NYIMBO 67
“Lalikira Mawu”
Losindikizidwa
1. Mulungu watilamula
Ndipo tikufunika kumvera.
Tizifotokozera anthu
Adziwe chiyembekezo chathu.
(KOLASI)
Lalikira,
Indetu onse amve.
Lalika
Dzikoli lisanathe.
Lalika
Ofatsa amvetsere
Lalika
M’dziko lonse.
2. Mavuto adzatiyesa.
Tingapezeke tikunyozedwa.
Kulalikira kungavute.
Tidzakhulupirirabe M’lungu.
(KOLASI)
Lalikira,
Indetu onse amve.
Lalika
Dzikoli lisanathe.
Lalika
Ofatsa amvetsere
Lalika
M’dziko lonse.
3. Nthawi zina tizipeza
Anthu ofuna kutimvetsera.
Tiziwaphunzitsa mwakhama.
Tiyeretse dzina la Yehova.
(KOLASI)
Lalikira,
Indetu onse amve.
Lalika
Dzikoli lisanathe.
Lalika
Ofatsa amvetsere
Lalika
M’dziko lonse.
(Onaninso Mat. 10:7; 24:14; Mac. 10:42; 1 Pet. 3:15.)