Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
JUNE 1-7
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 44-45
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 813
Kung’amba Zovala
Chizindikiro chofala pakati pa Ayuda komanso anthu a kum’mawa kwa Asia chosonyeza kumva chisoni, makamaka akalandira uthenga woti wachibale wawo wamwalira. Nthawi zambiri ankangong’amba zovalazo pachifuwa pokha osati kung’amba chovala chonse mpaka kufika poti sangathenso kuchivala.
Nkhani yoyamba yopezeka m’Baibulo yokhudza kung’amba zovala ndi ya Rubeni, yemwe anali mwana woyamba wa Yakobo. Rubeni atabwereranso kuchitsime n’kukapeza kuti Yosefe mulibe, anang’amba zovala zake n’kunena kuti: “Mwana ujatu kulibe! Kalanga ine, ndilowera kuti ine?” Monga woyamba kubadwa, Rubeni anali ndi udindo woyang’anira mng’ono wake. Yakobo bambo ake a Rubeni atauzidwa kuti mwana wawo wamwalira, nawonso anang’amba zovala zawo n’kuvala ziguduli (Gen. 37:29, 30, 34), komanso azichimwene ake a Yosefe ali ku Iguputo anang’amba zovala zawo chifukwa cha chisoni, Yosefe atachita zinthu zoti Benjamini aoneke ngati wakuba.—Gen. 44:13.
JUNE 8-14
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 46-47
“Chakudya pa Nthawi ya Njala”
Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala
2 Zaka 7 zokhala ndi chakudya chochuluka zinatha, ndipo njala inayamba monga mmene Yehova ananenera. Njalayi inagwa “padziko lonse lapansi,” osati ku Iguputo kokha. Pamene anthu anjala mu Iguputo anayamba kulirira Farao kuti awapatse chakudya, iye anawauza kuti: “Pitani kwa Yosefe! Zilizonse zimene akuuzeni, chitani zomwezo.” Yosefe anagulitsa tirigu kwa Aiguputo mpaka ndalama zawo zinatha. Kenako iye anayamba kulandira ziweto zawo monga malipiro. Pamapeto pake, anthuwo anabwera kwa Yosefe, ndi kumuuza kuti: “Mutigule limodzi ndi minda yathu potipatsa chakudya kuti tikhale akapolo a Farao.” Choncho Yosefe anagulira Farao dziko lonse la Aiguputo.—Genesis 41:53-57; 47: 13-20.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 220 ¶1
Zochita Zosonyeza Mmene Ukumvera
Kutseka maso a munthu amene wamwalira. Mawu amene Yehova anamuuza Yakobo kuti, “Yosefe ndi amene adzakutseke maso” (Gen. 46:4), ankasonyeza kuti Yosefe ndi amene adzatseke maso a Yakobo pa imfa yake, womwe unali udindo wa mwana wamwamuna woyamba kubadwa. Choncho zikuoneka kuti apa Yehova ankauza Yakobo kuti udindo wa mwana woyamba kubadwa unkayenera kupita kwa Yosefe.—1 Mbiri 5:2.
nwtsty mfundo zophunzirira, Mac. 7:14
Onse pamodzi analipo anthu 75: Sitefano sanagwire mawu vesi linalake m’Malemba Achiheberi pamene ananena kuti anthu onse a m’banja la Yakobo omwe anapita ku Iguputo analipo 75. Nambalayi sipezeka m’Malemba Achiheberi Achimasorete. Lemba la Gen. 46:26 limati: “Ana onse a Yakobo otuluka m’chiuno mwake, amene anali nawo ku Iguputo, analipo 66 onse pamodzi, osawerengera akazi a ana ake.” Vesi 27 limapitiriza kuti: “Onse a m’nyumba ya Yakobo amene anali nawo ku Iguputo analipo 70.” Pamavesiwa, anthuwa akuwerengedwa m’njira ziwiri zosiyana. Zikuoneka kuti chiwerengero choyamba ndi cha mbadwa zake zenizeni, pamene chiwerengero chachiwiri ndi cha anthu onse omwe anapita ku Iguputo. Chiwerengero cha mbadwa za Yakobo chimatchulidwanso pa Eks. 1:5 ndi pa Deut. 10:22, kuti ndi “70.” Zikuoneka kuti Sitefano akutchula chiwerengero chachitatu chomwe chikuphatikizapo achibale enanso a Yakobo. Anthu ena amanena kuti achibalewa akuphatikizapo ana aamuna ndi zidzukulu za Manase ndi Efuraimu, omwe amatchulidwa m’Baibulo la Septuagint pa Gen. 46:20. Manase ndi Efuraimu anali ana a Yosefe. Anthu enanso amanena kuti chiwerengerochi chikuphatikizapo akazi a ana a Yakobo omwe sanaphatikizidwe pa chiwerengero cha pa Gen. 46:26. Choncho nambala ya “75” ikhoza kukhala chiwerengero cha anthu onse. Komabe, chiwerengerochi chiyenera kuti chinkapezeka m’mipukutu ya Malemba Achiheberi omwe ankagwiritsidwa ntchito m’nthawi ya atumwi. Kwa zaka zambiri, akatswiri amaphunziro akhala akunena kuti nambala yopezeka pa Gen. 46:27 ndi pa Eks. 1:5 m’Baibulo la Chigiriki la Septuagint, ndi “75.” Kuwonjezera pamenepo, cha m’ma 1950, zidutswa ziwiri za Mpukutu wa ku Nyanja Yakufa pomwe panali lemba la Eks. 1:5 m’Chiheberi, zinapezeka. Zidutswazi zinalinso ndi nambala ya “75.” Nambala yomwe Sitefano anatchula iyenera kuti inachokera pa chimodzi mwa zidutswa zakalekalezi. Kaya mfundo yolondola ndi iti, nambala imene Sitefano anatchula ikungosonyeza njira ina yowerengera kuchuluka kwa mbadwa za Yakobo.
JUNE 15-21
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 48-50
“Achikulire Angatiphunzitse Zambiri”
it-1 1246 ¶8
Yakobo
Yakobo atatsala pang’ono kufa anadalitsa zidzukulu zake, Efraimu ndi Manase, omwe anali ana a Yosefe. Motsogoleredwa ndi Mulungu, iye anaika Efraimu yemwe anali wamng’ono patsogolo pa Manase yemwe anali wamkulu. Kenako Yakobo, anauza Yosefe yemwe anali kudzalandira cholowa cha mwana woyamba kubadwa kuwirikiza kawiri, kuti: “Ndikukuwonjezera gawo limodzi la dziko kuposa abale ako, limene ndinalanda Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.” (Gen. 48:1-22; 1 Mbiri 5:1) Popeza kuti Yakobo anagula malo amene anali pafupi ndi Sekemu kwa ana a Hamori mwamtendere (Gen. 33:19, 20), zikuoneka kuti Yakobo ankasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro pamene ankauza Yosefe lonjezoli, lomwe analifotokoza monga ulosi kuti mbadwa zake m’tsogolo zidzalanda dziko la Kanani, zomwe zinali ngati zachitika kale pogwiritsa ntchito lupanga ndi uta wake. (Onani AAMORI.) Dziko la Kanani litagonjetsedwa, cholowa chowirikiza kawiri cha Yosefe chinali malo awiri omwe anaperekedwa ku mafuko a Efraimu ndi Manase.
it-2 206 ¶1
Masiku Otsiriza
Ulosi wa Yakobo Atatsala Pang’ono Kufa. Pamene Yakobo anauza ana ake kuti “Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzachitika kwa inu m’masiku am’tsogolo” kapena kuti “m’masiku omaliza,” ankatanthauza za nthawi ya m’tsogolo pamene mawu ake adzayambe kukwaniritsidwa. (Gen. 49:1) Zaka zoposa 200 m’mbuyomo, Yehova anauza Abulahamu yemwe anali agogo ake a Yakobo kuti mbewu yake idzakumana ndi mavuto kwa zaka 400. (Gen. 15:13) Choncho, masiku am’tsogolo omwe Yakobo anawatchula kuti “masiku omaliza,” sakanayamba mpaka zaka 400 za kuvutika kwa mbewu yake zitatha. Ulosiwu unali kudzakwaniritsidwanso m’tsogolo pa “Isiraeli wa Mulungu” wauzimu.—Agal. 6:16; Aroma 9:6.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 289 ¶2
Benjamini
Ulosi womwe Yakobo ananena atatsala pang’ono kufa unasonyeza kuti mbadwa za Benjamini zidzakhala ndi luso lomenya nkhondo. Iye anati: “Benjamini adzapitiriza kukhadzula ngati mmbulu. M’mawa adzadya nyama imene wagwira, ndipo madzulo adzagawa zimene wafunkha.” (Gen. 49:27) Omenya nkhondo a fuko la Benjamini ankadziwika ndi luso loponya miyala pogwiritsa ntchito mkono wamanja kapena wamanzere “ndipo sanali kuphonya.” (Ower. 20:16; 1 Mbiri 12:2) Woweruza Ehudi yemwe ankagwiritsa ntchito mkono wamanzere, amene anapha Mfumu Egiloni yomwe inali yankhanza, anali wa fuko la Benjamini. (Ower. 3:15-21) Komanso unali “m’mawa” wa ufumu wa Isiraeli pamene m’fuko la Benjamini, ngakhale kuti linali “fuko laling’ono kwambiri pa mafuko onse,” munachokera mfumu yoyamba ya Isiraeli, Saulo mwana wa Kisi, yemwe anali msilikali wamphamvu pomenyana ndi Afilisiti. (1 Sam. 9:15-17, 21) Komanso inali nthawi ya “madzulo” pamene mtundu wa Isiraeli unapulumutsidwa ndi Mfumukazi Esitere komanso Nduna Yaikulu Moredekai, omwe anali ochokera m’fuko la Benjamini, pa chiwembu chofuna kupha Aisiraeli onse pa nthawi ya Ufumu Waukulu wa Perisiya.—Esitere 2:5-7.
JUNE 29–JULY 5
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 4-5
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 12 ¶5
Yehova
Choncho, “kudziwa” sikutanthauza kungodziwa kuti chinthu chinachake kapena munthu winawake alipo. Nabala, yemwe anali munthu wopusa, ankadziwa dzina la Davide koma anafunsabe kuti, “Kodi Davide ndani?” potanthauza kuti, “Kodi Davide ali n’chiyani?” (1 Sam. 25:9-11; yerekezani ndi 2 Sam. 8:13.) Nayenso Farao anafunsa Mose kuti: “Yehova ndani kuti ndimvere mawu ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite? Ine sindikum’dziwa Yehova ngakhale pang’ono, komanso, sindilola kuti Aisiraeli apite.” (Eks. 5:1, 2) Ponena zimenezi, Farao ankatanthauza kuti sankaona Yehova kukhala Mulungu woona komanso kuti analibe udindo wolamulira mfumu ya Iguputo komanso kulowerera m’zochita zake. Iye ankaonanso kuti Mulungu analibe mphamvu zochitira zimene Mose ndi Aroni ananena. Koma Farao ndi Aiguputo onse, kuphatikizapo Aisiraeli, anadziwa tanthauzo lenileni la dzina lakuti Yehova. Monga mmene Yehova anauzira Mose, zimenezi zinachitika pamene Mulungu anakwaniritsa pangano lomwe anapangana ndi makolo a mtundu wa Isiraeli, pamene anamasula Aisiraeliwo ku ukapolo n’kuwapatsa Dziko Lolonjezedwa. Pochita zimenezi, zinali ngati Yehova akuwauza kuti: “Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.”—Eks. 6:4-8.