Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr23 May tsamba 1-16
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Timitu
  • MAY 1-7
  • MAY 8-14
  • MAY 15-21
  • MAY 22-28
  • MAY 29–​JUNE 4
  • Tsanzirani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova
  • JUNE 5-11
  • JUNE 12-18
  • JUNE 19-25
  • JUNE 26–JULY 2
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwbr23 May tsamba 1-16

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

MAY 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 17–19

“Muziona Ena Mmene Yehova Amawaonera”

w17.03 24 ¶7

Kodi Mumatsatira ndi Mtima Wonse Zimene Zinalembedwa?

7 Tiyeni tsopano tikambirane chitsanzo cha mwana wa Asa dzina lake Yehosafati. Iye anali ndi makhalidwe abwino ambiri. Pa nthawi imene ankadalira Yehova zinthu zinkayenda bwino kwambiri. Koma iye analakwitsanso zinthu zina. Mwachitsanzo, anakonza zoti mwana wake wamwamuna akwatire mwana wamkazi wa Mfumu Ahabu ya Isiraeli, yomwe inali yoipa kwambiri. Kenako anagwirizana ndi Ahabu kuti akamenyane ndi Asiriya ngakhale kuti anachenjezedwa ndi mneneri Mikaya kuti asapite. Kunkhondoko, Yehosafati anapulumukira m’kamwa mwa mbuzi ndipo anabwerera ku Yerusalemu. (2 Mbiri 18:1-32) Ndiyeno mneneri Yehu anamufunsa kuti: “Kodi chithandizo chiyenera kuperekedwa kwa oipa, ndipo kodi muyenera kukonda anthu odana ndi Yehova?”​—Werengani 2 Mbiri 19:1-3.

w15 8/15 11-12 ¶8-9

Tiziganizira Kwambiri Chikondi cha Yehova

8 Yehova amafuna kuti tidziwe kuti amatikonda ndiponso samangoyang’ana zimene talakwitsa. Iye amafufuza zinthu zabwino mumtima mwathu. (2 Mbiri 16:9) Mwachitsanzo, anachita zimenezi ndi Mfumu Yehosafati ya ku Yuda. Pa nthawi ina, Yehosafati anagwirizana ndi Mfumu Ahabu ya ku Isiraeli kuti akalande Ramoti-giliyadi kwa Asiriya. Aneneri onyenga 400 ananamiza Ahabu kuti akapambana nkhondoyo. Koma mneneri wa Yehova dzina lake Mikaya ananena kuti akagonjetsedwa. Ahabu anaphedwa pa nkhondoyo ndipo Yehosafati anapulumukira mkamwa mwa mbuzi. Yehosafati atabwerera ku Yerusalemu anadzudzulidwa chifukwa chogwirizana ndi mfumu yoipayo. Ngakhale zinali choncho, Yehu mwana wa Haneni anauza Yehosafati kuti: “Pali zinthu zabwino zimene zapezeka mwa inu.”​—2 Mbiri 18:4, 5, 18-22, 33, 34; 19:1-3.

9 Kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Yehosafati analamula akalonga, Alevi ndiponso ansembe kuti azikaphunzitsa Chilamulo cha Yehova m’mizinda yonse ya Yuda. Zimenezi zinathandiza kwambiri moti anthu a m’mayiko ozungulira Yuda anayamba kuopa Yehova. (2 Mbiri 17:3-10) N’zoona kuti Yehosafati anachita zinthu zosayenera koma Yehova anakumbukirabe zabwino zimene anachita. Nafenso nthawi zina timachita zinthu zosayenera. Koma nkhani ya Yehosafatiyi ikutitsimikizira kuti Yehova adzapitirizabe kutikonda tikamayesetsa ndi mtima wonse kuchita zinthu zomusangalatsa.

Mfundo Zothandiza

w17.03 20 ¶10-11

Tizitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

10 Yehosafati “anapitiriza kuyenda m’njira za Asa bambo ake.” (2 Mbiri 20:31, 32) Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye analimbikitsa anthu kuti afunefune Yehova. Anayambitsa ntchito yapadera yophunzitsa anthu “pogwiritsira ntchito buku la chilamulo cha Yehova.” (2 Mbiri 17:7-10) Yehosafati anafika mpaka kudera la Efuraimu lomwe linali mu ufumu wa kumpoto wa Isiraeli ndipo anathandiza anthu kuti abwerere kwa Yehova. (2 Mbiri 19:4) Baibulo limati Mfumu Yehosafati “anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”​—2 Mbiri 22:9.

11 Ifenso tikhoza kuthandiza kwambiri pa ntchito yophunzitsa anthu imene Yehova akufuna kuti izigwiridwa masiku ano. Kodi inuyo mumafunitsitsa kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu mwezi uliwonse n’cholinga choti ayambe kutumikira Yehova? Ngati titachita khama, Yehova angatithandize kuti tiyambe kuphunzira Baibulo ndi munthu. Kodi mumapempha Yehova kuti akuthandizeni pa nkhaniyi? Nanga mumayesetsa kuphunzira ndi anthu ngakhale pa nthawi imene mukanafuna kupuma? Paja Yehosafati anakathandiza anthu a ku Efuraimu kuti abwerere kwa Yehova. Nafenso tingachite bwino kuthandiza anthu amene anafooka kuti ayambirenso kutumikira Mulungu. Nawonso akulu ayenera kuyendera anthu a m’gawo la mpingo wawo amene anachotsedwa, koma asintha.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w21.05 17-18 ¶11-15

Pitirizani Kuona Utumiki Wanu Moyenera

11 Anthu ena sachita chidwi ndi uthenga wathu. Iwo saona kufunika kodziwa Mulungu kapena mfundo za m’Baibulo. Samakhulupirira Mulungu chifukwa amaona mavuto ambiri amene akuchitika m’dzikoli. Iwo safuna kumvetsera uthenga wa m’Baibulo chifukwa cha chinyengo cha atsogoleri a chipembedzo omwe amati amatsatira mfundo za m’Baibulo. Ena amatanganidwa ndi ntchito, kusamalira banja kapenanso kulimbana ndi mavuto awo ndipo amalephera kuzindikira mmene Baibulo lingawathandizire. Ndiye tingatani kuti tizisangalalabe ngati anthu amene timawalalikira saona kufunika kwa uthenga wathu?

12 Muzisonyeza kuti mumawaganizira. Anthu ambiri amene poyamba sankachita chidwi ndi uthenga wabwino anayamba kumvetsera chifukwa choti ofalitsa anasonyeza kuti amawaganizira. (Werengani Afilipi 2:4.) Mwachitsanzo, David yemwe tamutchula kale uja anati, “Ngati munthu wina wanena kuti sakufuna tikambirane naye timaika Baibulo ndi mabuku athu m’chikwama n’kumuuza kuti: ‘Tingakonde kudziwa chifukwa chake simukufuna kuti tikambirane.’” Anthu amatha kudziwa ngati tasonyeza kuti timawaganizira. Akhoza kuiwala zimene tanena, koma sangaiwale zimene tinachita posonyeza kuti timawaganizira. Ngakhale mwininyumba asatilole kuti tilankhule naye, zochita komanso nkhope yathu zingasonyeze kuti timamuganizira.

13 Timasonyeza kuti timaganizira ena tikamasintha uthenga wathu kuti ugwirizane ndi eni nyumba. Mwachitsanzo, kodi pali chinachake chimene chikusonyeza kuti pakhomopo pali ana? Ngati zili choncho mwina makolowo angasangalale kudziwa malangizo a m’Baibulo okhudza kulera ana kapena mfundo zothandiza kukhala ndi banja losangalala. Kodi pachitseko cha mwininyumbayo pali maloko angapo? Ngati ndi choncho mwina mungakambirane naye zokhudza uchigawenga komanso mantha amene anthu ambiri ali nawo m’dzikoli, ndipo mwininyumbayo angasangalale kudziwa kuti zimenezi zidzatha. Mulimonse mmene zingakhalire, tizithandiza anthu amene akufuna kumvetsera uthenga wathu kudziwa mmene malangizo a m’Baibulo angawathandizire. Katarína yemwe tamutchula kale uja ananena kuti, “Nthawi zonse ndimaganizira mmene mfundo za m’Baibulo zandithandizira pa moyo wanga.” Zimenezi zimamuthandiza Katarína kuti azilankhula mochokera pansi pamtima ndipo anthu amatha kuona kuti iye amakhulupirira kwambiri zimene akufotokozazo.

14 Muzilola kuti ena akuthandizeni. Mu nthawi ya Atumwi, Paulo anaphunzitsa Timoteyo mmene angalalikirire komanso kuphunzitsa ndipo anamulimbikitsa kuti aziphunzitsanso ena zimenezo. (1 Akor. 4:17) Mofanana ndi Timoteyo, ifenso tingaphunzire zambiri kwa ena amene ali ndi luso mumpingo. (Werengani Miyambo 27:17.) Taganizirani chitsanzo cha m’bale wina dzina lake Shawn. Kwa kanthawi iye anachita upainiya m’dera lina lakumudzi kumene anthu ambiri ankakonda kwambiri chipembedzo chawo. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti azisangalala ndi utumiki wake? Iye anati, “Ndinkayesetsa kuti ndikamalalikira ndikhale ndi munthu wina ndipo tikamachoka nyumba ina kupita nyumba ina tinkakambirana zimene tingachite kuti tiwonjezere luso lathu lophunzitsa. Mwachitsanzo, tinkakambirana zimene tachita pakhomo limene tangomaliza kulalikira n’kuona zomwe tingachite ngati titakumananso ndi zomwe takumana nazo pakhomo limenelo.”

15 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni pa nthawi iliyonse imene mukugwira ntchito yolalikira. Tikutero chifukwa popanda kuthandizidwa ndi mzimu wake womwe ndi wamphamvu, sitingakwanitse kugwira ntchitoyi. (Sal. 127:1; Luka 11:13) Mukamapemphera kwa Yehova, muzitchula zenizeni zimene mukufuna kuti akuthandizeni. Mwachitsanzo, mungamupemphe kuti akutsogolereni kwa anthu oyenerera omwe akufuna kumvetsera. Kenako muzichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lanu polalikira kwa aliyense amene mwakumana naye.

MAY 8-14

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 20–21

“Khulupirirani Yehova Mulungu Wanu”

w14 12/15 23 ¶8

Tizigwirizana Kwambiri Pamene Mapeto Akuyandikira

8 M’nthawi ya Mfumu Yehosafati, anthu a Mulungu anakumananso ndi mavuto. Kunabwera “khamu lalikulu” la adani ochokera m’madera ozungulira. (2 Mbiri 20:1, 2) Chosangalatsa n’chakuti Aisiraeliwo anadalira Yehova osati mphamvu zawo. (Werengani 2 Mbiri 20:3, 4.) Iwo anachita zinthu mogwirizana osati mmene aliyense ankafunira. Baibulo limati: “Anthu onse a ku Yuda anali ataimirira pamaso pa Yehova, kuphatikizapo akazi awo ndi ana awo, ngakhalenso ana awo ang’onoang’ono.” (2 Mbiri 20:13) Anthu a misinkhu yonse anamvera Yehova mogwirizana ndipo iye anawateteza. (2 Mbiri 20:20-27) Nafenso tiyenera kuchita zimenezi tikakumana ndi mavuto.

w21.11 16 ¶7

Amene Mwangokwatirana Kumene, Muziika Kutumikira Yehova Pamalo Oyamba

7 Yehova analankhula ndi Yehosafati kudzera mwa Mlevi wina dzina lake Yahazieli. Yehova anati: “Khalani m’malo anu, imani chilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani.” (2 Mbiri 20:13-17) N’zoona kuti imeneyi si njira imene anthu amagwiritsa ntchito pomenya nkhondo. Komatu malangizowa sikuti anachokera kwa munthu. Anali ochokera kwa Yehova. Yehosafati anadalira kwambiri Mulungu ndipo anachita zomwe anauzidwa. Iye ndi anthu ake atapita kukakumana ndi adani awo anaika patsogolo pa asilikali ake, osati asilikali aluso kwambiri, koma oimba omwe analibe zida zomenyera nkhondo. Yehova sanamugwiritse fuwa lamoto Yehosafati, koma anamugonjetsera adani ake.​—2 Mbiri 20:18-23.

Mfundo Zothandiza

it-1 1271 ¶1-2

Yehoramu

Chimodzi mwa zifukwa zimene zinachititsa kuti Yehoramu asayende m’njira ya chilungamo ngati mmene anachitira bambo ake a Yehosafati, ndi zochita za mkazi wake Ataliya. (2Mf 8:18) Sikuti Yehoramu anangopha azibale ake 6 ndi akalonga ena a Yuda okha, koma anachititsanso kuti anthu amene ankawalamulira asiye kulambira Yehova n’kuyamba kulambira milungu yonyenga. (2Mb 21:1-6, 11-14) Ulamuliro wake wonse unaipitsidwa ndi mavuto amene ankachitika m’dzikolo komanso nkhondo zimene ankamenyana ndi mitundu ina. Choyamba Edomu anagalukira, kenako Libina anagalukiranso Yuda. (2Mf 8:20-22) Mneneri Eliya analembera Yehoramu kalata yomuchenjeza kuti: “Tamvera tsopano! Yehova adzalanga mwamphamvu anthu ako, ana ako ndi akazi ako, ndipo adzawononga katundu wako yense. Iweyo udzakhala wodwaladwala popeza udzadwala matenda a m’matumbo, mpaka matumbo ako adzatuluka chifukwa chodwala tsiku ndi tsiku.”​—2Mb 21:12-15.

Zinachitikadi monga mmene anachenjezera. Yehova analola kuti Aluya ndi Afilisiti aukire dzikolo ndipo anatenga akazi ndi ana a Yehoramu kupita nawo ku ukapolo. Mulungu analola mwana wamng’ono kwambiri yekha wa Yehoramu dzina lake Yehoahazi (yemwe ankadziwikanso kuti Ahaziya) kuti athawe chifukwa cha pangano la Ufumu limene anapanga ndi Davide. “Pambuyo pa zonsezi, Yehova anamudwalitsa matenda a m’matumbo osachiritsika. Patatha zaka ziwiri zathunthu iye akudwala, matumbo ake anatuluka” ndipo anafa mwapang’onopang’ono. Moyo wa munthu woipayu unathera pamenepa ndipo “anapita popanda womumvera chisoni. Anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide, koma osati m’manda a mafumu.” Mwana wake Ahaziya anakhala mfumu m’malomwake.​—2Mb 21:7, 16-20; 22:1; 1Mb 3:10, 11.

MAY 15-21

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 22–24

“Yehova Amadalitsa Anthu Amene Amachita Zinthu Molimba Mtima”

w09 4/1 24 ¶1-2

Yoasi Anasiya Kutumikira Yehova Chifukwa Chocheza ndi Anthu Ochita Zoipa

INALI nthawi yovuta kwambiri ku Yerusalemu, mzinda umene kunali kachisi wa Mulungu. Panthawiyi, Mfumu Ahaziya anali atangophedwa kumene. Ndipo zimene Ataliya, yemwe anali mayi wake wa Ahaziya anachita zinali zovuta kumvetsa. Iye anapha zidzukulu zake, ana aamuna a Ahaziya. Kodi ukudziwa chifukwa chimene anachitira zimenezi?​— Iye anatero kuti akhale wolamulira m’malo mwa zidzukulu zakezo.

Komabe Yoasi, mmodzi mwa zidzukulu za Ataliya amene panthawiyi anali wakhanda, anapulumuka ndipo agogo akewo sanadziwe chilichonse. Kodi ukufuna kudziwa kuti anapulumuka bwanji?​— Mwanayo anali ndi azakhali ake a Yoseba ndipo iwo anam’tenga n’kukamubisa mu kachisi wa Mulungu. Iwo anatha kukamubisa m’kachisi chifukwa amuna awo a Yehoyada anali mkulu wa ansembe. Choncho, awiriwa anaonetsetsa kuti mwanayo akutetezedwa.

w09 4/1 24 ¶3-5

Yoasi Anasiya Kutumikira Yehova Chifukwa Chocheza ndi Anthu Ochita Zoipa

Yoasi anabisidwa m’kachisi kwa zaka 6, ndipo ali m’kachisimo, anaphunzitsidwa mfundo zonse zokhudza Yehova Mulungu ndi malamulo Ake. Kenako Yoasi atafika zaka 7, Yehoyada anachita zinthu zoti Yoasi akhale mfumu. Kodi ungakonde kudziwa mmene Yehoyada anachitira zimenezi ndiponso zimene zinachitikira mfumukazi yoipa Ataliya, yomwe inali agogo ake a Yoasi?​—

Yehoyada anaitanitsa mwamseri asilikali olondera mafumu a ku Yerusalemu. Ndipo iye anawafotokozera mmene iye ndi mkazi wake anapulumutsira Yoasi, mwana wa Mfumu Ahaziya. Kenako, Yehoyada anatenga Yoasi n’kumusonyeza kwa asilikaliwo, ndipo iwo anaona kuti iye ndi amene anali woyenera kukhala mfumu. Choncho, anakonza njira yoti amulonge ufumu.

Yehoyada anatulutsira Yoasi kunja, n’kumuveka korona wachifumu. Zitatero anthu anayamba ‘kuwomba m’manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.’ Asilikali olondera mfumu aja anam’zungulira Yoasi pomuteteza. Koma Ataliya atamva anthu akufuula chifukwa cha chisangalalo, anathamanga kuti akawaletse. Ndipo Yehoyada analamula kuti Ataliya aphedwe, ndipo asilikaliwo anamuphadi.​—2 Mafumu 11:1-16.

it-1 379 ¶5

Kuika M’manda

Mkulu wa Ansembe Yehoyada analandira ulemu wapadera woikidwa “m’manda a mafumu mu Mzinda wa Davide.” Ndi munthu yekhayu amene sanali wa m’banja lachifumu yemwe analandira ulemu wapadera chonchi.​—2Mb 24:15, 16.

Mfundo Zothandiza

it-2 1223 ¶13

Zekariya

12. Mwana wa Mkulu wa Ansembe Yehoyada. Yehoyada atamwalira, Mfumu Yehoasi inayamba kumvera malangizo olakwika m’malo momvera aneneri a Yehova ndipo inasiya kulambira koona. Zekariya, yemwe anali msuweni wa Yehoasi (2Mb 22:11), anachenjeza anthuwo mwamphamvu, koma m’malo molapa, iwo anamuponya miyala m’bwalo la kachisi. Pakufa Zekariya ananena kuti: “Yehova aone zimene mwachitazi ndi kubwezera.” Mawu aulosiwa anakwaniritsidwa, osati panthawi imene Asiriya anawononga mzinda wa Yuda yokha, koma pamenenso Yehoasi anaphedwa ndi atumiki ake awiri “chifukwa cha magazi a ana a wansembe Yehoyada.” Baibulo Lachigiriki la Septuagint ndi Lachilatini la Vulgate limanena kuti Yehoasi anaphedwa pofuna kubwezera magazi a “mwana” wa Yehoyada. Malemba achimasorete komanso Baibulo Lachisiriya la Peshitta, limanena mochulukitsa kuti “ana,” mwina pofuna kusonyeza ulemu komanso kufunika kwa mwana wa Yehoyada, Zekariya, yemwe anali mneneri komanso wansembe.​—2Mb 24:17-22, 25.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w10 2/15 6-8 ¶6-10

‘Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima’

6 Njira yosavuta imene tingalandirire mzimu woyera wa Mulungu, ndi mwa kupempha Mulungu kuti atipatse mzimuwo. Yesu anauza anthu amene ankamumvetsera kuti: “Ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Ndithudi, nthawi zonse tifunika kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera. Ngati mbali zina za utumiki monga kulalikira mumsewu, mwamwayi, kapena m’gawo la malonda kumatichititsa mantha, tingapemphe Yehova kuti atipatse mzimu wake ndiponso kuti atithandize kukhala olimba mtima.​—1 Ates. 5:17.

7 Izi n’zimene mkazi wina wachikhristu dzina lake Rosa anachita. Tsiku lina iye ali ku ntchito, mphunzitsi wina yemwe amagwira naye ntchito ankawerenga lipoti lochokera kusukulu ina lomwe linkanena zakuti ana ena ankazunzidwa. Mphunzitsiyo anasokonezeka maganizo ndi zimene anawerengazo, ndipo anati: “Kodi dzikoli likulowera kuti?” Rosa anaona kuti uwu unali mwayi wake woti alalikire. Kodi iye anatani kuti alimbe mtima kulalikira? Iye anati: “Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize ndi mzimu wake.” Atatero, Rosa anakwanitsa kulalikira ndipo anagwirizana zoti adzakambiranenso nkhaniyi. Taganiziraninso za Milane, mtsikana wina wa zaka 5 amene amakhala ku New York City. Iye anati: “Nthawi zonse ndisanapite kusukulu, ine ndi amayi anga timapemphera kwa Yehova.” Kodi iwo amapempha chiyani? Kuti Milane akhale wolimba mtima n’cholinga choti adzitha kufotokoza zimene amakhulupirira zokhudza Mulungu. Amayi ake anati: “Zimenezi zathandiza Milane kufotokoza zimene amakhulupirira pa nkhani ya kukumbukira masiku obadwa ndiponso maholide. Zathandizanso kuti asamachite nawo zinthu zimenezi.” Zitsanzo zimenezi zikusonyezadi kuti pemphero limathandiza munthu kukhala wolimba mtima.

8 Taganiziraninso zimene zinathandiza mneneri Yeremiya kuti akhale wolimba mtima. Yehova atamusankha kuti akhale mneneri wake kwa anthu amitundu, Yeremiya anati: “Sindithai kunena pakuti ndili mwana.” (Yer. 1:4-6) Koma Yeremiya anasintha maganizo akewa n’kuyamba kulalikira mwamphamvu, moti anthu ambiri anayamba kumuona ngati munthu wokonda kumangokamba za tsoka. (Yer. 38:4) Iye analengeza molimba mtima ziweruzo za Yehova kwa zaka zoposa 65. Anali wodziwika bwino m’dziko lonse la Isiraeli chifukwa cholalikira mopanda mantha ndiponso molimba mtima. Ndipo patatha zaka pafupifupi 600, kuchokera nthawi imeneyo, anthu ena ankati Yeremiya wauka ataona mmene Yesu ankalankhulira molimba mtima. (Mat. 16:13, 14) Kodi mneneri Yeremiya amene poyamba anali wamantha anatani kuti akhale wolimba mtima? Iye anati: ‘M’mtima mwanga [mawu a Mulungu] ali ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.’ (Yer. 20:9) Inde, mawu a Yehova anam’patsa mphamvu Yeremiya ndipo anamulimbitsa mtima kuti azilankhula.

9 M’kalata imene analembera Aheberi, mtumwi Paulo anati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amapyoza mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Amathanso kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.” (Aheb. 4:12) Uthenga wa Mulungu, kapena kuti mawu ake, ungatipatse mphamvu ngati mmene zinalili ndi Yeremiya. Ngakhale kuti anthu ndi amene anagwiritsidwa ntchito kulemba Baibulo, tisaiwale kuti anthuwo sanalembe nzeru zawo koma anauziridwa ndi Mulungu. Lemba la 2 Petulo 1:21 limati: “Ulosi sunayambe wadzapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” Tikamapeza nthawi yophunzira Baibulo patokha bwinobwino, m’maganizo mwathu mumakhala uthenga wouziridwa ndi mzimu woyera. (Werengani 1 Akorinto 2:10.) Uthenga umenewu ungakhale “ngati moto wotentha” m’maganizo mwathu, moti sitingathe kungousunga osauzako ena.

