndi zimene Labani anachita. Iye anafika potengana ndi abale ake n’kutsatira Yakobo pamtunda woyenda masiku 7 kuti akalande aterafiwo. (Ge 31:19-30) Yakobo sanadziwe kuti Rakele anali ataba aterafi a bambo ake. (Ge 31:32) Tikutero chifukwa palibe umboni wosonyeza kuti Yakobo ankafuna kutenga aterafiwo n’cholinga choti adzalandire cholowa chomwe ana aamuna a Labani ankayenera kulandira. Yakobo analibe nawo ntchito mafanowo. Umboni wake ndi woti anakwirira mafano onse omwe anthu a m’banja lake anali nawo. Anakwirira mafanowa pansi pamtengo wina waukulu pafupi ndi ku Sekemu.​—Ge 35:1-4.

APRIL 20-26

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 32-33

“Kodi Mukuyesetsa Kuchita Zonse Zomwe Mungathe Kuti Mupeze Madalitso?”

it-2 190

Kulumala

Yakobo Analumala. Yakobo ali ndi zaka pafupifupi 97, analimbana ndi mngelo wa Mulungu usiku wonse. Iye analimbana ndi mngeloyo mpaka pamene anamudalitsa. Pamene ankachita zimenezi, mngeloyo anagwira nsukunyu ya Yakobo ndipo inaguluka. Zimenezi zinachititsa kuti Yakobo aziyenda chotsimphina. (Ge 32:24-32; Ho 12:2-4) Chilema chimenechi chinkamukumbutsa kuti ‘analimbana ndi Mulungu [mngelo wa Mulungu] ndi anthu, ndipo potsirizira pake anapambana’ mogwirizana ndi zimene mngelo uja ananena. Koma sikuti zimenezi zikutanthauza kuti Yakobo anali ndi mphamvu zoti n’kulimbana ndi mngelo wamphamvu wa Mulunguyu. Izi zinatheka chifukwa Mulungu anangomulola kuti alimbane ndi mngeloyo n’cholinga choti aone ngati Yakobo ankafunitsitsa kulandira madalitso.

it-1 1228

Isiraeli

1. Limeneli ndi dzina limene Mulungu anapereka kwa Yakobo ali ndi zaka pafupifupi 97. Yakobo analandira dzinali atangodutsa chigwa cha Yaboki pamene ankapita kukakumana ndi m’bale wake Esau. Pa nthawiyi, Yakobo analimbana ndi mngelo usiku wonse. Chifukwa choti sanagonje polimbana ndi mngeloyo, Mulungu anamudalitsa posintha dzina lake kukhala Isiraeli. Pofuna kukumbukira zimene zinachitikazi, Yakobo anatchula malowa kuti Penueli. (Ge 32:22-31) Kenako atafika ku Beteli, Mulungu anamutsimikizira za kusintha kwa dzina lakeli ndipo kungochokera pamenepo, anayamba kudziwika kwambiri ndi dzina lakuti Isiraeli. (Ge 35:10, 15; 50:2; 1Mb 1:34) M’Baibulo, dzina lakuti Isiraeli limapezeka maulendo oposa 2,500 ndipo maulendo ambiri limakhala likunena za mtundu wa Isiraeli, omwe anali ana a Yakobo.​—Eks 5:1, 2.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 980

Mulungu, Mulungu wa Isiraeli

Yakobo anasinthidwa dzina atalimbana ndi mngelo wa Yehova ku Penueli. Kenako anakumana ndi m’bale wake Esau ndipo anakakhala ku Sukoti. Kenako anasamukira ku Sekemu. Kumeneko anagula malo kwa ana a Hamori n’kumangapo hema. (Ge 32:24-30; 33:1-4, 17-19) “Atatero, anamangapo guwa lansembe n’kulitcha Mulungu, Mulungu wa Isiraeli,” kapena kuti “Mulungu ndi Mulungu wa Isiraeli.” (Ge 33:20) Yakobo anagwiritsa ntchito dzina lake latsopano lija potchula guwa lansembeli. Anachita izi posonyeza kuti ankalikonda dzinali komanso kuyamikira kuti Mulungu anamutsogolera mpaka kukafika m’Dziko Lolonjezedwa. Mawu akuti “Mulungu, Mulungu wa Isiraeli” amapezeka malo amodzi okha m’Baibulo lonse.

APRIL 27–​MAY 3

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 34-35

“Kuopsa Kocheza ndi Anthu a Makhalidwe Oipa”

w97 2/1 30 ¶4

Mzinda wa m’Chigwa Wotchedwa Sekemu

Kodi anyamata a mumzinda wa Sekemu ankamva bwanji kuona Dina akumabwera yekhayekha mumzindawu kudzacheza ndi anzake? Mwana wa mmodzi wa atsogoleri a m’dzikolo “atamuona, anamutenga n’kumugwiririra.” N’chifukwa chiyani Dina anadzilowetsa m’mavuto amenewa pocheza ndi anthu okonda chiwerewere a ku Kanani? Kodi mwina n’chifukwa choti ankasowa atsikana a msinkhu wake oti azicheza nawo? Kapena anali wosamva ngati azichimwene ake ena? Mungachite bwino kuwerenga nkhani ya m’buku la Genesis kuti muone mmene Yakobo ndi Leya anamvera Dina atakumana ndi mavuto chifukwa chocheza ndi atsikana a mumzinda wa Sekemu.​—Ge 34:1-31; 49:5-7; onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 1985, tsamba 31.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 600 ¶4

Debora

1. Anali wantchito wolera mwana amene analera Rabeka. Pamene Rabeka ankachoka kunyumba kwa bambo ake a Betuele n’kupita kukakwatiwa ndi Isaki, Debora anapita naye limodzi. (Ge 24:59) Debora anagwira ntchito zaka zambiri kunyumba kwa Isaki. Koma kenako anayamba kugwira ntchito kunyumba kwa Yakobo. N’kutheka kuti pa nthawiyi Rabeka anali atamwalira. Zikuoneka kuti Rabeka atakwatirana ndi Isaki, panadutsa zaka 125 kuti Debora amwalire ndipo anaikidwa pansi pa mtengo wina waukulu ku Beteli. Dzina lomwe mtengo umenewu unapatsidwa (Aloni-bakuti limatanthauza “Chimtengo Chachikulu Cholirirapo”) likusonyeza kuti Yakobo komanso banja lake ankamukonda kwambiri Debora.​—Ge 35:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena