Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
JULY 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 6-7
“Tsopano Uona Zimene Ndichite kwa Farao”
it-2 436 ¶3
Mose
Akulu a ku Isiraeli nawonso anasintha kwambiri. Poyamba iwo anakhulupirira Mose, koma ataona kuti Farao akuwagwiritsa ntchito mwankhanza, anayamba kudandaula kwa Mose kuti iye sanachite zinthu zabwino moti Moseyo anafooka ndipo anapempha Yehova kuti achitepo kanthu. (Eks 4:29-31; 5:19-23) Koma pa nthawiyi, Wam’mwambamwamba analimbikitsa Mose pomuuza kuti tsopano akwaniritsa zimene analonjeza Abulahamu, Isaki, ndi Yakobo zomwe ndi kusonyeza tanthauzo la dzina la Yehova polanditsa Aisiraeli n’kuwapanga kukhala mtundu waukulu m’dziko lomwe anawalonjeza. (Eks 6:1-8) Komabe akulu a ku Isiraeli sanamvere Mose. Koma pambuyo pa mliri wa 9, iwo anayamba kumumvera kwambiri moti mliri wa 10 utachitika, Mose anawasonkhanitsa n’kuwatsogolera potuluka mu Iguputo “mwa dongosolo lomenyera nkhondo.”—Eks 13:18.
it-2 436 ¶1-2
Mose
Pamaso pa Farao ku Iguputo. Mose ndi Aroni anakhala anthu ofunika kwambiri ‘pa nkhondo ya milungu.’ Mwakuitana ansembe ochita zamatsenga, omwe n’kutheka kuti ankatsogoleredwa ndi Yane ndi Yambure (2Ti 3:8), Farao anasonkhanitsa mphamvu za milungu yonse ya ku Iguputo kuti zilimbane ndi mphamvu za Yehova. Chozizwitsa choyamba chimene Aroni anachita pamaso pa Farao atauzidwa ndi Mose, chinasonyeza kuti Yehova anali wamphamvu kuposa milungu ya Aiguputo, ngakhale kuti Farao anaumitsabe mtima wake. (Eks 7:8-13) Kenako, kutachitika mliri wachitatu, ngakhalenso ansembe anakakamizika kunena kuti “Chimenechi ndi chala cha Mulungu!” Ndipotu ansembewa anadwala kwambiri ndi mliri wa zithupsa, moti sanathe kuonekera pamaso pa Farao kuti atsutsane ndi Mose.—Eks 8:16-19; 9:10-12.
Miliri imachititsa anthu ena kufewetsa mitima yawo, komanso ena kuumitsa mitima yawo. Mose ndi Aroni ndi amene ankalengeza mliri uliwonse, pa miliri 10 yomwe inachitika. Miliriyo inachitikadi monga mmene ananenera, ndipo zimenezi zinasonyeza kuti Mose anatumidwadi ndi Yehova. Dzina la Yehova linalengezedwa ndipo anthu ambiri ku Iguputo ankangolankhula za dzinali, zomwe zinachititsa ena, monga Aisiraeli komanso Aiguputo ena, kufewetsa mitima yawo koma ena, monga Farao, alangizi ake komanso anthu omwe anali kumbali yake, kuumitsa mitima yawo. (Eks 9:16; 11:10; 12:29-39) Aiguputo anazindikira kuti Yehova ndi amene waweruza milungu yawo, m’malo moganiza kuti iwowo akhumudwitsa milungu yawoyo. Pa nthawi imene mliri wa 9 unkachitika, nayenso Mose “analemekezeka kwambiri m’dziko la Iguputo, pamaso pa atumiki a Farao ndi pamaso pa Aiguputo onse.”—Eks 11:3.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 78 ¶3-4
Wamphamvuyonse
Yehova anagwiritsa ntchito dzina laudindo lakuti “Wamphamvuyonse” (ʼEl Shad·daiʹ) pamene ankachita pangano ndi Abulahamu lokhudza kubadwa kwa Isaki. Abulahamu ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti Yehova anali ndi mphamvu zokwaniritsa lonjezoli. Dzinali linagwiritsidwanso ntchito posonyeza kuti Yehova adzadalitsa Isaki ndi Yakobo monga omwe adzalandire cholowa m’pangano la Abulahamu.—Ge 17:1; 28:3; 35:11; 48:3.