10 Kuti kuphunzira Baibulo patokha kukhale kothandiza kwambiri, tiyenera kuliphunzira m’njira yakuti uthenga wake utifike pamtima. Mwachitsanzo, mneneri Ezekieli m’masomphenya anauzidwa kuti adye mpukutu wa buku wokhala ndi uthenga wamphamvu woti akauze anthu osamvera. Iye anafunikira kuudziwa bwino uthengawo. Kuchita zimenezi kunachititsa kuti ntchito yofotokoza uthengawo ikhale yokoma ngati uchi.​—Werengani Ezekieli 2:8–3:4, 7-9.

MAY 22-28

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 25–27

“Yehova Akhoza Kukupatsani Zambiri Kuposa Pamenepa”

it-1 1266 ¶6

Yehoasi

Yehoasi anapereka asilikali aganyu masauzande ambiri kwa mfumu ya Yuda yomwe inkafuna kumenyana ndi Aedomu. Komabe, “munthu winawake wa Mulungu woona” ananena kuti asilikaliwo awabweze ngakhale anali atawalipira kale matalente asiliva okwana 100 ($660,600). Izi zinakwiyitsa kwambiri asilikaliwo chifukwa anataya mwayi wawo woti akapeze nawo zofunkha. Ndiye atabwerera kumpoto, iwo anaukira mizinda ya mu ufumu wa kummwera kuyambira ku Samariya (komwe mwina n’kumene kunali likulu lawo) mpaka ku Beti-horoni.​—2Mb 25:6-10, 13.

w21.08 30 ¶16

Kodi Tingatani Kuti ‘Tilawe’ Ubwino wa Yehova?

16 Muzilolera kudzimana kuti mutumikire Yehova. Sikuti timafunika kusiya zinthu zonse zabwino kuti tizisangalatsa Yehova. (Mlal. 5:19, 20) Komabe ngati titalephera kuchita zambiri potumikira Yehova, mwina pongofuna kusadzimana zinthu zina, tikhoza kukhala tikulakwitsa ngati munthu wamufanizo la Yesu. Iye anachita khama kuti azikhala moyo wawofuwofu koma sankaganizira za Mulungu. (Werengani Luka 12:16-21.) M’bale wina dzina lake Christian, yemwe amakhala ku France, ananena kuti, “Sindinkachita zonse zomwe ndingathe potumikira Yehova komanso kuthandiza banja langa.” Iye ndi mkazi wake anaganiza zoyamba upainiya. Koma kuti akwaniritse cholinga chawochi, ankafunika kusiya ntchito zawo. Kuti azipeza zinthu zofunikira pa moyo, iwo anayamba bizinezi yaing’ono yoyeretsa ma ofesi ndi nyumba za anthu ndipo anaphunzira kukhala okhutira ndi zochepa zimene ali nazo. Kodi iwo anayamba kusangalala chifukwa cha zimene anachitazi? Christian anati, “Timasangalala kwambiri ndi utumiki komanso kuona ophunzira Baibulo athu ndi maulendo obwereza akuphunzira za Yehova.”

Mfundo Zothandiza

w07 12/15 10 ¶1-2

Kodi Muli ndi Mlangizi pa Zauzimu?

UZIYA anakhala mfumu ya ufumu wa kum’mwera wa Yuda ali ndi zaka 16 zokha. Analamulira kwa zaka zoposa 50, kuyambira mu 829 B.C.E. mpaka mu 778 B.C.E. Kuyambira ali mwana, Uziya ‘anachita zoongoka pamaso pa Yehova.’ Kodi n’chiyani chinam’thandiza kuchita zinthu zoyenera? Nkhani ya m’Baibulo imati: ‘Uziya anali munthu wakufuna Mulungu m’masiku a Zekariya, . . . [wolangiza kuopa Mulungu woona] ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anam’lemereza.’​—2 Mbiri 26:1, 4, 5.

Ndi nkhani yokhayi m’Baibulo imene imafotokoza za Zekariya yemwe anali mlangizi wa mfumu. Komabe, Zekariya monga “wolangiza kuopa Mulungu woona,” anathandiza kwambiri mfumu yachinyamatayo kuchita zoyenera pa maso pa Yehova Mulungu. Buku lina lofotokoza Baibulo (lotchedwa Expositor’s Bible) limati, n’zodziwikiratu kuti Zekariya “anali munthu wodziwa bwino malemba ndiponso zinthu zauzimu komanso wodziwa kuphunzitsa zimene ankadziwazo.” Katswiri wina wa Baibulo anafika ponena za Zekariya kuti: “Ankadziwa kwambiri maulosi ndiponso . . . anali wanzeru, wodzipereka, munthu wabwino, ndipo zikuoneka kuti iyeyu ndi amene anathandiza kwambiri Uziya.”

MAY 29–​JUNE 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 28–29

“Mukhoza Kutumikira Yehova Ngakhale Makolo Anu Si Chitsanzo Chabwino”

w16.02 14 ¶8

Tsanzirani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova

8 Mosiyana ndi Rute, Hezekiya anabadwira mu mtundu wa Aisiraeli omwe anadzipereka kwa Yehova. Koma si Aisiraeli onse amene ankamvera Mulungu. Mwachitsanzo Ahazi, yemwe anali bambo ake a Hezekiya, anali mfumu yoipa kwambiri. Iye anachititsa kuti anthu a ku Yuda ayambe kulambira mafano ndipo sankalemekeza kachisi wa Yehova wa ku Yerusalemu. Ahazi anafika mpaka powotcha ana ake ena ali moyo n’kuwapereka nsembe kwa mulungu wonyenga. Choncho Hezekiya ali mwana, ankaona bambo ake akuchita zinthu zambiri zoipa.​—2 Maf. 16:2-4, 10-17; 2 Mbiri 28:1-3.

w16.02 14 ¶9-11

Tsanzirani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova

9 Zinthu zoipa zimene Hezekiya anaona bambo ake akuchita, zikanamukhumudwitsa kwambiri moti akanatha kukwiyira Yehova. Masiku ano, anthu ena amene anakumanapo ndi mavuto amaona kuti ali ndi zifukwa zomveka zoti ‘azikwiyira Yehova’ kapena gulu lake. (Miy. 19:3) Amachita zimenezi ngakhale kuti mavuto awo sakhala aakulu ngati a Hezekiya. Enanso amachita zinthu zoipa poganiza kuti sangachitire mwina chifukwa anakulira m’banja limene munkachitika zinthu zoipa. (Ezek. 18:2, 3) Koma kodi zimenezi ndi zoona?

10 Chitsanzo cha Hezekiya chimasonyeza kuti zimenezi si zoona. Palibe chifukwa chomveka chotichititsa kukwiyira Yehova popeza iye si amene amachititsa zinthu zoipa zimene timakumana nazo. (Yobu 34:10) N’zoona kuti zochita za makolo, zikhoza kuchititsa kuti ana awo azichita zabwino kapena zoipa. (Miy. 22:6; Akol. 3:21) Koma izi sizikutanthauza kuti munthu amene anakulira m’banja limene munkachitika zinthu zoipa sangakhale wabwino. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anatipatsa ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa. (Deut. 30:19) Kodi Hezekiya anagwiritsa ntchito bwanji ufulu umenewu?

