Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr24 March tsamba 1-16
  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2024
  • Timitu
  • MARCH 4-10
  • MARCH 11-17
  • MARCH 18-24
  • MARCH 25-31
  • APRIL 1-7
  • APRIL 8-14
  • APRIL 15-21
  • APRIL 22-28
  • APRIL 29–MAY 5
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2024
mwbr24 March tsamba 1-16

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu

© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

MARCH 4-10

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 16-17

“Zinthu Zonse Zabwino Zimachokera kwa Yehova”

w18.12 26 ¶11

Achinyamata, Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wosangalala

MUZIPEZA ANZANU ABWINO

11 Werengani Salimo 16:3. Davide ankadziwa zimene zingathandize munthu kupeza anzake abwino. Iye ankasangalala kwambiri kukhala limodzi ndi anthu okonda Yehova. Iye anati anzakewo anali “oyera” kutanthauza kuti anali amakhalidwe abwino. Munthu winanso wolemba masalimo ankasankha bwino anthu ocheza nawo. Iye analemba kuti: “Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani, ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.” (Sal. 119:63) Nkhani yapita ija inasonyeza kuti m’gulu la Yehova tikhoza kupezamo anzathu abwino. Anzathuwo akhoza kukhala anthu amisinkhu yosiyanasiyana.

w14 2/15 29 ¶4

‘Tiziona Ubwino wa Yehova’

Davide anaimba kuti: “Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa, komanso chikho changa. Inu mukundisungira bwino kwambiri cholowa changa. Zingwe zoyezera zandigwera m’malo abwino.” (Sal. 16:5, 6) Davide ankayamikira kwambiri “gawo” lake, kapena kuti mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso womutumikira. Mofanana ndi Davide, ife timakumana ndi mavuto ambiri koma tadalitsidwanso m’njira zambiri. Choncho tiyeni tipitirize kusangalala potumikira Mulungu woona komanso ‘kuyang’ana moyamikira’ kachisi wauzimu wa Yehova.

w08 2/15 3 ¶2-3

Ikani Yehova Patsogolo Panu Nthawi Zonse

2 Tonsefe timaphunzira zambiri pankhani za anthu odziwika bwino a m’Baibulo monga Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Davide, Estere, mtumwi Paulo ndi ena. Komanso tingapindule ndi nkhani za anthu omwe si odziwika kwambiri. Kusinkhasinkha nkhani za m’Babulo kungatithandize kuchita zimene wamasalmo anachita. Iye anati: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse: Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Sal. 16:8) Kodi mawuwa akutanthauza chiyani?

3 Kale msilikali anali kugwirira lupanga kudzanja lake lamanja. Chifukwa cha zimenezi, mbali ya kumanjayo inali yosatetezeka ndi chishango chomwe anali kunyamula ku dzanja lamanzere. Komabe, iye anali kukhala wotetezeka ngati msilikali mnzake akumenya nkhondo ataima chapafupi kudzanja lake lamanja. Ifenso tikamakumbukira Yehova ndi kuchita chifuniro chake nthawi zonse, adzatiteteza. Choncho tiyeni tione mmene nkhani za m’Baibulo zingalimbitsire chikhulupiriro chathu kuti ‘tiike Yehova patsogolo pathu nthawi zonse.’

Mfundo Zothandiza

it-2 714

Mwana wa Diso

Mawu a Chiheberi akuti ʼi·shohnʹ (De 32:10; Miy 7:2), akagwiritsidwa ntchito pamodzi ndi mawu akuti ʽaʹyin (diso), amatanthauza kuti “kamunthu kakamuna ka m’diso”; mofananamo mawu akuti bath (mwana wamkazi) anawagwiritsa ntchito pa lemba la Maliro 2:18 potanthauza “mwana wamkazi wa m’diso,” ndipo mawu onsewa amanena za mwana wa diso. Pofuna kutsindika ganizo lake, mawu awiriwa anawagwiritsa ntchito pa lemba la Salimo 17:8 (ʼi·shohnʹ bath-ʽaʹyin), lomwe pa Chiheberi limati, “kamunthu kakamuna, mwana wamkazi wa m’diso” (“mwana wa diso,” NW). Zikuoneka kuti amanena zimenezi potengera kachithunzi ka munthu kamene kamaoneka munthu akamayang’ana m’diso la mnzake.

Diso ndi lamantha kwambiri; silichedwa kuphethira ngakhale litangokhudzidwa ndi kanthu kakang’ono ngati tsitsi kapena fumbi. Mbali yakunja ya diso imene imateteza mwana wa diso, imafunika kuisamala bwino komanso kuiteteza, chifukwa ngati mbali imeneyi itakalika kapena kuchita khungu, munthu akhoza kumavutika kuona kapena kusiyiratu kuona. Ndi mawu amphamvu komanso osonyeza kufunika kosamala, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “mwana wa diso” ponena za chinthu chimene chifunika kuchiteteza mosamala kwambiri. Malamulo a Mulungu amafunika kutetezedwa moteremu. (Miy 7:2) Ponena za mmene Mulungu ankasamalira Aisiraeli monga bambo, lemba la Deuteronomo 32:10 limati iye ankateteza mtunduwo ngati “mwana wa diso lake.” Davide anapemphera kwa Mulungu kuti amuteteze ndi kumusamalira ngati “mwana wa diso.” (Sl 17:8) Iye ankafuna kuti Yehova amuthandize mwamsanga adani akamuukira. (Yerekezerani ndi Zek 2:8; pamene mawu a Chiheberi akuti ba·vathʹ ʽaʹyin, “mwana wa diso,” anagwiritsidwa ntchito.)

MARCH 11-17

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 18

“Yehova Ndi . . . Amene Amandipulumutsa”

w09 5/1 14 ¶4-5

Kodi Mafanizo a M’Baibulo Mumawamvetsa Bwino?

Baibulo limayerekezeranso Yehova ndi zinthu zina zopanda moyo. Mwachitsanzo, limati iye ndi “Thanthwe la Isiraeli,” “thanthwe,” ndiponso “linga.” (2 Samueli 23:3; Salmo 18:2; Deuteronomo 32:4) Kodi zinthu zimenezi zikufanana bwanji ndi Yehova? Monga mmene thanthwe lilili lolimba ndiponso losasunthika, Yehova Mulungu ndiye chitetezo chathu cholimba ndiponso chosasunthika.

5 M’buku la Masalmo muli mafanizo ambiri amene amalongosola makhalidwe osiyanasiyana a Yehova. Mwachitsanzo, Salmo 84:11 limanena kuti Yehova ali ngati “dzuwa ndi chikopa,” chifukwa chakuti iye amatipatsa kuunika, moyo, mphamvu ndiponso amatiteteza. Komanso, Salmo 121:5 limati “Yehova ndiye mthunzi wako wa ku dzanja lako lamanja.” Anthu amene amam’tumikira, Yehova amawateteza ku mavuto otentha kwambiri ngati dzuwa, mofanana ndi mmene mthunzi umatetezera munthu kuti asapse ndi dzuwa. Amachita zimenezi powaphimba ndi mthunzi wa “dzanja” lake kapena wa “mapiko” ake.​—Yesaya 51:16; Salmo 17:8; 36:7.

it-2 1161 ¶7

Mawu

Mulungu amamva mawu a atumiki ake. Anthu amene amatumikira Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, amakhala otsimikiza kuti Mulungu amva mawu awo akamapemphera, kaya agwiritse ntchito chilankhulo chiti. Kuwonjezera pamenepo, ngakhale munthu azipemphera chamumtima osatulutsa mawu, Mulungu amene amadziwa mitima ya anthu, “amamva” kapena amatchera khutu. (Sl 66:19; 86:6; 116:1; 1Sa 1:13; Ne 2:4) Anthu amene akuvutika akamapemphera, Mulungu amamvetsera kuti awathandize komanso amamva ndi kudziwa maganizo a anthu otsutsa amene amakonzekera chiwembu atumiki ake.​—Ge 21:17; Sl 55:18, 19; 69:33; 94:9-11; Yer 23:25.

w22.04 3 ¶1

Zimene Zingatithandize Tikakhala ndi Nkhawa

2. Muziganizira mmene Yehova anakuthandizirani m’mbuyomo. Mukaganizira mmene zinthu zakhala zikuyendera pa moyo wanu, kodi pali mayesero amene munakwanitsa kuwapirira chifukwa chakuti Yehova anakuthandizani? Tikamaganizira mmene Yehova watithandizirapo komanso mmene anathandizira atumiki ake m’mbuyomo, timapeza mphamvu ndipo timayamba kumudalira kwambiri. (Sal. 18:17-19) Joshua yemwe ndi mkulu ananena kuti, “Sindimaiwala mapemphero anga amene anayankhidwa. Zimenezi zimandithandiza kukumbukira nthawi zimene ndakhala ndikupempha Yehova zinazake ndipo iye anandipatsa zimene ndinkafunikira.” Tikamaganizira mmene Yehova wakhala akutithandizira, timapeza mphamvu zotithandiza kulimbana ndi nkhawa.

Mfundo Zothandiza

it-1 432 ¶2

Kerubi

Zizindikiro za akerubi zimenezi sikuti zinali zithunzi zosaoneka bwino za zinthu zoopsa zokhala ndi mapiko zimene mitundu ina ya chikunja inkalambira, ngati mmene anthu ena amanenera. Miyambo yosiyanasiyana yakale ya Chiyuda imagwirizana pa mfundo imodzi (Baibulo silinena chilichonse pa nkhani imeneyi) yakuti akerubi amenewa ankaoneka ngati anthu. Zinali zithunzi zojambulidwa mwaluso kwambiri, zomwe zinkaimira angelo aulemerero waukulu ndipo anazipanga “mogwirizana ndendende” ndi zimene Yehova mwiniwakeyo anasonyeza Mose. (Eks 25:9) Mtumwi Paulo anawafotokoza kuti “akerubi aulemerero amene zithunzithunzi zawo zinkafika pachivundikiro.” (Ahe 9:5) Akerubi ankakonda kutchulidwa pamene pali Yehova: “Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo nʼkulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikirocho. . . . Kuchokera pakati pa akerubi awiriwo, amene ali pamwamba pa likasa la Umboni.” (Eks 25:22; Nu 7:89) N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Yehova ankakhala “pamwamba [kapena kuti, pakati] pa akerubi.” (1Sa 4:4; 2Sa 6:2; 2Mf 19:15; 1Mb 13:6; Sl 80:1; 99:1; Yes 37:16) Mophiphiritsira, akerubi anali ngati “chifaniziro cha galeta” lomwe Yehova ankakweramo (1Mb 28:18), ndipo mapiko awo amateteza komanso amathandiza kuti aziyenda mofulumira. Choncho Davide, anaimba nyimbo yomwe anafotokoza kuti Yehova anabwera mofulumira kudzamuthandiza ngati kuti “anakwera pakerubi ndipo anabwera akuuluka” komanso anali pa “pamapiko a mngelo.”​—2Sa 22:11; Sl 18:10.

MARCH 18-24

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 19-21

“Zinthu Zakumwamba Zikulengeza Ulemerero wa Mulungu”

w04 1/1 8 ¶1-2

Anthu Onse Alengeze Ulemerero wa Yehova

DAVIDE, mwana wa Jese, anakula monga mbusa ku dera la ku Betelehemu. Ayenera kuti nthawi zambiri ankayang’anitsitsa kumwamba kodzaza ndi nyenyezi zambirimbiri usiku, kunja kuli zii, akuyang’anira ziweto za atate wake m’malo odyetserako nkhosa amene ankakhala kwaokha. Mosakayikira, anakumbukira zinthu zosaiwalika zimenezi pamene, motsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, analemba ndi kuyimba mawu ochititsa chidwi a mu Salmo 19, amene amati: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Muyeso wawo wapitirira pa dziko lonse lapansi, ndipo mawu awo ku malekezero a m’dziko muli anthu.”​—Salmo 19:1, 4.

2 Zakumwamba zochititsa chidwi zolengedwa ndi Yehova zimalengeza ulemerero wa Yehova usana ndi usiku popanda kulankhula, popanda mawu, popanda liwu lawo kumveka. Chilengedwe sichisiya kulengeza ulemerero wa Mulungu, ndipo tikaganizira kuti umboni wopanda mawu umenewu umapita “pa dziko lonse lapansi” kuti anthu onse okhalamo awuone, zimatichititsa kuzindikira kuti ndife ochepa mphamvu kwambiri. Komabe, umboni wopanda mawu wa chilengedwe si wokwanira. Anthu okhulupirika akulimbikitsidwa kulengeza nawo umboni umenewu ndi mawu awo. Wolemba salmo wina, amene dzina lake silinatchulidwe, anauza olambira okhulupirika kuti: “M’patseni Yehova ulemerero ndi mphamvu. M’patseni Yehova ulemerero wa dzina lake.” (Salmo 96:7, 8) Anthu amene ali ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova amasangalala kumvera langizo limeneli. Koma kodi kupatsa Mulungu ulemerero kumatanthauza chiyani?

w04 6/1 11 ¶8-10

Chilengedwe Chimalengeza Ulemerero wa Mulungu

8 Kenako, Davide anafotokoza chinthu china chodabwitsa m’chilengedwe cha Yehova. Anati: “Iye anaika hema la dzuwa mmenemo [m’mwamba], ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m’chipinda mwake, likondwera ngati chimphona kuthamanga m’njira. Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira kumalekezero ake: ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.”​—Salmo 19:4-6.

9 Dzuwa ndi locheperapo poyerekezera ndi nyenyezi zina. Komabe, ndi nyenyezi yaikulu, moti mapulaneti amene amazungulira dzuwalo amaoneka aang’ono kwambiri. Buku lina limanena kuti dzuwa ndi lolemera matani 2 biliyoni, biliyoni, biliyoni. Kulemera kumeneku kumaposeratu kutalitali kulemera kwa mapulaneti onse amene amazungulira dzuwa kuwaphatikiza pamodzi. Mphamvu ya dzuwa imachititsa kuti dziko lapansili lizizungulira dzuwalo pa mtunda wa makilomita 150 miliyoni popanda kupatuka n’kupita kutali kapena kukokeka n’kuliyandikira kwambiri. Ndi mphamvu yochepa chabe ya dzuwa imene imafika padziko lapansi koma ndi yokwanira kuti zamoyo zikhalepobe padzikoli.