Mogwirizana ndi zimenezi, Yehova anadzauza Mose kuti: “Ndinali kuonekera kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo monga Mulungu Wamphamvuyonse [beʼElʹ Shad·daiʹ]. Koma za dzina langa lakuti Yehova, ine sindinadzidziwikitse kwa iwo.” (Eks 6:3) Zimenezi sizikutanthauza kuti Abulahamu, Isaki ndi Yakobo sankadziwa dzina lakuti Yehova, chifukwa iwowo komanso atumiki ena a m’mbuyomo ankaligwiritsa ntchito pafupipafupi. (Ge 4:1, 26; 14:22; 27:27; 28:16) Ndipotu m’buku la Genesis, lomwe limafotokoza kwambiri za moyo wa atumikiwa, mawu akuti “Wamphamvuyonse” amapezekamo maulendo 6 okha, pomwe dzina lakuti Yehova limapezeka maulendo 172 mu Chiheberi choyambirira. Ngakhale kuti kudzera n’zimene zinawachitikira, atumiki akalewa ankadziwa kuti Mulungu anali ndi ufulu komanso kuti anali woyenerera kudziwika ndi dzina la ulemu lakuti “Wamphamvuyonse,” komabe iwo analibe mwayi wodziwa tanthauzo lonse la dzina lakuti Yehova. Pa nkhani imeneyi, buku lina limanena kuti: “zinthu zimene zinachitikira atumiki akalewa zinali zokhudza malonjezo a m’tsogolo, iwo ankayenera kutsimikizira kuti, Yahweh, ndi amene anali Mulungu ndipo ndi amene anali ndi mphamvu zokwaniritsa malonjezowo. Zimene zinachitika ndi chitsamba zinali zazikulu komanso zofunika kwambiri, zinasonyeza mphamvu za Mulungu ndipo pasanapite nthawi anthu anayamba kulidziwa bwino dzina la Mulungu.”—The Illustrated Bible Dictionary, Vol. 1, p. 572, lolembedwa ndi J. D. Douglas, 1980.
it-2 435 ¶5
Mose
Mose sanaonedwe kuti ndi wosayenera chifukwa chodzikayikira. Mose ankadzikayikira, ndipo ankanena kuti saatha kulankhula. Apatu tikuona Mose wina, wosiyana kwambiri ndi Mose amene tikumudziwa, amene zaka 40 m’mbuyomu ankadziona kuti akhoza kupulumutsa Aisiraeli. Iye anapitiriza kupereka zifukwa kwa Yehova, ndipo pamapeto pake anapempha Yehova kuti apereke ntchitoyi kwa munthu wina chifukwa iyeyo sangakwanitse. Ngakhale kuti zimenezi zinakwiyitsa kwambiri Mulungu, iye sanamusiye Mose koma anamupatsa m’bale wake Aroni kuti akhale womulankhulira. Choncho Mose ankaimira Mulungu, zimene zikutanthauza kuti anakhala ngati “Mulungu” kwa Aroni amene ankalankhula moimira Moseyo. Pamene Mose ankakumana ndi akulu a ku Isiraeli komanso Farao, zikuoneka kuti Mulungu anamupatsa malangizo ndipo Mose, anapereka malangizowo kwa Aroni n’cholinga choti Aroniyo akalankhule pamaso pa Farao (Farao ameneyu ndi amene analowa m’malo mwa Farao yemwe Mose anamuthawa zaka 40 m’mbuyomo). (Eks 2:23; 4:10-17) Kenako, Yehova ananena kuti Aroni anali “mneneri” wa Mose kutanthauza kuti, monga mmene Mose analili mneneri wa Mulungu, n’kumatsogoleredwa ndi Mulunguyo, nayenso Aroni ankayenera kumatsogoleredwa ndi Mose. Komanso Mulungu anamuuza Mose kuti wamuika kukhala “Mulungu kwa Farao,” kutanthauza kuti Mose anapatsidwa mphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu pa Farao, choncho panthawiyi sankafunika kuopa mfumu ya Iguputoyi.—Eks 7:1, 2.
JULY 13-19
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 8-9
“Farao Yemwe Anali Wonyada Anathandiza Kukwaniritsa Cholinga cha Mulungu Mosadziwa”
it-2 1040-1041
Kuumitsa Mtima
Pochita zinthu ndi anthu, Yehova Mulungu amaleza mtima kuti anthuwo kapena mtunduwo, ngakhale kuti ndi oyenera kuphedwa, ukhalebe ndi moyo. (Ge 15:16; 2Pe 3:9) Anthu ena amapezerapo mwayi n’kusintha kuti athe kuchitiridwa chifundo (Yos 2:8-14; 6:22, 23; 9:3-15), koma ena amaumitsabe mitima yawo n’kumapitiriza kutsutsana ndi Yehova komanso anthu ake. (De 2:30-33; Yos 11:19, 20) Popeza Yehova saletsa anthu kuchita zofuna za mtima wawo, Baibulo limati iye amalola anthu ‘kuumitsa mitima yawo.’ Koma pamapeto pake amapereka chilango kwa anthuwo, ndipo zimenezi zimachititsa kuti mphamvu zake ziwonekere komanso kuti dzina lake lilengezedwe.—Yerekezerani ndi Eks 4:21; Yoh 12:40; Aro 9:14-18.
it-2 1181 ¶3-5
Kuipa
Kuwonjezera pamenepo, Yehova Mulungu amagwiritsa ntchito zochitika zinazake kuti anthu oipa athandize kukwaniritsa cholinga chake mosadziwa. Ngakhale kuti iwo amatsutsa Mulungu, iye amateteza atumiki ake okhulupirika kwa anthu oipawo, ndipo akhoza kupangitsa kuti zochita za anthuwo zithandize kuti chilungamo chake chionekere. (Aro 3:3-5, 23-26; 8:35-39; Sl 76:10) Mfundo imeneyi ikufotokozedwanso bwino pa lemba la Miyambo 16:4: “Yehova anapanga chilichonse n’cholinga, ndipo ngakhale woipa anamusungira tsiku loipa.”
Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi Farao, yemwe kudzera mwa Mose ndi Aroni, Yehova anamuuza kuti amasule Aisiraeli ku ukapolo. Sikuti Mulungu ndi amene anachititsa mfumu ya Iguputoyi kukhala yoipa, koma anamulola kupitirizabe kukhala ndi moyo. Anachitanso zinthu zomwe zinachititsa kuti Faraoyo aonekere poyera kuti anali munthu woipa ndi woyenera kuphedwa. Cholinga cha Yehova pochita zimenezi chimatchulidwa pa Ekisodo 9:16: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”
Yehova anasonyeza mphamvu zake m’njira yodabwitsa kwambiri pamene anagwetsera Aiguputo Miliri 10, komanso pamene anawonongeratu Farao ndi asilikali ake onse pa Nyanja Yofiira. (Eks 7:14–12:30; Sl 78:43-51; 136:15) Patadutsa zaka zambiri, anthu a mitundu ina omwe ankakhala mozungulira Aisiraeli ankalankhulabe za zinthu zomwe zinachitikazi, ndipo zimenezi zinachititsa kuti dzina la Mulungu lilengezedwe padziko lonse lapansi. (Yos 2:10, 11; 1Sa 4:8) Yehova akanati aphe Farao mwamsanga, mphamvu zake zodabwitsazi zomwe zinachititsa kuti alemekezedwe komanso kuti apulumutse anthu ake, sizikanaonekera.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 878
Tizilombo Touluka Toyamwa Magazi
Tizilombo teniteni tomwe Malemba amafotokoza kuti tinali mliri wa 4 ku Iguputo, sitidziwika bwinobwino. Mliri umenewu unali woyamba kuti Aisiraeli omwe ankakhala ku Goseni usawakhudze.—Eks 8:21, 22, 24, 29, 31; Sl 78:45; 105:31.
Tizilombo touluka toyamwa magazi tomwe tinali mliri wa 4 ku Iguputo tiyenera kuti tinkaluma nyama kapena munthu n’kuyamwa magazi ake. Tizilomboti tisanakule timakhala kaye mbozi, ndipo mbozizi zimakhala pathupi la nyama kapena anthu. Koma mbozi zimene zimakhala pamatupi a anthu, zimapezeka m’madera otentha. Choncho mliri wa tizilombo touluka toyamwa magazi uyenera kuti unali wosautsa kwambiri kwa Aiguputo komanso ziweto zawo, chifukwa nthawi zina, ziwetozo kapena anthuwo, ankafa.
JULY 20-26
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 10-11
“Mose ndi Aroni Anasonyeza Kulimba Mtima Kwambiri”
it-2 436 ¶4
Mose
Kukumana ndi Farao kunkafunika kulimba mtima komanso chikhulupiriro. Mose ndi Aroni anakwanitsa kuchita utumiki umene Yehova anawapatsa, mothandizidwa ndi mphamvu zake komanso motsogoleredwa ndi mzimu wake woyera. Taganizirani za bwalo lomwe Farao, yemwe panthawiyo anali mfumu yamphamvu kwambiri padziko lonse, ankagwiriramo ntchito zake monga mfumu. Anali malo a ulemelero amene Farao, yemwe anali wonyada kwambiri mpaka kumadziona ngati mulungu, ankakhala atazunguliridwa ndi alangizi ake, akuluakulu a asilikali, alonda komanso akapolo ake. Panalinso atsogoleri azipembedzo komanso ansembe ochita zamatsenga, omwe ankatsutsa kwambiri Mose. Kupatulapo Farao, magulu awiriwa analinso ndi mphamvu kwambiri mu ufumuwu. Anthu onsewa anali ku mbali ya Farao kuti ateteze milungu ya Iguputo. Koma Mose ndi Aroni sanapite kwa Farao kamodzi kokha, koma kambirimbiri, ndipo ulendo uliwonse umene apitako, Farao ankaumitsabe mtima wake chifukwa ankafunitsitsa kumalamulirabe akapolo ake a Chiheberi omwe anali akhama kwambiri. Ndipotu atangolengeza za mliri wa 8, Mose ndi Aroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao. Kenako atalengeza mliri wa 9, anauzidwa kuti asadzaonekerenso pamaso pa Farao, chifukwa akadzangoonekeranso, adzafa.—Eks 10:11, 28.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Mboni Zotsutsa Milungu Yonama
11 Pamene Aisiraeli anali ku Iguputo, Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao pakuti ndalola iye pamodzi ndi atumiki ake kuumitsa mitima yawo, kuti ndichite zizindikiro zanga pamaso pake. Ndachita zimenezi kuti mufotokozere ana anu, ndi ana a ana anu, mmene ndakhaulitsira Iguputo ndi zizindikiro zimene ndachitira Aiguputo. Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Ekisodo 10:1, 2) Aisiraeli omvera ankayenera kuuza ana awo ntchito zamphamvu za Yehova. Ana awonso, ankayenera kudzauza ana awo, zinkayenera kukhala choncho ku mibadwomibadwo. Zimenezi zikanawathandiza kuti azikumbukira ntchito zamphamvu za Yehova. Masiku anonso, makolo ali ndi udindo wouza ana awo ntchito za mphamvu za Yehova.—Deuteronomo 6:4-7; Miyambo 22:6.
it-1 783 ¶5
Ulendo Wochoka ku Iguputo
Choncho zimene Yehova anachita posonyeza mphamvu zake m’njira yodabwitsa kwambiri, zinachititsa kuti dzina lake likwezedwe komanso Aisiraeli apulumuke. Atafika bwinobwino kum’mawa kwa Nyanja Yofiira, Mose anatsogolera ana a Isiraeli poimba nyimbo, ndipo Miriamu mlongo wake, yemwe anali mneneri wamkazi, anatenga maseche m’manja mwake ndipo anatsogolera akazi enanso omwe anatenga maseche komanso omwe ankavina, ndipo ankathirira mang’ombe nyimbo imene amuna ankaimba. (Eks 15:1, 20, 21) Apa Aisiraeli anali atasiyaniranatu ndi adani awo onse. Pamene ankatuluka mu Iguputo, panalibe munthu kapena chiweto chawo chimene chikanavulazidwa. Ndipo ngakhalenso galu sakanauwa aliyense wa iwo. (Eks 11:7) Ngakhale kuti buku la Ekisodo silifotokoza kuti Farao anafa limodzi ndi asilikali ake panyanja, lemba la Salimo 136:15 limanena kuti Yehova “anakutumulira Farao ndi gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiira.”
JULY 27–AUGUST 2
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 12
“Kufunika kwa Mwambo wa Pasika kwa Akhristu”
it-2 583 ¶6
Pasika
Zinthu zina zomwe zinkachitika pa mwambo wa Pasika zinakwaniritsidwa ndi Yesu. Mwachitsanzo, magazi omwe anapakidwa pa nyumba za Aisiraeli pamene anali ku Iguputo anathandiza kuti mngelo wowononga asaphe mwana woyamba kubadwa wa m’nyumbamo. Paulo anati Akhristu odzozedwa ndi mpingo wa woyamba kubadwa (Ahe 12:23), ndipo Khristu ndi mpulumutsi wawo kudzera m’magazi ake. (1At 1:10; Aef 1:7) Pa Pasika, mafupa a mwanawankhosa sankayenera kuthyoledwa. Kunaloseredwanso kuti palibe fupa la Yesu ngakhale limodzi limene lidzathyoledwe, ndipo zimenezi zinakwaniritsidwa pa imfa yake. (Sl 34:20; Yoh 19:36) Choncho mwambo wa Pasika umene Ayuda anakhala akuchita kwa zaka zambiri unali chimodzi mwa zinthu zimene Chilamulo chinkachitira mthunzi zinthu zimene zinkabwera. Mwambowu unkanena za Yesu Khristu, “Mwanawankhosa wa Mulungu.”—Ahe 10:1; Yoh 1:29.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 582 ¶2
Pasika
Miliri yonse 10 imene inagwera Aiguputo kunali kuweruza milungu yawo, makamaka wa 10 womwe ana oyamba kubadwa anafa. (Eks 12:12) Nkhosa yamphongo inali yopatulika chifukwa inkaimira mulungu wawo dzina lake Ra, choncho kuwaza magazi a nkhosa pamafelemu a nyumba zawo pa Pasika, kunali ngati kunyoza mulungu pamaso pa Aiguputo. Komanso ng’ombe yamphongo inali yopatulika, choncho kupha ng’ombe zamphongo zoyamba kubadwa kunali ngati kukhaulitsa mulungu wawo Osirisi. Farao nayenso ankalambiridwa chifukwa anthu ankamuona ngati mwana wa Ra. Choncho kuphedwa kwa mwana woyamba kubadwa wa Farao kunasonyeza kuti mulungu wawoyo komanso Farao alibe mphamvu.
it-1 504 ¶1
Misonkhano
Chinthu chapadera kwambiri ndi “misonkhano yopatulika” yonseyi ndi chakuti panthawiyi anthu sankagwira ntchito iliyonse. Mwachitsanzo, tsiku loyamba komanso la 7 la Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa anali masiku a “misonkhano yopatulika,” omwe Yehova ananena kuti: “Masiku amenewa musamadzagwire ntchito. Koma chakudya choti munthu aliyense adye, chimenecho chokha muzidzaphika.” (Eks 12:15, 16) Komabe pa ‘misonkhano yopatulikayi,’ ansembe ankatanganidwa ndi kupereka nsembe kwa Yehova. (Le 23:37, 38) Pamenepatu sikuti iwo ankaphwanya lamulo lililonse loletsa anthu kugwira ntchito zawo za tsiku ndi tsiku. Nthawi ya zochitikazi sikuti inali yoti anthu azingokhala osachita chilichonse koma m’malomwake inali yoti azipindula ndi zinthu zauzimu. Pa Tsiku la Sabata mlungu uliwonse, anthu ankasonkhana pamodzi kuti alambire komanso alandire malangizo ndipo kenako ankaphunzitsidwa Mawu a Mulungu. Munthu wina ankawerenga mawuwo kenako n’kuwafotokozera ngati mmene zinalili m’masunagoge ena. (Mac 15:21) Chifukwa chakuti anthuwa sankagwira ntchito iliyonse pa tsiku la sabata kapena pa masiku a “misonkhano yopatulika,” ankakhala ndi nthawi yambiri yopemphera komanso yosinkhasinkha za Mlengi ndi zolinga zake.