Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/15 tsamba 2
  • Pitirizani Kuwonjezera Luso Lanu Lophunzitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kuwonjezera Luso Lanu Lophunzitsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Yofanana
  • “Mubale Chipatso Chambiri”
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Khalani Mtumiki Wopita Patsogolo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Kusangalala ndi Unansi Wathithithi
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Lalikirani ndi Cholinga Chopanga Ophunzira
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 1/15 tsamba 2

Pitirizani Kuwonjezera Luso Lanu Lophunzitsa

1. Tchulani zitsanzo za m’nthawi ya atumwi zosonyeza kuti tiyenera kupitirizabe kuwonjezera luso lathu lophunzitsa?

1 Akhristufe tiyenera kupitiriza kuwonjezera luso lathu lophunzitsa. N’chifukwa chake Yesu sanasiye kuphunzitsa otsatira ake kuti azilalikira mwaluso. (Luka 9:1-5; 10:1-11) N’chifukwa chakenso Akula ndi Purisikila anatenga Apolo “ndi kumufotokozera njira ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:24-26) Nayenso Paulo analimbikitsa Timoteyo, yemwe anali kale ndi luso lolalikira, kuti apitirize kuwonjezera luso lakelo n’cholinga choti ‘anthu onse aone kuti akupita patsogolo.’ (1 Tim. 4:13-15) Choncho kaya takhala nthawi yaitali bwanji tikutumikira Ambuye monga kapolo, tiyenera kupitirizabe kuwonjezera luso lathu pophunzitsa.

2. Kodi tingaphunzire bwanji kuchokera kwa anthu ena?

2 Muziphunzira Kuchokera kwa Ena: Tingawonjezerenso luso lathu lophunzitsa, pophunzira kwa Akhristu anzathu. (Miy. 27:17) Choncho munthu amene tayenda naye akamalalikira, tizimvetsera mwatcheru. Tingathenso kufunsa malangizo kwa abale ndi alongo omwe amalalikira mwaluso. (Miy. 1:5) Kodi mumavutika kuchita maulendo obwereza, phunziro la Baibulo kapena kulalikira pogwiritsa ntchito njira zina? Funsani woyang’anira kagulu kanu kapena wofalitsa waluso kuti akuthandizeni. Musaiwalenso kuti mzimu wa Mulungu ungakuthandizeni kuti muzilalikira mwaluso, choncho muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimuwo.—Luka 11:13.

3. Kodi mungatani munthu wina akakupatsani malangizo?

3 Ngati munthu wina wakupatsani malangizo musakhumudwe, ngakhale zitakhala kuti simunam’pemphe. (Mlal. 7:9) Muyenera kutengera chitsanzo cha Apolo yemwe analandira modzichepetsa malangizo omwe anapatsidwa. Zimenezi zingasonyeze kuti ndinu wanzeru.—Miy. 12:15.

4. Kodi Yesu anati n’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuwonjezera luso lathu lophunzitsa?

4 Kulalikira Mwaluso Kumachititsa Kuti Yehova Alemekezedwe: Yesu anagwiritsa ntchito fanizo pofuna kulimbikitsa otsatira ake kuti apitirize kuwonjezera luso lophunzitsa. Anati iye ali ngati mtengo wa mpesa ndipo ophunzira ake odzozedwa ali ngati nthambi za mtengowo. Ananenanso kuti Atate wake amatengulira nthambi iliyonse yobala zipatso “kuti ibale zipatso zambiri.” (Yoh. 15:2) Yehova amafuna kuti tipitirize kuwonjezera luso lathu n’cholinga choti tibale “chipatso cha milomo yathu.” (Aheb. 13:15) Kodi tikamachita zimenezi zotsatira zake zimakhala zotani? Yesu anati: “Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri.”—Yoh. 15:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena