Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr24 May tsamba 1-15
  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu”
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2024
  • Timitu
  • MAY 6-12
  • MAY 13-19
  • MAY 20-26
  • MAY 27–JUNE 2
  • JUNE 3-9
  • JUNE 10-16
  • JUNE 17-23
  • JUNE 24-30
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2024
mwbr24 May tsamba 1-15

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu

© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

MAY 6-12

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 36-37

‘Musamakhumudwe Chifukwa cha Anthu Oipa’

w17.04 10 ¶4

Kodi Ufumu wa Mulungu Ukadzabwera Udzachotsa Zinthu Ziti?

4 Kodi zochita za anthu oipa zimatikhudza bwanji? Mtumwi Paulo ananeneratu kuti masiku ano adzakhala “nthawi yapadera komanso yovuta.” Iye analembanso kuti “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe.” (2 Tim. 3:1-5, 13) Kodi inuyo mwaonapo umboni wa zimenezi? Ambirife tavutikapo chifukwa cha zochita za anthu achiwawa, okwiya komanso achiwembu. Ena amachita kuonetsera kuipa kwawo pomwe ena amachita mwakabisira. Ngakhale zitakhala kuti anthu oterewa sanatichitire zoipa mwachindunji, zochita zawo zimatikhudzabe ndithu. Mwachitsanzo, timakhumudwa komanso timachita mantha tikamva za zinthu zimene anthu oipa achitira achikulire, ana komanso osauka. Anthu oipa amasonyeza mtima wauchinyama ndiponso wauchiwanda. (Yak. 3:15) Komabe anthu a Mulungufe timadziwa kuti pali uthenga wabwino.

w22.06 10 ¶10

Yehova Amadalitsa Anthu Omwe Amakhululuka

10 Timadzivulaza tokha tikamasunga chakukhosi. Yehova amafuna tizisangalala komanso kupepukidwa mumtima chifukwa chosasunga chakukhosi. (Werengani Aefeso 4:31, 32.) Iye amatilimbikitsa kuti ‘tisamapse mtima ndipo tizipewa kukwiya.’ (Sal. 37:8) Kutsatira malangizo amenewa n’kothandiza kwambiri. Kusunga chakukhosi kungawononge thanzi lathu komanso maganizo athu. (Miy. 14:30) Kusunga chakukhosi sikuvulaza munthu yemwe watilakwirayo, ngati mmene zingakhalire titamwa poizoni n’kumayembekezera kuti avulale ndi mnzathuyo. Choncho tikakhululukira ena zimakhala ngati tadzipatsa mphatso. (Miy. 11:17) Timakhala ndi mtendere wa mumtima ndi m’maganizo ndipo timapitirizabe kutumikira Yehova.

w03 12/1 13 ¶20

‘Kondwerani mwa Yehova’

20 Ndiyeno, “ofatsa adzalandira dziko lapansi.” (Salmo 37:11a) Koma kodi “ofatsa” amenewa ndani? Liwu limene analimasulira kuti “ofatsa” likuchokera ku liwu limene limatanthauza “kuzunza, kuchepetsa, kunyozetsa.” Inde, “ofatsa” ndi anthu amene amadikira Yehova modzichepetsa kuti adzakonza kupanda chilungamo kumene anthu ena akuwachitira. ‘Adzakondwera nawo mtendere wochuluka.’ (Salmo 37:11b) Ngakhale pakadali pano, tikupeza mtendere wochuluka m’paradaiso wauzimu amene ali mumpingo wachikristu woona.

Mfundo Zothandiza

it-2 445

Phiri, Mapiri

Kulimba, kukhazikika kapena kukula. Baibulo limasonyeza kuti mapiri amakhala olimba komanso amakhala okhazikika. (Yes 54:10; Hab 3:6; yerekezerani ndi Sl 46:2) Choncho pamene wolemba masalimo ankalemba kuti chilungamo cha Yehova “chili ngati mapiri a Mulungu” (Sl 36:6, mawu a m’munsi), n’kutheka kuti ankatanthauza kuti ndi chosasunthika. Kapena popeza kuti mapiri amakhala aatali zingatanthauze kuti chilungamo cha Mulungu ndi chapamwamba kwambiri kuposa cha anthu. (Yerekezerani ndi Yes 55:8, 9.) Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kuthira mbale ya 7 ya mkwiyo wa Mulungu, lemba la Chivumbulutso 16:20 limati: “Mapiri sanapezeke.” Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti ngakhale zinthu zimene ndi zazitali kwambiri ngati mapiri, sizingathawe mkwiyo wa Mulungu.​—Yerekezerani ndi Yer 4:23-26.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

ijwbv 45

Salimo 37:4​—“Udzikondweretsenso Mwa Yehova”

“Komanso sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.”​—Salimo 37:4, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Udzikondweretsenso mwa Yehova, ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.”​​—Salimo 37:4, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Salimo 37:4

Wolemba masalimo analimbikitsa atumiki a Mulungu kuti azisangalala chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulunguyo. Anthu onse amene ali pa ubwenzi umenewu, amakhala otsimikiza kuti Yehova Mulungu adzakwaniritsa zinthu zabwino zimene amalakalaka.

“Sangalala mwa Yehova.” Mawuwa angatanthauzenso kuti “sangalala kwambiri mwa Yehova,” “sangalala potumikira Yehova,” kapena “sangalala ndi zimene Yehova wakulonjeza.” Mwachidule, tiyenera “kumasangalala kwambiri” pamene tikulambira Mulungu woona. (Salimo 37:4, mawu a m’munsi Baibulo la Dziko Latsopano la Chingelezi) N’chifukwa chiyani zili choncho?

Anthu amene amalambira Yehova amaona zinthu mmene iye amazionera mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Si kuti iwo amangodziwa Mulungu, koma amaonanso kuti n’zofunika kwambiri kuti azimumvera. Zimenezi zimawathandiza kuti azikhala ndi chikumbumtima chabwino, azisankha bwino zinthu komanso azipewa mavuto ambiri. (Miyambo 3:5, 6) Mwachitsanzo, sapsa mtima kapena kuchita nsanje akamaona kuti anthu adyera komanso opanda chilungamo zinthu zikuwayendera bwino. (Salimo 37:1, 7-9) Anthu a Mulungu amasangalala podziwa kuti posachedwapa iye adzathetsa zopanda chilungamo zonse ndi kupereka mphoto kwa onse omwe amachita zinthu mokhulupirika. (Salimo 37:34) Iwo amasangalalanso podziwa kuti Atate wawo wa kumwamba akusangalala nawo.​​—Salimo 5:12; Miyambo 27:11.

“Adzakupatsa zokhumba za mtima wako.” Mawuwa angamasuliridwenso kuti “adzayankha mapemphero anu” kapena “adzakupatsani zomwe mukufunitsitsa.” Koma sikuti Yehova amayankha pemphero lililonse. Mofanana ndi kholo labwino, iye amadziwa zimene ana ake angafunikiredi. Ndipo zopempha zathu komanso mmene timachitira zinthu pa moyo wathu, ziyenera kukhala zogwirizana ndi chifuniro chake. (Miyambo 28:9; Yakobo 4:3; 1 Yohane 5:14) Zikatero tingakhale otsimikiza kuti “Wakumva pemphero” atiyankha pemphero lathu.​—Salimo 65:2; Mateyu 21:22.

Nkhani yonse ya pa Salimo 37:4

Salimo 37 linalembedwa ndi Davide yemwe anali Mfumu ya Isiraeli. Iye analemba salimoli potsatira afabeti.

Davide anavutika ndi zinthu zambiri zopanda chilungamo. Iye ankasakidwa ndi Mfumu Sauli komanso anthu ena omwe ankafuna kumupha. (2 Samueli 22:1) Komabe, Davide ankadalira Mulungu nthawi zonse. Iye ankadziwa kuti tsiku lina Yehova adzalanga anthu onse oipa. (Salimo 37:10, 11) Ngakhale ataoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino ngati “msipu watsopano wobiriwira” n’kupita kwa nthawi iwo sadzapezekaponso.​—Salimo 37:2, 20, 35, 36.

Salimo 37 limasiyanitsa zimene zimachitikira anthu amene amatsatira malamulo a Mulungu ndi amene samumvera. (Salimo 37:16, 17, 21, 22, 27, 28) Choncho salimoli limatithandiza kuti tikhale anzeru komanso anthu amene Mulungu amasangalala nawo.

MAY 13-19

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 38-39

Musamangokhalira Kudziimba Mlandu

w20.11 27 ¶12-13

Maso Ako Aziyang’ana pa Zinthu Zakutsogolo

12 Werengani 1 Yohane 3:19, 20. Nthawi zina tonsefe timadziimba mlandu. Mwachitsanzo, ena amadziimba mlandu chifukwa cha zinthu zimene ankachita asanaphunzire choonadi. Enanso amadziimba mlandu chifukwa cha zolakwa zimene anachita atabatizidwa. Ndipotu si zachilendo kumva choncho. (Aroma 3:23) N’zoona kuti timafuna kuchita zabwino, koma “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yak. 3:2; Aroma 7:21-23) Ngakhale kuti kudziimba mlandu sikosangalatsa, koma kumatithandiza m’njira zina. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa kudziimba mlandu n’kumene kungatithandize kuti tisinthe n’kutsimikiza mtima kuti tisadzabwerezenso zimene tinalakwitsazo.​—Aheb. 12:12, 13.

13 Komabe n’zotheka kumadziimba kwambiri mlandu. Zimenezi zikutanthauza kupitirizabe kudziimba mlandu ngakhale zitakhala kuti munthuyo analapa ndiponso Yehova anamukhululukira. Kudziimba mlandu kotereku kungakhale koopsa. (Sal. 31:10; 38:3, 4) N’chifukwa chiyani? Tiyeni tikambirane chitsanzo cha mlongo wina amene ankadziimbabe mlandu chifukwa cha machimo amene anachita m’mbuyo. Iye anati: “Ndikuona kuti palibe chifukwa chakuti ndizichitira khama potumikira Yehova, chifukwa olo nditadzipereka bwanji sindidzapulumuka.” N’kutheka kuti ambirife tingamamve ngati mmene mlongoyu ankamvera. Choncho tiyenera kusamala kuti tisamadziimbe mlandu mopitirira muyezo. Tikutero chifukwa Satana angasangalale kwambiri ngati titasiya kutumikira Yehova ngakhale kuti Yehovayo amatikondabe komanso anatikhululukira.​—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 2:5-7, 11.

w02 11/15 20 ¶1-2

Kodi Tingatani Kuti Masiku a Moyo Wathu Asangalatse Yehova?

MASIKU a moyo wathu amaoneka kuti ndi ochepa ndiponso amatha mofulumira. Wamasalmo Davide anasinkhasinkha kufupika kwa moyo wa munthu ndipo zimenezi zinamuchititsa kupemphera kuti: “Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa, ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati; ndidziwe malekezero anga. Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu.” Nkhawa ya Davide inali yoti akhale ndi moyo umene ungasangalatse Mulungu, mwa zolankhula ndiponso zochita zake. Polankhula za kudalira kwake Mulungu, iye anati: “Chiyembekezo changa chili pa Inu.” (Salmo 39:4, 5, 7) Yehova anamumvera. Anaonadi zimene Davide anachita ndipo anam’patsa mphoto malinga ndi zochita zakezo.

N’zosavuta kukhala wotanganidwa nthawi zonse ndi kukhala ndi moyo wodzala ndi zochita. Zimenezi zingatiyambitse nkhawa, makamaka chifukwa chokhala ndi zochita zambiri pamene nthawi yoti tichite zimenezo ndi yochepa kwambiri. Kodi nkhawa yathu ili ngati ya Davide, yoti tikhale ndi moyo umene ungasangalatse Mulungu? Kunena zoona, Yehova amationa ndipo amatipenda mosamala tonsefe. Yobu, mwamuna amene ankaopa Mulungu anazindikira zaka pafupifupi 3,600 zapitazo kuti Yehova anaona njira zake zonse ndipo anawerenga moponda mwake monse. Yobu anafunsa kuti: “Pondizonda Iye ndidzam’yankha chiyani?” (Yobu 31:4-6, 14) Tingathe kuchita zoti masiku a moyo wathu asangalatse Mulungu ngati tiika zinthu zauzimu patsogolo, kumvera malamulo ake, ndi kugwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru. Tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane mbali zimenezi.

w21.10 15 ¶4

Kukonzanso Ubwenzi Wanu ndi Yehova

Muzilankhula ndi Yehova pafupipafupi. Atate wanu amadziwa kuti mukamangodziimba mlandu nthawi zonse, zingakhale zovuta kuti muzipemphera kwa iye. (Aroma 8:26) Komabe “Limbikirani kupemphera” ndipo muzimuuza Yehova kuti mukufunitsitsa kukhala nayenso pa ubwenzi. (Aroma 12:12) Andrej ananena kuti: “Ndinkadziimba mlandu kwambiri ndipo ndinkachita manyazi. Koma nthawi iliyonse imene ndapemphera, ndinkamva bwino komanso ndinkapeza mtendere wamumtima.” Ngati simukudziwa zomwe mungatchule popemphera, muziganizira mapemphero a Mfumu Davide amene anapemphera atalapa, opezeka mu Salimo 51 ndi 65.

Mfundo Zothandiza

w22.09 13 ¶16

16 Kudziletsa ndi kofunikanso kwambiri kuti tikhale munthu wodalirika. Khalidwe limeneli lingatithandize kuti tizikhala chete pamene tayesedwa kuti tiulule nkhani zinazake zachinsinsi. (Werengani Miyambo 10:19.) Nthawi zina kudziletsa kungakhale kovuta pamene tikugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti. Ngati sitingasamale, mosadziwa tingaulule nkhani zachinsinsi kwa anthu ambiri. Tikangotumiza uthenga pamalo ochezera a pa intaneti, sitingadziwe mmene anthu amene alandira uthengawo angaugwiritsire ntchito komanso sitingachitepo kathu pa mavuto amene angatsatirepo. Komanso kudziletsa kungatithandize kuti tikhale chete otsutsa akamatinyengerera kuti tiulule zinthu zimene zingaike pangozi moyo wa abale ndi alongo athu. Zimenezi zingachitike tikamafunsidwa mafunso ndi apolisi m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Tingatsatire mfundo yakuti ‘timange pakamwa pathu kuti patetezeke’ pazochitika ngati zimenezi komanso zina. (Sal. 39:1) Timafunika kukhala odalirika kaya tikuchita zinthu ndi anthu a m’banja lathu, anzathu, abale ndi alongo kapena wina aliyense. Ndipo kuti tikhale odalirika tiyenera kukhala odziletsa.

MAY 20-26

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 40-41

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuthandiza Ena?

w18.08 22 ¶16-18

Anthu Opatsa Amakhala Osangalala

16 Anthu amene amapereka zinthu kuchokera pansi pa mtima sakhala ndi cholinga choti adzapezepo kenakake. Yesu ankaganizira mfundo imeneyi pamene ananena kuti: “Ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu. Ukatero udzakhala wodala, chifukwa alibe choti adzabweze.” (Luka 14:13, 14) Wolemba Baibulo wina ananena kuti munthu wopatsa “adzadalitsidwa.” Winanso ananena kuti: “Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.” (Miy. 22:9; Sal. 41:1) Choncho, tiyenera kukhala opatsa chifukwa timasangalala tikamathandiza anthu.

17 Kodi pamene Paulo anagwira mawu a Yesu akuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira,” ankangonena za kupatsa anthu zinthu? Ayi. Ankatanthauzanso kupereka malangizo, kuthandiza anthu amene akuvutika komanso kuwalimbikitsa. (Mac. 20:31-35) Zolankhula komanso zochita za Paulo zimatithandiza kudziwa zimene tiyenera kuchita pa nkhani imeneyi. Tiyenera kukonda kwambiri anthu, kuwaganizira komanso kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu kuti tiwathandize.

18 Anthu ochita kafukufuku apezanso kuti anthu opatsa amakhala osangalala. Nkhani ina imanena kuti “anthu akathandiza anzawo amayamba kumva bwino kwambiri komanso kusangalala.” Ochita kafukufukuwo ananena kuti munthu akamathandiza ena “amaona kuti moyo wake uli ndi cholinga.” Zili choncho chifukwa chakuti tinalengedwa m’njira yoti tizisangalala tikamathandiza ena. Chifukwa cha zimenezi, akatswiri amalimbikitsa anthu kuti azidzipereka kugwira ntchito zothandiza ena n’cholinga choti azimva bwino komanso azikhala osangalala. Zimenezi n’zosadabwitsa kwa anthu amene amaona kuti Baibulo ndi mphatso imene Mlengi wathu Yehova anatipatsa.​—2 Tim. 3:16, 17.

w15 12/15 24 ¶7

Yehova Adzakuthandizani Pamene Mukudwala

7 Komabe tikadwala, Mulungu angatilimbikitse, kutipatsa nzeru komanso kutithandiza ngati mmene anachitira ndi atumiki ake akale. Mfumu Davide analemba kuti: “Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka. Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa. Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo.” (Sal. 41:1,2) Davide sankatanthauza kuti anthu amene amachita zinthu moganizira ovutika, sangafe. M’malomwake, ankangotanthauza kuti Mulungu amawathandiza anthu oterewa. Koma kodi amawathandiza bwanji? Davide anati, ‘Yehova adzawachirikiza pamene akudwala ndi kuwasamalira bwino kwambiri.’ (Sal. 41:3) Munthu amene amachita zinthu moganizira ovutika ayenera kudziwa kuti Mulungu amaona zabwino zimene amachitazo ndiponso kukhulupirika kwake. Komanso Mulungu amatithandiza chifukwa ndi amene anapanga thupi lathu m’njira yoti lizitha kuchira.

w17.09 12 ¶17

Tizitsanzira Yehova pa Nkhani ya Chifundo

17 Koma sikuti tizingochitira ena chifundo n’cholinga choti ifeyo tipezepo phindu. Cholinga chachikulu pochitira ena chifundo chizikhala kutsanzira Yehova Mulungu wathu wachifundo komanso kumulemekeza. (Miy. 14:31) Iye amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Ndiye tiyeni tonse tizichita zonse zimene tingathe pomutsanzira. Tikamachita zimenezi, tidzayamba kukondana kwambiri ndi abale ndi alongo athu komanso kugwirizana ndi anthu ena.​—Agal. 6:10; 1 Yoh. 4:16.

Mfundo Zothandiza

it-2 16

Yehova

Mfundo yaikulu ya nkhani zonse za m’Baibulo ndi yakuti Yehova ndi amene ali woyenera kulamulira. Zimenezi zimasonyeza bwino cholinga chachikulu chimene ali nacho, chomwe ndi kuyeretsedwa kwa dzina lake. Kuti dzina lake liyeretsedwe pakufunika kuti zonse zimene zimadetsa dzinali zichotsedwe. Koma koposa pamenepo, pakufunikanso kuti zolengedwa zonse zanzeru kaya kumwamba kapena padziko lapansi, zizilemekeza dzinali chifukwa ndi lopatulika. Zolengedwazi zikamachita zimenezi zimasonyeza kuti zikuzindikira komanso kulemekeza udindo wa Yehova monga wolamulira ndipo chifukwa chakuti zimamukonda, zimachita zimenezi ndi mtima wonse, zimafunitsitsa kumutumikira komanso zimasangalala kuchita zimene iye amafuna. Pemphero limene Davide anapereka pa Salimo 40:5-10 limafotokoza bwino za zimenezi komanso za kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova. (Onani mmene mtumwi anagwiritsira ntchito mfundo zina za musalimoli ponena za Khristu Yesu pa Ahe 10:5-10.)

MAY 27–JUNE 2

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 42-44

Muzigwiritsa Ntchito Mokwanira Malangizo Omwe Yehova Amatipatsa

w06 6/1 9 ¶4

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachiwiri cha Masalimo

42:4, 5, 11; 43:3-5. Ngati sitingathe kusonkhana limodzi ndi mpingo wachikristu kwa kanthawi chifukwa cha zinthu zina zimene sitingazisinthe, tingalimbikitsidwe tikakumbukira chimwemwe chimene tinkakhala nacho panthawi imene tinkasonkhana limodzi ndi mpingo. Ngakhale kuti poyamba zingakulitse ululu umene tingakhale nawo chifukwa cha kusungulumwa, zingatikumbutsenso kuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndipo tiyenera kuyembekezera iye kuti atithandize.

w12 1/15 15 ¶2

Zomwe Mungachite Kuti Muzipindula Ndiponso Kusangalala Mukamaphunzira Baibulo

1 KUPEMPHERA: Choyamba tiyenera kupemphera. (Sal 42:8) N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyenera kuona kuti kuphunzira Mawu a Mulungu ndi mbali ya kulambira kwathu. Choncho tiyenera kupempha Yehova kutithandiza kuti tikhale ndi maganizo oyenera ndiponso kuti atipatse mzimu wake woyera. (Luka 11:13) Barbara, yemwe wakhala akuchita umishonale kwa nthawi yaitali anati: “Ndimapemphera nthawi zonse ndisanayambe kuwerenga kapena kuphunzira Baibulo. Ndikatero, ndimamva kuti Yehova ali nane ndipo akusangalala ndi zimene ndikuchita.” Kupemphera tisanayambe kuphunzira kumathandiza kuti titseguke maganizo ndiponso mtima n’cholinga choti tipindule mokwanira ndi chakudya chauzimu cha mwanaalirenji chimene tikulandira.

w16.09 5 ¶11-12

Manja Anu ‘Asalefuke’

11 Mulungu amatipatsanso mphamvu pogwiritsa ntchito zimene timaphunzira pa misonkhano yampingo, yadera, yachigawo komanso masukulu osiyanasiyana. Zimene timaphunzirazi zimatithandiza kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Mulungu. Zimatithandizanso kukhala ndi zolinga zauzimu komanso kuti tizitha kukwaniritsa maudindo athu. (Sal. 119:32) Kodi nanunso mumayesetsa kuti muzipeza mphamvu kuchokera pa zimene timaphunzira?

