Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JULY 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 4-6
“Musakalowerere Ntchito Yomanga”
Kodi Mukuona Zimene Zekariya Anaona?
13 Ntchito yomanganso kachisi inali italetsedwa. Komabe amuna amene ankatsogolera ntchitoyo, omwe ndi mkulu wa ansembe Yesuwa (Yoswa) ndi Bwanamkubwa Zerubabele, “ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu.” (Ezara 5:1, 2) Kwa Ayuda ena, zimenezi zikanaoneka zosamveka. Adani awo akanadziwa kuti iwo ayambiranso ntchito yomanga kachisi ndipo akanachita chilichonse kuti awalepheretse kugwira ntchitoyi. Amuna awiriwa, Yoswa ndi Zerubabele, ankafunika umboni wowatsimikizira kuti Yehova akuwathandiza. Iwo anapezadi umboni umenewu. Motani?
w86 2/1 29, bokosi ¶2-3
Maso a Yehova Anali pa Akulu
Ayuda omwe anatsalira ku Babulo atabwerera kwawo, anakhala zaka 16 asakugwira ntchito. Mneneri Hagai ndi Zekariya analimbikitsa Ayuda kuti asachite ulesi ndipo ntchito yomanganso kachisi wa Yehova inayambiranso. Komabe, posakhalitsa, akuluakulu aboma a Chiperisiya analetsa ntchitoyi. Otsutsawo anafunsa kuti: “Kodi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi?”—Ezara 5:1-3.
Yankho la funsoli linali lofunika kwambiri. Ngati akuluwo akanachita mantha, ntchito yomanganso kachisiyo ikanaima. Ngati akanatsutsana ndi akuluakulu abomawo, ntchitoyo ikanaletsedwa nthawi yomweyo. Choncho akuluwo (omwe ankatsogoleredwa ndi Bwanamkubwa Zerubabele komanso Mkulu wa Ansembe Yoswa) anayankha mwaluso komanso mogwira mtima. Iwo anakumbutsa akuluakuluwo za lamulo limene Koresi anakhazikitsa zaka zambiri m’mbuyo mwake, lomwe linapereka chilolezo kwa Ayuda kuti apitirize kugwira ntchitoyo. Podziwa kuti a Perisiya sasintha malamulo amene akhazikitsidwa, akuluakulu abomawo mwanzeru anasankha kusiya nkhaniyo posafuna kutsutsana ndi lamulo la mfumu ndipo ntchitoyo inapitirira. Kenako Mfumu Dariyo inapereka lamulo lake la boma lakuti ntchitoyo ipitirire.—Ezara 5:11-17; 6:6-12.
Kodi Mukuona Zimene Zekariya Anaona?
7 Kusintha kwina kunachititsa kuti mtima wa omanga kachisiwo ukhale m’malo. Kusintha kotani? Mu 520 B.C.E., Dariyo Woyamba, anayamba kulamulira ku Perisiya. M’chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, iye anazindikira kuti kuletsa ntchito yomanga kachisiyo kunali kosemphana ndi malamulo. Choncho Dariyo anapereka chilolezo kuti ntchitoyo imalizidwe. (Ezara 6:1-3) Nkhani imeneyi inadabwitsa aliyense. Komatu panalinso zina zomwe zinachitika. Mfumu inalamula kuti anthu ozungulira kumeneko asiye kusokoneza komanso azipereka ndalama ndi zinthu zina zofunika pa ntchitoyo. (Ezara 6:7-12) Zotsatira zake, mu 515 B.C.E., Ayuda anamaliza kumanga kachisiyo patangopita zaka 4 zokha.—Ezara 6:15.
Kodi Mukuona Zimene Zekariya Anaona?
16 Njira ina imene Yehova amatipatsira malangizo ndi kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Nthawi zina kapoloyu angatipatse malangizo omwe sitikuwamvetsa bwino. Mwachitsanzo, angatipatse malangizo enaake otikonzekeretsa kuti tidzapulumuke pa nthawi ya ngozi za m’chilengedwe zimene tikuona ngati sizingachitike m’dera lathu. Kapenanso tingaone ngati kapoloyu akukhwimitsa zinthu pa nthawi ya mliri winawake. Ndiye kodi tingatani ngati tikuona kuti malangizo amene tapatsidwa ndi osathandiza? Tiyenera kuganizira mmene Aisiraeli anapindulira chifukwa chotsatira malangizo amene anapatsidwa kudzera mwa Yoswa ndi Zerubabele. Tingaganizirenso nkhani zina za m’Baibulo zimene tinawerenga. Nthawi zina anthu a Mulungu ankapatsidwa malangizo ooneka ngati osathandiza koma akawatsatira ankapulumutsa moyo wawo.—Ower. 7:7; 8:10.
Mfundo Zothandiza
Kodi Mungakhulupirire Baibulo?
Ndalamayi inapangidwa ku Tariso, mzinda umene uli kum’mwera chakum’mawa kwa dziko limene panopa limadziwika kuti Turkey. Ndalama yachitsuloyi inapangidwa mu ulamuliro wa bwanamkubwa wa Perisiya dzina lake Mazaeus cha m’ma 300 B.C.E. Limamutchula kuti ndi bwanamkubwa wa “Kutsidya lina la Mtsinje,” kutanthauza mtsinje wa Firate.
Koma n’chifukwa chiyani mawuwa ali ochititsa chidwi? Chifukwa chakuti mawu ofanana ndi amenewa amapezekanso m’Baibulo. Lemba la Ezara 5:6–6:13, limafotokoza za Mfumu Dariyo ya Perisiya ndi bwanamkubwa wina dzina lake Tatenai kuti analemberana makalata. Nkhani yake inali yonena za ntchito yomanganso kachisi wa ku Yerusalemu imene Ayuda ankagwira. Ezara anali katswiri wodziwa kukopera Chilamulo cha Mulungu, ndipo mosakayikira, ankalemba zinthu mwachindunji komanso molondola. Pa lemba la Ezara 5:6 ndi 6:13, anatchula Tatenai kuti anali “bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje.”
Ezara analemba zimenezi cha m’ma 460 B.C.E., zaka 100 ndalamayo isanapangidwe. Komabe anthu ena angaganize kuti kutchulidwa munthu wakalekaleyu ndi nkhani yaing’ono. Koma ngati mungakhulupirire olemba Baibulo pankhani zazing’ono ngati zimenezi, kodi izi siziyenera kuwonjezera chikhulupiriro chanu mu zinthu zinanso zimene analemba?
JULY 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 7-8
“Zochita za Ezara Zinachititsa Kuti Dzina la Yehova Lilemekezedwe”
Kuphunzira—N’kothandiza ndi Kosangalatsa
8 Tiyenera kukonda Mawu a Yehova kuchokera mumtima. Tikawerenga mfundo inayake yatsopano, tikuyenera kumaiganizirabe kuti ikhazikike mumtima mwathu. Tiziganizira mozama mfundo za choonadi kuti tizidziwe bwino. Kuti zimenezi zitheke, timafunika kupemphera komanso kuchita zinthu modekha. Mofanana ndi Ezara, tifunika kukonzekeretsa mitima yathu kuti tiwerenge ndi kuphunzira Mawu a Mulungu. Baibulo limati: “Ezara anakonza mtima wake kuti aphunzire chilamulo cha Yehova ndi kuchichita ndiponso kuti aphunzitse mu Isiraeli malamulo ndi chilungamo.” (Eza 7:10) Onani zifukwa zitatu zomwe Ezara anakonzekeretsera mtima wake: kuphunzira, kuzigwiritsa ntchito payekha, ndi kuphunzitsa ena. Tiyenera kutsanzira chitsanzo chake.
si 75 ¶5
Buku la M’Baibulo la Nambala 13—1 Mbiri
5 Panalibe aliyense woyenerera amene akanalemba mbiri m’njira yotsatirika komanso yodalirika kuposa Ezara. “Ezara anakonza mtima wake kuti aphunzire chilamulo cha Yehova ndi kuchichita ndiponso kuti aphunzitse mu Isiraeli malamulo ndi chilungamo.” (Ezara 7:10) Yehova anamuthandiza ndi mzimu woyera. Wolamulira wa dziko lonse wa ku Perisiya anazindikira kuti Ezara anali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu ndipo anamupatsa udindo waukulu ku Yuda. (Ezara 7:12-26) Chifukwa choti Ezara anali ndi udindo wochokera kwa Mulungu komanso kwa mfumu, anali ndi mwayi wolemba mabuku m’njira yabwino kwambiri chifukwa ankagwiritsa ntchito zipangizo zabwino kwambiri zimene zinkapezeka pa nthawiyo.
it-1 1158 ¶4
Kudzichepetsa
Kumathandiza Munthu Kuti Alandire Malangizo Mosavuta. Munthu amene amadzichepetsa pamaso pa Mulungu, amatsogoleredwa ndi Mulunguyo. Ezara anali ndi udindo waukulu kwambiri wotsogolera amuna oposa 1,500 kuphatikizapo ansembe, Anetini komanso akazi ndi ana pamene ankachokera ku Babulo kupita ku Yerusalemu. Kuwonjezera pamenepo, ananyamula golide komanso siliva wambiri woti akagwiritse ntchito pokongoletsa kachisi ku Yerusalemu. Ankafunikira chitetezo pa ulendowu, koma Ezara sanafune kupempha kwa mfumu ya Perisiya asilikali oti awaperekeze, chifukwa akanachita zimenezi, akanasonyeza kuti akudalira mphamvu za anthu. Komanso anali atauza kale mfumu kuti: “Dzanja la Mulungu wathu lili ndi onse om’funafuna kuti awachitire zabwino.” Choncho iye anauza anthu onse kuti asale kudya ndi cholinga choti adzichepetse pamaso pa Yehova. Iwo anapempha Mulungu ndipo anawamvetsera mwa kuwateteza kwa adani awo komanso achifwamba a m’njira moti anayenda ulendo owopsawo bwinobwino. (Eza 8:1-14, 21-32) Mneneri Danieli, pamene anali ku ukapolo ku Babulo, ankakondedwa kwambiri ndi Mulungu mwakuti anamutumizira mngelo chifukwa anadzichepetsa pamaso pa Mulungu pamene ankafunafuna kuti amutsogolere komanso amuthandize kumvetsa zinthu.—Da 10:12.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara
7:28–8:20—N’chifukwa chiyani Ayuda ambiri ku Babulo sanafune kupita ku Yerusalemu ndi Ezara? Ngakhale kuti panali patadutsa zaka 60 gulu loyamba la Ayuda litabwerera kwawo, ku Yerusalemu kunali anthu ochepa chabe. Munthu wobwerera ku Yerusalemu anayenera kukayamba moyo watsopano wokhala ndi zovuta ndiponso zoopsa zosiyanasiyana. Panthawi imeneyo kwa Ayuda omwe zinthu zinali kuwayendera ku Babulo, ku Yerusalemu kunalibe moyo wapamwamba woti angaukhumbire. Komanso ulendo wake unali woopsa. Anthu obwerera ku Yerusalemuwo anayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Yehova, changu pa kulambira koona, ndiponso anayenera kulimba mtima kuti asamuke. Ngakhale Ezara mwiniwakeyo anadzilimbikitsa chifukwa dzanja la Yehova linali naye. Ezara analimbikitsa mabanja 1,500, omwe mwina anali anthu 6,000, motero nawonso anasamuka. Ezara anapitirizabe kulimbikitsa anthu ndipo Alevi 38 ndi Anetini 220 anasamukanso.
JULY 17-23
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 9-10
“Kusamvera Kumapweteketsa”
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara
9:1, 2—Kodi kukwatirana ndi anthu a mayikowa kunali koopsa motani? Mtundu wobwezeretsedwawu unayenera kukhala chimake cha olambira Yehova mpaka Mesiya atabwera. Kukwatirana ndi anthu a mitundu ina kukanasokoneza kulambira koona. Popeza kuti anthu ena anali atakwatirana ndi a mitundu yolambira mafano, mtundu wonsewo ukanatha kutengera zochita za anthu akunjawa. Motero, kulambira koona kukanatheratu padziko lonse. Choncho kodi Mesiya akanabwera ku mtundu uti? N’chifukwa chaketu Ezara anakhumudwa kwambiri ataona zimene zinali kuchitikazi.
Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?
Mulungu adzatidalitsa kwambiri ngati timamumvera mwakufuna kwathu. Mose analemba kuti: ‘Sungani malamulo amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni.’ (Vesi 13) Inde, chilichonse chimene Yehova amatiuza kuti tizichita chimakhala chotikomera kapena kuti chotithandiza. Choncho, sichingatilepheretse kusangalala. Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) N’chifukwa chake anatipatsa malamulo amene angatithandize kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. (Yesaya 48:17) Kuchita zonse zimene Yehova amafuna kuti tizichita kumatithandiza kupewa zokhumudwitsa zambiri panopa ndipo kudzatithandiza kuti mtsogolo muno, tidzapeze madalitso ambiri mu ulamuliro wa Ufumu wake.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara
10:3, 44—N’chifukwa chiyani ana anachotsedwa pamodzi ndi akazi? Anawo akanatsalira, akazi ochotsedwawo akanatha kudzabwereranso mosavuta pofuna anawo. Komanso, ana aang’ono nthawi zambiri amafuna chisamaliro cha mayi awo.
JULY 24-30
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 1-2
“Nthawi Yomweyo Ndinapemphera”
Ikani Yehova Patsogolo Panu Nthawi Zonse
5 Nthawi zina tingafunikire kupempha thandizo la Mulungu mwachidule. Tsiku lina, Mfumu Aritasasta ya Perisiya inaona kuti Nehemiya, yemwe anali woperekera chikho, anali wachisoni. Mfumuyo inafunsa kuti: ‘Ufunanji iwe? Pamenepo [Nehemiya] anapemphera kwa Mulungu wa Kumwamba.’ Apa n’zoonekeratu kuti sizikanatheka Nehemiya kupereka pemphero lalitali la mumtima. Koma Mulungu anayankhabe pemphero lake, chifukwa mfumuyo inathandiza Nehemiya kuti amange linga la Yerusalemu. (Werengani Nehemiya 2:1-8.) Zoonadi, Mulungu amayankha pemphero ngakhale litakhala lachidule ndi la mumtima.
Kulankhula Kuchokera mu Mtima
Ngati mwafunsidwa mosayembekezera kuti mupereke zifukwa pankhani yokhudza chikhulupiriro chanu, n’chiyani chingakuthandizeni kulankhula mawu ogwira mtima? Tengerani chitsanzo cha Nehemiya, amene anapemphera mu mtima asanayankhe funso lochokera kwa Mfumu Aritasasta. (Neh. 2:4) Mukatero, msangamsanga konzani autilaini ya m’maganizo. Mungatsatire masitepe ofunikira aŵa: (1) Sankhani mfundo imodzi kapena ziŵiri zimene mukufuna kufotokoza (mfundozo zingakhale zimene zimapezeka m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba) (2) Sankhani malemba amene mukufuna kugwiritsa ntchito ngati maziko a mfundo zanu. (3) Konzani mmene muyambire nkhani yanu mosamala kuti wofunsayo akhale ndi chidwi chomvetsera. Pamenepo yambani kulankhula.
Mfundo Zothandiza
w86 2/15 25
Kulambira Koona Kupeza Chipambano
Nehemiya anakhala akupemphera za mzinda wa Yerusalemu umene unali utawonongedwa “usana ndi usiku” kwa nthawi yaitali ndithu. (1:4, 6) Atapeza mwayi ouza Mfumu Aritasasita zimene ankafuna, zomwe ndi kumanganso makoma a Yerusalemu, Nehemiya anapempheranso, ndipo pamenepa, anachita zimene anali atachita kale. Yankho la Yehova linachititsa kuti pakhazikitsidwe lamulo lakuti makoma a mzindawo amangidwenso.
Tikuphunzirapo Chiyani?: Nehemiya anadalira Yehova kuti amutsogolere. Nafenso, tikamasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu, ‘tizilimbikira kupemphera’ ndipo tizichita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yehova.—Aroma 12:12.
JULY 31–AUGUST 6
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 3-4
“Kodi Mumagwira Ntchito Zonyozeka?”
Mfundo Zazikulu za M’buku la Nehemiya
3:5, 27. Tisamadzione ngati apamwamba kwambiri moti sitingathe kugwira ntchito zimene zimaoneka ngati zonyozeka zopititsa patsogolo kulambira koona, monga mmene anachitira Atekoa “omveka,” kapena kuti apamwamba. M’malo mwake, titsanzire Atekoa omwe sanali omveka aja amene anadzipereka mwa kufuna kwawo.
Kodi Yehova Adzakuthandizani Kuchita Chiyani?
11 Patapita zaka zambiri, ana aakazi a Salumu anathandiza nawo pa ntchito yokonza mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:20; 3:12) Ngakhale kuti bambo awo anali kalonga, iwo anadzipereka kugwira nawo ntchito yovuta komanso yoopsa imeneyi. (Neh. 4:15-18) Zimene anachitazi zinali zosiyana ndi zimene anthu otchuka pakati pa Atekowa anachita. Anthu otchukawo sanali odzichepetsa ndipo anakana kugwira nawo ntchitoyi. (Neh. 3:5) Ana aakazi a Salumu ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona kuti ntchitoyo yatha patangopita masiku 52 okha. (Neh. 6:15) Masiku anonso, alongo ena amadzipereka kuti atumikire Yehova pa ntchito zomangamanga kapena kukonza malo amene anaperekedwa kwa Yehova. Luso lawo, khama lawo komanso kukhulupirika kwawo zimathandiza kwambiri kuti ntchitozi ziziyenda bwino.
Khalani ndi Maganizo A Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu
16 Akristu onse, ana ndi akulu omwe, ayenera kuyesetsa kukhala ndi maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu. Mu mpingo mumakhala ntchito zosiyanasiyana. Tisamadane nazo tikapemphedwa kugwira ntchito zimene zingaoneke ngati ntchito wamba. (1 Samueli 25:41; 2 Mafumu 3:11) Makolo, kodi mumalimbikitsa ana anu, ang’onoang’ono ndiponso achinyamata, kuti azigwira mosangalala ntchito iliyonse yomwe apatsidwa, kaya ndi pa Nyumba ya Ufumu, pamalo a msonkhano wadera, kapena wachigawo? Kodi amakuonani inuyo mukugwira ntchito wamba? Mbale wina amene tsopano akutumikira pa likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova, amakumbukira bwino chitsanzo cha makolo ake. Iye anati: “Mmene ankagwirira ntchito yoyeretsa pa Nyumba ya Ufumu kapena pamalo a msonkhano zinandisonyeza kuti iwo ankaona ntchitoyo kuti ndi yofunika. Nthaŵi zambiri ankadzipereka kugwira ntchito zothandiza pampingo kapena zothandiza abale athu onse, mosaganizira kuti ntchitoyo ikuoneka yonyozeka motani. Mtima umenewu wandithandiza kulandira mosanyinyirika ntchito iliyonse yomwe ndapatsidwa pa Beteli pano.”
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Nehemiya
4:17, 18—Kodi munthu angagwire bwanji ntchito yomanga ndi dzanja limodzi? Zimenezi sizinali zovuta kwa anthu amene ananyamula katundu wolemera. Akanangoika katundu pamutu kapena paphewa, n’kumugwira ndi dzanja limodzi ndipo dzanja ‘linalo akananyamula mkondo.’ Omanga amene anafunikira kugwiritsa ntchito manja onse awiri, ‘anamangirira lupanga lawo m’chiuno pamene anali kumanga.’ Anali okonzeka kudziteteza ngati adani akanawaukira.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Sangalalani Chifukwa Choti Mwagwira Ntchito Mwakhama
1 Anthufe tinalengedwa m’njira yakuti ‘tikagwira ntchito mwakhama, tizisangalala.’ (Mlal. 2:24) Komabe tikaona kuti utumiki wathu ulibe zotsatira zabwino, tingayambe kugwa ulesi ndipo zimenezi zingapangitse kuti tikhale osasangalala komanso khama lathu lingachepe. Kodi tingatani kuti tizikhalabe osangalala ndi utumiki?
2 Musamayembekezere Zinthu Zoti Sizingachitike: Tiyenera kukumbukira kuti ngakhale kuti ndi anthu ochepa okha amene anakhala otsatira a Yesu, utumiki wake unali wopindulitsa. (Yoh. 17:4) M’fanizo lake lonena za wofesa mbewu, Yesu ananeneratu kuti anthu ambiri sadzalandira uthenga wa Ufumu womwe uli ngati mbewu. (Mat. 13:3-8, 18-22) Ngakhale zili choncho, khama lathu limathandiza anthu ambiri.
3 Mmene Timabalira Zipatso Zochuluka: Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena m’fanizo lija, anthu amene amalandira uthenga wabwino ‘amabala zipatso.’ (Mat. 13:23) Mmera wachimanga ukakula n’kukhwima, umabereka chimanga osati mmera wina wachimanga ayi. Izi zikutanthauza kuti zipatso zimene Akhristu amabala si anthu atsopano amene amalowa m’choonadi ayi, koma mbewu zambiri za Ufumu, kapena kuti kulalikira kwambiri za Ufumu. Zotsatira zake n’zakuti timakhala okhutira ngakhale anthu atapanda kuphunzira choonadi. Izi zili choncho chifukwa timakhalabe titathandizira kuyeretsa dzina la Yehova. (Yes. 43:10-12; Mat. 6:9) Timasangalalanso chifukwa chakuti ndife antchito anzake a Mulungu. (1 Akor. 3:9) Ndipotu “chipatso cha milomo” yathu chimenechi chimasangalatsa Yehova.—Aheb. 13:15, 16.
4 Kuwonjezera pamenepa, khama lathu pa ntchitoyi likhoza kukhala ndi zotsatira zimene sitingazione. N’kutheka kuti anthu ena amene anamva ulaliki wa Yesu anakhala otsatira ake pambuyo poti Yesuyo wamaliza utumiki wake wa padziko lapansi. Mofanana ndi zimenezi, mbewu za Ufumu zimene timafesa sizingamere komanso kukula mumtima mwa munthu nthawi yomweyo. Koma mwina m’tsogolo akhoza kudzayamba choonadi ifeyo osadziwa. Zimenezi zikusonyeza kuti utumiki wathu umakhala ndi zotsatira zabwino kwambiri. Chotero tiyeni ‘tipitirize kubala zipatso zambiri’ ndi kusonyeza kuti ndifedi ophunzira a Yesu.—Yoh. 15:8.
AUGUST 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 5-7
“Nehemiya Ankafuna Kutumikira, Osati Kutumikiridwa”
Anthu Othandiza Kulambira Koona Akale ndi Amasiku Ano
Nehemiya anathandizira m’zinthu zambiri kuwonjezera pa kugwiritsira ntchito nthaŵi yake ndi luso lake lolinganiza zinthu. Anagwiritsiranso ntchito chuma chake pothandizira kulambira koona. Anagwiritsira ntchito ndalama zake kugula abale ake achiyuda kuukapolo. Anakongoletsa ndalama zake popanda chiwongola dzanja. Iye ‘sanalemetsa’ Ayuda mwa kuwauza kuti azimulipira monga kazembe, zomwe anayenerera kuchita. M’malo mwake, iye kunyumba kwake ankalandira ndi kudyetsa “amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga.” Tsiku lililonse ankapereka “ng’ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi . . . [ndi] nkhuku” kwa alendo ake. Kuwonjezera pamenepo, kamodzi pa masiku khumi alionse, iye ankawapatsa “vinyo wambiri wamitundumitundu,” zonsezi ankatero pogwiritsira ntchito ndalama za m’thumba mwake.—Nehemiya 5:8, 10, 14-18.
Manja Anu ‘Asalefuke’
16 Yehova anathandiza Nehemiya ndi anzake kuti alimbitse manja awo n’kumaliza ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. Ntchitoyi inatha patangodutsa masiku 52 okha. (Neh. 2:18; 6:15, 16) Sikuti Nehemiya ankangoyang’anira ntchitoyi koma nayenso ankagwira nawo. (Neh. 5:16) Masiku anonso, akulu ambiri amatsanzira Nehemiya pogwira nawo ntchito zomanga kapena kuyeretsa Nyumba za Ufumu. Iwo amalimbitsanso manja a anthu ofooka poyenda nawo mu utumiki komanso kuchita maulendo aubusa.—Werengani Yesaya 35:3, 4.
Kodi Yehova Adzakukumbukirani Motani?
Baibulo limasonyeza kuti kwa Mulungu, “kukumbukira” kumatanthauza kuchitapo kanthu. Mwachitsanzo, pamene dziko lapansi linamira ndi madzi a chigumula kwa masiku 150, “Mulungu anakumbukira Nowa . . . Ndiyeno Mulungu anachititsa chimphepo kuwomba padziko lapansi, ndipo madzi anayamba kuchepa.” (Genesis 8:1) Patatha zaka zambiri pambuyo pake, Samsoni, atachititsidwa khungu komanso kumangidwa ndi Afilisti, anapemphera kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, chonde, ndikumbukireni ndi kundipatsa mphamvu kamodzi kokhaka.” Yehova anakumbukira Samisoni mwa kum’patsa mphamvu zambiri mwakuti anakwanitsa kubwezera yekha adani a Mulungu. (Oweruza 16:28-30) Ponena za Nehemiya, Yehova anadalitsa zomwe anachita, ndipo kulambira koona kunabwezeretsedwa mu Yerusalemu.
Mfundo Zothandiza
“Pitirizani Kugonjetsa Choipa mwa Kuchita Chabwino”
15 Chachitatu, adani a Nehemiya anagwiritsa ntchito Semaya, Mwisiraeli wopanduka, kuti achititse Nehemiya kuswa Malamulo a Mulungu. Semaya anauza Nehemiya kuti: “Tikumane ku nyumba ya Mulungu m’kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe.” Semaya anauza Nehemiya kuti moyo wake uli pangozi koma akhoza kupulumuka mwa kubisala m’kachisi. Koma popeza Nehemiya sanali wansembe, akanachimwa ngati akanabisala m’nyumba ya Mulungu. Kodi Nehemiya anaswa Malamulo a Mulungu chifukwa chofuna kupulumutsa moyo wake? Nehemiya anayankha kuti: “Ndani wonga ine adzalowa m’Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo.” N’chifukwa chiyani Nehemiya sanagwere m’msampha umene anam’tchera? Chifukwa anazindikira kuti ngakhale Semaya anali Mwisiraeli mnzake, ‘sanatumidwe ndi Mulungu.’ Ndipotu, mneneri woona sangamuuze kuti aswe Malamulo a Mulungu. Nehemiya sanalolenso kuti agonjetsedwe ndi anthu oipa amene ankam’tsutsa. Patapita nthawi yochepa anatha kunena kuti: “Linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli.”—Nehemiya 6:10-15; Numeri 1:51; 18:7.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Muzigwira Bwino Ntchito Yanu Yolalikira
17 Yesu ankatumiza anthu awiriawiri kukalalikira. (Maliko 6:7; Luka 10:1) Nayenso Paulo anatchula ‘antchito anzake’ amene ‘anayesetsa limodzi naye pa ntchito ya uthenga wabwino.’ (Afil. 4:3) Potsatira nkhani za m’Malemba zimenezi, mu 1953, gulu linakonza pulogalamu yoti ena aziphunzitsa anzawo mu utumiki.
18 Kodi inuyo mungatani kuti muzithandizana ndi munthu amene mukulalikira naye. (Werengani 1 Akorinto 3:6-9.) Mnzanu akamawerenga Baibulo, inunso muzitsegula lanu. Muziyang’ana ndiponso kumvetsera pamene mnzanuyo kapena munthu winayo akulankhula. Muzitsatira bwino nkhani imene akukambirana kuti ngati munthuyo akutsutsa, muthe kuthandiza mnzanuyo. (Mlal. 4:12) Koma muyenera kusamala kuti musamam’dule pakamwa mnzanuyo akamafotokoza bwinobwino mfundo inayake. Mwina mungachite izi pofuna kuthandiza koma vuto ndi lakuti mukhoza kukhumudwitsa mnzanuyo komanso kusokoneza munthu winayo. Komabe nthawi zina mukhoza kulankhulapo. Koma polankhula, ndi bwino kungotchula mwachidule mfundo imodzi kapena ziwiri basi. Kenako perekani mpata kuti mnzanuyo apitirize.
19 Kodi mungatani kuti muzithandizana pochoka panyumba ina kupita ina? Mukhoza kukambirana zimene mungafunike kusintha kuti muphunzitse bwino panyumba yotsatira. Koma muyenera kupewa kulankhula zinthu zokhumudwitsa zokhudza anthu a m’dera lanu. Muzipewanso kulankhula zimene Akhristu anzanu amalakwitsa. (Miy. 18:24) Tingachite bwino kukumbukira kuti tili ngati zonyamulira zoumbidwa ndi dothi. Koma Yehova watikomera mtima kwambiri potipatsa mwayi wolalikira uthenga wabwino. (Werengani 2 Akorinto 4:1, 7.) Choncho tiyeni tonse tiziyamikira mwayi umenewu n’kumayesetsa kugwira bwino ntchito yathu yolalikira.
AUGUST 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 8-9
“Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka Ndicho Malo Anu Achitetezo”
Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Pemphero Limene Linakonzedwa Bwino?
2 Ayuda anachita msonkhanowu patadutsa mwezi umodzi kuchokera pamene anamaliza kumanga mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 6:15) Anthu a Mulungu anamaliza ntchitoyi pa masiku 52 okha ndipo kenako ankafuna kusonkhana kuti aphunzire za Mulungu. Choncho pa tsiku loyamba la mwezi watsopano wa Tishiri anasonkhana m’bwalo lalikulu kuti amvetsere Ezara ndiponso Alevi ena akuwerenga komanso kufotokoza Chilamulo cha Mulungu. (Mbali “1” ya chithunzi patsamba 22) Anthu onse m’banja omwe “akanatha kumvetsera ndi kuzindikira zimene zinali kunenedwa” anaimirira n’kumvetsera “kuyambira m’mawa mpaka masana.” Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife masiku ano amene timasonkhana m’Nyumba za Ufumu zabwino. Kodi nthawi zina muli pa misonkhano mumayamba kuganizira zinthu zina zosafunika kwenikweni? Ngati zili choncho, mungachite bwino kuganiziranso chitsanzo cha Aisiraeliwa. Iwo anamvetsera mwatcheru ndipo zimene anamvazo zinawafika pamtima moti anayamba kulira chifukwa choona kuti alephera kutsatira Chilamulo cha Mulungu.—Neh. 8:1-9.
Kodi ‘Mupitiriza Kuyenda mwa Mzimu’?
9 Mawu akuti chimwemwe amatanthauza chisangalalo chachikulu. Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo.” (1 Timoteyo 1:11; Salmo 104:31) Mwana wake amakondwera kuchita chifuniro cha Atate wake. (Salmo 40:8; Aheberi 10:7-9) Ndipo “chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu” yathu.—Nehemiya 8:10.
10 Tikamachita chifuniro cha Mulungu, ngakhale m’nthawi ya mavuto, chisoni, kapena chizunzo, timakhala osangalala chifukwa cha chimwemwe chimene Mulungu amatipatsa. Timasangalala ‘tikamudziwadi Mulungu.’ (Miyambo 2:1-5) Timakhala pa ubale wosangalatsa ndi Mulungu ngati timamudziwa bwino ndiponso ngati timamukhulupirira ndi kukhulupiriranso nsembe ya dipo ya Yesu. (1 Yohane 2:1, 2) Ndifenso achimwemwe chifukwa chakuti tili ndi ubale weniweni padziko lonse. (Zefaniya 3:9; Hagai 2:7) Chiyembekezo chathu cha Ufumu ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino zimatipatsanso chimwemwe. (Mateyo 6:9, 10; 24:14) Chiyembekezo chathu cha moyo wosatha chimatipatsanso chimwemwe. (Yohane 17:3) Popeza tili ndi chiyembekezo chodabwitsa chimenechi, tiyenera ‘kukondwera monsemo.’—Deuteronomo 16:15.
Mfundo Zothandiza
it-1 145 ¶2
Chiaramu
Patapita zaka zingapo kuchokera pamene Ayuda anabwerera kuchokera ku ukapolo ku Babulo, Ezara yemwe anali wansembe anawerenga buku la chilamulo kwa Ayuda omwe anasonkhana ku Yerusalemu ndipo Alevi osiyanasiyana ankachifotokozera kwa anthu. Lemba la Nehemiya 8:8 limati: “Iwo anapitiriza kuwerenga bukulo mokweza. Anapitiriza kuwerenga chilamulo cha Mulungu woona, kuchifotokozera ndi kumveketsa tanthauzo lake. Iwo anapitiriza kuthandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuwerenga.” Kufotokozera komwe ankachita kunkaphatikizapo kumasulira mawu a Chiheberi kupita m’chilankhulo cha Chiaramu, chomwe n’kutheka anachiphunzira pamene anali ku Babulo. Mosakayikira, kunkaphatikazanso kufotokozera tanthauzo lenileni n’cholinga choti Ayuda, ngakhale kuti ankadziwa bwino Chiheberi, amvetse bwino mfundo yeniyeni ya zimene zinkawerengedwa.
AUGUST 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 10-11
“Anasiya Zinthu Zina Chifukwa cha Yehova”
Yerusalemu Woyenereradi Dzina Lake
13 “Pangano lodalirika” lomwe linakhazikitsidwa m’nthawi ya Nehemiya linachititsa kuti anthu a Mulungu akonzekere za tsiku lotsegulira mpanda wa Yerusalemu. Koma panali nkhani inanso imene inkafunika kuti isamaliridwe mwamsanga. Ku Yerusalemu kunkafunika anthu ambiri chifukwa mzindawu unali ndi mpanda waukulu wokhala ndi mageti 12. Ngakhale kuti Aisiraeli ena ankakhala kumeneko, “mzindawo unali wotakasuka ndi waukulu. Mkati mwake munali anthu ochepa.” (Nehemiya 7:4) Pofuna kuthana ndi vutoli, anthu “anachita maere kuti apeze munthu mmodzi mwa anthu 10 alionse woti akakhale m’Yerusalemu, mzinda woyera.” Chifukwa choti anthu anachita zimenezi mofunitsitsa, “anthu anadalitsa amuna onse amene anadzipereka kukakhala m’Yerusalemu.” (Nehemiya 11:1, 2) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa Akhristu oona masiku ano, amene ngati zinthu pa moyo wawo zili bwino, amadzipereka kupita kukatumikira kudera limene kukufunika Akhristu ambiri olimba mwauzimu.
w86 2/15 31
Kulambira Koona Kupeza Chipambano
Kusiya cholowa chawo komanso kusamukira ku Yerusalemu kukanachititsa kuti awononge zinthu zina komanso akanakumana ndi mavuto ena. Kukhala mumzinda umenewu kukanawachititsanso kuti azikumana ndi zinthu zoopsa. Chifukwa cha zimenezi, ena anaona kuti anthu omwe anadziperekawo ankafunikira kuyamikiridwa, ndipo mosakayikira, anapemphera kwa Yehova kuti awadalitse.
Yehova Amadalitsa Anthu Okhulupirika
15 Pamene tinkadzipereka kwa Yehova tinamulonjeza kuti tizichita zonse zimene akufuna. Tinkadziwa kuti tiyenera kudzimana zinthu zina kuti tikwanitse kuchita zimenezi. Ngakhale zili choncho, nthawi zina zimakhala zovuta ngati tapemphedwa kuchita zinthu zimene sitinkaganiza kuti tingachite. Komabe tikamalolera timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova. Ndipotu zotsatira zake zimakhala zabwino chifukwa Yehova amatidalitsa kwambiri. (Mal. 3:10) Tsopano tiyeni tikambirane chitsanzo cha mwana wa Yefita.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Nehemiya
10:34—N’chifukwa chiyani anthu ankafunika kupereka nkhuni? M’Chilamulo cha Mose munalibe lamulo la chopereka cha nkhuni. Koma panthawiyi anayenera kutero. Chifukwa chake n’chakuti panafunika nkhuni zambiri zowotchera nsembe pa guwa. Zikuoneka ngati panalibe Anetini okwanira, akapolo a pakachisi omwe sanali Aisrayeli. Choncho, anachita maere otsimikiza kuti nkhuni zizipezeka nthawi zonse.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Anthu Ovomerezeka ndi Mulungu Adzapeza Moyo Wosatha
12 M’kalata imene mtumwi Paulo analembera Aroma anati: “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1) Kuti munthu ayanjidwe ndi Mulungu, nthawi zonse thupi lake liyenera kukhala lovomerezeka. Ngati munthu angadzidetse ndi fodya, chamba, mankhwala osokoneza bongo kapena kuledzera, nsembe yake ingakhale yopanda phindu. (2 Akor. 7:1) Komanso popeza munthu amene “amachita dama amachimwira thupi lake,” ndiye kuti khalidwe loipa la mtundu uliwonse limachititsa kuti nsembe yake ikhale yonyansa kwa Yehova. (1 Akor. 6:18) Kuti munthu akondweretse Mulungu ayenera ‘kukhala woyera m’makhalidwe ake onse.’—1 Pet. 1:14-16.
13 Nsembe ina imene Yehova amasangalala nayo ndi yokhudza zolankhula zathu. Nthawi zonse anthu amene amakonda Yehova amalankhula zinthu zabwino za iye akakhala pa gulu kapena pamene ali paokha kunyumba kwawo. (Werengani Salimo 34:1-3.) Werengani Masalimo 148 mpaka 150 kuti muone mmene masalimo atatu amenewa akutilimbikitsira mobwerezabwereza kutamanda Yehova. Ndithudi, “m’poyenera kuti owongoka mtima atamande Mulungu.” (Sal. 33:1) Ndipotu Yesu Khristu, amene ndi chitsanzo chathu, anagogomezera kufunika kotamanda Mulungu mwa kulalikira uthenga wabwino.—Luka 4:18, 43, 44.
14 Tikamalalikira mwakhama timasonyeza kuti timakonda Yehova ndiponso timafuna kukhala ovomerezeka ndi iye. Mwachitsanzo, taganizirani mmene mneneri Hoseya analimbikitsira Aisiraeli atayamba kulambira konyenga n’kusiya kukhala ovomerezeka ndi Mulungu. (Hos. 13:1-3) Hoseya anawalimbikitsa kuchonderera Yehova kuti: “Tikhululukireni zolakwa zathu. Landirani zinthu zabwino zochokera kwa ife, ndipo mawu apakamwa pathu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe kwa inu.”—Hos. 14:1, 2.
15 Mwana wamphongo wa ng’ombe anali nsembe ya mtengo wapatali kwambiri imene Mwisiraeli akanapereka kwa Yehova. Choncho mawu ochokera pansi pa mtima amene munthu analankhula atawaganizira bwino potamanda Mulungu woona, ankaimira “ana amphongo a ng’ombe.” Kodi Yehova ankawachitira chiyani anthu amene ankapereka nsembe zoterozo? Iye anati: “Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga.” (Hos. 14:4) Yehova ankakhululukira, kuyanja ndiponso kukhala pa ubwenzi ndi anthu amene anapereka nsembe zotamandazi.
AUGUST 28–SEPTEMBER 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 12-13
“Muzikhala Okhulupirika kwa Yehova Mukamasankha Anthu Ocheza Nawo”
it-1 95 ¶5
Aamoni
Tobiya atachotsedwa pa kachisi, chilamulo cha Mulungu chopezeka pa Deuteronomo 23:3-6 choletsa Aamoni ndi Amowabu kuti asalowe mumpingo wa Aisiraeli chinawerengedwa komanso chinatsatiridwa. (Ne 13:1-3) Chiletsochi, chomwe chinakhazikitsidwa zaka pafupifupi 1,000 m’mbuyo mwake, pa nthawi imene Aamoni ndi Amowabu anakana kuthandiza Aisiraeli pamene anatsala pang’ono kufika m’Dziko Lolonjezedwa, chinkatanthauza kuti anthuwo sakanagwirizana ndi mtundu wa Isiraeli mwalamulo n’kukhala ndi ufulu wochita nawo zinthu zonse. Zimenezi sizikutanthauza kuti Muamoni kapena Mmowabu sakanachita zinthu ndi Aisiraeli kapena kukhala nawo limodzi n’kumalandira madalitso ochokera kwa Mulungu, ndipo izi zikuonekera bwino pa kutchulidwa kwa Zeleki, kuti anali mmodzi wa asilikali a Davide komanso nkhani ya Rute yemwe anali Mmowabu.—Ru 1:4, 16-18.
Mwapatulidwa
5 Werengani Nehemiya 13:4-9. M’dzikoli muli zinthu zoipa zambirimbiri, choncho kukhalabe oyera si kophweka. Taganizirani za Eliyasibu ndi Tobia. Eliyasibu anali mkulu wa ansembe pomwe Tobia, yemwe anali wachiamoni, ayenera kuti anali ndi udindo winawake mu ulamuliro wa Perisiya ku Yudeya. Pa nthawi ina m’mbuyomo, Tobia ndi anzake anatsutsa Nehemiya pa ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:10) Komanso Aamoni sankaloledwa kupita kukachisi. (Deut. 23:3) Choncho funso n’kumati, N’chifukwa chiyani mkulu wa ansembe analola kuti Tobia akhale m’chipinda chodyera pakachisi?
6 Tobia ankagwirizana kwambiri ndi Eliyasibu. Tobia ndiponso mwana wake Yehohanani anakwatira akazi achiyuda. Ndipo Ayuda ambiri ankalemekeza Tobia. (Neh. 6:17-19) Mdzukulu wina wa Eliyasibu anakwatira mwana wa Sanibalati, yemwe anali bwanamkubwa wa Samariya komanso mnzake wapamtima kwambiri wa Tobia. (Neh. 13:28) Mwina izi n’zimene zinachititsa kuti Eliyasibu achite zimene Tobia ankafuna ngakhale kuti anali munthu wosakhulupirira ndiponso wotsutsa Yehova. Koma Nehemiya anasonyeza kuti anali wokhulupirika kwa Yehova potulutsa katundu wa Tobia m’chipinda chodyera chija.
Kupambana Chiyeso cha Kukhulupirika
6 Ngati tili okhulupirika kwa Yehova Mulungu, tidzapewa kukhala pa ubwenzi ndi adani ake. N’chifukwa chake Yakobo analemba kuti: “Achigololo inu, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu? Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Tiyenera kukhala okhulupirika ngati Mfumu Davide pamene inanena kuti: “Inu Yehova, pajatu ine ndimadana ndi anthu amene amadana nanu kwambiri, ndipo anthu okupandukirani ndimanyansidwa nawo. Ndimadana nawo kwambiri. Kwa ine akhala adani enieni.” (Salimo 139:21, 22) Sitifuna kumacheza ndi anthu amene amachita machimo mwadala chifukwa ndife osiyana nawo. Tikakhala okhulupirika kwa Mulungu sitidzalola kukhala pa ubwenzi ndi aliyense amene ndi mdani wa Yehova, kaya pamasom’pamaso kapena pa TV.
Mfundo Zothandiza
it-2 452 ¶9
Nyimbo
Nyimbo zinalinso zofunika kwambiri pakachisi. Umboni wa zimenezi umapezeka m’Malemba onena za oimba komanso pa mfundo yakuti iwo “sanali kupatsidwa ntchito zina,” mofanana ndi mmene zinalilinso ndi Alevi ena onse, n’cholinga choti azichita utumiki wawo ndi mtima wonse. (1Mb 9:33) Pamene Ayuda ankabwerera kwawo kuchokera Babulo, oimbawa anatchulidwa mwapadera pa gulu la Alevi, zomwe zinangotsimikizira kuti anapitirizabe kukhala anthu ofunika kwambiri. (Eza 2:40, 41) Ngakhale ulamuliro wa Mfumu Aritasasita (Longimenasi) wa ku Perisiya unkachitira zinthu zina oimba, ndipo limodzi ndi anthu ena omwe anali apadera, anauzidwa kuti asamakhome “msonkho umene munthu aliyense amakhoma, msonkho wakatundu, kapena msonkho wapanjira.” (Eza 7:24) Kenako, mfumu inalamula kuti pakhale “dongosolo loti aziwapatsa thandizo tsiku lililonse malinga ndi zofunikira za tsikulo.” Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti Aritasasita ndi amene anapereka lamuloli, zimaoneka kuti Ezara ndi amene analikhazikitsa pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Aritasasitayo anamupatsa. (Ne 11:23; Eza 7:18-26) Choncho ndi zomveka kuti, ngakhale kuti oimba onse anali Alevi, Baibulo limasonyeza kuti anali anthu apadera, ndipo limatchula za “oimba ndi Alevi.”—Ne 7:1; 13:10.