10 Wamasalmo anagwiritsa ntchito mawu okuluwika pofotokoza za dzuwa pamene ananena kuti dzuwa ndi “chimphona” chimene chimathamanga kuchokera kumalekezero ena kufika malekezero ena masana, ndipo usiku chimakagona mu “hema.” Nyenyezi yaikulu imeneyi ikamalowa kumadzulo, munthu akamaiona ali padziko lapansi imaoneka ngati imapita mu “hema,” ngati kuti ikukapuma. Kum’mawa imaoneka ngati ikutumphuka, n’kuwala kwambiri “ngati mkwati wakutuluka m’chipinda mwake.” Popeza anali mbusa, Davide ankadziwa kuti usiku kunali kuzizira kwambiri. (Genesis 31:40) Anali kukumbukira kuti dzuwa linkamuchititsa kumva kutenthera mofulumira komanso kutenthetsa malo amene iye anali. Mwachionekere, silinali kutopa pa “ulendo” wake wochoka kum’mawa kufika kumadzulo koma linali ngati “chimphona,” chokonzeka kubwerezanso ulendo wake.

g95 11/8 23 ¶2

Waluso Amene Akunyalanyazidwa Kwambiri Masiku Ano

Kuyamikira kwambiri zinthu zachilengedwe zimene timaona, kungatithandize kudziwa bwino Mlengi wathu. Pa nthawi ina Yesu anauza ophunzira ake kuti ayang’anitsitse maluwa akutchire omwe ankamera ku Galileya. Iye ananena kuti: “Phunzirani mmene maluwa akutchire amakulira. Sagwira ntchito ndiponso sawomba nsalu. Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.” (Mateyu 6:28, 29) Kukongola kwa duwa limene silichedwa kuwonongeka, kungatikumbutse kuti Mulungu amadziwa bwino kusamalira anthu.

Mfundo Zothandiza

it-1 1073

Chiheberi, II

Ndiyeno pali ndakatulo zina zimene mzere wachiwiri sikuti umangobwereza mfundo ya mzere woyamba kapenanso kunena mfundo yotsutsana nayo. Koma m’malomwake mzere wachiwiriwo umafutukula mfundo ya mzere woyambawo kapena kuwonjezerapo mfundo yatsopano. Salimo 19:7-9 ndi chitsanzo chabwino cha ndakatulo zoterezi:

Chilamulo cha Yehova ndi changwiro,

chimabwezeretsa mphamvu.

Zikumbutso za Yehova ndi zodalirika,

zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.

Malamulo ochokera kwa Yehova ndi olungama,

amasangalatsa mtima.

Chilamulo cha Yehova ndi choyera,

chimatsegula maso.

Kuopa Yehova nʼkoyera,

ndipo kudzakhalapo kwamuyaya.

Zigamulo za Yehova nʼzolondola,

ndipo pa mbali iliyonse ndi zolungama.

Onani kuti mzere wachiwiri wa chiganizo chilichonse ukumalizitsa mfundo ya mzere woyamba; choncho mbali ziwirizi zikudalirana kuti mfundo ya vesi lonse imveke bwino. Munthu akawerenga mizere yachiwiriyi monga yakuti “chimabwezeretsa mphamvu,” ndi “zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu,” ndi pamene akutha kuphunzira mmene ‘chilamulo chilili changwiro’ komanso mmene ‘zikumbutso za Yehova zilili zodalirika.’ M’ndakatulo zoterezi, kugawa ziganizo m’njira imeneyi kumathandiza kuti polakatula azitha kuima pang’ono asananene chiganizo chotsatira. Choncho pamene mfundo ikupitirira kutambasulidwa, ndime yonse ya ndakatuloyo imakhalanso kuti yalembedwa m’njira yoti ziganizo zake ziziyenda ziwiriziwiri.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwfq 45

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?

Ifeyo timayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pochita mwambo wa “chakudya chamadzulo cha Ambuye,” womwe umadziwikanso ndi dzina lakuti “mgonero wa Ambuye,” kapena kuti Chikumbutso cha imfa ya Yesu. (1 Akorinto 11:20; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Koma zinthu zambiri zimene zipembedzo zina zimachita komanso kukhulupirira zokhudza mwambowu sizichokera m’Baibulo.

Cholinga chake

Cholinga chochitira mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndi kukumbukira Yesu ndiponso kusonyeza kuti timayamikira nsembe imene anapereka chifukwa cha ife. (Mateyu 20:28; 1 Akorinto 11:24) Koma sikuti munthu amakhululukidwa machimo ake chifukwa chochita mwambowu. Baibulo limanena kuti munthu amakhululukidwa machimo ake akamakhulupirira Yesu osati chifukwa chochita mwambo winawake wachipembedzo.​—Aroma 3:25; 1 Yohane 2:1, 2.

Kodi tiyenera kuchita kangati?

Yesu anauza ophunzira ake kuti azichita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye koma sanawauze kuti azichita kangati. (Luka 22:19) Anthu ena amaona kuti ayenera kuchita mwambowu kamodzi pa mwezi, ena kamodzi pa mlungu, ena kamodzi pa tsiku, pomwe ena amaona kuti ayenera kuchita kangapo pa tsiku. Pali enanso omwe amaona kuti angachite mwambowu mobwerezabwereza mmene angafunire. Ngakhale zili choncho, pali mfundo zina zimene tiyenera kuziganizira.

Yesu anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye pa tsiku limene Ayuda ankachita Pasika. Iye anamwaliranso tsiku lomwelo. (Mateyu 26:1, 2) Koma sikuti zimenezi zinangochitika mwangozi. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limayerekezera nsembe ya Yesu ndi nkhosa imene ankagwiritsa ntchito pa tsiku la Pasika. (1 Akorinto 5:7, 8) Ayuda ankachita Pasika kamodzi pa chaka. (Ekisodo 12:1-6; Levitiko 23:5) Choncho Akhristu oyambirira ankachita mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu kamodzi pa chaka. Nawonso a Mboni za Yehova amachita zimenezi.

Tsiku komanso nthawi

Nthawi imene Yesu anayambitsa mwambowu imatithandizanso kudziwa tsiku ndiponso nthawi imene tiyenera kuchita mwambo wa Chikumbutso. Iye anachita zimenezi pa Nisani 14 dzuwa litalowa m’chaka cha 33 C.E. (Mateyu 26:18-20, 26) Tsiku limeneli ndi la m’kalendala yoyendera mwezi imene Ayuda ankagwiritsa ntchito. A Mboni amachitabe mwambo wa Chikumbutso pa tsiku limeneli chaka chilichonse ngati mmene Akhristu oyambirira ankachitira.

