Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr20 September tsamba 1-5
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
  • Timitu
  • SEPTEMBER 7-13
  • SEPTEMBER 14-20
  • SEPTEMBER 21-27
  • SEPTEMBER 28–​OCTOBER 4
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
mwbr20 September tsamba 1-5

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

SEPTEMBER 7-13

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 23-24

“Musamatsatire Khamu la Anthu”

it-1 11 ¶3

Aroni

N’zochititsa chidwi kuti pa nthawi zitatu zimene Aroni anayamba kuchita zinthu zolakwika kwambiri, si iye amene anayambitsa zolakwikazo. Koma zikuoneka kuti anatengeka ndi zimene anthu ena ankafuna kapena ndi mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Iye akanachita bwino kutsatira mfundo ya lamulo lakuti: “Usatsatire khamu pochita zoipa,” makamaka pa nthawi yoyamba imene anachita zolakwika. (Eks 23:2) Koma Malemba amanenabe zinthu zolemekeza Aroni ndipo Mwana wa Mulungu ali padzikoli ankalemekeza unsembe wa m’banja la Aroni.​—Sl 115:10, 12; 118:3; 133:1, 2; 135:19; Mt 5:17-19; 8:4.

it-1 343 ¶5

Vuto Losaona

Kuweruza nkhani mopanda chilungamo chifukwa cha chiphuphu kapena tsankho kunkayerekezeredwa ndi vuto losaona. M’Chilamulo munali malangizo ambiri okhudza chiphuphu kapena tsankho chifukwa zinthu ngati zimenezi zingalepheretse woweruza kuona zinthu moyenera poweruza nkhani. Paja Chilamulo chimati: “Chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa.” (Eks 23:8) Chimanenanso kuti: “Chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru.” (De 16:19) Woweruza akalandira mphatso kwa munthu amene wakhudzidwa ndi mlandu, akhoza kuweruza mopanda chilungamo ndipo zimenezi zingachitike akufuna kapena asakufuna. Angachite zimenezi ngakhale kuti ndi woweruza wabwino komanso wanzeru. Malamulo a Mulungu amafotokoza momveka bwino mmene kupatsidwa mphatso kapena kukondera kungachititsire kuti munthu asaone zinthu moyenera. Paja lamulo lina limati: “Musamakondere munthu wosauka, ndiponso musamakondere munthu wolemera.” (Le 19:15) Choncho woweruza sankayenera kuweruza anthu achuma mopanda chilungamo chifukwa chokondera kapena kufuna kusangalatsa anthu ambiri.​—Eks 23:2, 3.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 393

Mikayeli

1. Mikayeli komanso Gabirieli ndi angelo oyera okha amene Baibulo limatchula mayina awo koma Mikayeli yekha ndi amene amatchulidwa kuti “mkulu wa angelo.” (Yuda 9) Dzina loti Mikayeli limatchulidwa koyamba m’chaputala 10 cha buku la Danieli pamene limanena kuti iye ndi “mmodzi mwa akalonga aakulu” ndipo anathandiza mngelo wamng’ono amene ankalimbana ndi “kalonga wa ufumu wa Perisiya.” Mikayeli anatchulidwa kuti “kalonga wa anthu [a Danieli]” komanso “kalonga wamkulu amene waimirira kuti athandize anthu a [Danieli].” (Da 10:13, 20, 21; 12:1) Izi zimasonyeza kuti Mikayeli anali mngelo amene anatsogolera Aisiraeli m’chipululu. (Eks 23:20, 21, 23; 32:34; 33:2) Timadziwanso zimenezi chifukwa Baibulo limanena kuti “Mikayeli mkulu wa angelo anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose.”​—Yuda 9.

SEPTEMBER 14-20

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 25-26

“Chinthu Chofunika Kwambiri M’chihema”

it-1 165

Likasa la Pangano

Mapulani a Kapangidwe Kake. Popatsa Mose malangizo okhudza kupanga chihema, choyamba Yehova anamuuza mapulani opangira Likasa chifukwa linali chinthu chofunika kwambiri m’chihema komanso mumsasa wonse wa Aisiraeli. Likasa lenilenilo linali mikono iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake (pafupifupi masentimita 111 × 67 × 67). Linapangidwa ndi mtengo wa mthethe ndipo linakutidwa ndi golide woyenga bwino. Linali ndi “mkombero wagolide kuzungulira Likasalo” umene unkalikongoletsa. Chivundikiro cha Likasa chinapangidwa ndi golide woyenga bwino, osati matabwa okutidwa ndi golide basi, ndipo chinakutira pamwamba ponse pa Likasalo. Pachivundikiro panali akerubi awiri agolide osula omwe anakhala moyang’anizana ndipo anali kumbali zosiyana zakumapeto kwa chivundikirocho. Nkhope zawo zinaweramira pansi, mapiko awo anali okwezedwa m’mwamba komanso otambasuka ndipo ankaphimba chivundikirocho. (Eks 25:10, 11, 17-22; 37:6-9) Chivundikirocho chinkatchedwanso ‘chivundikiro chophimba machimo.’​—Ahe 9:5.

it-1 166 ¶2

Likasa la Pangano

Likasa linali chinthu choyera chosungiramo zikumbutso zopatulika kapena umboni. Zinthu zofunika kwambiri zimene ankasungamo zinali miyala iwiri ya umboni, kapena kuti Malamulo 10. (Eks 25:16) Patapita nthawi ‘mtsuko wagolide wokhala ndi mana komanso ndodo ya Aroni imene inaphuka’ zinaikidwanso mu Likasa koma zinachotsedwamo pa nthawi ina kachisi wa Solomo asanamangidwe. (Ahe 9:4; Eks 16:32-34; Nu 17:10; 1Mf 8:9; 2Mb 5:10) Mose atatsala pang’ono kumwalira, anapatsa Alevi amene anali ansembe ‘buku la chilamulo’ n’kuwauza kuti asaliike mkati koma ‘pambali pa likasa la pangano la Yehova Mulungu kuti likhale mboni ya Mulungu yowatsutsa.’​—De 31:24-26.

it-1 166 ¶3

Likasa la Pangano

Linkaimira kukhalapo kwa Mulungu. Nthawi zonse Likasa linkaimira kukhalapo kwa Mulungu. Yehova analonjeza kuti: “Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo ndi kulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikiro, pakati pa akerubi awiriwo amene ali pamwamba pa likasa la umboni.” “Ndidzaonekera mu mtambo pamwamba pa chivundikirocho.” (Eks 25:22; Le 16:2) Samueli analemba kuti Yehova “akukhala pa akerubi.” (1Sa 4:4) Choncho akerubi anali “chifaniziro cha galeta” la Yehova. (1Mb 28:18) Mogwirizana ndi zimenezi, “nthawi zonse Mose akalowa m’chihema chokumanako kukalankhula ndi Mulungu, anali kumva mawu kuchokera pamwamba pa likasa la umboni akulankhula naye. Mawuwo anali kuchokera pachivundikiro chimene chinali palikasa la umboni, pakati pa akerubi awiri. Mulungu anali kulankhula naye motero.” (Nu 7:89) Pa nthawi ina, Yoswa komanso Pinihasi, yemwe anali mkulu wa ansembe, anafunsira kwa Yehova patsogolo pa Likasa. (Yos 7:6-10; Owe 20:27, 28) Koma mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankalowa Malo Oyera Koposa n’kuona Likasa tsiku limodzi pa chaka. Ankachita zimenezi pogwira ntchito yake pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, osati kuti alankhule ndi Yehova.​—Le 16:2, 3, 13, 15, 17; Ahe 9:7.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 432 ¶1

Kerubi

M’chihema chimene chinapangidwa m’chipululu, anaikamo zifaniziro za akerubi. Pachivundikiro cha Likasa panali akerubi awiri agolide osula ndipo anali kumapeto alionse a Likasali. Iwo ankayang’anizana ataweramira pansi posonyeza kulambira. Aliyense anali ndi mapiko awiri otambasula komanso okweza omwe ankaphimba chivundikiro ngati kuti akuchiteteza. (Eks 25:10-21; 37:7-9) Pansalu zopangira hema komanso pansalu yotchinga ya pakati pa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa anapetapo akerubi.​—Eks 26:1, 31; 36:8, 35.

it-2 936

Mkate Wachionetsero

Unali mitanda 12 ya mkate imene inkaikidwa patebulo m’Malo Oyera a chihema kapena kachisi ndipo inkachotsedwa Sabata lililonse kuti yatsopano iikidwe. (Eks 35:13; 39:36; 1Mf 7:48; 2Mb 13:11; Ne 10:32, 33) Dzina lenileni la Chiheberi la mkate wachionetsero linkatanthauza kuti “mkate wa nkhope.” Nthawi zina mawu oti kukhala pa nkhope ya munthu angatanthauze kukhala pamaso pake. Choncho mkate wachionetsero unali pa nkhope ya Yehova ngati kuti ukuperekedwa kwa iye nthawi zonse. (Eks 25:30) Mkate wachionetsero umatchedwanso “mkate wosanjikiza” (2Mb 2:4) komanso “mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu.”​—Mko 2:26.

SEPTEMBER 21-27

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 27-28

“Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Zovala za Ansembe?”

it-2 1143

Urimu ndi Tumimu

Akatswiri ena a mawu a m’Baibulo amakhulupirira kuti Urimu ndi Tumimu anali maere. M’Baibulo lomasuliridwa ndi James Moffatt mawu oti Urimu ndi Tumimu anamasuliridwa kuti “maere opatulika” pa Ekisodo 28:30. Akatswiri ena amaganiza kuti Urimu ndi Tumimu anali ndi mbali zitatu, imodzi yokhala ndi mawu oti “inde,” ina yokhala ndi mawu oti “ayi” ndipo inayo yosakhala ndi mawu alionse. Pakakhala funso linalake, munthu ankasankha mbali ina ndipo inkayankha funsolo koma ngati anasankha mbali yosakhala ndi mawu ndiye kuti funsolo silinayankhidwe. Koma akatswiri ena amaganiza kuti Urimu ndi Tumimu anali miyala iwiri yafulati yomwe mbali ina inali yoyera ndipo mbali inayo inali yakuda. Anthu ankaponya miyalayo ndipo ngati miyala yonse mbali zoyera zinkaoneka, yankho linali “inde.” Koma ngati miyala yonse mbali zakuda ndi zimene zinkaoneka, yankho linali “ayi” ndipo ngati mbali yoyera inkaoneka pamwala umodzi pomwe mwala winawo mbali yakuda inkaoneka, panalibe yankho lililonse. Nthawi ina pamene Sauli anafunsira kwa Yehova kudzera mwa wansembe kuti adziwe ngati aukire Afilisti kapena ayi, sanalandire yankho lililonse. Ndiye iye anaganiza kuti mmodzi mwa anthu ake anachimwa ndipo anapempha Yehova kuti: “Mulungu wa Isiraeli inu, tiyankheni kudzera mwa Tumimu!” Kenako Sauli ndi Yonatani anatengedwa ndipo anthuwo anachita maere kuti asankhe pakati pa awiriwo. Munkhaniyi pamene Sauli anati “tiyankheni kudzera mwa Tumimu,” zikuoneka kuti Tumimu anali wosiyana ndi maere amene anachita koma mwina zinkayendera limodzi.​—1Sa 14:36-42.

it-1 849 ¶3

Pamphumi

Mkulu wa Ansembe wa Aisiraeli. Ku Isiraeli panduwira imene mkulu wa ansembe ankavala pamphumi pake panali kachitsulo kaphanthiphanthi kagolide, komwe kanali “chizindikiro chopatulika cha kudzipereka,” ndipo panalembedwa “mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo” mawu oti “Chiyero n’cha Yehova.” (Eks 28:36-38; 39:30) Mkulu wa ansembe ndi amene ankaimira kulambira Yehova kuposa wina aliyense choncho ankafunika kukhala woyera pokwaniritsa udindo wake koma mawu olembedwa mogobawo ankakumbutsanso Aisiraeli onse kuti nthawi zonse ayenera kukhala oyera potumikira Yehova. Mawuwa ankaimiranso bwino udindo wa Yesu Khristu wokhala Mkulu wa Ansembe wamkulu amene amalemekeza kuyera kwa Mulungu. Yesu anasankhidwa ndi Yehova kuti akhale ndi udindo umenewu.​—Ahe 7:26.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 1130 ¶2

Kuyera

Zinyama ndi Zokolola. Ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi mbuzi zamphongo zoyamba kubadwa zinali zopatulika kwa Yehova ndipo zinkayenera kuperekedwa nsembe. Komanso mbali ina ya nsembeyo inkaperekedwa kwa ansembe. (Nu 18:17-19) Zokolola zoyambirira kucha komanso chakhumi zinali zopatulika mofanana ndi mmene zinalili nsembe ndiponso mphatso zonse zopatulidwa kuti zizigwiritsidwa ntchito m’malo opatulika. (Eks 28:38) Zinthu zonse zopatulika kwa Yehova sizinkayenera kugwiritsidwa ntchito pa zinthu wamba kapena zosayenera. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi lamulo lokhudza chakhumi. Munthu akaika padera chakhumi cha zinthu ngati tirigu kenako iye kapena munthu wa m’banja lake mosadziwa n’kuphika, munthuyo ankakhala ataphwanya lamulo la Mulungu lokhudza zinthu zopatulika. Lamuloli linanena kuti munthuyo ankayenera kupereka kumalo opatulika chakhumicho n’kuwonjezerapo magawo awiri pa magawo 10 a chakhumicho. Ankayeneranso kupereka nsembe nkhosa yamphongo yopanda chilema. Lamuloli linkathandiza anthu kuti azilemekeza zinthu zopatulika kwa Yehova.​—Le 5:14-16.

SEPTEMBER 28–​OCTOBER 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 29-30

“Chopereka kwa Yehova”

it-2 764-765

Kalembera

Ku Sinai. Yehova analamula kuti Aisiraeli apange kalembera woyamba pamene anali ku Sinai m’mwezi wachiwiri wa chaka chachiwiri atachoka ku Iguputo. Kuti Mose athe kuchita zimenezi, anasankha mtsogoleri wa fuko lililonse kuti ayang’anire kalembera wa fuko lake. Chilamulo chinanena kuti aliyense wolembedwa m’kaundula azilipira msonkho wa hafu ya sekeli (kapena kuti ndalama zopitirira pang’ono dola limodzi la ku United States) pothandiza utumiki wapachihema. Pa kalemberayo ankalembanso amuna azaka 20 kapena zoposerapo omwe anali oyenerera kupita kunkhondo. (Ex 30:11-16; Nu 1:1-16, 18, 19) Anthu onse amene analembedwa m’kaundula anakwana 603,550. Chiwerengerochi sichinaphatikize Alevi chifukwa sanalandire nawo cholowa m’dzikolo. Iwo sankalipira msonkho wa chihema ndipo sankayenera kupita kunkhondo.​—Nu 1:44-47; 2:32, 33; 18:20, 24.

it-1 502

Chopereka

Panali zopereka zina zimene Chilamulo chinanena kuti anthu ayenera kupereka. Pamene Mose anachita kalembera wa Aisiraeli, mwamuna aliyense wazaka 20 kapena kuposerapo ankayenera kupereka dipo m’malo mwa moyo wake la “hafu ya sekeli [mwina ndalama zopitirira pang’ono dola limodzi la ku United States] yolingana ndi sekeli la kumalo oyera.” Ndalamazo zinkakhala “chopereka kwa Yehova” chophimba machimo awo komanso chothandiza pa “utumiki wa pachihema chokumanako.” (Eks 30:11-16) Malinga ndi wolemba mbiri wa Ayuda dzina lake Josephus (The Jewish War, VII, 218 [vi, 6]), “msonkho wopatulika” umenewu unapitiriza kuperekedwa chaka ndi chaka.​—2Mb 24:6-10; Mt 17:24.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 1029 ¶4

Dzanja

Kuika manja. Kuwonjezera pa kungogwira zinthu, manja ankaikidwa pamunthu kapena pazinthu pa zifukwa zosiyanasiyana. Kuchita zimenezi kunkasonyeza kuti munthuyo kapena zinthuzo zilandira zinazake kapena kugwiritsidwa ntchito pa zinthu zina. Pa mwambo woika ansembe oyamba, Aroni ndi ana ake anaika manja pamutu pa ng’ombe yamphongo komanso mbuzi zamphongo ziwiri zimene zinkayenera kuperekedwa nsembe. Zimenezi zinasonyeza kuti nyamazi zinkayenera kuperekedwa nsembe chifukwa cha kuikidwa kwa Aroni ndi ana ake kukhala ansembe a Yehova Mulungu. (Eks 29:10, 15, 19; Le 8:14, 18, 22) Pamene Mose ankaika Yoswa kuti alowe m’malo mwake chifukwa chosankhidwa ndi Mulungu, iye anaika manja ake pa Yoswa kenako Yoswayo ‘anadzazidwa ndi mzimu wa nzeru’ ndipo anatha kutsogolera bwino Aisiraeli. (De 34:9) Aisiraeli ankaikanso manja pa munthu posonyeza kuti munthuyo alandira madalitso. (Ge 48:14; Mko 10:16) Yesu Khristu ankaika manja pa anthu ena amene ankawachiritsa. (Mt 8:3; Mko 6:5; Lu 13:13) Atumwi ankaika manja pa anthu ena kuti alandire mphatso ya mzimu woyera.​—Mac 8:14-20; 19:6.

it-1 114 ¶1

Kudzozedwa, Kudzoza

M’Chilamulo chimene anapatsa Mose, Yehova anafotokoza msanganizo wa mafuta odzozera. Unali wopangidwa ndi zinthu zabwino kwambiri monga mule, sinamoni wonunkhira bwino, kalamasi wonunkhira, kasiya ndi mafuta a maolivi. (Eks 30:22-25) Linali tchimo lalikulu kwambiri ngati munthu atasakaniza zinthuzi n’kumazigwiritsa ntchito pa zinthu wamba kapena zosayenera. (Eks 30:31-33) Zimenezi zinasonyeza kufunika kwa kuikidwa pa udindo winawake komanso kutsimikizira kuikako ndi mafuta odzozera ndiponso opatulika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena