-
Ndandanda ya Mlungu wa January 19Utumiki wa Ufumu—2015 | January
-
-
Ndandanda ya Mlungu wa January 19
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 19
Nyimbo Na. 131 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 7 ndime 9-17 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 1-4 (Mph. 8)
Na. 1: Oweruza 3:1-11 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Yehova Amadana ndi Chinyengo—bt tsa. 35 ndime 18-20 (Mph. 5)
Na. 3: Yehova Akhoza Kulepheretsa Mapulani a Anthu Oipa Ngati Ahitofeli—2 Sam. 16:23; 17:1-14 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
MUTU WA MWEZI UNO: ‘Tumikirani Ambuye Monga Kapolo Modzichepetsa Kwambiri.’—Mac. 20:19.
Mph. 10: Kodi Mukugwiritsa Ntchito Zakumapeto mu Baibulo la Dziko Latsopano? Nkhani yokambirana. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Zakumapeto zomwe zili mu Baibulo la Dziko Latsopano kuti tithandize munthu amene tikuphunzira naye Baibulo kumvetsa zokhudza (a) Gehena (b) Manda a anthu onse (Sheoli, Hade) (c) Dama.
Mph. 10: Kutumikira Mulungu Monga Kapolo Kumafuna Khama Komanso Kudzipereka. Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2014, tsamba 59 ndime 1 mpaka tsamba 62 ndime 1 komanso tsamba 67 ndime 2. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Mph. 10: “Pitirizani Kuwonjezera Luso Lanu Lophunzitsa.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 20 ndi Pemphero
-
-
Pitirizani Kuwonjezera Luso Lanu LophunzitsaUtumiki wa Ufumu—2015 | January
-
-
Pitirizani Kuwonjezera Luso Lanu Lophunzitsa
1. Tchulani zitsanzo za m’nthawi ya atumwi zosonyeza kuti tiyenera kupitirizabe kuwonjezera luso lathu lophunzitsa?
1 Akhristufe tiyenera kupitiriza kuwonjezera luso lathu lophunzitsa. N’chifukwa chake Yesu sanasiye kuphunzitsa otsatira ake kuti azilalikira mwaluso. (Luka 9:1-5; 10:1-11) N’chifukwa chakenso Akula ndi Purisikila anatenga Apolo “ndi kumufotokozera njira ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:24-26) Nayenso Paulo analimbikitsa Timoteyo, yemwe anali kale ndi luso lolalikira, kuti apitirize kuwonjezera luso lakelo n’cholinga choti ‘anthu onse aone kuti akupita patsogolo.’ (1 Tim. 4:13-15) Choncho kaya takhala nthawi yaitali bwanji tikutumikira Ambuye monga kapolo, tiyenera kupitirizabe kuwonjezera luso lathu pophunzitsa.
2. Kodi tingaphunzire bwanji kuchokera kwa anthu ena?
2 Muziphunzira Kuchokera kwa Ena: Tingawonjezerenso luso lathu lophunzitsa, pophunzira kwa Akhristu anzathu. (Miy. 27:17) Choncho munthu amene tayenda naye akamalalikira, tizimvetsera mwatcheru. Tingathenso kufunsa malangizo kwa abale ndi alongo omwe amalalikira mwaluso. (Miy. 1:5) Kodi mumavutika kuchita maulendo obwereza, phunziro la Baibulo kapena kulalikira pogwiritsa ntchito njira zina? Funsani woyang’anira kagulu kanu kapena wofalitsa waluso kuti akuthandizeni. Musaiwalenso kuti mzimu wa Mulungu ungakuthandizeni kuti muzilalikira mwaluso, choncho muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimuwo.—Luka 11:13.
3. Kodi mungatani munthu wina akakupatsani malangizo?
3 Ngati munthu wina wakupatsani malangizo musakhumudwe, ngakhale zitakhala kuti simunam’pemphe. (Mlal. 7:9) Muyenera kutengera chitsanzo cha Apolo yemwe analandira modzichepetsa malangizo omwe anapatsidwa. Zimenezi zingasonyeze kuti ndinu wanzeru.—Miy. 12:15.
4. Kodi Yesu anati n’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuwonjezera luso lathu lophunzitsa?
4 Kulalikira Mwaluso Kumachititsa Kuti Yehova Alemekezedwe: Yesu anagwiritsa ntchito fanizo pofuna kulimbikitsa otsatira ake kuti apitirize kuwonjezera luso lophunzitsa. Anati iye ali ngati mtengo wa mpesa ndipo ophunzira ake odzozedwa ali ngati nthambi za mtengowo. Ananenanso kuti Atate wake amatengulira nthambi iliyonse yobala zipatso “kuti ibale zipatso zambiri.” (Yoh. 15:2) Yehova amafuna kuti tipitirize kuwonjezera luso lathu n’cholinga choti tibale “chipatso cha milomo yathu.” (Aheb. 13:15) Kodi tikamachita zimenezi zotsatira zake zimakhala zotani? Yesu anati: “Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri.”—Yoh. 15:8.
-