MARCH 25-31

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | SALIMO 22

Baibulo Linaneneratu Zinthu Zina Zokhudza Imfa ya Yesu

w11 8/15 15 ¶16

Anapeza Mesiya

16 Mesiya adzaoneka ngati wasiyidwa ndi Mulungu. (Werengani Salimo 22:1.) Maliko ananena kuti cha m’ma 3 koloko, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “‘Eli, Eli, lama sabachthani?’ Mawu amenewa akawamasulira amatanthauza kuti: ‘Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?’” (Maliko 15:34) Ponena zimenezi, sikuti Yesu anali atasiya kukhulupirira Atate wake wakumwamba. Iye anadziwa kuti Mulungu sadzamuteteza kwa adani ake pa nthawi ya imfa yake. Unali mwayi woti Yesu asonyeze kuti adzakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale pamene akuyesedwa. Kufuula kwa Yesu kumeneku kunakwaniritsa ulosi wa pa Salimo 22:1.

w11 8/15 15 ¶13

Anapeza Mesiya

13 Davide analosera kuti Mesiya adzanyozedwa. (Werengani Salimo 22:7, 8.) Yesu atapachikidwa pamtengo wozunzikirapo ananyozedwa. Mateyu analemba kuti: “Tsopano anthu odutsa anayamba kunena mawu onyoza Yesu. Anali kupukusa mitu yawo n’kumanena kuti: ‘Iwe wogwetsa kachisi ndi kum’manga m’masiku atatu, dzipulumutse! Ngati ulidi mwana wa Mulungu, tsikatu pamtengo wozunzikirapowo!’” Nawonso ansembe aakulu, alembi komanso akulu anayamba kumuchita chipongwe ndi kunena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ameneyutu ndi Mfumu ya Isiraeli, atsiketu pamtengo wozunzikirapowo kuti ife timukhulupirire. Suja amakhulupirira Mulungu? Mulunguyo am’pulumutse tsopano ngati akumufunadi. Ndi ujatu anali kunena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’” (Mat. 27:39-43) Yesu anapirira zonsezi popanda kupsa mtima kapena kubwezera. Iye ndiye chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.

w11 8/15 15 ¶14

Anapeza Mesiya

14 Adzachita maere pazovala za Mesiya. Wamasalimo analemba kuti: “Iwo akugawana zovala zanga pakati pawo, ndipo akuchita maere pazovala zanga.” (Sal. 22:18) Zimenezi zinachitikadi. Baibulo limanena kuti asilikali achiroma “atam’pachika [Yesu] anagawana malaya ake akunja mwa kuchita maere.”​—Mat. 27:35; werengani Yohane 19:23, 24.

Mfundo Zothandiza

w06 11/1 29 ¶7

Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika

7 Pali njira zoonekeratu zimene tingalemekezere misonkhano yathu. Njira imodzi ndiyo kuimba nawo nyimbo za Ufumu. Zambiri mwa nyimbo zimenezi zinalembedwa ngati mapemphero, choncho tiyenera kuziimba mwaulemu. Pogwira mawu Salmo 22, mtumwi Paulo analemba za Yesu kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga, pakati pa mpingo ndidzakutamandani ndi nyimbo.” (Aheberi 2:12) Choncho tiziyesetsa kukhala pansi tcheyamani asanatchule nyimbo imene tiimbe kenaka n’kuimba moganizira kwambiri tanthauzo la mawu a nyimboyo. Kuimba kwathu kuzisonyeza mmene wamasalmo ankamvera, amene analemba kuti: “Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.” (Salmo 111:1) Zoonadi, kuimbira Yehova zitamando n’chifukwa chimodzi chabwino kwambiri choti tizifikira mwamsanga pa misonkhano yathu n’kukhalapo mpaka pamapeto.

w03 9/1 20 ¶1

Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano”

Masiku ano, monga mmene zinthu zinalili kale, anthu okhulupirira amapatsidwa mwayi woti azitha kulankhula za chikhulupiriro chawo “pakati pa msonkhano.” Aliyense ali ndi mwayi woyankha mafunso amene amafunsidwa kwa omvetsera pa misonkhano ya mpingo. Musamapeputse mphamvu ya ndemanga zimenezi. Mwachitsanzo, ndemanga zimene zimasonyeza zimene tingachite kuti tithane ndi mavuto kapena tiwapewe zimalimbikitsa abale kuti apitirizebe kutsatira mfundo za m’Baibulo. Ndemanga zofotokoza malemba a m’Baibulo amene atchulidwa koma sanawagwire mawu pandimepo, kapena zofotokoza mfundo zimene munthu wapeza atachita kafukufuku payekha, zingalimbikitse ena kukulitsa chizolowezi chophunzira paokha.

APRIL 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 23-25

“Yehova Ndi Mʼbusa Wanga”

w11 5/1 31 ¶3

“Yehova Ndi Mʼbusa Wanga”

Yehova amatsogolera nkhosa zake. Nkhosa zikakhala zopanda m’busa zimasochera. N’chimodzimodzinso anthufe, pa moyo wathu timafunika wotitsogolera. (Yeremiya 10:23) Davide anafotokoza kuti Yehova amatsogolera anthu ake “m’mabusa a msipu wambiri,” ndi “m’malo opumira a madzi ambiri.” Amawatsogoleranso “m’tinjira tachilungamo.” (Vesi 2 ndi 3) Zimene Yehova amachitazi zikufanana ndi zimene m’busa amachita posamalira nkhosa zake ndipo zikutitsimikizira kuti tiyenera kumukhulupirira. Tikamatsatira malangizo a Mulungu opezeka m’Baibulo, tingakhale ndi moyo wokhutira, wosangalala ndiponso tingakhale ndi tsogolo labwino.

w11 5/1 31 ¶4

“Yehova Ndi Mʼbusa Wanga”

Yehova amateteza nkhosa zake. Nkhosa zikakhala zopanda m’busa zimachita mantha komanso zimasowa wozithandiza. Yehova amauza anthu ake kuti asachite mantha ngakhale ‘poyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani.’ Imeneyi ingakhale nthawi imene munthu amaona kuti ali pa mavuto adzaoneni. (Vesi 4) Pa nthawi imeneyi Yehova amaona zimene zikuchitikira atumiki ake ndipo amakhala wokonzeka kuwathandiza. Iye amapatsa atumiki ake nzeru ndi mphamvu kuti athe kupirira mayesero awo.​—Afilipi 4:13; Yakobo 1:2-5.

w11 5/1 31 ¶5

“Yehova Ndi Mʼbusa Wanga”

Yehova amadyetsa nkhosa zake. Nkhosa zimadalira m’busa wawo kuti azipezere chakudya. Anthufe tili ndi zosowa zauzimu zimene Mulungu yekha ndi amene angatithandize kuti tizipeze. (Mateyu 5:3) Tikuyamikira kuti Yehova ndi Wowolowa manja ndipo amapatsa atumiki ake chakudya chauzimu chambiri. (Vesi 5) Tikamawerenga zinthu monga Baibulo komanso mabuku othandiza anthu kuphunzira Baibulo, ngati Nsanja ya Olonda imene mukuwerengayi, timapeza chakudya chauzimu chimene chimatithandiza kudziwa cholinga cha moyo komanso zimene Mulungu akufuna kudzatichitira.

Mfundo Zothandiza

w11 2/15 24 ¶1-3

Muzikonda Chilungamo ndi Mtima Wanu Wonse

YEHOVA akutsogolera anthu ake “m’tinjira tachilungamo” kudzera m’Mawu ake ndiponso mwa mzimu wake woyera. (Sal. 23:3) Komabe popeza anthufe ndife opanda ungwiro, nthawi zina timachoka panjira yachilungamo. Zikatere pamafunika khama kuti tiyambirenso kuchita zinthu zabwino. Kodi chingatithandize n’chiyani? Mofanana ndi Yesu, tiyenera kukonda kuchita zinthu zolungama.​—Werengani Salimo 45:7.

2 Kodi palembali “tinjira tachilungamo” n’chiyani? “Tinjira” timeneti ndi moyo umene munthu amakhala chifukwa chotsatira mfundo zolungama za Yehova. Mawu achiheberi ndiponso achigiriki amene amamasuliridwa kuti “chilungamo” amatanthauza “kuwongoka” potsatira kwambiri makhalidwe abwino. Popeza Yehova ndi “malo okhalamo chilungamo,” anthu amene amamulambira amadalira iyeyo kuti awauze njira za makhalidwe abwino zimene iwowo ayenera kutsatira.​—Yer. 50:7.

3 Kuti tikondweretsedi Mulungu, tiyenera kuyesetsa ndi mtima wathu wonse kutsatira zimene iye amaona kuti ndi zolungama. (Deut. 32:4) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuphunzira zambiri za Yehova Mulungu kuchokera m’Mawu ake, Baibulo. Tikamaphunzira zambiri za Mulungu ndiponso kumuyandikira tsiku lililonse, m’pamenenso timakonda kwambiri chilungamo chake. (Yak. 4:8) Komanso tikamasankha zinthu zofunika pa moyo wathu, tiyenera kulola kuti Mawu ouziridwa a Mulungu azititsogolera.

APRIL 8-14

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 26-28

Zomwe Davide Anachita Kuti Akhalebe Wokhulupirika kwa Yehova

w04 12/1 14 ¶8-9

Yendani mu Umphumphu

8 Davide anapemphera kuti: “Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.” (Salmo 26:2) Impso zili m’katikati mwa thupi lathu. Impsozo, mophiphiritsira zimaimira maganizo a munthu a pansi penipeni pa mtima. Ndipo mtima wophiphiritsira umaimira m’kati mwa munthu, kapena kuti zimene zimamusonkhezera kuchita zinazake, mmene amamvera mumtima mwake, ndiponso nzeru zake. Popempha Yehova kuti amuyesere kapena kuti amuyese, Davide kwenikweni anali kupemphera kuti Yehova afufuze ndi kuyesa zoganiza zake za pansi pa mtima wake ndiponso mmene amamvera mumtima mwakemo.

9 Davide anapempha kuti impso ndi mtima wake ziyeretsedwe. Kodi Yehova amatiyeretsa motani m’kati mwathu? Davide anaimba kuti: “Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu: Usikunso impso zanga zindilangiza.” (Salmo 16:7) Kodi izi zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti malangizo a Mulungu anam’fika pamtima Davide n’kukhazikika mumtimamo, ndi kukonza maganizo am’katikati mwa mtima wake. Zimenezi zingatichitikirenso ifeyo ngati timasinkhasinkha ndi mtima woyamikira malangizo amene timalandira kudzera m’Mawu a Mulungu, anthu omuimira, ndiponso gulu lake, ndi kulola kuti malangizowo akhazikike mumtima mwathu. Kupemphera nthawi zonse kwa Yehova kuti atiyeretse moteremu kungatithandize kuti tiyende mu umphumphu.

w04 12/1 15 ¶12-13

Yendani mu Umphumphu

12 Pofotokoza chinthu chinanso chomwe chinalimbitsa umphumphu wake, Davide anati: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu othyasika. Ndidana nawo msonkhano wa ochimwa, ndipo sindidzakhala nawo pansi ochita zoipa.” (Salmo 26:4, 5) Davide sankakhala pansi, ngakhale pang’ono chabe, ndi anthu oipa. Sankafuna kugwirizana nawo.

13 Nanga bwanji ifeyo? Kodi timakana kukhala ndi anthu achabe, kudzera m’mapulogalamu a pa TV, m’mavidiyo, m’makanema, pa Intaneti, kapena m’njira zina? Kodi timapewa anthu amene amabisa umunthu wawo? Anthu ena kusukulu kapena kuntchito kwathu anganamizire kuti ndi anzathu pamene ali ndi zolinga zachabe. Ndithudi, sitingafune kugwirizana ndi anthu amene sayenda m’choonadi cha Mulungu. Ngakhale kuti ampatuko amati ndi anthu oona mitima, nawonso angabise cholinga chawo pofuna kuti atisiyitse kutumikira Yehova. Kodi tingatani ngati mumpingo wachikristu muli ena amene ali ndi moyo wachiphamaso? Nawonso ndiye kuti amabisa umunthu wawo weniweni. Jayson, yemwe tsopano ndi mtumiki wotumikira, anali ndi anzake ngati amenewa ali wamng’ono. Pofotokoza za anthu amenewa, iye anati: “Tsiku lina mmodzi wa anzangawa anandiuza kuti: ‘Zimene timachita panopa zilibe ntchito chifukwa dziko latsopano likamadzafika, tidzakhala titafa basi. Sitidzadziwa kuti tikumanidwa chilichonse.’ Zimene ananenazi zinandigalamutsa. Ineyo sindikufuna kuti ndidzakhale nditafa dziko latsopano likamadzabwera.” Jayson anachita zanzeru posiya kugwirizana ndi anthu amenewa. Mtumwi Paulo anachenjeza motere: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Motero kupewa kugwirizana ndi anthu oipa n’kofunika kwambiri.

w04 12/1 16 ¶17-18

Yendani mu Umphumphu

17 Chihema, pamodzi ndi ntchito zake za nsembe, chinali likulu lolambirirapo Yehova ku Israyeli. Pofotokoza mmene ankasangalalira ndi malo amenewo, Davide anapemphera kuti: “Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.”​—Salmo 26:8.

17 Kodi timakonda kusonkhana pamalo amene timaphunzira za Yehova? Nyumba ya Ufumu iliyonse, chifukwa cha maphunziro auzimu amene amachitikirapo, imakhala likulu la kulambira koona m’dera limene muli nyumbayo. Komanso, chaka n’chaka timakhala ndi misonkhano yachigawo, yadera, ndiponso masiku a misonkhano yapadera. Pamisonkhanoyi pamafotokozedwa “mboni,” kapena kuti zikumbutso za Yehova. Tikaphunzira ‘kuzikonda kwambiri’ zikumbutsozi, timakhala ofunitsitsa kupita kumisonkhano ndi kukatchera khutu tikafika kumisonkhanoko. (Salmo 119:167) N’zotsitsimutsa kwambiri kukhala ndi okhulupirira anzathu amene amadera nkhawa za moyo wathu ndiponso amene amatithandiza kupitiriza kuyenda mu umphumphu.​—Ahebri 10:24, 25.

Mfundo Zothandiza

w06 7/15 28 ¶15

Yehova Amalanditsa Wovutika

15 Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) N’zolimbikitsa kudziwa kuti chikondi cha Yehova chimaposa cha kholo lina lililonse. Ngakhale kuti kukanidwa ndiponso kuzunzidwa ndi makolo kungakhale kowawa kwambiri, sikungasinthe mmene Yehova amatisamalirira. (Aroma 8:38, 39) Kumbukirani kuti Yehova amakoka munthu yemwe wakonda. (Yohane 3:16; 6:44) Zilibe kanthu kuti anthu akhala akukuchitirani zotani, Atate wanu wakumwamba amakukondani.

APRIL 15-21

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 29-31

Chilango Chimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

it-1 802 ¶3

Nkhope

Mawu akuti ‘kubisa nkhope’ ali ndi matanthauzo osiyanasiyana malinga ndi zimene zikuchitika. Yehova Mulungu akabisa nkhope yake, nthawi zambiri zimatanthauza kuti sakuonanso munthuyo ngati mnzake kapena wasiya kumuthandiza ndi mphamvu zake. Zimenezi zingachitike chifukwa cha kusamvera kwa munthuyo kapena kwa gulu la anthu amene akhudzidwa, monga mmene zinalili ndi mtundu wa Aisiraeli. (Yob 34:29; Sl 30:5-8; Yes 54:8; 59:2) Nthawi zina zimatanthauza kuti Yehova sakufuna kudzionetsera mwa kuchitapo kanthu kapena kuyankha pamene akudikira kuchita zimenezi pa nthawi yake yoikidwiratu. (Sl 13:1-3) Pamene Davide anati “bisani nkhope yanu kuti isaone machimo anga,” iye ankapempha Mulungu kuti amukhululukire kapena kuti achotse machimowo.​—Sl 51:9 mawu a m’munsi; yerekezerani ndi Sl 10:11.

w07 3/1 19 ¶1

Osangalala Kudikira Yehova

Njira imene chilango cha Yehova chimatipindulitsira tingaiyerekezere ndi mmene zipatso zimakhwimira. Baibulo limanena mawu otsatirawa pankhani ya kulanga kwa Mulungu: “Kwa aja amene aphunzitsidwa nako, kumabala chipatso cha mtendere, ndicho chilungamo.” (Aheberi 12:11) Zipatso zimatenga nthawi kuti zipse, motero kusintha maganizo athu kuti agwirizane ndi zimene mawu a Mulungu amatiphunzitsa, kumatenganso nthawi. Mwachitsanzo, ngati khalidwe lathu linalake losayenera litachititsa kuti titaye mwayi winawake wotumikira mumpingo, mtima wodikira Mulungu ungatithandize kuti tisafooke kwambiri n’kufika potayiratu mtima. Pamenepa, mawu ouziridwa a Davide otsatirawa angatilimbikitse: “Mkwiyo [wa Mulungu] ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.” (Salmo 30:5) Tikakhala ndi mtima wodikira ndi kutsatira malangizo a Mawu a Mulungu ndi gulu lake, nthawi yathu ya “kufuula kokondwera” idzafika.

w21.10 6 ¶18

Kodi Kulapa Kwenikweni N’kutani?

18 Posonyeza kuti walapa kuchokera pansi pamtima, munthu amene wachotsedwa amafika pamisonkhano mokhazikika, ndipo amatsatira malangizo a akulu oti azipemphera nthawi zonse komanso kuphunzira Baibulo. Iye amayesetsanso kupewa zinthu zimene zinamuchititsa kuti achite tchimo. Ngati atayesetsa kukonza ubwenzi wake ndi Yehova sangakayikire kuti iye amukhululukira ndi mtima wonse komanso akulu angamubwezeretse mumpingo. Komabe akulu akamafuna kudziwa ngati munthu walapadi, amaganizira nkhani iliyonse payokha ndipo amafufuza mosamala kuti asaweruze mopupuluma.

Mfundo Zothandiza

w06 5/15 19 ¶12

Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo

31:23​—Kodi munthu wodzitama amabwezeredwa motani zochuluka? Zimene akutchula pano kuti adzabwezeredwa ndi chilango. Munthu wolungama amabwezeredwa m’njira ya chilango chochokera kwa Yehova chifukwa cha zimene waphonyetsa mwangozi. Popeza munthu wodzitama sasiya kuchita zoipa, amabwezeredwa zochuluka ndi chilango chokhwima.​—Miyambo 11:31; 1 Petro 4:18.

APRIL 22-28

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 32-33

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuulula Tchimo Lalikulu?

w93 3/15 9 ¶7

Chifundo cha Yehova Chimatithandiza

7 Ngati sitinamvere malamulo a Mulungu ndipo tachita tchimo lalikulu, tikhoza kuvutika kuulula tchimolo, ngakhale kwa Yehova. Kodi chingachitike n’chiyani zikatere? Mu Salimo 32, Davide anavomereza kuti: “Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa ndinkavutika mumtima mwanga tsiku lonse. Dzanja lanu linkandilemera masana ndi usiku. Mphamvu zanga zinauma ngati madzi mʼnyengo yotentha yachilimwe.” (Vesi 3, 4) Davide anafooka chifukwa choti ankabisa tchimo lake komanso kunyalanyaza chikumbumtima chake. Mphamvu zake zinatha chifukwa cha nkhawa, ndipo anangokhala ngati wauma mofanana ndi mtengo womwe ukusowa madzi m’nthawi yachilala. Ndipo n’kutheka kuti zimenezi zinkamuvutitsa maganizo komanso zinakhudza thanzi lake. Mulimonsemo, iye anasiya kukhala wosangalala. Kodi ifenso zangati zimenezi zitatichitikira, tingatani?

cl 262 ¶8

Mulungu “Wokhululukira”

8 Davide atalapa ananena mawu awa: ‘Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. . . . Ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.’ (Salmo 32:5) Mawu akuti “munakhululukira” atembenuzidwa kuchokera ku mawu achihebri amene makamaka amatanthauza kuti “kunyamula” kapena “kutenga.” Mmene agwiritsidwira ntchito pa lembali akusonyeza kuchotsa “cholakwa, tchimo, kapena choipa.” Motero tingati Yehova ananyamula machimo a Davide n’kuwachotsa. Mosakayikira izi zinachepetsa malingaliro amene Davide anali nawo odziona kuti anali wolakwa. (Salmo 32:3) Ifenso tingakhale n’chidaliro chonse mwa Mulungu yemwe amachotsa machimo a anthu ofuna kuti awakhululukire chifukwa cha kukhulupirira kwawo nsembe ya dipo ya Yesu.​—Mateyu 20:28.

w01 6/1 29 ¶7

Kulapa Komwe Kumachiritsa

Davide atavomereza machimo ake sanadzione monga wopanda pake. Mawu ake m’masalmo omwe analemba onena za kuulula machimo, akusonyeza kuti anali womasuka ndi wotsimikiza kutumikira Mulungu mokhulupirika. Mwachitsanzo, taonani Salmo 32. Vesi 1 limati: “Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake.” Ngakhale tchimo litakhala lalikulu bwanji, zotsatira zake zimakhala zosangalatsa ngati munthu alapa moona mtima. Njira imodzi yosonyeza kuona mtima kumeneku, ndiyo kuvomereza zomwe tachita monga anachitira Davide. (2 Samueli 12:13) Iye sanapeze zifukwa zopeputsira kuchimwa kwake kwa Yehova kapena kuyesa kuloza ena chala. Vesi 5 likuti: “Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.” Kulapa kwenikweni kumakhazikitsa mtima pansi, choncho munthu savutikanso ndi chikumbumtima chake poganiza zomwe anachita kale.

Mfundo Zothandiza

w06 5/15 19 ¶13

Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo

33:6​—Kodi “mpweya” wa m’kamwa mwa Yehova n’chiyani? Mpweya umenewu ndi mphamvu yomwe Mulungu amagwiritsa ntchito, kapena kuti mzimu woyera, imene anagwiritsa ntchito polenga miyamba yomwe timaonayi. (Genesis 1:1, 2) Umatchedwa mpweya wa m’kamwa mwake chifukwa chakuti, mofanana ndi kupuma mwamphamvu, mzimuwu ungathe kutumizidwa kukagwira ntchito kutali kwambiri.

APRIL 29–MAY 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 34-35

“Muzitamanda Yehova Nthawi Zonse”

w07 3/1 22 ¶11

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

11 “Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kum’lemekeza kwake kudzakhala m’kamwa mwanga kosalekeza.” (Salmo 34:1) Popeza Davide ankakhala mothawathawa, ayenera kuti ankada nkhawa kuti azipeza bwanji zosowa za moyo wake. Koma mawu amenewa akusonyeza kuti Davide anapitirizabe kukhala ndi mtima wofuna kulemekeza Yehova, ngakhale kuti anali ndi nkhawa zimenezi. Iye alidi chitsanzo chabwino kwa ife tikamakumana ndi mavuto. Kaya tili ku sukulu, ku ntchito, tili limodzi ndi Akhristu anzathu, kapena tikulalikira, cholinga chathu chachikulu chizikhala chofuna kulemekeza Yehova. Tangoganizirani zifukwa zambirimbiri zomwe tili nazo zochitira zimenezi. Mwachitsanzo, pali zinthu zambiri zomwe tingaziphunzire ndi kusangalala nazo m’chilengedwe cha Yehova chochititsa chidwichi. Ndipo taganizirani zimene Yehova wachita pogwiritsira ntchito mbali yapadziko lapansi ya gulu lake. Yehova wagwiritsira ntchito anthu okhulupirika kuchita zinthu zazikulu, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro. Kodi ntchito za Mulungu tingaziyerekezere ndi za anthu amene dzikoli limawalambira? Kodi simukugwirizana ndi Davide, amene analemba kuti: “Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye; ndipo palibe ntchito zonga zanu.”​—Salmo 86:8.

w07 3/1 22 ¶13

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

13 “Moyo wanga udzatamanda Yehova; ofatsa adzakumva nadzakondwera.” (Salmo 34:2) Apa, Davide sanali kudzitama chifukwa cha zinthu zimene anachita bwino. Mwachitsanzo, sanadzitame chifukwa cha mmene ananamizira mfumu ya ku Gati. Anazindikira kuti Yehova anam’teteza ali ku Gati, ndi kuti anathawa chifukwa cha thandizo lake. (Miyambo 21:1) Choncho Davide sanadzitame, koma anatamanda Yehova. Zimenezi zinachititsa anthu ofatsa kuyamba kukonda Yehova. Yesu nayenso anakweza dzina la Yehova, ndipo zimenezi zinachititsanso anthu odzichepetsa ndi ophunzitsika kuyamba kukonda Yehova. Masiku ano, anthu ofatsa a m’mayiko onse akulowa mu mpingo wapadziko lonse wa Akhristu odzozedwa, womwe Yesu ndiye Mutu wake. (Akolose 1:18) Anthu ofatsawa amakhudzidwa mtima akamva dzina la Mulungu likulemekezedwa ndi atumiki ake odzichepetsa ndiponso akamvetsetsa uthenga wa m’Baibulo mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.​—Yohane 6:44; Machitidwe 16:14.

w07 3/1 23 ¶15

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

15 “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m’mantha anga onse.” (Salmo 34:4) Zinthu ngati zimenezi zinali zofunika kwambiri kwa Davide. Choncho anawonjezera kuti: “Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nam’pulumutsa m’masautso ake onse.” (Salmo 34:6) Tikakhala ndi okhulupirira anzathu, timakhala ndi mipata yambiri yofotokoza zinthu zolimbikitsa zosonyeza momwe Yehova watithandizira kupirira mavuto. Zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro cha okhulupirira anzathu, monga momwe zimene Davide ananena zinalimbitsira chikhulupiriro cha anthu omwe anali ku mbali yake. Anthu omwe anali ndi Davide ‘anayang’ana [Yehova] nasanguluka: ndipo pankhope pawo sipanachite manyazi.’ (Salmo 34:5) Iwo sanachite manyazi ngakhale kuti ankathawa Mfumu Sauli. Anali ndi chikhulupiriro choti Mulungu anali ndi Davide, ndipo nkhope zawo zinali zosangalala. Mofanana ndi zimenezi, anthu amene akungophunzira kumene choonadi komanso amene akhala Akhristu kwa nthawi yaitali amadalira Yehova kuti awathandize. Popeza adzionera okha Yehova akuwathandiza, nkhope zawo n’zosangalala ndipo zimasonyeza kuti ndi otsimikiza mtima kukhalabe okhulupirika.

Mfundo Zothandiza

w06 5/15 20 ¶1

Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo

35:19​—Kodi pempho la Davide loti asalole adani ake kum’tsinzinira likutanthauza chiyani? Kutsinzina kukanasonyeza kuti adani a Davide akusangalala chifukwa cha kuyenda bwino kwa zolinga zawo zomuchitira zoipa. Davide anapempha kuti zimenezi zisachitike.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwfq 59

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sachita Nawo Maholide Ena?

A Mboni za Yehova asanasankhe kuchita nawo holide inayake, amafufuza kaye zimene Baibulo limanena. Maholide komanso zikondwerero zina zimaphwanya mfundo za m’Baibulo ndipo a Mboni za Yehova sachita nawo zoterozo. Koma pali maholide ena omwe wa Mboni aliyense amayenera kusankha yekha pochita zinthu ‘mozindikira kuti asapalamule kwa Mulungu kapena kwa anthu.’​—Machitidwe 24:16.

Ena mwa mafunso omwe a Mboni za Yehova amadzifunsa asanasankhe kuchita nawo holide ndi awa:

● Kodi holide imeneyi ndi yochokera m’Baibulo?

Mfundo ya m’Baibulo: “‘Tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova. ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa.’”​—2 Akorinto 6:15-17.

Pofuna kusonyeza kuti sakufuna kugwirizana ndi ziphunzitso zosemphana ndi zimene Baibulo limanena, a Mboni za Yehova sachita nawo:

Maholide amene anachokera pa kukhulupirira kapena kulambira milungu. Yesu ananena kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Mateyu 4:10) Potsatira langizo limeneli, a Mboni za Yehova sakondwerera nawo Khirisimasi, Isitala, kapena May Day, chifukwa chiyambi cha maholide amenewa chinali kulambira milungu ina osati Yehova.

Maholide omwe anachokera pa kukhulupirira zamatsenga komanso kukhulupirira mwayi. Baibulo limanena kuti inu amene “mumayalira tebulo mulungu wa Mwayi,” ndiye kuti “mwamusiya Yehova.”​—Yesaya 65:11.

Maholide omwe anachokera pa chiphunzitso choti pali chinachake chimene chimakhalabe ndi moyo munthu akafa. Baibulo limanena momveka bwino kuti moyo umafa.​—Ezekieli 18:4.

Maholide okhudzana ndi zamatsenga. Baibulo limanena kuti: “Wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa . . . ndi wonyansa kwa Yehova.” (Deuteronomo 18:10-12) Choncho pofuna kupewa chilichonse chokhudzana ndi zamatsenga, kuphatikizaponso kukhulupirira nyenyezi komwenso kumakhudzana ndi kulosera zam’tsogolo, a Mboni za Yehova sachita nawo chikondwerero cha Halowini kapenanso maholide ena okhudzana ndi zimenezi.

Miyambo yokhudzana ndi kulambira yomwe inali pansi pa Chilamulo cha Mose, yomwe inatha ndi nsembe ya Yesu. Baibulo limanena kuti: “Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo.” (Aroma 10:4) N’zoona kuti Akhristu amagwiritsabe ntchito mfundo za m’Chilamulo cha Mose zomwe Aisiraeli ankatsatira. Komabe sachita nawo zikondwerero zomwe zinkachitika nthawi imeneyo, makamaka zokhudzana ndi kubwera kwa Mesiya, yemwe Akhristu amakhulupirira kuti anabwera kale. Baibulo limanena kuti: “Zinthu zimenezo ndi mthunzi wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni zake zili mwa Khristu.” (Akolose 2:17) Popeza kuti cholinga cha zikondwererozo chinakwaniritsidwa kale komanso kuti panopa zikondwerero zoterezi zikumaphatikizidwa ndi miyambo ina yosemphana ndi Malemba, a Mboni za Yehova sachita nawo.

● Kodi holideyi imalimbikitsa kuti anthu a m’zipembedzo zosiyanasiyana azichitira zinthu pamodzi?

Mfundo ya M’Baibulo: “Munthu wokhulupirira angagawane chiyani ndi wosakhulupirira? Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?”​—2 Akorinto 6:15-17.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amayesetsa kukhala mwamtendere ndi anzawo komanso kulemekeza ufulu wa aliyense wosankha chipembedzo chomwe angafune, sachita nawo zikondwerero zomwe zimalimbikitsa kuti anthu azipembedzo zosiyanasiyana azichitira zinthu limodzi, pochita zinthu zotsatirazi.

Zikondwerero zokhudzana ndi kulambira chinthu chinachake kapena zochitika zomwe zimalimbikitsa anthu azipembedzo zosiyanasiyana kuti azipempherera pamodzi. Pa nthawi imene Mulungu anatsogolera anthu ake akale kupita kudera latsopano komwe kunali anthu olambira milungu ina, anawauza kuti: “Usachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo. . . . Udzakhala msampha kwa iwe.”​—Ekisodo 23:32, 33.

Miyambo yomwe inachokera pa ziphunzitso zachipembedzo zosagwirizana ndi Baibulo. Yesu anauza atsogoleri achipembedzo kuti: “Mwasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake chifukwa cha miyambo yanu.” Anawauzanso kuti kulambira kwawo n’kopanda phindu chifukwa “amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.” (Mateyu 15:6, 9) A Mboni za Yehova amamvera chenjezo limeneli ndipo sachita nawo miyambo yokhudza zipembedzo yomwe sigwirizana ndi Baibulo.

● Kodi holideyi imapereka ulemu wapadera kwa munthu, bungwe kapena chizindikiro chinachake choimira dziko?

Lemba lothandiza: “Yehova wanena kuti: ‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wokhulupirira mwa munthu aliyense wochokera kufumbi. Wotembereredwa ndi munthu amene amadalira mphamvu za dzanja la munthu, komanso amene mtima wake wapatuka kuchoka kwa Yehova.’”​—Yeremiya 17:5.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amayamikira anzawo komanso kuwapempherera, sachita nawo zochitika ndiponso zikondwerero zotsatirazi:

Maholide omwe amalemekeza wolamulira kapena munthu wina wolemekezeka. Baibulo limanena kuti: “Kuti zinthu zikuyendereni bwino, musadalire munthu wochokera kufumbi amene mpweya wake uli m’mphuno mwake, pakuti palibe chifukwa choti mum’ganizire iyeyo.” (Yesaya 2:22) N’chifukwa chake a Mboni za Yehova sachita nawo zinthu monga kukondwerera tsiku lobadwa la mfumu kapena mfumukazi.

Zikondwerero za mbendera ya dziko. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova samakondwerera nawo Tsiku Lokumbukira Mbendera? Baibulo limanena kuti: “Pewani mafano.” (1 Yohane 5:​21) Anthu ena masiku ano sazindikira kuti kulemekeza mbendera n’chimodzimodzi ndi kulambira mafano. Koma wolemba mbiri wina dzina lake Carlton J. H. Hayes analemba kuti: “Chizindikiro chosonyeza kuti munthu amakonda kwambiri dziko lake komanso kulikhulupirira ndi kulambira mbendera.”

Maholide kapena zikondwerero zomwe cholinga chake ndi kulemekeza oyera mtima. Munthu wina woopa Mulungu atagwadira mtumwi Petulo, Baibulo limanena kuti: “Petulo anamuimiritsa, ndi kunena kuti: ‘Imirira, inenso ndine munthu chabe.’” (Machitidwe 10:25, 26) Popeza kuti Petulo komanso atumwi ena onse sanavomereze kulandira ulemu wapadera kapena kulambiridwa, nawonso a Mboni za Yehova sachita zikondwerero zolemekeza anthu omwe amati ndi oyera mtima.

Zikondwerero za andale kapena zofuna kukonza zinthu m’dziko. Baibulo limanena kuti: “Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino kusiyana ndi kudalira munthu wochokera kufumbi.” (Salimo 118:8, 9) Pofuna kusonyeza kuti amakhulupirira kuti Mulungu ndi amene adzathetse mavuto osati anthu, a Mboni za Yehova satenga nawo mbali pa zikondwerero zokhudzana ndi Tsiku la Achinyamata kapena Tsiku la Amayi, zomwe cholinga chake ndi kuthandizira zandale kapena kukonza zinthu m’dziko. A Mboni za Yehova satenganso mbali pa Tsiku Lokondwerera Kutha Kwa Ukapolo kapena zikondwerero zina zofanana ndi zimenezi. M’malomwake amayembekezera kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto obwera chifukwa cha kusankhana mitundu.​—Aroma 2:11; 8:21.

● Kodi holideyi imachititsa anthu kuona kuti mtundu wina ndi wofunika kwambiri kuposa unzake?

Lemba lothandiza: “Mulungu alibe tsankho, Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehova ambiri amakonda dziko lawo, iwo amapewa zikondwerero zomwe zingachititse kuti mtundu wawo kapena dziko lawo lizioneka lapamwamba kwambiri. Zikondwerero zake ndi monga:

Zochitika zomwe zimalemekeza asilikali. M’malo molimbikitsa nkhondo, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mateyu 5:44) Choncho a Mboni za Yehova sachita nawo zikondwerero zomwe zimalemekeza asilikali.

Zikondwerero za mbiri ya dziko kapena tsiku limene dziko linalandira ufulu. Ponena za otsatira ake, Yesu ananena kuti: “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:16) Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amasangalala kudziwa mbiri ya dziko lawo, iwo sachita nawo zikondwerero za mbiri ya dziko kapena tsiku limene dziko linalandira ufulu.

● Kodi holideyi imadziwika ndi makhalidwe oipa?

Lemba lothandiza: “Nthawi imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”​—1 Petulo 4:3.

Potsatira mfundo imeneyi, a Mboni za Yehova sapita ku zikondwerero komwe anthu amaledzera komanso kumaphwando a phokoso. Komabe amasangalala kucheza ndi anzawo, ndipo ngati akufuna, amatha kusankha kumwa mowa pang’ono. Iwo amayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.”​—1 Akorinto 10:31.

Choncho a Mboni za Yehova sachita nawo zikondwerero zimene zimalimbikitsa makhalidwe oipa amene Baibulo limaletsa. Zimenezi zikuphatikizapo phwando la Ayuda la Purim. Ngakhale kuti kwa zaka zambiri Ayuda akhala akuchita mwambo wa Purimu pokumbukira tsiku limene anamasulidwa ku ukapolo zaka za m’ma 400 B.C.E., buku la Essential Judaism limanena kuti: “Masiku ano mwambowu si odziwikanso kwambiri ndipo ukulowedwa m’malo ndi chikondwerero chachiyuda cha Mardi Gras kapena kuti Carnival.” Bukuli limapitirizanso kuti paphwandoli, “nthawi zambiri amuna amavala zovala za akazi, pamachitika zipolowe, anthu amaledzera, ndiponso pamakhala phokoso lokhalokha.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena