Ndandanda ya Mlungu wa January 26
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 26
Nyimbo Na. 60 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 7 ndime 18-22 ndi bokosi patsamba 75 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 5-7 (Mph. 8)
Na. 1: Oweruza 7:12-25 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kumvera Mulungu Kuposa Anthu?—bt tsa. 39 ndime 9-11 (Mph. 5)
Na. 3: Njira Zotithandiza Kuphunzira za Yehova—igw tsa. 5 ndime 1-4 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
MUTU WA MWEZI UNO: ‘Tumikirani Ambuye Monga Kapolo Modzichepetsa Kwambiri.’—Mac. 20:19.
Mph. 10: Mabuku Ogawira mu January ndi February. Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zomwe anakumana nazo pogawira kabuku ka Uthenga Wabwino. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingagawirire kabukuka. Pomaliza kambiranani nkhani yakuti, “Tizinyamuka Tikangomaliza.”
Mph. 10: Akulu Omwe Amatumikira Ambuye Monga Akapolo—Wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Funsani wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda mafunso otsatirawa. Kodi ntchito yanu ndi yotani? Kodi mumakonzekera bwanji Phunziro la Nsanja ya Olonda? N’chifukwa chiyani zimakhala zovuta kuloza aliyense amene waimika dzanja? Kodi wowerenga, oyankha komanso abale a maikolofoni angathandize bwanji kuti Phunziro la Nsanja ya Olonda likhale lolimbikitsa komanso losangalatsa? Kodi Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yomwe mwalowa posachedwapa yakuthandizani bwanji kuti muzichititsa bwino Phunziro la Nsanja ya Olonda?
Mph. 10: “Muzigwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu mu Utumiki—‘Khalani Bwenzi la Yehova’” Nkhani yokambirana. Kambiranani zinthu zina zomwe zikupezeka pa mbali imeneyi. Ndipo ngati n’zotheka, ikani kavidiyo kamodzi kopezeka pa mbali imeneyi kuti omvera aonere. Pemphani omvera kuti afotokoze njira zomwe tingagwiritsire ntchito gawo lakuti “Khalani Bwenzi la Yehova” tikamalalikira mwamwayi, kunyumba ndi nyumba komanso m’malo opezeka anthu ambiri.
Nyimbo Na. 135 ndi Pemphero