Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
MAY 4-10
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 36-37
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 678
Edomu
Edomu linali dzina lina limene Esau, yemwe anabadwa mapasa ndi Yakobo, anapatsidwa. (Gen. 36:1) Iye anapatsidwa dzinali chifukwa anagulitsa ukulu wake monga woyamba kubadwa ndi chakudya chofiira. (Gen. 25:30-34) Ndiye zinangochitikanso kuti Esau anabadwa ndi thupi lofiira (Gen. 25:25), komanso malo ambiri m’dera limene pambuyo pake iye ndi mbadwa zake anakakhala anali amtundu womwewu.
it-1 561-562
Kuteteza
M’busa akanena kuti azisamalira kapena kuyang’anira ziweto, zinkasonyeza kuti wavomera mwalamulo kuti aziteteza nyamazo. M’busayo ankakhala kuti akutsimikizira mwini ziwetoyo kuti azizidyetsa komanso kuti sizidzabedwa, ndipo kuti ngati ziwetozo zingabedwe m’busayo adzalipira. Komabe, udindo wa m’busayo unkakhala ndi malire chifukwa lamulo lili pamwambali linkanena kuti m’busayo analibe mlandu ngati chinachake choopsa chachitikira nyamazo moti palibe zomwe iye akanachita kuti aziteteze, monga kugwidwa ndi zilombo zolusa. Koma kuti asakhale ndi mlandu, m’busayo ankafunika kupereka umboni kwa mwini ziwetoyo, monga nyama yakufa yomwe yakhadzulidwa ndi zilombo zolusazo. Mwini ziwetozo akaona umboniwo, ankathetsa nkhaniyo chifukwa ankaona kuti m’busayo sanalakwe.
Mfundo imeneyi inkagwiranso ntchito munthu akapatsidwa zinazake kuti aziziyang’anira, ndipo inkagwiranso ntchito kwa anthu apachibale. Mwachitsanzo, mwana wamwamuna woyamba kubadwa ankakhala ndi udindo mwalamulo woyang’anira azichimwene ndi azichemwali ake. Choncho tingathe kumvetsa chifukwa chake Rubeni, yemwe anali woyamba kubadwa, zinamukhudza atamva azichimwene ake akupangana kuti aphe Yosefe, monga mmene lemba la Genesis 37:18-30 limafotokozera. “Iye anati: ‘Ayi, tisachite kuwononga moyo wake.’ . . . ‘Musakhetse magazi ayi. . . . musamuvulaze.’ Cholinga chake chinali chakuti amupulumutse kwa iwo ndi kum’bwezera kwa bambo ake.” Ndipo Rubeni atazindikira kuti Yosefe mulibe m’chitsime muja, anada nkhawa kwambiri moti “anang’amba zovala zake” n’kufuula kuti: “Mwana ujatu kulibe! Kalanga ine, ndilowera kuti ine?” Iye anadziwa kuti akhoza kuimbidwa mlandu chifukwa cha kusowa kwa Yosefe. Pofuna kubisa zomwe anachitazo, azichimwene akewo anapanga umboni wabodza kuti zikhale ngati Yosefe waphedwa ndi chilombo cholusa. Iwo anachita zimenezi poviika mkanjo wa Yosefe wamizeremizere m’magazi a mbuzi. Kenako anatumiza mkanjowo kwa Yakobo bambo awo, amenenso anali ngati woweruza. Iye anathetsa nkhaniyi ndipo anati Rubeni anali wosalakwa chifukwa cha umboni umene azichimwene ake anabweretsa wa mkanjo wa Yosefe womwe unali ndi magazi, zomwe zinachititsa Yakobo kukhulupirira kuti Yosefe waphedwadi.—Gen. 37:31-33.
MAY 11-17
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 38-39
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 555
Onani
Onani anali mwana wachiwiri wamwamuna wa Yuda yemwe anabereka ndi mkazi wachikanani dzina lake Sua. (Gen. 38:2-4; 1 Mbiri 2:3) Mchimwene wake wa Onani dzina lake Ere, yemwe analibe mwana, anaphedwa ndi Yehova chifukwa chochita zoipa. Ere atafa, Yuda anauza Onani kuti akwatire Tamara yemwe anali mkazi wa mchimwene wakeyo. Ngati Onani ndi Tamara akanabereka mwana wamwamuna, mwanayo sakanakhala wa Onani koma ndi amene akanalandira cholowa cha Ere, monga woyamba kubadwa. Koma ngati Onani ndi Tamara akanapanda kubereka mwana, cholowacho chikanakhala cha Onani. Choncho nthawi zonse akagona ndi Tamara, Onani “anali kutaya pansi umuna wake.” Zimene Onani ankachitazi sizinali kudziseweretsa maliseche, chifukwa nkhaniyi imati “nthawi zonse akagona ndi mkazi wa m’bale wakeyo,” iye ankataya pansi umuna wake. Zikuoneka kuti akamagonana ndi Tamara, mwadala Onani ankaimitsa kaye kugonanako akazindikira kuti watsala pang’ono kutulutsa umuna n’cholinga choti asathire umunawo m’maliseche a Tamara. Choncho Yehova anaphanso Onani alibe mwana, osati chifukwa chodziseweretsa maliseche, koma chifukwa sanamvere bambo ake, chifukwa cha dyera, ndiponso chifukwa sanamvere zimene Mulungu ankafuna pa nkhani ya ukwati.—Gen. 38:6-10; 46:12; Num. 26:19.
MAY 25-31
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 42-43
“Yosefe Anasonyeza Kudziletsa Kwambiri”
it-2 108 ¶4
Yosefe
Chifukwa cha zimene zinachitikazi, azichimwene ake a Yosefe anayamba kuganiza kuti Mulungu akuwalanga chifukwa choti anagulitsa Yosefe monga kapolo zaka zingapo m’mbuyomu. Iwo anayamba kukambirana zokhudza kulakwa kwawo Yosefe ali pompo, koma sanamuzindikire. Koma Yosefe atamva zimene ankakambiranazo zomwe zinkasonyeza kuti alapa, zinamukhudza mtima kwambiri moti anachoka n’kupita payekha kukalira. Atabwerako, anamanga Simiyoni ndipo anawauza kuti adzamumasula akadzabwera ndi mng’ono wawo.—Gen. 42:21-24.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 795
Rubeni
Makhalidwe ena abwino a Rubeni anaonekera pamene anachonderera azichimwene ake 9 kuti aponye Yosefe m’chitsime chopanda madzi m’malo momupha, ndipo cholinga chake ponena zimenezi chinali choti abwerere kuchitsimeko mozemba kuti akapulumutse Yosefe. (Gen. 37:18-30) Kenako patatha zaka zoposa 20, azichimwene ake a Yosefe anaimbidwa mlandu waukazitape ku Iguputo ndipo iwo ankaganiza kuti zimenezi zikuwachitikira chifukwa cha nkhanza zomwe anachitira Yosefe. Pa nthawiyi Rubeni anakumbutsa abale akewo kuti iye sanachite nawo chiwembu chofuna kupha Yosefe. (Gen. 42:9-14, 21, 22) Komanso, Yakobo atakana kuti Benjamini apite limodzi ndi abale ake ku Iguputo paulendo wawo wachiwiri, Rubeni ndi amene anapereka ana ake awiri monga chikole. Iye anati: “Ndikapanda kudzam’bwezera kwa inu Benjamini, mudzaphe ana anga awiri.”—Gen. 42:37.