Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr20 October tsamba 1-3
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
  • Timitu
  • OCTOBER 5-11
  • OCTOBER 12-18
  • OCTOBER 26–​NOVEMBER 1
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
mwbr20 October tsamba 1-3

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

OCTOBER 5-11

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 31-32

Kufufuza Mfundo Zothandiza

w87 9/1 29

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Sikuti Mulungu akavomereza munthu (kapena kuti kulemba dzina lake “m’buku la moyo”) ndiye kuti adzapatsidwa moyo wosatha zivute zitani ngati kuti zinasankhidwiratu kuti adzapulumuka. Ponena za Aisiraeli, Mose anapempha Yehova kuti: “Ngati mukufuna kuwakhululukira tchimo lawo, . . . koma ngati simukufuna, ndifafanizeni chonde, m’buku lanu limene mwalemba.” Ndiye Mulungu anamuyankha kuti: “Amene wandichimwirayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.” (Eks 32:32, 33) Choncho munthu amene Mulungu wamuvomereza n’kumulemba “m’buku” lake akhoza kusintha n’kukhala wosakhulupirika. Izi zikachitika, Mulungu ‘adzafafaniza dzina lake m’buku la moyo.’​—Chivumbulutso 3:5.

OCTOBER 12-18

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 33-34

“Makhalidwe Abwino Kwambiri a Yehova”

it-2 466-467

Dzina

Chilengedwe chimapereka umboni wakuti Mulungu aliko koma sichitiuza dzina lake. (Sl 19:1; Aro 1:20) Kudziwa dzina la Mulungu kumatanthauza zambiri osati kungodziwa mawuwo. (2Mb 6:33) Kumatanthauza kudziwa zolinga zake, zochita zake komanso makhalidwe ake omwe amafotokozedwa m’Mawu ake. (Yerekezerani ndi 1Mf 8:41-43; 9:3, 7; Ne 9:10.) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Mose, yemwe Yehova ‘ankamudziwa bwino, ndi dzina lake lomwe.’ (Eks 33:12) Mose anali ndi mwayi woona ulemerero wa Yehova komanso kumva ‘dzina la Yehova likulengezedwa.’ (Eks 34:5) Chilengezo chimenechi sichinali chongotchula dzina lakuti Yehova koma chinali chofotokoza makhalidwe ndi zochita zake. Chinati: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo, koma wosalekerera konse wolakwa osam’langa. Wolanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.” (Eks 34:6, 7) Mofanana ndi zimenezi, nyimbo ya Mose, yomwe imati “pakuti ndidzalengeza dzina la Yehova,” imafotokoza zinthu zimene Mulungu anachita ndi Aisiraeli komanso makhalidwe ake.​—De 32:3-44.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

w98 9/1 20 ¶5

Muzionetsetsa Kuti Mukuika Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba

Mwamuna aliyense wa Chiisiraeli komanso wotembenukira ku Chiyuda analamulidwa kuti azikaonekera kwa Yehova katatu pa chaka. Amuna ambiri anazindikira kuti maulendowa akhoza kuthandizanso onse a m’banja lawo ndipo anakonza zoti akazi awo komanso ana awo azipita nawo limodzi. Koma kodi ndani akanateteza nyumba zawo komanso minda yawo kwa adani akachoka pakhomo pawo? Yehova analonjeza kuti: “Palibe aliyense adzasirira dziko lanu pamene mwachoka kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu katatu pa chaka.” (Ekisodo 34:24) Aisiraeli ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti azikhulupirira kuti akaika zinthu zauzimu pamalo oyamba sadzataya chuma chawo. Koma kodi Yehova anakwaniritsa lonjezo lakelo? Inde, anachitadi zimenezi.

OCTOBER 26–​NOVEMBER 1

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 37-38

“Maguwa Ansembe a Chihema Anali Ofunika pa Kulambira Koona”

it-1 82 ¶3

Guwa Lansembe

Guwa Lansembe Zofukiza. Guwa lansembe zofukiza (lotchedwanso kuti “guwa lansembe lagolide” [Eks 39:38]) linapangidwa ndi mtengo wa mthethe. Pamwamba pake komanso m’mbali mwake linakutidwa ndi golide ndipo mkombero wagolide unazungulira pamwambapo. Guwali linali masentimita 44.5 m’litali ndi m’lifupi ndipo kutalika kwake kuchokera pansi kufika m’mwamba kunali masentimita 89. Linalinso ndi “nyanga” pamakona onse 4 apamwamba pake. Mphete 4 zagolide zinapangidwa kuti azilowetsamo mitengo ya mthethe yokutidwa ndi golide yonyamulira guwali. Mphetezi zinaikidwa m’munsi mwa mkombero wagolide, ziwiri kumbali ina ndi ziwiri zina kumbali inayo. (Eks 30:1-5; 37:25-28) Ankafukiza zofukiza zonunkhira paguwapo kawiri pa tsiku, m’mawa ndi madzulo. (Eks 30:7-9, 34-38) Baibulo limatchulanso chiwaya chofukizira zonunkhira ndipo zikuoneka kuti chinkagwiritsidwanso ntchito pa guwa lansembe zofukiza. (Le 16:12, 13; Ahe 9:4; Chv 8:5; yerekezerani ndi 2Mb 26:16, 19.) Guwa lansembe zofukiza linali m’chihema patsogolo pa nsalu yotchinga ya Malo Oyera Koposa moti Baibulo limanena kuti linali “patsogolo pa likasa la umboni.”​—Eks 30:1, 6; 40:5, 26, 27.

it-1 1195

Zofukiza

Zofukiza zopatulika zomwe Aisiraeli ankagwiritsa ntchito m’chipululu zinkapangidwa ndi zinthu zamtengo wapatali zomwe Aisiraeliwo anapereka. (Eks 25:1, 2, 6; 35:4, 5, 8, 27-29) Yehova anapereka malangizo kwa Mose opangira msanganizo umenewu. Iye anati: “Tenga zonunkhira izi: madontho a sitakate, onika, mafuta onunkhira a galibanamu ndi lubani weniweni. Zonsezi zikhale za muyezo wofanana. Zinthu zimenezi upangire zofukiza, msanganizo wa zonunkhiritsa zosakaniza mwaluso, wothira mchere, msanganizo weniweni wopatulika. Kenako upere wina mwa msanganizo umenewu kuti ukhale ufa wosalala kwambiri. Uike wina mwa ufawo patsogolo pa Umboni m’chihema chokumanako, kumene ndidzaonekera kwa iwe. Msanganizowu ukhale wopatulika koposa kwa inu.” Kenako Yehova anatsindika kuti msanganizo umenewu ndi wopatulika komanso woyera powauza kuti: “Aliyense wopanga zofukiza zofanana ndi zimenezi pofuna kudzisangalatsa ndi kununkhira kwake, adzaphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.”​—Eks 30:34-38; 37:29.

it-1 82 ¶1

Guwa Lansembe

Maguwa Ansembe a Chihema. Pamene anapanga chihema, maguwa ansembe awiri anapangidwa potsatira malangizo a Mulungu. Guwa lansembe zopsereza (lotchedwanso kuti “guwa lansembe lamkuwa” [Eks 39:39]) linapangidwa ndi matabwa a mthethe ndipo linali losatseka pamwamba komanso pansi pake. Linali mamita 2.2 m’litali ndi m’lifupi ndipo kutalika kwake kuchokera pansi kufika m’mwamba kunali mamita 1.3. Pamwamba pake panali “nyanga” m’makona onse 4. Guwali linakutidwa ndi mkuwa. Sefa wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana anaikidwa ‘chapakati pa guwalo, m’munsi mwa mkombero.’ Mphete 4 zinaikidwa kumakona onse 4 pafupi ndi sefayo ndipo zikuoneka kuti m’mphetezi ndi mmene mitengo iwiri ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi mkuwa inkalowetsedwa ponyamula guwalo. N’kutheka kuti zimenezi zikutanthauza kuti anaboola mbali ziwiri za guwalo n’kulowetsa sefa wafulati uja ndipo mphetezo zinakhala kumbali ziwiri za sefayo. Koma akatswiri amasiyana maganizo pa nkhani ya mphetezi. Ambiri amaganiza kuti payenera kuti panali magulu awiri a mphete ndipo gulu limodzi linali loti mitengo yonyamulira guwalo izilowetsedwamo ndipo linaikidwa paguwa penipenipo. Anapanganso ziwiya zamkuwa monga mafosholo ndi ndowa zochotsera phulusa, mbale zolowa zoti magazi a nyama azigweramo, mafoloko ogwirira nyama komanso zopalira moto.​—Eks 27:1-8; 38:1-7, 30; Nu 4:14.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 36

Mthethe

Mtengo wa mthethe umakhala ndi minga yaitali panthambi zake zomwe zimatambasuka kwambiri. Nthawi zambiri nthambizi zimalukana ndi nthambi za mitengo ina ya mthethe zimene zili pafupi ndipo zimakhala zokolanakolana. N’chifukwa chake mawu a m’Baibulo akuti Sitimu nthawi zambiri amanena za mitengo ingapo osati umodzi. Mtengo wa mthethe ukhoza kutalika mpaka kufika mamita 6 kapena 8 koma umaonekabe ngati chitsamba. Masamba ake ndi ofewa ngati nthenga komanso amakhala ndi maluwa achikasu onunkhira bwino. Maluwawa amapanga zipatso zopindika zomwe zimakhala zazikulu pakati ndipo zimakhala zazing’ono kumapeto kwake. Mtengowu ndi wolimba komanso wolemera kwambiri moti tizilombo sitidya ndipo makungwa ake amakhala akuda. Chifukwa cha mmene mtengo wa mthethe ulili komanso popeza kuti umapezeka kwambiri m’chipululu, unali wabwino kupangira chihema komanso zinthu zokhala m’chihemacho. Anaugwiritsa ntchito popanga likasa la pangano (Eks 25:10; 37:1), tebulo lokhala ndi mkate wachionetsero (Eks 25:23; 37:10), maguwa ansembe (Eks 27:1; 37:25; 38:1), mitengo yonyamulira zinthuzi (Eks 25:13, 28; 27:6; 30:5; 37:4, 15, 28; 38:6), zipilala za nsalu yotchinga (Eks 26:32, 37; 36:36), mafelemu oimika (Eks 26:15; 36:20) komanso mipiringidzo yogwira mafelemuwo (Eks 26:26; 36:31).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena