Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
AUGUST 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 13-14
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 1117
Msewu Waukulu, Msewu
Kuyambira kalekale misewu ikuluikulu komanso misewu ina, kuphatikizapo njira zambiri zofunika kwa amalonda, zinkalumikiza mizinda komanso maufumu ku Palesitina. (Nu 20:17-19; 21:21, 22; 22:5, 21-23; Yos 2:22; Owe 21:19; 1Sa 6:9, 12; 13:17, 18) Njira imene anthu ambiri ankagwiritsa ntchito inkachokera ku Iguputo kupita kumizinda ya Afilisiti ya Gaza ndi Asikeloni ndipo kenako inkalowera kumpoto chakum’mawa kupita ku Megido. Inkapitirira ku Hazori kumpoto kwa Nyanja ya Galileya, mpaka kukafika ku Damasiko. Njirayi, yomwe inkadutsa m’dera la Afilisiti, ndi imene inali yaifupi kuchokera ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa. Koma mwachikondi Yehova anatsogolera Aisiraeli kuti adutse njira ina kuopera kuti angataye mtima ngati Afilisti angawaukire.—Eks 13:17.
it-1 782 ¶2-3
Ulendo Wochoka ku Iguputo
Kodi ndi pati pamene Nyanja Yofiira inagawikana kuti Aisiraeli awoloke?
Atafika pamalo achiwiri omwe anamanga msasa wawo ku Etamu “m’malire a chipululu,” Mulungu anauza Mose kuti “abwerere ndi kumanga msasa pafupi ndi Pihahiroti . . . pafupi ndi nyanja.” Zimenezi zikanachititsa Farao kuganiza kuti Aisiraeli “asokonezeka ndipo akungoyendayenda.” (Eks 13:20; 14:1-3) Akatswiri omwe amanena kuti Aisiraeli anagwiritsa ntchito njira ya el Haj, amati mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “abwerere” amasonyeza kulamula ndipo samangotanthauza “kusintha kopita” koma amanena za kubwerera kapena kugwiritsa ntchito njira ina. Iwo amanena kuti Aisiraeli atafika malo enaake kumpoto kwa nyanja yotchedwa Gulf of Suez, anayamba kubwerera n’kumalowera kum’mawa kwa mapiri a Jebel ʽAtaqah, omwe ali m’mbali yakumadzulo kwa nyanja ya Gulf of Suez. M’dera limeneli, lomwe mbali ina kunali nyanja, gulu lalikulu ngati la Aisiraeli likanavutika kuthawa mofulumira ngati adani awo akanayamba kuwathamangitsa kuchokera kumpoto.
Zimenezi zikugwirizana ndi zimene mabuku a Chiyuda a m’nthawi ya atumwi amanena. Koma chofunika kwambiri n’chakuti zikugwirizananso ndi zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Komatu zimene akatswiri ambiri amanena sizigwirizana ndi zimene Baibulo limafotokoza. (Eks 14:9-16) Zikuoneka kuti Aisiraeli sanawolokere Nyanja Yofiira kumapeto kwenikweni kwa Gulf of Suez (womwe ndi mkono wakumadzulo wa Nyanja Yofiira). Koma anawolokera pamalo enaake apatali moti Farao ndi asilikali ake sakanatha kungozungulira Gulf of Suez n’kupeza Aisiraeliwo mosavuta kutsidya lina.—Eks 14:22, 23.
AUGUST 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 15-16
“Tamandani Yehova Poimba Nyimbo”
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Mulungu Woona Panopa?
11 Yehova atawononga asilikali a Aiguputo, atumiki ake anayamba kumulemekeza kwambiri ndipo dzina lake linadziwika kumadera ambiri. (Yoswa 2:9, 10; 4:23, 24) Dzina lake linakhala lolemekezeka kwambiri kusiyana ndi mayina a milungu yonyenga ya ku Iguputo yomwe inalibe mphamvu ndipo inalephera kupulumutsa anthu awo. Aiguputo anagwiritsidwa mwala chifukwa chokhulupirira anthu, zida zankhondo komanso milungu yawo. (Salimo 146:3) M’pake kuti Aisiraeli anaimba nyimbo zotamanda Mulungu wawo, yemwe ndi wamoyo komanso amapulumutsa anthu ake. Pochita zimenezi anasonyeza kuti ankamuopa.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Mulungu Woona Panopa?
15 Ngati ifenso tikanapulumuka limodzi ndi Mose pa nthawiyo, n’zosachita kufunsa kuti tikanaimba nawo nyimbo iyi: “Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova? Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu? Ndinu woyenera kuopedwa ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda. Inu ndinu wochita zodabwitsa.” (Ekisodo 15:11) Kuyambira nthawi imeneyo, anthu akhala akunena mawu ngati amenewa. M’buku lomaliza la Baibulo, mtumwi Yohane anafotokoza za gulu la atumiki odzozedwa komanso okhulupirika a Mulungu kuti: “Iwo akuimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa.” Kodi nyimboyi ndi iti? Ndi yakuti: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njira zanu ndi zolungama ndi zoona, inu Mfumu yamuyaya. Kodi ndani sadzakuopani, inu Yehova? Ndani sadzalemekeza dzina lanu? Pakuti inu nokha ndinu wokhulupirika.”—Chivumbulutso 15:2-4.
16 Masiku anonso pali anthu amene akulambira Mulungu omwe anamasulidwa ku ukapolo wauzimu ndipo amayamikira zinthu zimene iye analenga komanso amakonda malamulo ake. Anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana amasulidwa ku ukapolo wauzimu ndi ku zinthu zoipa zam’dzikoli chifukwa chozindikira kuti malamulo a Mulungu ndi olungama ndipo anayamba kuwatsatira. Chaka chilichonse anthu masauzande ambiri amachoka m’dziko loipali n’kulowa m’gulu loyera la atumiki a Yehova. Posachedwapa, Mulungu akadzawononga chipembedzo chonyenga komanso zinthu zonse zoipa zam’dzikoli, atumiki a Yehovawa adzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lamtendere.
it-2 454 ¶1
Nyimbo
Ku Isiraeli, akamaimba nyimbo pagulu, nthawi zambiri ankaimba molandizana mawu. Pena gulu limodzi linkaimba mzere umodzi ndipo gulu lina linkaimba mzere wotsatira. Kapenanso munthu mmodzi ankaimba mzerewo kenako gulu la anthu linkaimba mzere wina pomuyankha. Malemba amatchula kuimba kotereku kuti ‘kuthirira mang’ombe’ kapena “kuimba molandizana mawu.” (Eks 15:21; 1Sa 18:6, 7) Masalimo ena monga Salimo 136 amasonyeza kuti Aisiraeli ankaimba m’njira imeneyi. Zimene Baibulo limafotokoza zokhudza magulu awiri oimba nyimbo zoyamika m’nthawi ya Nehemiya komanso zimene anachita pa mwambo wotsegulira mpanda wa Yerusalemu zimasonyezanso kuti ankaimba m’njira imeneyi.—Ne 12:31, 38, 40-42.
it-2 698
Mneneri Wamkazi
Mkazi woyamba amene Baibulo limanena kuti anali mneneri ndi Miriamu. Zikuoneka kuti Mulungu anamugwiritsa ntchito kuti apereke uthenga kapena mauthenga ndipo mwina anapereka mauthengawo poimba nyimbo. (Eks 15:20, 21) N’chifukwa chake Baibulo limasonyeza kuti iye ndi Aroni ananena kwa Mose kuti: “Kodi [Yehova] sanalankhulenso kudzera kwa ife?” (Nu 12:2) Nayenso Yehova ananena kudzera mwa mneneri Mika kuti anatumiza “Mose, Aroni ndi Miriamu” kuti akathandize Aisiraeli kuchoka ku Iguputo. (Mik 6:4) Ngakhale kuti Miriamu anali ndi mwayi wogwiritsidwa ntchito ndi Yehova kuti apereke mauthenga, udindo wake pa nkhaniyi unali wochepa poyerekezera ndi wa mchimwene wake Mose. Pamene iye anafuna udindo woposa umene anali nawo, analangidwa kwambiri ndi Mulungu.—Nu 12:1-15.
AUGUST 17-23
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 17-18
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 406
Mabuku Ovomerezeka
Tikaona zimene zili m’mabuku amene Mose analemba, pali umboni wosatsutsika wosonyeza kuti mabuku amenewa ndi ouziridwa ndi Mulungu, oyenera kukhala m’Baibulo komanso othandiza polambira Mulungu moyenera. Mose sanadziike yekha kukhala mtsogoleri wa Aisiraeli. Paja pamene Mulungu ankamuuza kuti awatsogolere iye ankakayikakayika. (Eks 3:10, 11; 4:10-14) Koma Mulungu anathandiza Mose kuchita zimenezi ndipo anamupatsa mphamvu zochita zodabwitsa moti ngakhale ansembe a Farao ochita zamatsenga anafika povomereza kuti mphamvu za Mose zinachokera kwa Mulungu. (Eks 4:1-9; 8:16-19) Choncho sikuti poyamba Mose ankafuna kumalankhula pagulu kapenanso kumalemba mabuku. Koma anachita zimenezi pomvera Mulungu komanso chifukwa chopatsidwa mzimu woyera.—Eks 17:14.
AUGUST 24-30
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 19-20
“Mmene Malamulo 10 Amakukhudzirani”
Kodi Malamulo 10 Amakukhudzani Bwanji?
Malamulo oyambirira 4 amasonyeza zimene tiyenera kuchitira Yehova. (Loyamba) Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti tizimutumikira iye yekha basi. (Mateyu 4:10) (Lachiwiri) Anthu omulambira sayenera kugwiritsa ntchito mafano. (1 Yohane 5:21) (Lachitatu) Nthawi zonse tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu moyenera komanso mwaulemu, osati momunyoza. (Yohane 17:26; Aroma 10:13) (La Nambala 4) Tiyenera kuika kutumikira Mulungu pamalo oyamba pa moyo wathu. Zimenezi zimatithandiza kusiya kuchita zinthu zodzisonyeza kuti ndife olungama ndipo tikatero timakhala ngati tapuma kapena kuti ‘tasunga sabata.’—Aheberi 4:9, 10.
Kodi Malamulo 10 Amakukhudzani Bwanji?
(La Nambala 5) Ngakhale masiku ano, ana akamamvera makolo awo zimathandiza kwambiri kuti banja likhale logwirizana komanso kuti Yehova azilidalitsa. Ili ndi “lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo” ndipo ndi lothandizadi kwambiri. Paja Baibulo limatilimbikitsa kumvera lamuloli ‘kuti zinthu zitiyendere bwino’ komanso kuti ‘tikhale ndi moyo wautali padziko lapansi.’ (Aefeso 6:1-3) Popeza tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dziko loipali, kumvera lamulo la Mulungu limeneli kungathandize achinyamata kuti apitirize kukhala ndi moyo mpaka kalekale.—2 Timoteyo 3:1; Yohane 11:26.
Kukonda anzathu kungatithandize kuti tisawachitire zoipa monga (La Nambala 6) kupha munthu, (La Nambala 7) kuchita chigololo, (La Nambala 8) kuba komanso (La Nambala 9) kunama. (1Yohane 3:10-12; Aheberi 13:4; Aefeso 4:28; Mateyu 5:37; Miyambo 6:16-19) Koma kodi Malamulo 10 amenewa amakhudzanso zolinga zathu? Lamulo (La Nambala 10) loletsa kusirira limatikumbutsa kuti Yehova amafuna kuti zolinga zathu zizikhalanso zomusangalatsa.—Miyambo 21:2.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 687 ¶1-2
Wansembe
Ansembe a Chikhristu. Yehova analonjeza Aisiraeli kuti akasunga pangano limene anapangana nawo adzakhala ‘ufumu wake wa ansembe ndi mtundu wake woyera.’ (Eks 19:6) Koma unsembe wa m’banja la Aroni unali mthunzi chabe wa unsembe wofunika kwambiri wam’tsogolo ndipo unkangoyenera kukhalapo mpaka unsembe winawo utayamba. (Ahe 8:4, 5) Unsembewo unkayenera kupitirira mpaka pamene pangano la Chilamulo linatha komanso pangano latsopano linayamba. (Ahe 7:11-14; 8:6, 7, 13) Poyamba Yehova anaitana Aisiraeli kuti adzakhale ansembe mu Ufumu umene analonjeza koma kenako anaitananso anthu amitundu ina.—Mac 10:34, 35; 15:14; Aro 10:21.
Ayuda ochepa ndi amene anatsatira Khristu choncho mtundu wa Isiraeli unalephera kukhala ndi anthu okwanira kuti apange ufumu weniweni wa ansembe ndi mtundu woyera. (Aro 11:7, 20) Mulungu anali atachenjeza Aisiraeli za zimenezi zaka zambiri m’mbuyomu chifukwa choti sanali okhulupirika. Kudzera mwa mneneri Hoseya, anawachenjeza kuti: “Anthu anga adzawonongedwa chifukwa sakundidziwa. Popeza iwo akana kundidziwa, inenso ndidzawakana kuti azinditumikira ngati wansembe wanga. Popeza iwo aiwala lamulo la ine Mulungu wawo, inenso ndidzaiwala ana awo.” (Ho 4:6) Mogwirizana ndi mawuwa, Yesu anauza atsogoleri a Chiyuda kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” (Mt 21:43) Ngakhale zinali choncho, Chilamulo chinkagwirabe ntchito pamene Yesu Khristu anali padzikoli ndipo iye ankalemekeza ansembe a m’banja la Aroni moti anauza anthu odwala khate omwe anawachiritsa kuti apite kwa wansembe n’kukapereka nsembe yoyenera.—Mt 8:4; Mko 1:44; Lu 17:14.
AUGUST 31–SEPTEMBER 6
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 21-22
“Muzisonyeza Kuti Mumaona Moyo Mmene Yehova Amauonera”
it-1 271
Kumenya
Mheberi amene anali ndi akapolo ankaloledwa kumenya kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi ndi ndodo ngati sakumumvera. Koma ngati kapoloyo anafa chifukwa chomenyedwa, mbuyeyo ankafunika kulangidwa. Ngati kapoloyo anakhalabe moyo kwa tsiku limodzi kapena masiku awiri pambuyo pomenyedwa, zimenezi zinkakhala umboni wakuti mbuyeyo sankafuna kumupha. Mbuyeyo anali ndi ufulu wolanga kapolo wake chifukwa kapoloyo anali “chuma chake.” Ndipo palibe munthu amene angafune kuchita zinthu zimene zingawononge chuma chake. Komanso ngati kapolo angafe patapita tsiku limodzi kapena masiku angapo, sizingadziwike ngati anafa chifukwa chomenyedwa kapena chifukwa cha zinthu zina. Choncho ngati kapolo anakhalabe ndi moyo kwa tsiku limodzi kapena masiku awiri, mbuye wake sankalangidwa.—Eks 21:20, 21.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 1143
Nyanga
Mawu a pa Ekisodo 21:14 angatanthauze kuti ngakhale wansembe amene wapha munthu ankayenera kuphedwa. Kapena angatanthauzenso kuti kugwira nyanga za guwa lansembe sikunkateteza munthu amene wapha mwadala munthu wina.—Yerekezerani ndi 1Mf 2:28-34.