11 Ngakhale kuti Hezekiya anali mwana wa mfumu yoipa kwambiri, atakula anakhala mfumu yabwino. (Werengani 2 Mafumu 18:5, 6.) Iye anasankha kutsatira chitsanzo cha anthu abwino osati cha bambo ake. Ankatsanzira chitsanzo cha anthu monga Yesaya, Mika ndi Hoseya omwe anali aneneri a Yehova. Hezekiya ankamvera zimene aneneriwo ankanena ndipo zinamuthandiza kuti akonze zinthu zoipa zimene bambo ake analakwitsa. Anayeretsa kachisi, kuchotsa mafano m’dziko lonse ndiponso kupempha Yehova kuti akhululukire anthu machimo awo. (2 Mbiri 29:1-11, 18-24; 31:1) Pamene Senakeribu mfumu ya Asuri anaopseza kuti aukira mzinda wa Yerusalemu, Hezekiya anachita zinthu molimba mtima ndipo anasonyeza kuti ankakhulupirira Yehova. Iye anadalira Yehova ndipo analimbikitsa anthu ake kuchita chimodzimodzi. (2 Mbiri 32:7, 8) Pa nthawi ina, Hezekiya anayamba mtima wodzikuza koma Yehova atamudzudzula, anadzichepetsa n’kusintha. (2 Mbiri 32:24-26) Iye ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe chifukwa sanalole kuti chitsanzo choipa cha bambo ake chimulepheretse kukhala munthu wabwino. M’malomwake anachita zinthu zimene zinamuthandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

Mfundo Zothandiza

w12 2/15 24-25

Natani Anali Wokhulupirika Ndipo Ankalimbikitsa Kulambira Koona

Popeza Natani ankalambira Yehova mokhulupirika, analimbikitsa Davide kuti amange nyumba yoyamba yoti azilambiriramo Mulungu padziko lapansi. Koma zikuoneka kuti pa nthawiyi, Natani anangonena maganizo ake m’malo monena zinthu m’dzina la Yehova. Ndiyeno usiku womwewo Mulungu anauza mneneriyu kuti akanene kwa mfumuyo uthenga wosiyana ndi umene ananena poyamba. Anakamuuza kuti samanga kachisi wa Yehova. Munthu woti adzamange kachisiyu anali mwana wa Davide. Koma Natani ananenanso kuti Mulungu akuchita pangano ndi Davide lakuti mpando wake wachifumu “udzakhazikika mpaka kalekale.”​—2 Sam. 7:4-16.

Maganizo a Mulungu anasiyana ndi zimene Natani ananena zokhudza kumanga kachisi. Izi zitachitika, mneneri wodzichepetsayu sananyinyirike, m’malomwake anagonjera ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Yehova. Apatu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha zimene tiyenera kuchita ngati Mulungu akutiwongolera pa nkhani inayake. Zimene Natani anachita pambuyo pa nkhani imeneyi zikusonyeza kuti ubwenzi wake ndi Mulungu unali wabwinobe. Ndipotu zikuoneka kuti Yehova anauzira Natani ndi Gadi, yemwe anali wamasomphenya, kuti alimbikitse Davide kukhazikitsa anthu 4,000 oti azidzaimbira Yehova pakachisi.​—1 Mbiri 23:1-5; 2 Mbiri 29:25.

JUNE 5-11

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 30–31

“Kusonkhana Pamodzi Kumatithandiza”

it-1 1103 ¶2

Hezekiya

Anali Wodzipereka pa Kulambira Koona. Hezekiya anasonyeza kuti anali wodzipereka polambira Yehova atangokhala kumene mfumu ali ndi zaka 25. Chinthu choyamba chimene anachita chinali kutsegula ndi kukonzanso kachisi. Kenako anasonkhanitsa pamodzi ansembe ndi Alevi n’kuwauza kuti: “Ineyo ndikufunitsitsa mumtima mwanga kuchita pangano ndi Yehova Mulungu wa Isiraeli.” Limeneli linali pangano la kukhulupirika, komwe kunali ngati kupangana kuti ku Yuda ayambirenso kutsatira pangano la Chilamulo chomwe anthu ankachinyalanyaza. Iye anachita zinthu mwakhama pamene anakonza zoti Alevi azichita utumiki wawo ndipo anabwezeretsanso zida zoimbira komanso kuti aziimba nyimbo zotamanda. Unali mwezi wa Nisani, umene ankayenera kuchita chikondwerero cha Pasika koma kachisi, ansembe ndi Alevi anali odetsedwa. Pofika tsiku la 16 la mwezi wa Nisani, kachisi anali atayeretsedwa komanso ziwiya zake zitabwezeretsedwa. Kenako anafunika kuchita mwambo wophimba machimo a Aisiraeli onse. Choyamba, akalonga anabweretsa nsembe yamachimo ya ufumuwo, ya malo opatulika ndi ya anthu onse ndipo kenako anthu onse anapereka nsembe zopsereza masauzande ambiri.​—2Mb 29:1-36.

it-1 1103 ¶3

Hezekiya

Chifukwa choti anthu akakhala odetsedwa sankayenera kuchita mwambo wa Pasika panthawi yake, Hezekiya anagwiritsa ntchito lamulo limene linkalola anthu odetsedwa kuchita mwambowu m’mwezi wotsatira. Iye anaitana anthu onse a ku Yuda komanso ku Isiraeli kudzera mwa asilikali othamanga omwe anakapereka makalata kuyambira ku Beere-seba mpaka ku Dani. Othamangawo anatsutsidwa ndi anthu ambiri, komabe anthu ena makamaka a fuko la Aseri, la Manase, ndi la Zebuloni anadzichepetsa ndipo anapita kumwambowo kuphatikizaponso ena a m’fuko la Efraimu ndi la Isakala. Kuwonjezera pa amenewa, kunafikanso anthu ena ambiri omwe sanali Aisiraeli koma ankalambira Yehova. Zikuoneka kuti zinali zovuta kwambiri kwa anthu olambira Yehova omwe ankakhala mu ufumu wa kumpoto kuti afike kumwambowo. Mofanana ndi asilikali othamanga aja, iwo akanatsutsidwa ndi kunyozedwa chifukwa ufumu wa mafuko 10wu unali utaipa kwambiri, unalowerera mu kulambira konyenga komanso unkavutitsidwa ndi Asuri.​—2Mb 30:1-20; Nu 9:10-13.

it-1 1103 ¶4-5

Hezekiya

Pambuyo pa mwambo wa Pasika, Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa chinachitika kwa masiku 7, ndipo anthu onse amene anasonkhana anasangalala moti anagwirizana kuti achiwonjezere ndi masiku enanso 7. Ngakhale pa nthawi yovuta ngati imeneyo, Yehova anadalitsa anthu ake moti “munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira m’masiku a Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli, kunali kusanachitike chikondwerero ngati chimenechi ku Yerusalemu.”​—2Mb 30:21-27.

Zomwe zinachitika kenako zimasonyeza kuti kumeneku kunali kubwezeretsedwa kwa kulambira koona osati chabe chikondwerero chosangalatsa chakanthawi. Asanabwerere kwawo, anthu amene ankachita chikondwererowo anapita kukaphwanya zipilala zopatulika, kukagwetsa malo okwezeka ndi maguwa ansembe komanso kukadula mizati yopatulika mu Yuda, mu Benjamini ngakhalenso mu Efraimu ndi mu Manase yense. (2Mb 31:1) Hezekiya anasonyeza chitsanzo chabwino pophwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga chifukwa anthu anaipanga kukhala fano ndipo ankaiperekera nsembe zautsi. (2Mf 18:4) Pambuyo pa chikondwerero, Hezekiya anaonetsetsa kuti anthu akupitiriza kulambira koona pokonza zoti ansembe azigwira ntchito m’magulu komanso kukonza kuti ena azithandiza utumiki wa pakachisi; analimbikitsanso anthuwo kumvera Chilamulo, monga kupereka chakhumi komanso zipatso zoyambirira kucha kwa Alevi ndi ansembe ndipo anthuwo anayambadi kuchita zimenezi ndi mtima wonse.​—2Mb 31:2-12.

Mfundo Zothandiza

w18.09 6 ¶14-15

“Ngati Zimenezi Mukuzidziwa, Ndinu Odala Mukamazichita”

14 Chinthu china chimene chimasonyeza kuti ndife odzichepetsa ndi zimene timachita anthu ena akamatilankhula. Paja lemba la Yakobo 1:19 limanena kuti tiyenera ‘kukhala ofulumira kumva.’ Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. (Gen. 18:32; Yos. 10:14) Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya pa Ekisodo 32:11-14. (Werengani.) Ngakhale kuti Yehova akanatha kuchita zinthu popanda kumva maganizo a Mose, anamupatsa mpata kuti afotokoze zimene ankaganiza. Anthu ambiri sangataye nthawi kumvetsera maganizo a munthu yemwe nthawi zina maganizo ake sakhala olondola ndipo sangatsatire zimene wanena. Koma Yehova amamvetsera moleza mtima anthu amene amapemphera kwa iye mwachikhulupiriro.

15 Yehova anadzichepetsa kuti amvetsere anthu monga Abulahamu, Rakele, Mose, Yoswa, Manowa, Eliya komanso Hezekiya. Choncho aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Ngati Yehova anamvetsera anthuwa, kuli bwanji ineyo? Kodi inenso ndimayesetsa kulemekeza abale ndi alongo n’kumawamvetsera akamalankhula ndiponso kutsatira maganizo awo omwe ndi othandiza? Nanga pali munthu wina mumpingo kapena m’banja langa amene akufunika kwambiri kuti ndizimumvetsera? Kodi ndiyenera kuchita chiyani?​—Gen. 30:6; Ower. 13:9; 1 Maf. 17:22; 2 Mbiri 30:20.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w19.01 11-12 ¶13-18

Tizitamanda Yehova Mumpingo

13 Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzipereka ndemanga zolimbikitsa kumisonkhano? Tiyeni tikambirane zina mwa zinthu zimenezi.

14 Muzikonzekera misonkhano yonse. Mukakonzekera bwino, mukhoza kulimba mtima kuti muyankhe. (Miy. 21:5) Koma sikuti tonsefe timakonzekera m’njira yofanana. Mwachitsanzo, Mlongo Eloise, yemwe ndi wamasiye komanso wazaka za m’ma 80, amayamba kukonzekera Nsanja ya Olonda chakumayambiriro kwa mlungu. Iye anati: “Ndikayambiratu kukonzekera ndimasangalala kwambiri ndi misonkhano.” Mlongo winanso dzina lake Joy, yemwe amagwira ntchito yolembedwa, amakonzekera Nsanja ya Olonda Loweruka. Iye anati: “Ndikakonzekera Loweruka zimandithandiza kuti ndikumbukire mosavuta mfundo zake.” M’bale Ike, yemwe ndi mkulu komanso mpainiya, anati: “Sindikonzekera phunziro lonse nthawi imodzi. Ndimakonda kukonzekera pang’onopang’ono mkati mwa mlungu.”

15 Kodi tingatani kuti tizikonzekera bwino? Musanayambe kukonzekera, muzipempha Yehova kuti akupatseni mzimu woyera. (Luka 11:13; 1 Yoh. 5:14) Kenako muziona mwachidule zimene zili munkhaniyo. Mwachitsanzo, muziona mutu, timitu ting’onoting’ono, zithunzi komanso mabokosi. Ndiyeno mukayamba kuphunzira ndime iliyonse, muziyesetsa kuwerenga malemba osagwidwa mawu. Muziganizira kwambiri nkhaniyo n’kuona mfundo zimene mungakayankhe. Mukakonzekera bwino, nkhaniyo imakufikani pamtima kwambiri ndipo zimakhala zosavuta kuti mukayankhe.​—2 Akor. 9:6.

16 Ngati n’zotheka muzigwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Gulu la Yehova latipatsa zinthu zambiri zapazipangizo zamakono zimene zingatithandize pokonzekera misonkhano. Mwachitsanzo, pulogalamu ya JW Library® imatithandiza kuti tikhale ndi mabuku komanso zinthu zina pazipangizo zathu. Izi zimathandiza kuti tizitha kuphunzira, kuwerenga kapena kumvetsera zinthuzo pa nthawi iliyonse komanso kwina kulikonse. Ena amagwiritsa ntchito zinthu zimenezi kuti aziphunzira pa nthawi yopuma kuntchito kapena kusukulu ngakhalenso poyenda. Zinthu ngati Watchtower Library komanso LAIBULALE YA PA INTANETI™ zimathandiza tikamafufuza nkhani zimene tikufuna kuziphunzira mozama.

17 Ngati n’zotheka muzikonzekera ndemanga zingapo pa phunziro lililonse. Tikutero chifukwa chakuti nthawi zina wochititsa phunzirolo sangakutchuleni pamene mwakweza dzanja. Popeza enanso amakweza manja, wochititsa angasankhe munthu wina osati inuyo. Pofunanso kusunga nthawi, wochititsa sangalole kuti anthu ambirimbiri ayankhe pa mfundo imodzi. Ndiye musamakhumudwe ngati simunatchulidwe chakumayambiriro kwa phunziro. Koma ngati mwakonzekera ndemanga zingapo, zingakhale zosavuta kuti mupeze mwayi woyankha pa nthawi ina. Mukhozanso kukonzekera kuti mukawerenge lemba. Ngati n’zotheka, muziyesetsanso kukonzekera kuti mukayankhe m’mawu anuanu.

18 Muzipereka ndemanga zachidule. Nthawi zambiri ndemanga zachidule komanso zosavuta kumva n’zimene zimakhala zolimbikitsa kwambiri. Choncho muziyesetsa kupereka ndemanga zachidule. Muziyesetsa kuti ndemanga yanu isapitirire masekondi 30. (Miy. 10:19; 15:23) Ngati mwakhala mukuyankha pamisonkhano kwa zaka zambiri, muyenera kupereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopereka ndemanga zachidule. Mukamapereka ndemanga zitalizitali komanso zovuta, anthu ena amaganiza kuti kuyankha kwabwino n’kumeneko ndipo iwo sangakwanitse. Chinanso n’chakuti mukamapereka ndemanga zachidule anthu ambiri amakhala ndi mpata woyankha pamisonkhano. Ngati ndinu woyamba kuyankha pa ndime, muzingopereka yankho lachindunji komanso losavuta. Musamafotokoze mfundo zonse zamundimeyo. Koma ngati munthu wina wayankha mfundo yaikulu mukhoza kufotokoza mfundo zina.​—Onani bokosi lakuti “Kodi ndinganene zinthu zotani poyankha?”

JUNE 12-18

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 32–33

“Muzilimbikitsa Abale ndi Alongo Anu Akakumana ndi Mavuto”

it-1 204 ¶5

Asuri

Senakeribu. Senakeribu, mwana wa Sarigoni Wachiwiri, anaukira ufumu wa Yuda m’chaka cha 14 cha ulamuliro wa Hezekiya (732 B.C.E.). (2Mf 18:13; Yes 36:1) Hezekiya anapandukira Asiriya amene ankawatumikira chifukwa cha zochita za bambo ake Ahazi. (2Mf 18:7) Senakeribu anabwezera mwa kukachita nkhondo ku Yuda ndipo analanda mizinda 46 (yerekezerani ndi Yes 36:1, 2), kenako ali pa msasa wake ku Lakisi, analamula Hezekiya kuti apereke matalente 30 a golide (c. $11,560,000) komanso matalente 300 a siliva (c. $1,982,000). (2Mf 18:14-16; 2Mb 32:1; yerekezerani ndi Yes 8:5-8) Ngakhale kuti ndalamazi zinaperekedwa, Senakeribu anatumiza atumiki ake kuti akawauze kuti agonje ndi kupereka mzinda wa Yerusalemu m’manja mwawo. (2Mf 18:17–19:34; 2Mb 32:2-20) Zimenezi zinachititsa kuti Yehova awononge asilikali ake 185,000 mu usiku umodzi, ndipo mfumu yodzikuza ya Asuriyo inachoka n’kubwerera kwawo ku Nineve. (2Mf 19:35, 36) Kumeneko inaphedwa ndi ana ake awiri ndipo mwana wake wina Esari-hadoni anakhala mfumu m’malo mwake. (2Mf 19:37; 2Mb 32:21, 22; Yes 37:36-38) Zochitika zimenezi, kupatulapo za kuwonongedwa kwa asilikali a Asuri, zinalembedwa mu zinthu zimene ofukula za m’mabwinja anapeza zokhudza Senakeribu ndi Esari-hadoni.

w13 11/15 19 ¶12

Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?

12 Yehova ndi wofunitsitsa kutithandiza kwambiri koma amayembekezera kuti nafenso tichite mbali yathu. Hezekiya “anagwirizana ndi akalonga ake ndi amuna ake amphamvu kuti atseke akasupe a madzi amene anali kunja kwa mzindawo . . . Kuwonjezera apo, [Hezekiya] analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka. Anamanga nsanja pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina . . . ndipo anapanga zida zambiri ndi zishango.” (2 Mbiri 32:3-5) Kuti ateteze ndiponso kutsogolera anthu ake, Yehova anagwiritsa ntchito amuna amphamvu ambiri monga Hezekiya, akalonga ake komanso aneneri okhulupirika.

w13 11/15 19 ¶13

Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?

13 Kenako Hezekiya anachita chinthu chofunika kwambiri kuposa kutseka akasupe a madzi kapena kumanga makoma onse a mpanda. Iye anali m’busa woganizira kwambiri anthu ake ndipo anawasonkhanitsa ndi kuwalimbikitsa ndi mawu akuti: “Musaope kapena kuchita mantha ndi mfumu ya Asuri . . . , chifukwa ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi mfumuyo. Iyo ikudalira mphamvu za anthu, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kuti atithandize ndi kutimenyera nkhondo zathu.” Mawuwa anali olimbikitsa kwambiri ndipo anakumbutsa anthuwo kuti Yehova adzawamenyera nkhondoyo. Ayuda atamva zimenezi “anayamba kulimba mtima chifukwa cha mawu a Hezekiya mfumu ya Yuda.” Onani kuti “mawu a Hezekiya” ndi amene anathandiza anthu kuti alimbe mtima. Mfumuyo, akalonga ake, amuna ake amphamvu ndiponso mneneri Mika ndi Yesaya analidi abusa abwino ngati amene Yehova analosera kudzera mwa mneneri wake.​—2 Mbiri 32:7, 8; werengani Mika 5:5, 6.

Mfundo Zothandiza

w21.10 4-5 ¶11-12

Kodi Kulapa Kwenikweni N’kutani?

11 Patapita nthawi Yehova anayankha mapemphero a Manase ndipo anaona kuti wasinthadi chifukwa cha zinthu zimene ankatchula m’mapemphero ake. Choncho anamukhululukira ndipo anamubwezeretsa pa ufumu wake. Manase anachita zonse zimene akanatha posonyeza kuti anali atalapadi kuchokera pansi pamtima. Anachita zosiyana ndi zimene Ahabu anachita moti anasintha khalidwe lake. Anayesetsa kutsutsa kulambira konyenga n’kulimbikitsa anthu kuti azilambira Yehova. (Werengani 2 Mbiri 33:15, 16.) Zimenezi zinkafunika kulimba mtima komanso chikhulupiriro chifukwa kwa zaka zambiri Manase anali chitsanzo choipa kwa anthu a m’banja lake, anthu a udindo mu ufumu wake komanso anthu omwe ankawalamulira. Koma chakumapeto kwa moyo wake, anayesetsa kukonza zina mwa zoipa zimene anachita. N’kutheka kuti iye ndi amene anapereka chitsanzo chabwino kwa Yosiya yemwe anadzakhala mfumu yabwino kwambiri.​—2 Maf. 22:1, 2.

12 Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Manase? Iye anadzichepetsa komanso anachita zina zambiri. Anapemphera kwa Mulungu kuti amuchitire chifundo ndipo anasintha khalidwe lake. Anakonza zimene analakwitsa ndipo anachita zonse zimene akanatha kuti azilambira Yehova komanso kuthandiza ena kuti azichita chimodzimodzi. Chitsanzo cha Manase chingathandizenso ngakhale anthu amene achita zoipa kwambiri. Pamenepa tikuona umboni wamphamvu wakuti Yehova ndi Mulungu wabwino ndipo ndi “wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5) Iye amakhululukira anthu amene alapadi kuchokera pansi pamtima.

JUNE 19-25

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 34–36

“Kodi Mawu a Mulungu Amakuthandizani Mokwanira?”

it-1 1157 ¶4

Hulida

Yosiya atamva kuwerengedwa kwa “buku la chilamulo” lomwe linapezedwa ndi Mkulu wa Ansembe Hilikiya panthawi imene ankakonzanso kachisi, anatumiza anthu kuti akafunsire kwa Yehova. Anapita kwa Hulida, amene anawafotokozera mawu a Yehova osonyeza kuti masoka onse opita kwa anthu osamvera omwe analembedwa ‘m’bukulo,’ adzagwera mtundu wosamverawo. Hulida anawonjezera kuti chifukwa choti Yosiya anadzichepetsa pamaso pa Yehova, sadzaona tsokalo koma adzaikidwa m’manda a makolo ake mu mtendere.​—2Mf 22:8-20; 2Mb 34:14-28.

w09 6/15 10 ¶20

Khalani Achangu pa Nyumba ya Yehova

20 Mfumu Yosiya anauza anthu kuti akonzenso kachisi. Pa ntchito imeneyi, Hilikiya yemwe anali Mkulu wa Ansembe, “anapeza buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.” Iye anapereka bukulo kwa Safani yemwe anali mlembi ndipo Safaniyo anamuwerengera Yosiya bukulo. (Werengani 2 Mbiri 34:14-18.) Ndiye kodi mfumu Yosiya anatani? Nthawi yomweyo iye anang’amba zovala zake chifukwa cha chisoni ndipo anauza anthu kuti apemphere kwa Yehova. Kudzera mwa mneneri wamkazi, dzina lake Hulida, Mulungu anapereka uthenga wodzudzula miyambo ya chipembedzo imene inkachitika mu Yuda. Ngakhale kuti Yehova analosera za tsoka limene mtundu wonsewo unadzakumana nalo, Iye anaona ndiponso anayamikira khama limene Yosiya anasonyeza pochotsa kulambira mafano. (2 Mbiri 34:19-28) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tiyenera kukhala ndi mtima umene Yosiya anali nawo. Tikamva malangizo a Yehova tiyenera kuwatsatira mwamsanga. Tiyeneranso kukumbukira zimene zingachitike ngati mwapang’onopang’ono tikuyamba kuchita za mpatuko kapena zosakhulupirika. Tikamatero sitikayika ngakhale pang’ono kuti Yehova akuona ndipo akuyamikira khama limene tikusonyeza pa kulambira koona, ngati mmene anachitira ndi Yosiya.

Mfundo Zothandiza

w17.03 27 ¶15-17

Kodi Mumatsatira ndi Mtima Wonse Zimene Zinalembedwa?

15 Pomaliza tiyeni tikambirane zimene tingaphunzire pa zimene zinachitikira Mfumu Yosiya. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti iye agonjetsedwe n’kufa? (Werengani 2 Mbiri 35:20-22.) Yosiya “anapita kukamenyana” ndi Mfumu Neko ya ku Iguputo ngakhale kuti mfumuyo inanena kuti sinabwere kudzamenyana ndi iyeyo. Baibulo limanena kuti mawu a Neko anali “ochokera pakamwa pa Mulungu.” Ndiye n’chifukwa chiyani Yosiya anapita kukamenyana ndi Neko? Baibulo silinena chifukwa chake.

16 Koma kodi Yosiya akanadziwa bwanji kuti mawu a Neko analidi ochokera kwa Yehova? Iye akanatha kufunsa Yeremiya, yemwe anali mneneri wokhulupirika. (2 Mbiri 35:23, 25) Koma palibe umboni woti anachita zimenezi. Chinanso chimene akanachiganizira ndi choti Neko ankapita ku Karikemisi kumenyana ndi “mtundu wina” osati Yerusalemu. Ndipotu nkhaniyi sinkakhudza dzina la Yehova chifukwa Neko sananyoze Yehova kapena anthu ake. Choncho Yosiya sanaganize bwino popita kukamenyana ndi Neko ndipo Yehova sanamuteteze. Ndiye kodi tingaphunzirepo chiyani? Tikakumana ndi vuto tizifufuza kaye maganizo a Yehova pa nkhaniyo.

17 Tikakumana ndi vuto tiyenera kufufuza mfundo zonse za m’Baibulo zimene zikukhudzana ndi vutolo n’kuona kuti tingazitsatire bwanji. Nthawi zina tingafunike kufunsa nzeru kwa akulu. N’zoona kuti ifeyo tingadziwe zinthu zina zokhudza nkhaniyo ndipo mwina tafufuza kale mfundo zina. Koma n’kutheka kuti pangakhale mfundo zinanso zimene akulu angatithandize kuti tiziganizire. Tiyerekeze kuti pali mlongo wina amene mwamuna wake si Mboni. Mlongoyu akudziwa kuti ayenera kumalalikira uthenga wabwino. (Mac. 4:20) Ndiyeno wakonza zoti tsiku lina adzalowe mu utumiki. Koma mwamuna wake akufuna kuti pa tsikulo adzapitire limodzi kwinakwake. Mwamunayo akuona kuti n’kale pamene anakhalapo ndi nthawi yochita zinthu limodzi. Mkaziyo angaganizire lamulo la Yesu loti tiziphunzitsa anthu komanso mfundo yakuti tiyenera kumvera Mulungu. (Mat. 28:19, 20; Mac. 5:29) Koma angachitenso bwino kuganizira mfundo yakuti akazi ayenera kugonjera amuna awo ndiponso azikhala ololera. (Aef. 5:22-24; Afil. 4:5) Kodi mwamuna wakeyo amamuletsa kupita kolalikira kapena akungofuna kuti pa tsikuli asachoke kuti achitire limodzi zinthu zina? Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti tiyenera kukhala osamala pochita zinthu kuti tizikhala ndi chikumbumtima chabwino potumikira Mulungu.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w17.09 25-26 ¶7-10

‘Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu’

7 Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu mu utumiki? Choyamba, tizikonda kuwawerenga tikamalalikira kapena kuphunzitsa anthu. Pa nkhani imeneyi, m’bale wina ananena kuti: “Tiyerekeze kuti inuyo mukulalikira kunyumba ndi nyumba limodzi ndi Yehova. Kodi mungamalankhule nokha kapena mungamupatse mpata kuti alankhulenso?” Apatu ankatanthauza kuti tikamawerenga Mawu a Mulungu mu utumiki timakhala ngati tikupatsa Yehova mpata woti alankhule ndi munthuyo. Lemba losankhidwa bwino likhoza kuthandiza kwambiri munthu kuposa mawu alionse amene ifeyo tingalankhule. (1 Ates. 2:13) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayesetsa kuwerengera Baibulo anthu amene ndimawalalikira?’

8 Komabe, kungowerengera munthu lemba si kokwanira. Tikutero chifukwa chakuti anthu ambiri salimvetsa bwino Baibulo. Vuto limeneli linalipo nthawi ya atumwi ndipo liliponso masiku ano. (Aroma 10:2) Choncho tisamaganize kuti tikangowerengera munthu lemba ndiye kuti adzamvetsa tanthauzo lake. Tiyenera kusankha mawu ofunika kwambiri palembalo, mwina n’kuwawerenganso kenako n’kufotokoza tanthauzo lake. Tikatero tidzathandiza kuti uthenga wa m’Baibulo ufike m’maganizo komanso mumtima mwa anthu amene tikukambirana nawo.​—Werengani Luka 24:32.

9 Tiyeneranso kutchula malemba m’njira yothandiza munthu kuti azilemekeza Baibulo. Mwachitsanzo tinganene kuti, “Tiyeni tione zimene Mlengi wathu akunena pa nkhaniyi.” Tikamakambirana ndi munthu yemwe si Mkhristu tinganene kuti, “Taonani zimene Malemba Oyera akunena pa nkhaniyi.” Ngati munthu amene tikukambirana nayeyo sakonda za Mawu a Mulungu tinganene kuti, “Kodi mwambi uwu munaumvapo?” Mwachidule tingati tiyenera kusintha ulaliki wathu kuti ugwirizane ndi munthu aliyense amene tikukambirana naye.​—1 Akor. 9:22, 23.

10 Akhristu ambiri amaona kuti kuwerenga Baibulo mu utumiki kumathandiza kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina amene anachita ulendo wobwereza kwa munthu wina wachikulire. Munthuyo anali atawerenga magazini athu kwa zaka zambiri. M’malo mongomupatsa Nsanja ya Olonda yatsopano, m’baleyo anaganiza zomuwerengera lemba limene linali m’magaziniyo. Anamuwerengera lemba la 2 Akorinto 1:3, 4 lomwe limanena kuti: “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.” Wachikulireyo analikonda kwambiri lembali moti anapempha m’baleyo kuti aliwerengenso. Kenako ananena kuti iye ndi mkazi wake ankafunitsitsa kutonthozedwa. Zimenezi zinachititsa kuti afune kuphunzira zambiri. Uwutu ndi umboni wakuti Mawu a Mulungu amakhala amphamvu tikamawagwiritsa ntchito mu utumiki.​—Mac. 19:20.

JUNE 26–JULY 2

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 1–3

“Muzilola Kuti Yehova Azikugwiritsani Ntchito”

w22.03 14 ¶1

Kodi Mukuona Zimene Zekariya Anaona?

AYUDA anasangalala kwambiri. Yehova “analimbikitsa mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya” kuti imasule Aisiraeli omwe anakhala zaka zambiri ku Babulo monga akapolo. Mfumuyo inalengeza kuti Ayuda angabwerere kwawo “n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (Ezara 1:1, 3) Zimenezitu zinali zosangalatsa kwambiri. Izi zinatanthauza kuti Ayuda akayambiranso kulambira Mulungu woona m’dziko limene iye anawapatsa.

w17.10 26 ¶2

Timatetezedwa ndi Magaleta Komanso Chisoti Chachifumu

2 Zekariya ankadziwa kuti Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu anali anthu okhulupirika. Paja anali anthu amene ‘Mulungu woona analimbikitsa mitima yawo’ kuti asiye nyumba zawo komanso mabizinezi awo. (Ezara 1:2, 3, 5) Ayudawo anachoka m’dziko limene analizolowera n’kusamukira kudziko lomwe ambiri mwa iwo anali asanalionepo. Ngati analolera kuyenda ulendo wovuta wa makilomita 1,600 wodutsa m’mapiri ndi m’zipululu, ndiye kuti ankaona kuti kumanganso kachisi wa Yehova ndi kofunika kwambiri.

Mfundo Zothandiza

w06 1/15 19 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara

1:3-6. Monga Aisrayeli ena amene anatsalira ku Babulo, pali a Mboni za Yehova ambiri amene sangathe kuchita utumiki wa nthawi zonse kapena kutumikira kumadera komwe kulibe olalikira okwanira. Komabe amachirikiza ndi kulimbikitsa anthu amene angathe kutero, ndipo mwakufuna kwawo, amapereka thandizo lopititsa patsogolo ntchito yolengeza Ufumu ndi kupanga ophunzira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena