Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 16 tsamba 19
  • Kulankhula Molimbikitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula Molimbikitsa
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwafika Pamtima Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Khalani Wolimbikitsa
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kulankhula ndi Mtima Wonse
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 16 tsamba 19

PHUNZIRO 16

Kulankhula Molimbikitsa

Lemba

Yobu 16:5

MFUNDO YAIKULU: M’malo mongotchula mavuto okhaokha, muzifotokoza njira yothetsera mavutowo komanso mfundo zimene zingalimbikitse anthu.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muziona kuti anthu amene mukulankhula nawo ali ndi mtima wabwino. Muziona kuti Akhristu anzanu amafuna kusangalatsa Yehova. Ngakhale pamene mukufuna kuwapatsa malangizo, muziyamba ndi kuwayamikira kuchokera pansi pa mtima.

    Mfundo yothandiza

    Muzilankhula zinthu chifukwa chokonda anthu osati chifukwa choti akupsetsani mtima. Muzimwetulira kuti anthu aziona kuti mumawakonda.

  • Chepetsani mfundo zosalimbikitsa. Zinthu zina zosalimbikitsa mukhoza kuzitchula ngati mukufuna kutsimikizira mfundo inayake. Koma nkhani yanu yonse iyenera kukhala yolimbikitsa.

  • Muzigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu. Thandizani anthu kuganizira zimene Yehova wachita m’mbuyomu, zimene akuchita panopa, ndiponso zimene adzachite m’tsogolo. Thandizani anthu kukhala ndi chiyembekezo komanso kuti alimbe mtima.

MU UTUMIKI

Muziona kuti munthu aliyense akhoza kukhala mtumiki wa Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena