Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
JULY 4-10
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 18-19
“Barizilai Anali Wodzichepetsa”
Barizilai Anali Munthu Wodzichepetsa
N’zosakayikitsa kuti Davide anayamikira kwambiri thandizo la Barizilai lija. Zikuoneka kuti Davide sanamuitane Barizilai pofuna kungobweza zabwino zimene anam’chitirazo. Chifukwatu Barizilai anali munthu wachuma moti sakanafunikira thandizo lotere. N’kutheka kuti Davide ankafuna kuti Barizilai akakhale m’nyumba yachifumu chifukwa choti munthu wachikulireyu anali ndi makhalidwe abwino. Unali ulemu waukulu kwambiri kwa Barizilai kukakhala ku nyumba imeneyi nthawi zonse, n’kukhala paubwenzi ndi mfumu.
Barizilai Anali Munthu Wodzichepetsa
N’kutheka kuti chimodzi mwa zifukwa zimene Barizilai anakanira pempholi chinali chakuti iye anali wokalamba ndipo sakanatha kuchita zinthu zina ndi zina. Mwinanso ankaona kuti watsala pang’ono kufa. (Salmo 90:10) Iye anachita zonse zimene akanatha pothandiza Davide, komabe ankadziwanso kuti pali malire a zimene angathe kuchita malingana ndi msinkhu wake. Barizilai sanalole kuti kuganizira za ulemerero wake ndiponso kudziwika kwake kum’sokoneze maganizo n’kulephera kuona kuti sangathe kuchita zinthu zina. Mosiyana ndi Abisalomu, yemwe anali odzithemba kwambiri, Barizilai anachita zinthu mwanzeru podzichepetsa.—Miyambo 11:2.
Barizilai Anali Munthu Wodzichepetsa
Nkhani ya Barizilai ikutithandiza kuti tiziona zinthu m’njira yoyenera. Koma sikuti zimene iye anachitazi zizitipangitsa kukana mwayi wautumiki poganiza kuti sitingakwanitse, mwinanso pofuna kungokhala ndi moyo wosatanganidwa. Komanso zisamatipangitse kusafuna udindo mumpingo. M’malo mwake tiyenera kudalira Mulungu kuti atipatse mphamvu ndiponso nzeru kuti tim’tumikire.—Afilipi 4:13; Yakobe 4:17; 1 Petulo 4:11.
Ngakhale zili choncho, tiyenera kuzindikira zinthu zomwe sitingakwanitse. Mwachitsanzo, zingatheke kuti munthu ali ndi maudindo ambiri mumpingo. N’zodziwikiratu kuti kulandira maudindo enanso owonjezera pamenepa, kungam’chititse kunyalanyaza maudindo ena a m’malemba monga kusamalira banja lake. Ngati zitakhala choncho, kodi sizingakhale bwino kukana maudindo ena owonjezerawo? Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti munthuyo amaona zinthu m’njira yoyenera ndiponso ndi wodzichepetsa.—Afilipi 4:5; 1 Timoteyo 5:8.
Mfundo Zothandiza
‘Tizithamanga Panjirayo Mpaka pa Mapeto’
19 Ngati muli ndi vuto limene mukuona kuti anthu ena salimvetsa, mukhoza kulimbikitsidwa ndi chitsanzo cha Mefiboseti. (2 Sam. 4:4) Iye anali wolumala ndipo Mfumu Davide anamuganizira zolakwika. Palibe chilichonse chimene Mefiboseti analakwitsa kuti akumane ndi mavutowa. Koma m’malo mongokhalira kukhumudwa, iye ankayamikira zinthu zabwino zimene zinkachitika pa moyo wake. Mwachitsanzo, ankayamikira kukoma mtima kumene Davide anali atamusonyeza. (2 Sam. 9:6-10) Choncho pamene Davide anamuganizira zolakwika, maganizo ake sanali pa nkhani yokhayo. Iye sanalole kuti akhumudwe kwambiri ndi zimene Davide analakwitsazi. Komanso sanaimbe mlandu Yehova chifukwa cha zimene Davide anachita. Koma Mefiboseti ankaganizira kwambiri zimene akanatha kuchita pothandiza mfumu yosankhidwa ndi Yehova. (2 Sam. 16:1-4; 19:24-30) Ndipo Yehova anachititsa kuti chitsanzo chabwino cha Mefiboseti chilembedwe m’Mawu ake kuti chizitithandiza.—Aroma 15:4.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Muzisangalala ndi Utumiki Wanu
15 Kodi ndi zolinga ziti zimene mungadziikire? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kudziwa zolinga zimene mungazikwaniritse. (Miy. 16:3; Yak. 1:5) Kodi n’zotheka kuti mukhale ndi zolinga zimene zatchulidwa mundime yoyamba munkhaniyi, monga kuchita upainiya wothandiza, kapena wokhazikika, kutumikira pa Beteli kapenanso kuchita nawo utumiki wa zomangamanga? Mukhozanso kuphunzira chinenero china n’cholinga choti muzilalikira uthenga wabwino m’gawo limene amalankhula chinenerocho. Mungadziwe zambiri powerenga mutu 10 m’buku lakuti Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova komanso pokambirana ndi akulu a mumpingo mwanu. Mukamayesetsa kukwaniritsa zolinga zanu, kupita kwanu patsogolo kudzaonekera ndipo mudzawonjezera chimwemwe chanu.
16 Koma bwanji ngati n’zosatheka kuti mukwaniritse zolinga zimene zatchulidwazi? Mungachite bwino kudziikira cholinga china chimene mungathe kuchikwaniritsa. Taganizirani zolinga zotsatirazi.
17 Werengani 1 Timoteyo 4:13, 15. Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, mungamachite khama kuti muwonjezere luso lanu lokamba nkhani komanso kuphunzitsa. Chifukwa chiyani? Chifukwa ‘kudzipereka’ kwanu pa kuwerenga, luso lakulankhula komanso kuphunzitsa kungathandize kwambiri anthu okumvetserani. Mukhozanso kudziikira cholinga chakuti muziphunzira komanso kugwiritsa ntchito mfundo zamuphunziro lililonse m’kabuku kakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso. Muziyesa kuphunzira luso limodzi n’kuliyeserera muli kunyumba komanso kugwiritsa ntchito mfundo zake mukamakamba nkhani. Muzipemphanso malangizo kwa mlangizi wothandiza kapena akulu ena omwe “amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” (1 Tim. 5:17) Mukamakulitsa luso lomwe mwaphunzira mu phunziro linalake, muzithandizanso omvetsera anu kulimbitsa chikhulupiriro chawo kapenanso kuwalimbikitsa kuti azigwiritsa ntchito zimene aphunzira. Mukamachita zimenezi mudzawonjezera chimwemwe chanu komanso chawo.
18 Tonsefe tinapatsidwa ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa. (Mat. 28:19, 20; Aroma 10:14) Kodi mukufuna kuwonjezera luso lanu pa ntchito yofunika kwambiri imeneyi? Mukamaphunzira mfundo za m’kabuku ka Kuphunzitsa, muzidziikira zolinga zoti mugwiritse ntchito zimene mwaphunzirazo. Mungapezenso malangizo ena othandiza mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndiponso mavidiyo a zitsanzo za ulaliki omwe amaonetsedwa pamisonkhano ya mkati mwa mlungu. Muziyeserera njira zosiyanasiyana n’kuona imene ili yabwino kwambiri kwa inu. Mukamatsatira malangizo amenewa, mudzakhala mphunzitsi waluso ndipo zimenezi zidzathandiza kuti muzisangalala kwambiri.—2 Tim. 4:5.
19 Mukamaganizira zolinga zimene mukufuna kukhala nazo, musamanyalanyaze chinthu chofunika kwambiri chomwe ndi kukulitsa makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo. (Agal. 5:22, 23; Akol. 3:12; 2 Pet. 1:5-8) Kodi mungatani kuti mukhale ndi makhalidwe amenewa? Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukufuna mutakhala ndi chikhulupiriro cholimba. Muyenera kuwerenga m’mabuku athu nkhani zimene zili ndi malangizo amene angakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Mukhozanso kupindula kwambiri ndi mavidiyo a JW Broadcasting® onena za abale ndi alongo ena omwe anasonyeza chikhulupiriro polimbana ndi mayesero osiyanasiyana amene anakumana nawo. Kenako muziganizira njira zimene mungatsanzirire chikhulupiriro chawo pa moyo wanu.
JULY 11-17
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 20-21
“Yehova ndi Mulungu Wachilungamo”
it-1 932 ¶1
Gibeoni
Kwa zaka zambiri, Agibeoni oyambirira ankapezekabe ngakhale kuti Mfumu Sauli inakonza zoti iwawononge. Komabe Agibeoni anayembekezera Yehova moleza mtima kuti aulule zinthu zopanda chilungamozi. Yehova anaulula zinthuzi pamene kunagwa njala kwa zaka zitatu pa nthawi imene Davide anali mfumu. Davide atafunsira kwa Yehova, zinadziwika kuti panachitika mlandu wa magazi ndipo anafunsa Agibeoni zimene angachite kuti aphimbe tchimolo. Agibeoni anayankha momveka bwino kuti “sitikufuna siliva kapena golide” chifukwa mogwirizana ndi Chilamulo, sipankayenera kuperekedwa dipo lowombolera munthu amene wapha mnzake. (Nu 35:30, 31) Ankazindikiranso kuti sankayenera kupha munthu popanda chilolezo. Choncho iwo anadikira mpaka pamene Davide anawafunsa ndipo anapempha kuti awapatse “ana aamuna” 7 a Sauli. Mfundo yakuti mlandu wa magaziwo unali pa Sauli ndi nyumba yake, ikusonyeza kuti, ngakhale kuti Sauliyo ndi amene anatsogolera popha Agibeoniwo, n’kuthekanso kuti “ana” ake anatengapo mbali, kaya mwachindunji kapena ayi. (2Sa 21:1-9) Pamenepa sizikusonyeza kuti anawa anafa chifukwa cha machimo a abambo awo, (De 24:16) koma chifukwa cha mfundo ya chilungamo yogwirizana ndi lamulo lakuti “moyo kulipira moyo.”—De 19:21.
Mfundo Zothandiza
Akulu Achikhristu Ndi Antchito Anzathu Otipatsa Chimwemwe
14 Anthu a Yehovafe padziko lonse lapansi tikutumikira Mulungu ngakhale kuti Satana ndi anthu ake akuyesetsa kutisokoneza. Ena a ife talimbana ndi mavuto akuluakulu okhala ngati Goliati ndipo tawagonjetsa chifukwa chodalira Yehova. Komabe nthawi zina timatopa ndiponso kukhumudwa chifukwa chokhalira kulimbana ndi mavuto a m’dzikoli. Tikafooka choncho, timakhala pa ngozi yogonjetsedwa ndi mavuto amene tikanatha kulimbana nawo bwinobwino. Pa nthawi ngati zimenezi, thandizo limene mkulu angapereke lingatilimbikitse ndiponso kutithandiza kukhalanso ndi chimwemwe. Zimenezi zachitikira abale ndi alongo ambiri. Mwachitsanzo, mlongo wina wa zaka zoposa 60, amene akuchita upainiya, anati: “Nthawi ina m’mbuyomu, sindinkamva bwino m’thupi ndipo ndinkatopa kwambiri ndikalowa mu utumiki. Mkulu wina anazindikira kuti ndikuoneka wofooka ndipo anandithandiza. Tinakambirana nkhani ina yolimbikitsa ya m’Baibulo. Ndinatsatira malangizo ake ndipo zinandithandiza.” Mlongoyu ananenanso kuti: “Ndimathokoza kwambiri kuti mkuluyo anandisonyeza chikondi. Anazindikira kuti ndinafooka n’kundithandiza.” Zimatilimbikitsa kwambiri kudziwa kuti akulu amatikonda ndipo amachita nafe chidwi. Komanso, mofanana ndi Abisai, iwo amakhala okonzeka kutithandiza.
JULY 18-24
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 22
“Muzidalira Yehova Kuti Akuthandizeni”
Kodi ‘Mungayandikiredi kwa Mulungu’?
11 Munthu angawerenge kuti Mulungu ali “wolimba mphamvu.” (Yesaya 40:26) Komatu akhoza kumva mfundoyi mosiyana pamene awerenga za mmene Mulungu analanditsira Isiraeli pa Nyanja Yofiira ndiyeno n’kukhala akusamalira mtunduwo m’chipululu kwa zaka 40. Mungathe kuona m’maganizo mwanu madzi oyenda mwamphamvu akugawikana. Mungauone mtunduwo, mwinamwake anthu 3,000,000 onse pamodzi, akuyenda pansi pa nyanjayo pouma, madzi oundanawo ataima ngati makoma akuluakulu kumbali zonse ziwiri. (Eksodo 14:21; 15:8) Mukhoza kuona umboni wakuti Mulungu anali kuwasamalira bwino m’chipululu. Madzi anatuluka m’thanthwe. Chakudya, chokhala ngati zipatso zoyera, chinali kupezeka pansi. (Eksodo 16:31; Numeri 20:11) Pano Yehova akuulula kuti si kuti ali ndi mphamvu zokha, komanso kuti amazigwiritsa ntchito pothandiza anthu ake. Kodi si zokhazika mtima pansi kudziwa kuti mapemphero athu amapita kwa Mulungu wamphamvu amene “ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso”?—Salmo 46:1.
“Mudzakhala Wokhulupirika”
Tiyeni tiganizire mofatsa mawu a Davide amenewa. Mawu a Chiheberi omasuliridwa kuti “mudzakhala wokhulupirika” angatanthauzenso “kuchita zinthu mokoma mtima.” Choncho, munthu wokhulupirikadi amachita zinthu chifukwa cha chikondi ndipo Yehova amakonda anthu amene ali okhulupirika kwa iye.
Chinanso n’chakuti munthu wokhulupirika samangomva mumtima mwake kuti ndi wokhulupirika koma amachita zinthu zosonyeza kuti ndi wokhulupirika. Yehova amachita zinthu mokhulupirika ndipo Davide anaona yekha kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Panthawi imene iye anakumana ndi mavuto aakulu, Yehova anamuthandiza pomuteteza mokhulupirika ndi kumutsogolera. Davide anazindikira kuti Yehova ndi amene anamuteteza ‘pomupulumutsa m’dzanja la adani ake onse.’—2 Samueli 22:1.
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa mawu a Davide amenewa? Tikuphunzira kuti Yehova sasintha. (Yakobe 1:17) Iye amachita zinthu motsatira mfundo zake ndipo amakwaniritsa malonjezo ake mokhulupirika. Mu Salmo lina limene Davide analemba, iye anati: “Yehova . . . sataya okondedwa [okhulupirika ake].”—Salmo 37:28.
Mfundo Zothandiza
Yesetsani Kukhala Ngati Wamng’ono
7 Davide anakhudzidwa kwambiri ataona kudzichepetsa kwa Mulungu. Iye anaimbira Yehova kuti: “Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso, ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.” (2 Sam. 22:36) Davide ankaona kuti udindo uliwonse umene anali nawo mu Isiraeli anaupeza chifukwa cha kudzichepetsa kwa Yehova. Zili ngati Mulungu anadzichepetsa n’kutsika m’munsi kuti amuone Davideyo. (Sal. 113:5-7) Izitu n’zimene Yehova amachitanso ndi ifeyo. Kaya tili ndi khalidwe linalake labwino, kaya luso kapena udindo winawake, tizikumbukira kuti ‘tinangochita kulandira’ kuchokera kwa Yehova. (1 Akor. 4:7) Munthu amene amakhala ngati wamng’ono amakhala “wamkulu” chifukwa Yehova akhoza kumugwiritsa ntchito kwambiri. (Luka 9:48) N’chifukwa chiyani tikutero?
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
w06 8/15 21 7-8
Yobu Anali Munthu Wopirira ndi Wosunga Umphumphu
Ngakhale kuti Akhristu ambiri masiku ano savutika ngati mmene Yobu anavutikira, iwo amakumanabe ndi masautso osiyanasiyana. Ambiri amakumana ndi chizunzo kapena mavuto a m’banja. Umphawi kapena matenda zingakhale zinthu zothetsa nzeru kwambiri. Ena ataya moyo wawo chifukwa cha zimene amakhulupirira. N’zoona kuti sitiyenera kuganiza kuti Satana ndi amene amachititsa vuto lililonse limene takumana nalo. Kwenikweni, mavuto ena angayambe chifukwa chakuti talakwitsa zinthu zina kapena chifukwa cha chibadwa chomwe tinatengera kwa makolo athu. (Agalatiya 6:7) Ndipo tonse timavutika ndi ukalamba ndiponso masoka achilengedwe. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti panthawi ino, Yehova sateteza atumiki ake mozizwitsa ku mavuto amenewa.—Mlaliki 9:11.
Komabe, Satana angagwiritse ntchito mavuto amene timakumana nawo kuti afooketse chikhulupiriro chathu. Mtumwi Paulo anatchula kuti anali kuvutika ndi “munga m’thupi, mngelo wa Satana” amene anakhala ‘akum’tundudza’ nthawi zonse. (2 Akorinto 12:7) Kaya limeneli linali vuto linalake la m’thupi, monga kusatha kupenya bwino kapena ayi, Paulo ankadziwa kuti Satana angathe kugwiritsa ntchito vutolo ndi zotsatirapo zake zokhumudwitsa, n’kum’landa chimwemwe ndi chikhulupiriro chake. (Miyambo 24:10) Masiku ano, Satana angachititse anthu a m’banja mwathu, anzathu a kusukulu, kapena maboma olamula mwankhanza, kuzunza atumiki a Mulungu m’njira inayake.
JULY 25-31
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 23-24
“Kodi Mumapereka Nsembe?”
it-1 146
Arauna
Zimaoneka kuti Arauna ananena kuti apereka mwaulere malo, ng’ombe komanso nkhuni zoti aperekere nsembe, koma Davide ananena kuti agula. Nkhani imene ili pa 2 Samueli 24:24, imasonyeza kuti Davide anagula malo opunthira mbewu ndi ng’ombe ndipo analipira ndalama zokwana masekeli 50 asiliva ($110). Koma nkhani imene ili pa 1 Mbiri 21:25, imasonyeza kuti Davide analipira ndalama zokwana masekeli 600 agolide (pafupifupi $77,000). Amene analemba buku la 2 Samueli ananena zimene zinachitika pogula malo amene panamangidwa guwa la nsembe komanso zinthu zimene zinafunika popereka nsembe panthawiyo, choncho zikuoneka kuti mtengo umene anatchula unali wa zinthu zimenezi basi. Pomwe amene analemba buku la 1 Mbiri anafotokoza za kachisi amene pambuyo pake anadzamangidwa pa malo omwewa ndipo ndalama zimene anatchula ndi zokhudza malo a kachisiyo. (1 Mbiri 22:1-6; 2 Mbiri 3:1) Popeza kuti malo amene panali kachisi anali aakulu kwambiri, zikuoneka kuti ndalama zokwana masekeli 600 agolide zinali zogulira malo onsewa osati malo aang’ono aja amene ankafunika kuti Davide amangepo guwa la nsembe.
Phunzirani Kuchokera ku Choonadi cha M’chilamulo
8 Nthawi zina munthu wachiisiraeli ankasankha kupereka nsembe yaufulu posonyeza kuyamikira Yehova. Kapena ankasankha kupereka nsembe yopsereza imene inali yaufulu pofuna kuti asangalatse Yehova. Pa zochitika zimenezi iye sakanavutika kusankha nyama yabwino kwambiri. Masiku ano, Akhristu sapereka nsembe za nyama zimene zinatchulidwa m’Chilamulo cha Mose. Komabe iwo amapereka nsembe pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso chuma chawo kuti atumikire Yehova. Mtumwi Paulo ananena kuti pamene ‘tikulengeza’ chikhulupiriro chathu ndiponso “kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena” timakhala tikupereka nsembe zimene Mulungu amakondwera nazo. (Aheb. 13:15, 16) Mtima umene anthu a Yehova amakhala nawo pochita zinthu zimenezi umasonyeza ngati amayamikira kwambiri zinthu zonse zimene Mulungu wawapatsa. Choncho mofanana ndi Aisiraeli, tiyenera kuonanso mtima umene tili nawo potumikira Mulungu ndiponso zolinga zimene timakhala nazo.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Wachiwiri
23:15-17. Davide ankalemekeza kwambiri lamulo la Mulungu lokhudza moyo ndi magazi moti panthawiyi, anapewa kuchita zimene zinaoneka ngati zofanana ndi kuswa lamulo limenelo. Tiyenera kuphunzira kuwaona chimodzimodzi malamulo onse a Mulungu.
AUGUST 1-7
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 1–2
“Kodi Mumaphunzirapo Kanthu Mukalakwitsa Zinazake?”
it-2 987 ¶4
Solomo
Atamva phokoso la nyimbo ku Gihoni, komwe sikunali kutali kwambiri, komanso phokoso la anthu akufuula kuti “Mfumu Solomo ikhale ndi moyo wautali,” Adoniya ndi anthu amene anali naye anachita mantha ndipo anathawa. Pamenepa Solomo anasonyeza kuti ufumu wake udzakhala wabata chifukwa sanafune kubwezera mwa kupha munthu pa tsiku limene ankamulonga ufumu. Zikanakhala kuti Adoniya ndi amene anakhala mfumu, Solomo akanatha kuphedwa. Adoniya anathawira kumalo opatulika kukabisala choncho Solomo anatumiza uthenga kuti abwere adzaonekere pamaso pake. Atabwera anamuuza kuti amusiya kuti akhalebe ndi moyo, koma choipa chisadzapezeke mwa iye, kenako Solomo anamuuza kuti azipita kunyumba kwake.—1Mf 1:41-53.
it-1 49
Adoniya
Komabe Davide atamwalira, Adoniya anapita kwa Batiseba ndipo anamunyengerera kuti akamulankhulire kwa Solomo ndi kumupempha kuti amupatse Abisagi, mlezi amene ankasamalira Davide, kuti akhale mkazi wake. Mawu amene Adoniya analankhula akuti “ufumu unayenera kukhala wanga, ndipo Aisiraeli onse maso awo anali pa ine kuti ndikhala mfumu” anasonyeza kuti ankamva kuti anamuphera ufulu wokhala mfumu, ngakhale kuti anavomerezabe kuti Mulungu ndi amene anachititsa zimenezi. (1Mf 2:13-21) Ngakhale kuti anapempha zimenezi makamaka chifukwa chofuna chipepeso kuti sanapatsidwe ufumu, ndi zoonekeratu kuti Adoniya anali adakali ndi mtima wolakalaka udindo chifukwa pa nthawi imeneyo mayiko a Kum’mawa kunali lamulo lakuti akazi komanso adzakazi a mfumu ankakhala a munthu amene walowa m’malo mwa mfumuyo. (Yerekezerani ndi 2Sa 3:7; 16:21.) Umu ndi mmene Solomo anaonera zimene Adoniya anapemphazi kudzera mwa mayi ake ndipo analamula kuti Adoniya aphedwe. Benaya anamuphadi nthawi yomweyo.—1Mf 2:22-25.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Woyamba
2:37, 41-46. N’zoopsa kwabasi kuganiza kuti munthu angaswe malamulo a Mulungu koma osalandira chilango. Amene amapatuka mwadala pa njira ‘yochepetsa yakumuka nayo kumoyo’ adzakumana ndi zotsatira za chosankha chawo chopanda nzerucho.—Mateyu 7:14.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
km 1/15 2 1-3
Pitirizani Kuwonjezera Luso Lanu Lophunzitsa
1 Akhristufe tiyenera kupitiriza kuwonjezera luso lathu lophunzitsa. N’chifukwa chake Yesu sanasiye kuphunzitsa otsatira ake kuti azilalikira mwaluso. (Luka 9:1-5; 10:1-11) N’chifukwa chakenso Akula ndi Purisikila anatenga Apolo “ndi kumufotokozera njira ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:24-26) Nayenso Paulo analimbikitsa Timoteyo, yemwe anali kale ndi luso lolalikira, kuti apitirize kuwonjezera luso lakelo n’cholinga choti ‘anthu onse aone kuti akupita patsogolo.’ (1 Tim. 4:13-15) Choncho kaya takhala nthawi yaitali bwanji tikutumikira Ambuye monga kapolo, tiyenera kupitirizabe kuwonjezera luso lathu pophunzitsa.
2 Muziphunzira Kuchokera kwa Ena: Tingawonjezerenso luso lathu lophunzitsa, pophunzira kwa Akhristu anzathu. (Miy. 27:17) Choncho munthu amene tayenda naye akamalalikira, tizimvetsera mwatcheru. Tingathenso kufunsa malangizo kwa abale ndi alongo omwe amalalikira mwaluso. (Miy. 1:5) Kodi mumavutika kuchita maulendo obwereza, phunziro la Baibulo kapena kulalikira pogwiritsa ntchito njira zina? Funsani woyang’anira kagulu kanu kapena wofalitsa waluso kuti akuthandizeni. Musaiwalenso kuti mzimu wa Mulungu ungakuthandizeni kuti muzilalikira mwaluso, choncho muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimuwo.—Luka 11:13.
3 Ngati munthu wina wakupatsani malangizo musakhumudwe, ngakhale zitakhala kuti simunam’pemphe. (Mlal. 7:9) Muyenera kutengera chitsanzo cha Apolo yemwe analandira modzichepetsa malangizo omwe anapatsidwa. Zimenezi zingasonyeze kuti ndinu wanzeru.—Miy. 12:15.
AUGUST 8-14
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 3–4
“Nzeru Ndi Zamtengo Wapatali”
Kodi Solomo Ndi Chitsanzo Chabwino Kapena Choipa?
4 Kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Mulungu anaonekera kwa Solomo m’maloto n’kumuuza kuti apemphe zimene akufuna. Chifukwa chakuti Solomo ankazindikira zoti sadziwa zambiri iye anapempha nzeru. (Werengani 1 Mafumu 3:5-9.) Ndiyeno Mulungu anasangalala kuti Solomo wapempha nzeru osati chuma kapena ulemerero choncho anamupatsa “mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu” komanso chuma. (1 Maf. 3:10-14) Malinga ndi zimene Yesu ananena, nzeru za Solomo zinamveka patali kwambiri moti mfumukazi ya ku Sheba inamva n’kuyenda mtunda wautali kwambiri kuti ikadzionere yokha.—1 Maf. 10:1, 4-9.
5 Ife sitiyembekezera kulandira nzeru m’njira yozizwitsa. Solomo ananena kuti “Yehova amapereka nzeru” koma analemba kuti tiyenera kuchita khama kuti tipeze nzeruzo. Iye anati tiyenera ‘kumvetsera nzeru ndi khutu lathu ndi kuika mtima wathu pa kuzindikira.’ Pa nkhani yopeza nzeruyi, iye anagwiritsanso ntchito mawu ngati ‘kuitana,’ ‘kufunafuna’ ndiponso ‘kufufuza.’ (Miy. 2:1-6) Izi zikusonyezeratu kuti tikhoza kupeza nzeru.
6 Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikutsatira chitsanzo cha Solomo pa nkhani yoona kuti nzeru yochokera kwa Mulungu ndi yamtengo wapatali?’ Mavuto a zachuma achititsa anthu ambiri kuganizira kwambiri za ntchito komanso ndalama zawo. Ena amalola kuti zimenezi ziwachititse kusankha maphunziro apamwamba. Nanga bwanji za inu ndi banja lanu? Kodi zosankha zanu zimasonyeza kuti mumaona kuti nzeru yochokera kwa Mulungu ndi yamtengo wapatali ndipo mukufuna kuipeza? Kodi kusintha zolinga zanu kungakuthandizeni kuti mupeze nzeru zambiri? Dziwani kuti kupeza nzeru ndiponso kuitsatira kudzakuthandizani kwa moyo wanu wonse. Solomo analemba kuti: “Ukachita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.”—Miy. 2:9.
Mfundo Zothandiza
Yehova ndi Mulungu Wamapangano
15 Ana a Abulahamu atakhala monga mtundu n’kupatsidwa Chilamulo, Yehova anawadalitsa mogwirizana ndi lonjezo limene anapanga ndi kholo lawo. Mu 1473 B.C.E., Yoswa yemwe analowa m’malo mwa Mose, anatsogolera Aisiraeli kukalowa mu Kanani. Lonjezo la Yehova loti adzapereka dzikolo kwa ana a Abulahamu linakwaniritsidwa pamene mafuko anagawana dzikolo. Pamene Aisiraeli anali okhulupirika, Yehova anakwaniritsa lonjezo lake lakuti adzawathandiza kugonjetsa adani awo. Zimenezi zinaonekera bwino pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Davide. Pofika nthawi ya Solomo, yemwe anali mwana wa Davide, mbali yachitatu ya pangano la Abulahamu inakwaniritsidwa. “Ayuda ndi Aisiraeli anachuluka kwambiri. Kuchuluka kwake anali ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja, ndipo anali kudya, kumwa, ndi kusangalala.”—1 Mafumu 4:20.
AUGUST 15-21
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 5-6
“Anagwira Ntchito Mwamphamvu Komanso ndi Mtima Wonse”
Kodi Mukudziwa?
Matabwa a ku Lebanoni anali odziwika kwambiri chifukwa anali olimba, okongola, akafungo kabwino ndiponso sankafumbwa. Choncho Solomo anagwiritsa ntchito matabwa apamwamba kwambiri pomanga kachisi. Masiku ano dera lamapiri ku Lebanoni kumene kalelo kunali nkhalango yaikulu ya mikungudza, kunangotsala nkhalango zing’onozing’ono za apo ndi apo.
it-1 424
Mtengo wa Mkungudza
Matabwa a mtengo wa mkungudza oti akwanire ntchito zonsezo anafunika kuti anthu ambiri agwire ntchito yodula mitengo, kuisamutsira ku Tulo kapena ku Sidoni, mizinda imene inali m’mbali mwa nyanja ya Mediterranean, kuimanga pamodzi ngati phaka n’kuiyandamitsa pa nyanja kuti ikafike kudoko lina, mwina ku Yopa. Kenako ankayenda nayo pamtunda kukafika ku Yerusalemu. Zimenezi zinatheka chifukwa cha mgwirizano umene Solomo ndi Hiramu anachita. (1Mf 5:6-18; 2Mb 2:3-10) Ntchito zimenezi zitatha, matabwa anapitirizabe kubwera ku Yerusalemu moti zinanenedwa kuti mu ulamuliro wake, Solomo anachititsa kuti “matabwa a mkungudza akhale ochuluka kwambiri ngati mitengo yamkuyu.”—1Mf 10:27; yerekezerani ndi Yes 9:9, 10.
it-2 1077 ¶1
Kachisi
Pamene ankakonzekera, Solomo analemba ntchito yokakamiza amuna 30,000 a Chiisiraeli ndipo ankawatumiza mosinthanasinthana ku Lebanoni m’magulu a anthu 10,000. Ankakhala kumeneko kwa mwezi umodzi kenako kwa miyezi iwiri ankakhala ku nyumba kwawo. (1Mf 5:13, 14) Analembanso ntchito anthu 70,000 omwe “anali alendo m’dziko la Isiraeli” kuti azinyamula katundu, ndi enanso 80,000 osema miyala. (1Mf 5:15; 9:20, 21; 2Mb 2:2) Solomo anasankha akapitawo oyang’anira ntchitoyo okwana 550, komanso ena owathandizira okwana 3,300. (1Mf 5:16; 9:22, 23) Zikuoneka kuti mwa anthu amenewa, 250 anali Aisiraeli, pomwe 3,600 anali “alendo m’dziko” la Isiraeli.—2Mb 2:17, 18.
Mfundo Zothandiza
g 5/12 17, bokosi
Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 1
BAIBULO LIMANENA NDENDENDE NTHAWI YOMWE ZINTHU ZINACHITIKA
Pa lemba la 1 Mafumu 6:1 pali chitsanzo chosonyeza kuti Baibulo limanena ndendende nthawi yomwe zinthu zinachitika. Lembali limanena za nthawi imene Mfumu Solomo inayamba ntchito yomanga kachisi ku Yerusalemu. Limati: “Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova. Anayamba kuchita zimenezi m’chaka cha 480 [patatha zaka 479] kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo, m’mwezi wachiwiri wa Zivi. Ichi chinali chaka chachinayi cha ulamuliro wake monga mfumu ya Isiraeli.”
Baibulo limasonyeza kuti chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomo chinali 1034 B.C.E. Tikawerengetsera chobwerera m’mbuyo, zaka 479 zikutifikitsa m’chaka cha 1513 B.C.E., chaka chomwe Aisiraeli anatuluka mu Iguputo.
AUGUST 22-28
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 7
“Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Zipilala Ziwiri”
“M’mapiri Ake Mudzakumbamo Mkuwa”
Mfumu Solomo inagwiritsa ntchito mkuwa wambiri pomanga kachisi ku Yerusalemu. Wambiri mwa mkuwa umene Solomo anagwiritsa ntchitowu, unali wochokera kwa Davide, bambo ake, womwe anaupeza atagonjetsa Asiriya kunkhondo. (1 Mbiri 18:6-8) “Thanki yamkuwa” imene ansembe ankagwiritsa ntchito pa utumiki wawo inali yaikulu malita 66,000 ndipo mwina inkalemera matani 30. (1 Mafumu 7:23-26, 44-46) Ndiye panalinso zipilala ziwiri za mkuwa zomwe zinali pakhomo la kachisi. Zipilalazi zinali ndi zibowo zazikulu kuposa mita imodzi, khoma lake linali lonenepa masentimita 7 ndi hafu ndipo zinali zazitali mamita 8. Pamwamba pa zipilalazi panali mitu yotalika kupitirira pang’ono mamita awiri. (1 Mafumu 7:15, 16; 2 Mbiri 4:17) Ndiye tangoganizani kuchuluka kwa mkuwa umene anagwiritsa ntchito kupanga zinthu zimenezi.
it-1 348
Boazi, II
Pakhonde la kachisi wa ulemerero amene Solomo anamanga, anaikapo zipilala ziwiri zikuluzikulu zamkuwa. Chomwe chinali kumpoto anachipatsa dzina lakuti Boazi, lomwe mwina linkatanthauza “Mu Mphamvu.” Chakumwera anachipatsa dzina lakuti Yakini, lomwe limatanthauza “Iye [Yehova] Akhazikitse.” Munthu amene waima moyang’ana kum’mawa n’kumaona zipilala ziwirizi pamodzi, akawerenga kuchokera kumanja kupita kumanzere, mayinawa ali ndi tanthauzo lakuti, ‘Iye [Yehova] akhazikitse [kachisi] mwa mphamvu.’—1Mf 7:15-21.
Mfundo Zothandiza
it-1 263
Kusamba
Ukhondo ndi wofunika kwa anthu amene amalambira Yehova m’njira yoyera. Zimenezi zinasonyezedwa bwino ndi zimene zinkachitika pa chihema komanso zimene zinkachitika ku kachisi pambuyo pake. Pa nthawi imene ankawalonga unsembe, Mkulu wa Ansembe Aroni komanso ana ake, anasamba asanavale zovala za unsembe. (Eks 29:4-9; 40:12-15; Le 8:6, 7) Posamba m’manja komanso mapazi, ansembe ankagwiritsa ntchito madzi omwe anali m’beseni la mkuwa lomwe linali mu bwalo la chihema, komanso omwe anali mu thanki yamkuwa pa kachisi amene Solomo anamanga. (Eks 30:18-21; 40:30-32; 2Mb 4:2-6) Pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, mkulu wa ansembe ankasamba kawiri. (Le 16:4, 23, 24) Amene ankanyamula mbuzi ya Azazeli, zotsalira za nsembe ya nyama komanso ng’ombe yaikazi yofiira yomwe inkaperekedwa nsembe kupita nazo kunja kwa msasa, ankafunika kusamba thupi lonse komanso kuchapa zovala zawo asanabwerere kumsasa.—Le 16:26-28; Nu 19:2-10.
AUGUST 29–SEPTEMBER 4
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 8
“Solomo Anapemphera Modzichepetsa Komanso Mochokera Pansi pa Mtima”
Kuphunzira Baibulo Kungathandize Kuti Mapemphero Anu Azikhala Atanthauzo
9 Kuti Mulungu ayankhe pemphero lathu, liyenera kuchokera mumtima. Anthu asanasonkhane ku Yerusalemu pa mwambo wotsegulira kachisi wa Yehova mu 1026 B.C.E., Solomo anapemphera kuchokera mumtima ndipo pemphero limeneli linalembedwa pa 1 Mafumu chaputala 8. Solomo anatamanda Mulungu likasa la chipangano litaikidwa m’Malo Opatulikitsa ndiponso mtambo wa Yehova utadzaza m’kachisi.
10 Werengani bwinobwino pemphero la Solomo ndipo onani mmene akutchulira mobwerezabwereza mawu akuti mtima. Solomo ananena kuti Yehova yekha ndi amene amadziwa mtima wa munthu. (1 Maf. 8:38, 39) Pempheroli limasonyezanso kuti pali chiyembekezo chakuti wochimwa amene ‘wabwerera kwa Mulungu ndi mtima wake wonse,’ angakhululukidwe. Ngati anthu a Mulungu atagwidwa kukhala akapolo, mapemphero awo akanamvedwa ngati mtima wawo unali wangwiro ndi Yehova. (1 Maf. 8:48, 58, 61) Motero mapemphero anu ayenera kuchokera mumtima.
Kwezani Manja Okhulupirika m’Pemphero
7 Kaya tikupemphera pagulu kapena patokha, mfundo yofunika ya m’Malemba imene tiyenera kukumbukira ndi yakuti tiyenera kuonetsa mtima wodzichepetsa m’mapemphero athu. (2 Mbiri 7:13, 14) Mfumu Solomo inapemphera modzichepetsa pagulu pamene ankapereka kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Solomo anali atangomaliza kumanga imodzi mwa nyumba zapamwamba kwambiri zimene zinamangidwapo padziko lapansi. Komabe, anapemphera modzichepetsa kuti: “Kodi Mulungu angakhaledi padziko lapansi? Taonani! Kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, simungakwaneko. Kuli bwanji nyumba imene ndamangayi?”—1 Mafumu 8:27.
Monga Solomo, tiyenera kukhala odzichepetsa tikamapemphera m’malo mwa ena pagulu. Ngakhale kuti sitiyenera kulankhula ngati wopatulika kwambiri, koma mmene mawu athu amamvekera zingasonyeze kuti ndife odzichepetsa. Mapemphero odzichepetsa sakhala ndi mawu ovuta kumva kapena okokomeza. Amapangitsa anthu kuganiza za Mulungu osati za munthu amene akupempherayo. (Mateyu 6:5) Kudzichepetsa kumaonekeranso mwa zimene timanena popemphera. Tikamapemphera modzichepetsa, mawu athu samveka ngati tikulamula Mulungu kuti achite zinthu m’njira imene ifeyo tikufuna. M’malomwake, tidzapempha Yehova kuti achite zimene zikugwirizana ndi chifuniro chake. Chitsanzo chabwino ndi wolemba masalimo amene anachonderera Yehova kuti: “Haa! Inu Yehova, chonde tipulumutseni. Haa! Inu Yehova, chonde tithandizeni kuti zinthu zitiyendere bwino.”—Salimo 118:25; Luka 18:9-14.
Mfundo Zothandiza
it-1 1060 ¶4
Kumwamba
Solomo yemwe anamanga kachisi ku Yerusalemu ananena kuti Mulungu sangakwane “kumwamba, ngakhale kumwambamwamba.” (1Mf 8:27) Yehova yemwe analenga kumwamba ali ndi malo apamwamba kwambiri ndipo “dzina lake lokhalo lili pamwamba posafikirika. Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.” (Sl 148:13) Yehova savutika kuyeza kumwamba mofanana ndi mmene munthu savutikira kuyeza chinthu mwa kuchiika pa chikhato cha dzanja lake kuchoka pa chala cha manthu kufika ku chala chaching’ono. (Yes 40:12) Mawu a Solomowa, sakutanthauza kuti Mulungu alibe malo enieni amene amakhala. Komanso sakutanthauza kuti amapezeka kulikonse ndiponso m’chilichonse. Zimenezi zikuonekera bwino pa mfundo inanso imene Solomo ananena yakuti Yehova mumve muli “kumwamba, malo anu okhala okhazikika,” kutanthauza kumwamba kumalo a mizimu.—1Mf 8:30, 39.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Atumiki Achikhristu Ayenera Kupemphera
1 Sitingathe kukwaniritsa utumiki wathu popanda thandizo la Yehova. Iye amatipatsa mphamvu yofunikira kuti tigwire ntchitoyi. (Afil. 4:13) Iye amagwiritsa ntchito angelo ake kuti atithandize kupeza anthu onga nkhosa. (Chiv. 14:6,7) Yehova ndi amene amakulitsa mbewu za choonadi zimene timabzala ndiponso kuthirira. (1 Akor. 3:6, 9) Choncho, m’pofunika kwambiri kuti Atumiki achikhristu azipemphera kwa Yehova posonyeza kuti amamudalira.
2 Tizipemphera Patokha: Tiyenera kupemphera nthawi iliyonse tikamapita kolalikira. (Aef. 6:18) Kodi tiyenera kupempherera zinthu zotani? Tingapemphe kuti tiziwaona bwino anthu a m’gawo lathu ndiponso kuti tikhale olimba mtima. (Mac. 4:29) Tingam’pemphe Yehova kuti atitsogolere kwa anthu amitima yabwino omwe tingathe kuphunzira nawo Baibulo. Ngati mwininyumba watifunsa funso, tingapereke pemphero lachidule la mumtima lopempha Yehova kuti atithandize kuyankha moyenera. (Neh. 2:4) Tingapempherenso kuti tiziuona utumiki wathu kukhala chinthu chofunika kwambiri. (Yak. 1:5) Komanso Yehova amasangalala ngati popemphera timatchula mawu oyamikira chifukwa chotipatsa mwayi wapadera wokhala atumiki ake.—Akol. 3:15.
3 Tizipempherera Ena: Tiyeneranso “kupemphererana wina ndi mnzake,” ndipo nthawi zina ndi bwino kutchula mayina a atumiki anzathu m’pempherolo. (Yak. 5:16; Mac. 12:5) Kodi mavuto ena okhudza thanzi lanu akukulepheretsani kulalikira mokwanira? Ngati ndi choncho, mungapempherere atumiki ena amene ali ndi thanzi labwino. Nthawi zonse muzidziwa kuti pemphero limene mungapereke m’malo mwawo ndi lamtengo wapatali. Ndibwinonso kupemphera kuti atsogoleri andale asamatsutse ntchito yathu yolalikira, n’cholinga choti abale athu akhale ndi “moyo wabata ndi wamtendere.”—1 Tim. 2:1, 2.
4 Patokha sitingathe kukwanitsa kulengeza uthenga wabwino padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Koma ngati ‘titalimbikirabe kupemphera,’ Yehova angatithandize.—Aroma 12:12.