12 Yehova anathandiza Aisiraeli kugonjetsa Aamaleki ndi Aitiyopiya komanso anapatsa mphamvu Nehemiya ndi anzake kuti amalize ntchito yawo. Iye angatithandizenso ifeyo kuti tizilalikirabe m’gawo lovuta ndiponso tisamafooke tikamatsutsidwa kapena tikakhala ndi nkhawa. (1 Pet. 5:10) Sitiyembekezera kuti Yehova azitichitira zozizwitsa. M’malomwake tiyenera kuchita khama pa zinthu monga kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kukonzekera ndi kupezeka pamisonkhano mlungu uliwonse. Tiziphunziranso Baibulo patokha, kuchita kulambira kwa pabanja ndiponso kupemphera nthawi zonse. Tisamalole chilichonse kutilepheretsa kuchita zinthu zimene Yehova amagwiritsa ntchito potilimbikitsa komanso kutipatsa mphamvu. Ngati mukuona kuti simukuchita bwino pambali zina zimene tatchulazi, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Mukatero, mzimu wa Mulungu ‘udzalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.’ (Afil. 2:13) Koma kodi tingatani kuti nafenso tizilimbitsa manja a Akhristu anzathu?

Mfundo Zothandiza

it-1 1242

Mmbulu

M’Baibulo, mmbulu umagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa. Pamene Yobu ankafotokoza mmene ankamvera chifukwa cha mavuto ake ananena kuti wakhala “mʼbale wake wa mimbulu.” (Yob 30:29) Ponena za mmene anthu a Mulungu anagonjetsedwera mochititsa manyazi, wolemba masalimo wina, mwina pofotokoza za malo omenyerapo nkhondo amene kunkabwera mimbulu n’kudzadya anthu omwe aphedwawo (yerekezerani ndi Sl 44:19), analemba modandaula kuti: “Inu mwatiphwanya kumalo amene mimbulu imakhala.” (Sl 68:23; 44:19) Ababulo atazungulira mzinda wa Yerusalemu mu 607 B.C.E., anthu mumzindawo anavutika ndi njala yaikulu zomwe zinachititsa kuti azimayi azichitira nkhanza kwambiri ana awo. N’chifukwa chake Yeremiya anasiyanitsa nkhanza zimene anthu a Mulungu ankachita ndi mmene mimbulu inkasamalirira ana ake.​—Mlr 4:3, 10.

JUNE 3-9

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 45-47

Nyimbo ya Ukwati wa Mfumu

w14 2/15 9-10 ¶8-9

Sangalalani Chifukwa cha Ukwati wa Mwanawankhosa

8 Werengani Salimo 45:13, 14a. Mkwatibwiyu wakonzekera ukwati wake ndipo akuoneka kuti “ali pa ulemerero waukulu.” Pa Chivumbulutso 21:2, mkwatibwiyu akumuyerekezera ndi mzinda wa Yerusalemu Watsopano, ndipo ‘wakongoletsedwera mwamuna wake.’ Mzinda wakumwamba umenewu uli ndi “ulemerero wa Mulungu” ndipo ukunyezimira “ngati mwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.” (Chiv. 21:10, 11) Buku la Chivumbulutso limafotokoza bwino ulemerero wa Yerusalemu Watsopanoyu. (Chiv. 21:18-21) M’pake kuti wamasalimo ananena kuti mkwatibwiyu “ali pa ulemerero waukulu.” Alidi pa ulemerero chifukwa ukwatiwu ukuchitikiranso kumwamba.

9 Mkwatibwiyu akumubweretsa kwa Mkwati, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. Mfumuyi yakhala ikumukonzekeretsa ‘pomusambitsa m’madzi a mawu a Mulungu.’ Choncho ndi “woyera ndi wopanda chilema.” (Aef. 5:26, 27) Zovala za mkwatibwiyu ziyeneranso kukhala zokongola zogwirizana ndi mwambo wa ukwati. Ndipo ndi mmene zililidi chifukwa “zovala zake ndi zagolide,” ndipo “adzamubweretsa kwa mfumu atavala chovala choluka.” Pa ukwati wa Mwanawankhosawu, mkwatibwi “waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.”​—Chiv. 19:8.

w22.05 17 ¶10-12

Zimene Zili M’buku la Chivumbulutso Zimakhudza Tsogolo Lanu

10 Kodi Yehova adzatani ndi kuukira kwankhanza kumeneku? Iye amatiuza kuti: “Mkwiyo wanga udzatulukira m’mphuno mwanga.” (Ezek. 38:18, 21-23) Pa Chivumbulutso 19 amafotokoza zimene zidzachitike pambuyo pake. Yehova adzatumiza Mwana wake kuti akateteze anthu ake komanso kugonjetsa adani awo. Yesu adzamenya nkhondoyi pamodzi ndi ‘magulu a nkhondo amene ali kumwamba,’ omwe ndi angelo okhulupirika komanso a 144,000. (Chiv. 17:14; 19:11-15) Kodi zotsatirapo za nkhondoyi zidzakhala zotani? Anthu komanso mabungwe omwe amatsutsa Yehova adzawonongedweratu.​—Werengani Chivumbulutso 19:19-21.

11 Tangoganizani mmene anthu okhulupirika padzikoli adzamvere akadzapulumuka pakuwonongedwa kwa adani a Mulungu. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri. Ngakhale kuti kumwamba kudzakhala chisangalalo Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, pali chinthu chinanso chomwe chidzachititse kuti chisangalalocho chiwonjezereke kwambiri. (Chiv. 19:1-3) Kudzakhala “ukwati wa Mwanawankhosa,” womwe udzakhala pachimake pa zochitika za m’buku la Chivumbulutso.​—Chiv. 19:6-9.

12 Kodi ukwatiwu udzachitika liti? A 144,000 onse adzakhala atapita kumwamba nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Komatu iyi siidzakhala nthawi ya ukwati wa Mwanawankhosa. (Werengani Chivumbulutso 21:1, 2.) Ukwatiwu udzachitika pambuyo poti nkhondo ya Aramagedo yamenyedwa ndipo adani onse a Mulungu awonongedwa.​—Sal. 45:3, 4, 13-17.

it-2 1169

Nkhondo

Pambuyo pa nkhondoyi, padzikoli padzakhala mtendere wochuluka kwa zaka 1,000. Salimo limene limanena kuti “[Yehova] akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi. Wathyola uta ndi kupindapinda mkondo. Ndipo wawotcha pamoto magaleta ankhondo,” linakwaniritsidwa koyamba pamene Mulungu anabweretsa mtendere m’dziko la Isiraeli powononga zida zankhondo za adani awo. Yesu akadzagonjetsa anthu amene amalimbikitsa nkhondo pa Aramagedo, padzikoli padzakhala mtendere wosatha. (Sl 46:8-10) Anthu omwe adzalandire moyo wosatha adzakhala amene ‘asula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, komanso amene asula mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo’ ndipo “sadzaphunziranso nkhondo.” “Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena zimenezi.”​—Yes 2:4; Mik 4:3, 4.

Mfundo Zothandiza

w17.04 11 ¶9

Kodi Ufumu wa Mulungu Ukadzabwera Udzachotsa Zinthu Ziti?

9 N’chiyani chidzalowe m’malo mwa mabungwewa? Kodi pali bungwe kapena gulu lililonse limene lidzakhalepo pambuyo pa Aramagedo? Baibulo limanena kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Pet. 3:13) Maboma amene alipowa ali ngati kumwamba kwakale pomwe anthu ake ali ngati dziko lakale ndipo zonsezi sizidzakhalaponso. Ndiyeno adzalowedwa m’malo ndi kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Mawu oti “kumwamba kwatsopano” akutanthauza boma lakumwamba ndipo “dziko lapansi latsopano” ndi anthu amene adzakhale padzikoli n’kumalamulidwa ndi boma limeneli. Mfumu ya Ufumu umenewu ndi Yesu Khristu ndipo Ufumuwu udzasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wadongosolo. (1 Akor. 14:33) Choncho anthu amene azidzalamuliridwa ndi Ufumuwu adzakhala gulu logwirizana. Komanso padzakhala anthu amene azidzayang’anira ntchito zosiyanasiyana. (Sal. 45:16) Azidzalandira malangizo kuchokera kwa Khristu ndi a 144,000. Kodi mukuganiza kuti zidzakhala bwanji mabungwe onsewa akadzachoka n’kungotsala gulu limodzi lopanda chinyengo komanso la anthu ogwirizana?

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

ijwbv 26

Salimo 46:10​—“Khalani Chete, Ndipo Dziwani Kuti Ine Ndine Mulungu”

“Gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu. Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu, ndidzakwezedwa padziko lapansi.”​—Salimo 46:10, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.”​—Salimo 46:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Salimo 46:10

Mulungu akulimbikitsa anthu onse kuti azimulambira komanso kuvomereza kuti iye ndi woyenera kulamulira dziko lonse lapansi. Munthu aliyense amene akufuna kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale ayenera kuvomereza mfundo yosatsutsika yakuti iye ali ndi mphamvu zolamulira.​—Chivumbulutso 4:11.

“Gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu.” M’Mabaibulo ena, mawu akuti “gonjerani” anawamasulira kuti “khalani chete.” Zimenezi zachititsa kuti anthu ena aziganiza kuti limeneli ndi lamulo lakuti azichita zinthu mwamantha kapena azikhala chete m’tchalitchi. Komabe, mawu a Chiheberi omwe anamasuliridwa kuti “gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu” ndi pempho lomwe Yehovaa

Mulungu akuuza anthu amitundu yonse kuti asiye kumutsutsa ndipo azindikire kuti ayenera kulambira iye yekha basi.

Pempho lofanana ndi limeneli limapezeka pa Salimo 2. Palembali, Mulungu akulonjeza kuti adzawononga anthu onse amene amamutsutsa. Koma anthu amene amazindikira kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira amamudalira kuti aziwatsogolera, aziwapatsa mphamvu komanso nzeru. Anthu oterewa akakhala pamavuto, amakhala osangalala komanso otetezeka chifukwa “amathawira kwa Iye.”​—Salimo 2:9-12.

“Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu, ndidzakwezedwa padziko lapansi.” M’mbuyomu, Yehova Mulungu ankakwezedwa akagwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu poteteza anthu ake. (Ekisodo 15:1-3) M’tsogolomu, Yehova adzakwezedwa kwambiri pamene aliyense padzikoli azidzagonjera ulamuliro wake komanso kumulambira.​—Salimo 86:9, 10; Yesaya 2:11.

Nkhani yonse ya pa Salimo 46:10

Buku lina limanena kuti Salimo 46 ndi “nyimbo yotamanda Mulungu chifukwa cha mphamvu zake populumutsa anthu ake.” Pamene anthu a Mulungu ankaimba Salimo 46, ankasonyeza kuti amadalira Yehova kuti ali ndi mphamvu zowateteza ndiponso kuwathandiza. (Salimo 46:1, 2) Mawu amenewa ankawakumbutsa kuti Yehova ankakhala nawo nthawi zonse.​—Salimo 46:7, 11.

Salimoli linalimbikitsa anthu a Mulungu kuti azikhulupirira kwambiri mphamvu zake zodabwitsa n’kumaona kuti ali ndi mphamvu zowateteza. (Salimo 46:8) Mfundo yake yaikulu ndi yakuti iye ali ndi mphamvu zothetseratu nkhondo. Ndipotu, m’mbuyomu Yehova anachitapo kale zimenezi pothetsa nkhondo komanso kuteteza anthu ake kwa adani awo. Komabe, Baibulo likulonjeza kuti posachedwapa, Mulungu adzasonyeza mphamvu zake zazikulu pothetsa nkhondo padziko lonse lapansi.​—Yesaya 2:4.

Kodi Yehova akupitiriza kuthandiza atumiki ake masiku ano? Inde. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti akhale olimba mtima n’kumadalira Yehova kuti aziwathandiza. (Aheberi 13:6) Mfundo za mu Salimo 46 zimatilimbikitsa kuti tizikhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zotiteteza. Zimatithandizanso kuona kuti Mulungu “ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu.”​—Salimo 46:1.

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

g 12/10 22-23

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Pamwambo winawake wopereka mphoto, anthu anadabwa kwambiri ataona akazi awiri omwe ndi akatswiri a zisudzo akupsompsonana mwachikondi. Kenako anthuwo anayamba kuwombera m’manja komanso kukuwa mosangalala. Anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha ankaona kuti zimenezi n’zonyaditsa koma anthu ena ankaona kuti anthuwo akungofuna kuchita zinthu zoti atchukirepo. Kwa masiku angapo zithunzi zosonyeza akatswiriwa akupsompsonana zinaonetsedwa maulendo ambirimbiri pa TV komanso anthu mamiliyoni ambiri anaziona pa Intaneti.

MONGA mmene nkhaniyi ikusonyezera, munthu wotchuka akanena poyera kuti amagonana ndi amuna kapena akazi anzake, imakhala nkhani yaikulu pa TV, m’mawailesi komanso m’manyuzipepala. Anthu ena amawatamanda anthu amenewa kuti ndi olimba mtima, pamene ena amaona kuti limeneli ndi khalidwe lochititsa manyazi. Kuwonjezera pa magulu awiriwa, pali anthu enanso ambiri amene amaona kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi nkhani ya makonda chabe. Mnyamata wina wazaka 21, dzina lake Daniel, anati: “Ndili kusukulu, ngakhale ana amene sachita nawo khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha, ankaona kuti ngati umadana ndi khalidwe limeneli ndiye kuti uli ndi mtima watsankho komanso woweruza ena.”

Maganizo a anthu pa nkhani za kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha amasiyanasiyana mogwirizana ndi nthawi komanso dera limene anthu akukhala. Koma Akhristu ‘satengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso.’ (Aefeso 4:14) Iwo amayesetsa kutsatira zimene Baibulo limanena.

Ndiye kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha? Ndipo ngati mumatsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya makhalidwe abwino, kodi mungawayankhe bwanji anthu amene anganene kuti ndinu watsankho, wokonda kuweruza ena, kapena mumadana ndi anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha? Taganizirani zimene mungayankhe mutafunsidwa mafunso otsatirawa.

Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani yogonana amuna kapena akazi okhaokha? Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu amafuna kuti kugonana kuzichitika pakati pa mwamuna ndi mkazi omwenso ndi okwatirana. (Genesis 1:27, 28; Levitiko 18:22; Miyambo 5:18, 19) Baibulo likamaletsa dama, limatanthauza kugonana kwa pakati pa mwamuna ndi mkazi amene sanakwatirane komanso kwa amuna kapena akazi okhaokha.​—Agalatiya 5:19-21.

Ngati wina atakufunsani kuti: “Kodi maganizo anu ndi otani pa nkhani yogonana amuna kapena akazi okhaokha?”

Mungayankhe kuti: “Si kuti ndimadana ndi anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo, koma ndimadana ndi khalidwe lawolo.”

Kumbukirani izi: Inuyo muli ndi ufulu wosankha kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo ndipo palibe angakuletseni kuchita zimenezo. (Yoswa 24:15) Musamachite manyazi kufotokoza maganizo anu.​—Salimo 119:46.

Akhristu ayenera kulemekeza anthu onse, ngakhale amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha. Si choncho? Inde ndi zoona. Baibulo limati: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.” (1 Petulo 2:17) Choncho, Akhristu sadana ndi anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha. Iwo amachitira zabwino anthu onse, kuphatikizapo anthu oterewa.​—Mateyu 7:12.

Ngati wina atakufunsani kuti: “Popeza mumaona kuti n’kulakwa kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kodi zimenezi sizingakuchititseni kuti muziwasala?”

Mungayankhe kuti: “Ayi. Ndimangodana ndi khalidwelo, osati anthuwo.”

Mwinanso mungawonjezere kuti: “Mwachitsanzo, ineyo sindisuta. Ndipo ndimadana kwambiri ndi fodya. Koma tiyerekezere kuti inuyo mumasuta ndipo mumaona kuti fodya ndi wabwino. Sindingadane nanu chifukwa chokhala ndi maganizo amenewo komanso ndikukhulupirira kuti inuyo simungadane nane chifukwa choona kuti fodya ndi woipa, si choncho? N’chimodzimodzinso pa nkhani ya anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha.”

Yesu ananena kuti tizikhala ololera. Kodi zimenezi si zikutanthauza kuti Akhristu ayenera kungowasiya anthu ena kuti azigonana amuna kapena akazi okhaokha ngati akufuna? Yesu sanalimbikitse otsatira ake kuti azingololera khalidwe lililonse. M’malomwake, iye anawaphunzitsa kuti “aliyense wokhulupirira iye” adzapulumuka. (Yohane 3:16) Kukhulupirira Yesu kumaphatikizapo kutsatira malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino. Lina mwa malamulowo ndi loletsa kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.​—Aroma 1:26, 27.

Ngati wina atanena kuti: “Anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha sangasinthe chifukwa ndi chibadwa chawo.”

Mungayankhe kuti: “Zoti kaya anthu ena amabadwa ndi chikhumbo chofuna kugona ndi amuna kapena akazi anzawo, Baibulo silinena. Komabe limavomereza kuti makhalidwe ena ndi ovuta kuwasiya. (2 Akorinto 10:4, 5) Kaya anthu ena amakhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo, mfundo ndi yakuti Baibulo limalimbikitsa Akhristu kupewa makhalidwe amenewa.

Mfundo yothandiza: M’malo molimbana ndi kufotokoza kuti n’chiyani chimachititsa kuti anthu ena azikhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo, tsindikani mfundo yakuti Baibulo limaletsa khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha. Mungayerekezere chonchi: “Ambiri amanena kuti anthu ena amene amachita zachiwawa amachita zimenezi chifukwa chakuti ndi mmene anabadwira ndipo ngakhale atayesetsa bwanji sangasinthe. (Miyambo 29:22) Kaya zimenezi ndi zoona kapena ayi, koma mwina mukudziwa kuti Baibulo limaletsa kupsa mtima. (Salimo 37:8; Aefeso 4:31) Koma kodi tinganene kuti Baibulo limalakwa kuletsa anthu kuchita zoipa monga chiwawa, popeza kuti anthu ena mwachibadwa sachedwa kupsa mtima?”

Kodi si nkhanza kuti Mulungu amuletse munthu amene mwachibadwa amafuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzake? Anthu amakhala ndi maganizo olakwika amenewa chifukwa chokhulupirira kuti anthu ayenera kumangotsatira chilichonse chimene mtima wawo wawauza pa nkhani ya kugonana. Koma Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anawalemekeza anthu powapatsa ufulu wosankha. Ngati atafuna, iwo akhoza kusankha kupewa kutsatira zilakolako zawo zolakwika zokhudza kugonana.​—Akolose 3:5.

Ngati wina atanena kuti: “Ngakhale kuti simugona ndi amuna kapena akazi anzanu, ndikuona kuti muyenera kusintha mmene mumaonera anthu oterewa.”

Mungayankhe kuti: “Tiyerekeze kuti ineyo ndimadana ndi juga koma inuyo mumaona kuti juga ndi yabwino. Kodi inuyo mungandikakamize kusintha maganizo anga chifukwa chakuti anthu ambirimbiri amakonda juga?”

Kumbukirani izi: Anthu ambiri (kuphatikizapo ogonana amuna kapena akazi okhaokha) amakhala ndi mfundo zabwino zimene amayendera. Mwachitsanzo amadana ndi zinthu monga chinyengo, kupanda chilungamo komanso nkhondo. Baibulo nalonso limaletsa zinthu zimenezi, kuphatikizapo mitundu ina ya kugonana monga kugonana amuna kapena akazi okhaokha.​—1 Akorinto 6:9-11.

Zimene Baibulo limanena n’zoti anthu angakwanitse kuzitsatira komanso Baibulo sililimbikitsa tsankho. Limangouza anthu onse kuti “thawani dama,” kaya akhale amene amafuna kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kapenanso amuna ndi akazi amene amafuna kugonana asanakwatirane.​—1 Akorinto 6:18.

Zoona zake n’zakuti anthu amene amakhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna anzawo kapena akazi anzawo akhoza kudziletsa ngati akufunadi kukondweretsa Mulungu. Tikutero chifukwa pali anthu ambirimbiri amene amakhala ndi chilakolako chogonana ndi amuna kapena akazi koma amayesetsa kupewa dama chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Ena mwa anthu amenewa ndi osakwatira ndipo akusowa munthu womanga naye banja ndipo enanso ambiri ali m’banja koma mnzawoyo ali ndi vuto. Anthu amenewa amatha kukhala mosangalala, ngakhale kuti pali mavuto amenewa.​—Deuteronomo 30:19.

JUNE 10-16

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 48-50

Makolo, Muzithandiza Banja Lanu Kudalira Kwambiri Gulu la Yehova

w22.03 22 ¶11

Kulambira Koona Kumachititsa Kuti Muzisangalala Kwambiri

11 Timalambira Yehova tikamaphunzira Mawu ake komanso kuphunzitsa ana athu zokhudza iye. Pa tsiku la Sabata, Aisiraeli sankagwira ntchito zawo za tsiku ndi tsiku ndipo zimenezi zinkawapatsa mwayi woganizira za ubwenzi wawo ndi Yehova. (Eks. 31:16, 17) Aisiraeli okhulupirika ankaphunzitsa ana awo zokhudza Yehova komanso ubwino wake. Ifeyo patokha timafunika kukonza nthawi yowerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu. Imeneyi ndi mbali ya kulambira kwathu ndipo imatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Sal. 73:28) Ndipo tikamaphunzira limodzi monga banja, tingathandize ana athu kuti akhale pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wachikondi.​—Werengani Salimo 48:13.

w11 3/15 19 ¶5-7

Zinthu Zimene Mungakondwere Nazo

“Gubani mozungulira Ziyoni, anthu inu, ndipo yendayendani mmenemo, werengani nsanja zake. Ganizirani mofatsa za khoma lake lolimba. Yenderani nsanja zake zokhalamo, kuti mudzasimbire m’badwo wam’tsogolo.” (Sal. 48:12, 13) Pamenepa, wamasalimo analimbikitsa Aisiraeli kuti azikaona mzinda wa Yerusalemu. Kodi mukuganiza kuti mabanja achiisiraeli amene anapita kumzinda wopatulikawo kukachita nawo zikondwerero za pachaka ndiponso kuona kachisi wokongola kwambiri ankamva bwanji akabwerera kwawo? Iwo ayenera kuti ankalimbikitsidwa ‘kusimbira m’badwo wam’tsogolo’ zimene anaonazo.

Taganizirani za mfumukazi ya ku Sheba imene poyamba inkakayikira zimene inamva zokhudza ulamuliro wapamwamba wa Solomo ndiponso nzeru zake zodabwitsa. Kodi n’chiyani chinathandiza mfumukaziyi kukhulupirira zimene inamvazo? Mfumukaziyi inati: “Sindinakhulupirire mawuwo mpaka pamene ndabwera n’kuona ndi maso anga.” (2 Mbiri 9:6) N’zoona kuti zimene timaona ndi ‘maso athu’ zimatikhudza kwambiri.

Kodi mungathandize bwanji ana anu kuona ndi ‘maso awo’ zinthu zochititsa chidwi m’gulu la Yehova? Ngati pali ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova pafupi ndi kwanu, mungachite bwino kukaiona. Mwachitsanzo, Mandy ndi Bethany ndi atsikana amene anakulira m’dera lomwe lili pa mtunda wa makilomita 1,500 kuchokera ku Beteli ya m’dziko lawo. Koma makolo awo ankakonza zoti azikaona malowo makamaka pamene anawa ankakula. Atsikanawo anati: “Tisanapite ku Beteli tinkaganiza kuti ndi malo osasangalatsa a anthu okalamba okhaokha. Koma tinakumana ndi achinyamata amene ankatumikira Yehova mwakhama ndiponso mosangalala. Tinaona kuti gulu la Yehova silinkangopezeka m’dera lathu lokha ndipo ulendo uliwonse umene tinkapita ku Beteli tinkalimbikitsidwa kwambiri mwauzimu.” Mandy ndi Bethany ataona bwinobwino gulu la Mulungu analimbikitsidwa kuchita upainiya ndipo kenako anaitanidwa kukatumikira ku Beteli kwa kanthawi.

w12 8/15 12 ¶5

Muzichita Zinthu Monga Nzika za Ufumu

5 Ayenera kuphunzira mbiri ya dzikolo. Munthu amene akufuna kukhala nzika ya dziko linalake angafunike kudziwa zinthu zina zokhudza mbiri ya dzikolo. Nawonso anthu ofuna kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu ayenera kuphunzira zambiri zokhudza mbiri yake. Ana a Kora, amene ankatumikira mu Isiraeli, anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iwo ankakonda kwambiri mzinda wa Yerusalemu ndi malo ake olambirira ndipo ankakonda kuuza ena mbiri ya mzindawu. Chimene chinkawachititsa chidwi si kukongola kwa mzindawu koma zimene mzindawo komanso malo ake olambirira zinkaimira. Yerusalemu anali “mudzi wa Mfumu Yaikulu” chifukwa chakuti anthu ankalambira Yehova ndiponso kuphunzira Chilamulo chake kumeneko. Komanso Yehova ankakomera mtima anthu olamulidwa ndi Mfumu ya ku Yerusalemu. (Werengani Salimo 48:1, 2, 9, 12, 13.) Kodi nanunso mumakonda kuphunzira ndiponso kuuza ena mbiri ya anthu a Yehova? Mudzayamba kuyamikira kwambiri Ufumu wa Mulungu mukamaphunzira zambiri zokhudza anthu a Mulungu ndiponso mmene Yehova amawathandizira. Izi zidzakuthandizani kukhala ndi mtima wofuna kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.​—Yer. 9:24; Luka 4:43.

Mfundo Zothandiza

it-2 805

Chuma

Chifukwa chakuti Aisiraeli anali mtundu wolemera, ankasangalala ndi zakudya komanso zakumwa (1Mf 4:20; Mla 5:18, 19), ndipo chumacho chinkawateteza kuti asakhale osauka. (Miy 10:15; Mla 7:12) Komabe, ngakhale kuti chinali cholinga cha Mulungu kuti Aisiraeli azikhala ndi chuma akagwira ntchito mwakhama (yerekezerani ndi Miy 6:6-11; 20:13; 24:33, 34), Mulunguyo anawachenjeza kuti asamadalire kwambiri chuma n’kuiwala kuti iye ndi amene anawapatsa chumacho. (De 8:7-17; Sl 49:6-9; Miy 11:4; 18:10, 11; Yer 9:23, 24) Anakumbutsidwa kuti chuma sichikhalitsa (Miy 23:4, 5), sichingaperekedwe ngati nsembe kuti wina apulumutsidwe (Sl 49:6, 7)komanso sichithandiza anthu akufa (Sl 49:16, 17; Mla 5:15). Iwo anauzidwa kuti kukonda kwambiri chuma kungapangitse kuti munthu ayambe kuchita zachinyengo ndipo Yehova angasiye kumukonda. (Miy 28:20; yerekezerani ndi Yer 5:26-28; 17:9-11.) Anawalimbikitsanso kuti “uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.”​—Miy 3:9.

JUNE 17-23

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 51-53

Kodi Mungatani Kuti Mupewe Kuchita Machimo Akuluakulu?

w19.01 15 ¶4-5

Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?

4 Pa Miyambo 4:23, mawu akuti “mtima” akutanthauza “munthu wamkati” kapena kuti “munthu wobisika.” (Werengani Salimo 51:6.) Choncho tinganene kuti mawu akuti “mtima” amanena za maganizo athu, mmene tikumvera mumtima, zolinga zathu komanso zimene timalakalaka. Tingati ndi mmene tilili mkati mwathu osati mmene timaonekera kwa anthu ena.

5 Kuti timvetse za munthu wathu wamkati, tiyeni tikambirane za thupi lathu lenileni. Choyamba, kuti tikhale athanzi timafunika kudya chakudya chabwino komanso kuchita masewera olimbitsa thupi. N’chimodzimodzinso ndi munthu wathu wamkati. Kuti tikhale athanzi timafunika chakudya chauzimu komanso kuchita zinthu zosonyeza kuti timakhulupirira Yehova. Mwachitsanzo, tiyenera kutsatira zimene timaphunzira komanso kuuza anthu ena zimene timakhulupirira. (Aroma 10:8-10; Yak. 2:26) Chachiwiri, munthu akhoza kuoneka kuti ndi wathanzi koma mkati mwa thupi lake ali ndi matenda. Mofanana ndi zimenezi, tingaganize kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa choti timachita zinthu zokhudza kulambira koma mumtima mwathu titayamba kulakalaka zinthu zoipa. (1 Akor. 10:12; Yak. 1:14, 15) Tiyenera kukumbukira kuti Satana amafuna kutisokoneza kuti tiziyendera maganizo ake. Kodi iye angachite bwanji zimenezi? Nanga tingadziteteze bwanji?

w15 6/15 14 ¶5-6

N’zotheka Kukhalabe Oyera

5 Tingasonyeze kuti timadalira Yehova tikamamupempha kuti azitithandiza kupewa maganizo oipa. Tikamayandikira Mulungu popemphera iye amatiyandikiranso. Amatipatsa mzimu wake woyera kuti utithandize kukhalabe oyera n’kumapewa maganizo oipa. Choncho tizipempha Mulungu kuti azitithandiza kuganizira zinthu zomusangalatsa. (Sal. 19:14) Tiyenera kumupempha modzichepetsa kuti atithandize kuzindikira maganizo alionse amene angatichititse kuchimwa. (Sal. 139:23, 24) Tizimupempha nthawi zonse kuti azitithandiza kukhalabe okhulupirika tikakumana ndi mayesero.​—Mat. 6:13.

6 Mwina tisanaphunzire za Yehova tinkakonda kuchita zinthu zimene iye amadana nazo ndipo n’kutheka kuti zimabwerabe m’maganizo mwathu. Ngakhale zili choncho, Yehova angatithandize kukhalabe oyera. Davide ankadziwa bwino zimenezi. Iye atachita chigololo ndi Bati-seba, anapempha Yehova kuti: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” (Sal. 51:10, 12) N’zoona kuti tingalakelake zinthu zoipa ndipo zingativute kusiya maganizo oipawo. Koma Yehova akhoza kutitsogolerabe kuti tizimvera malamulo ake. Iye akhoza kutithandiza kuti tisamalamuliridwe ndi maganizo oipa.​—Sal. 119:133.

Mfundo Zothandiza

it-1 644

Doegi

Munthu wa ku Edomu yemwe anali ndi udindo woyang’anira ena chifukwa anali mkulu wa abusa a Mfumu Sauli. (1Sa 21:7; 22:9) Zikuoneka kuti Doegi analowa Chiyuda. “Chifukwa anali atamusunga pamaso pa Yehova” ku Nobu, mwina pa chifukwa chakuti anachita lumbiro linalake, anali wodetsedwa kapenanso ankamuganizira kuti anali ndi khate, iye anaona mkulu wa ansembe Ahimeleki akupatsa Davide mkate wachionetsero komanso lupanga la Goliyati. Kenako, Sauli atadzudzula atumiki ake kuti ankamukonzera chiwembu, Doegi anaulula zimene anaona ku Nobu. Sauli anaitanitsa mkulu wa ansembe komanso ansembe ena a ku Nobu ndipo anafunsa mafunso Ahimeleki, kenako Sauli anauza asilikali othamanga kuti aphe ansembewo. Asilikaliwo atakana, mosazengereza Doegi anapha ansembe 85 Sauli atamulamula. Pambuyo pochita zinthu zoipa zimenezi Doegi anawononga mzinda wa Nobu ndipo anapha anthu onse a mumzinda, ana ndi akulu omwe kuphatikizapo ziweto.​—1Sa 22:6-20.

Mawu a pa kamutu pa Salimo 52 amasonyeza kuti Davide analemba izi zokhudza Doegi: “Lilime lako limene ndi lakuthwa ngati lezala, limakonza chiwembu komanso kuchita zachinyengo. Umakonda kwambiri zinthu zoipa kuposa zabwino, umakonda kwambiri kunama kuposa kulankhula zoona. Umakonda mawu onse opweteka ena, iwe amene lilime lako limalankhula zachinyengo.”​—Sl 52:2-4.

JUNE 24-30

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 54-56

Mulungu Ali Kumbali Yanu

w06 8/1 22 ¶10-11

Khalani Anzeru mwa Kuopa Mulungu

10 Panthawi ina, Davide anapita kwa Akisi, mfumu ya mzinda wa Afilisti wa Gati, kwawo kwa Goliati. (1 Samueli 21:10-15) Atumiki a mfumuyo ananena kuti Davide ndi mdani wa mtundu wawo. Kodi Davide anatani zinthu zitafika poopsa chonchi? Iye anapemphera kwa Yehova mwamtima wonse. (Salmo 56:1-4, 11-13) Ngakhale kuti anachita kufika ponamizira misala, Davide ankadziwa kuti kwenikweni Yehova ndiye anamuwombola podalitsa nzeru imeneyi. Davide anadalira Yehova ndi mtima wonse, kusonyeza kuti analidi munthu woopa Mulungu.​—Salmo 34:4-6, 9-11.

11 Monga Davide, ifenso tingasonyeze kuti timaopa Mulungu podalira lonjezo lake lakuti atithandiza kuthana ndi mavuto athu. Davide anati: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.” (Salmo 37:5) Zimenezi sizikutanthauza kuti mavuto athuwo timangomusiyira Yehova kuti iyeyo ndiye athane nawo ifeyo n’kungopinda manja basi, osachitapo chilichonse. Davide sanangopemphera kuti Mulungu amuthandize n’kulekera pomwepo basi. Koma anagwiritsa ntchito mphamvu ndiponso nzeru zimene Yehova anam’patsa n’kuthana ndi vuto lakelo. Komatu Davide ankadziwa kuti zochita za munthu payekha sizingakhale zodalirika. Ifenso tizidziwa zimenezi. Tikachita mbali yathu ndi mphamvu zathu zonse, tiyenera kusiya zonse m’manja mwa Yehova. Kwenikweni, nthawi zambiri sipakhala chilichonse choti tingachite kupatulapo kudalira Yehova basi. Imeneyi ndiyo nthawi yoti ifeyo patokha tionetse kuti timaopadi Mulungu. Tingalimbikitsidwe ndi mawu amene Davide ananena mochoka pansi pa mtima akuti: “Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye.”​—Salmo 25:14.

cl 243 ¶9

Palibe Chikhoza “Kutisiyanitsa Ife ndi Chikondi cha Mulungu”

9 Yehova amayamikiranso kupirira kwathu. (Mateyu 24:13) Kumbukirani kuti Satana amafuna mutam’kana Yehova. Tsiku lililonse limene mumakhulupirikabe kwa Yehova mumathandiza kuyankha zotonza za Satana. (Miyambo 27:11) Nthaŵi zina kupirira kumakhala kovuta zedi. Matenda, mavuto azachuma, kuvutika maganizo, ndiponso mavuto ena zingakhale ziyeso za tsiku ndi tsiku. Tingagwenso mphwayi chifukwa chakuti zimene tikuyembekezera zikuchedwa kuchitika. (Miyambo 13:12) Kupirira pamene tikumana ndi mavuto oterowo n’kwamtengo wapatali kwambiri kwa Yehova. Ndicho chifukwa chake Mfumu Davide anapempha Yehova kuti amusungire misozi yake “m’nsupa.” Mwachidaliro anawonjezera kuti: “Kodi siikhala m’buku mwanu?” (Salmo 56:8) Inde, Yehova amasunga ndiponso amakumbukira misozi yonse ndi kuvutika konse kumene timapirira nako pokhalabe okhulupirika kwa iye. Misoziyo limodzi ndi kuvutikako ndi zamtengo wapatali m’maso mwake.

Mfundo Zothandiza

it-1 857-858

Kudziwiratu Zam’tsogolo

Zomwe Yudasi Isikariyoti anachita popereka Yesu zinakwaniritsa ulosi komanso zinasonyeza kuti Yehova ndi Mwana wake amadziwiratu zam’tsogolo. (Sl 41:9; 55:12, 13; 109:8; Mac 1:16-20) Komabe sitinganene kuti Mulungu anakonzeratu zoti Yudasi ndi amene adzachite zimenezi. Maulosi ananena kuti mnzake wina wapamtima wa Yesu ndi amene adzamupereke komabe sananeneretu kuti mnzakeyo adzakhala ndani. Ndiponso kunena kuti Mulungu anakonzeratu kuti Yudasi ndi amene adzachite zimenezi n’kosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mtumwi Paulo anafotokoza mfundo ina imene Mulungu anakhazikitsa yakuti: “Usafulumire kuika munthu aliyense pa udindo, kapena kugawana ndi anthu ena machimo awo. Pitiriza kukhala ndi khalidwe loyera.” (1Ti 5:22; yerekezerani ndi 3:6.) Pofuna kusonyeza kuti anachita zinthu mwanzeru komanso mosamala posankha atumwi ake 12, Yesu anapemphera kwa Atate wake usiku wonse asanasankhe atumwiwo. (Lu 6:12-16) Mulungu akanakonzeratu kuti Yudasi adzapereka Yesu, zikanasonyeza kuti Mulungu amachita zosiyana ndi zimene amauza ena kuti azichita ndipo mogwirizana ndi lamulo iyenso akanagawana nawo machimo a Yudasiyo.

Choncho zikuoneka kuti n’zomveka kunena kuti pa nthawi yomwe ankamusankha kukhala mtumwi, Yudasi analibe mtima woti adzapereka Yesu. Iye analola kuti ‘muzu wapoizoni utuluke’ n’kumuipitsa, zomwe zinachititsa kuti apatuke n’kulola kutsogoleredwa ndi Mdyerekezi kuti ayambe kuba komanso kuchita zachinyengo, m’malo moti Mulungu azimutsogolera. (Ahe 12:14, 15; Yoh 13:2; Mac 1:24, 25; Yak 1:14, 15.) Maganizo oterewa atayamba kukula, Yesu anayamba kudziwa zamumtima mwa Yudasi ndipo ananeneratu kuti adzamupereka.​—Yoh 13:10, 11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena