Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr24 July tsamba 1-16
  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2024
  • Timitu
  • JULY 1-7
  • JULY 8-14
  • JULY 15-21
  • JULY 22-28
  • JULY 29–AUGUST 4
  • AUGUST 5-11
  • AUGUST 12-18
  • AUGUST 19-25
  • AUGUST 26–SEPTEMBER 1
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2024
mwbr24 July tsamba 1-16

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu

JULY 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 57-59

Yehova Amasokoneza Anthu Amene Amatsutsa Atumiki Ake

bt 220-221 ¶14-15

“Mpaka Kumalekezero a Dziko Lapansi”

14 Sitefano analalikira molimba mtima asanaphedwe ndi adani ake. (Mac. 6:5; 7:54-60) Akhristu atayamba “kuzunzidwa koopsa” ophunzira onse kupatulapo atumwi, anabalalikira m’zigawo zonse za Yudeya ndi Samariya. Koma zimenezi sizinaimitse ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, Filipo anapita ku Samariya “n’kuyamba kulalikira za Khristu” ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwambiri. (Mac. 8:1-8, 14, 15, 25) Komanso Baibulo limatiuza kuti: “Anthu amene anabalalika chifukwa cha mavuto amene anayamba chifukwa cha zimene zinachitikira Sitefano, anakafika mpaka ku Foinike, ku Kupuro ndi ku Antiokeya. Ndipo ankangolalikira kwa Ayuda okha. Koma ena mwa anthuwa anali a ku Kupuro ndi ku Kurene. Iwowa atafika ku Antiokeya anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ambuye Yesu kwa anthu olankhula Chigiriki.” (Mac. 11:19, 20) Pa nthawiyo, kuzunzidwa kwa Akhristu kunachititsa kuti uthenga wa Ufumu ufalikire.

15 M’nthawi yathu ino, zinthu ngati zimenezi zinachitikanso m’mayiko amene kale ankadziwika kuti Soviet Union. Anthu ambirimbiri a Mboni za Yehova anawathamangitsira ku Siberia, makamaka m’zaka za m’ma 1950. Chifukwa cha kuthamangitsidwako, a Mboni za Yehova ambiri anakakhala kumadera akutali kwambiri ndi kwawo ndipo anamwazikana m’midzi yosiyanasiyana m’dziko lonselo. Zimenezi zinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikire m’dziko la Siberia, lomwe ndi lalikulu kwambiri. Choncho a Mboni za Yehova ambiri anakwanitsa kulalikira uthenga wabwino kumadera akutali kwambiri, mpaka mtunda wokwana makilomita 10,000 kuchokera kwawo. Iwo sakanakwanitsa kupeza ndalama zokafikira kumadera amenewa kuti akalalikire. Koma izi zinatheka chifukwa boma linawatumiza lokha kumeneko. M’bale wina anati: “Zimene akuluakulu a boma anachitazi zinathandiza kuti anthu ambirimbiri oona mtima a ku Siberia adziwe choonadi.”

Mfundo Zothandiza

w23.07 18-19 ¶16-17

“Khalani Olimba, Osasunthika”

16 Muziyesetsa kukhala ndi mtima wokhazikika. Davide anasonyeza kuti sankafuna kusiya kukonda Yehova pomwe anaimba kuti: “Mtima wanga wakhazikika, inu Mulungu.” (Sal. 57:7) Ifenso tingakhale ndi mtima wokhazikika, kapena kuti wosasunthika, n’kumakhulupirira kwambiri Yehova. (Werengani Salimo 112:7.) Taganizirani mmene zimenezi zinathandizira Bob yemwe tamutchula kale uja. Atauzidwa kuti padzasungidwa magazi oti amuike ngati patafunika kutero, nthawi yomweyo anayankha kuti ngati madokotalawo akuona kuti angadzamuike magazi, iye achoka kuchipatalako. Pambuyo pake Bob anadzafotokoza kuti: “Ndinali wotsimikiza mtima ndipo sindinkadanso nkhawa.”

17 Bob sanasunthike chifukwa anali atasankhiratu zimene angachite asanapite kuchipatalako. Choyamba, iye ankafuna kusangalatsa Yehova. Chachiwiri, anali ataphunzira mosamala zimene Baibulo ndi mabuku athu amanena pa nkhani yokhudza kupatulika kwa moyo ndi magazi. Ndipo chachitatu, iye sankakayikira kuti kutsatira malangizo a Yehova kukanachititsa kuti apeze madalitso osatha. Ifenso tingathe kukhala osasunthika kaya tikumane ndi mayesero otani.

JULY 8-14

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 60-62

Yehova Amatiteteza

it-2 1118 ¶7

Nsanja

Mawu Ophiphiritsa. Anthu amene amakhulupirira komanso kumvera Yehova ndi otetezeka kwambiri, monga mmene Davide anaimbira kuti: “Inu [Yehova] ndinu malo anga othawirako, nsanja yolimba imene imanditeteza kwa mdani.” (Sl 61:3) Anthu amene amazindikira tanthauzo la dzina lake, kumudalira ndiponso kusonyeza mokhulupirika kuti ali ku mbali yake palibe chimene amaopa, chifukwa: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.”​—Miy 18:10; yerekezerani ndi 1Sa 17:45-47.

it-2 1084 ¶8

Tenti

M’zochitika zosiyanasiyana, mawu akuti “tenti” amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsira. Tenti imene munthu anali nayo, inkamuteteza ku zinthu zosiyanasiyana komanso ankakhalamo akafuna kupuma. (Ge 18:1) Potengera chikhalidwe cha nthawi imeneyo pa nkhani yokhudza kuchereza, mlendo ankadzimva kuti walandiridwa komanso walemekezedwa akauzidwa kuti alowe mu tenti ya munthu amene wamupezayo. Choncho, pamene lemba la Chivumbulutso 7:15 limanena za a khamu lalikulu kuti Mulungu “adzawaphimba ndi tenti yake,” limatanthauza kuti adzawateteza komanso kuwasamalira. (Sl 61:3, 4) Yesaya ananena zimene Ziyoni, yemwe ndi mkazi wa Mulungu, adzachite pokonzekera ana amene adzabereke. Mkaziyo anauzidwa kuti “kulitsa tenti yako.” (Yes 54:2) Kutanthauza kuti akulitse malo otetezera ana ake.

w02 4/15 16 ¶14

Malamulo a Mulungu Amatipindulitsa

14 Chilamulo cha Mulungu n’chosasinthika. M’nthawi zovuta zimene tikukhala zino, Yehova ndiye mwala wosasunthika, amene alipo kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. (Salimo 90:2) Anadzinena yekha kuti: “Ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:6) Miyezo ya Mulungu imene ili m’Baibulo ndi yodalirika kwambiri osati monga malangizo a anthu amene amasinthasintha. (Yakobo 1:17) Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri akatswiri a zamaganizo ankalimbikitsa kuti anthu azilera ana mowalekerera, koma kenako akatswiri ena anasintha maganizo awo n’kuvomereza kuti malangizowo anali olakwika. Miyezo ndi malangizo a anthu m’dzikoli pankhani imeneyi amapita uku ndi uku ngati kuti akuwombedwa ndi mphepo. Koma, Mawu a Yehova sasintha. Kwa zaka zambirimbiri, Baibulo lapereka malangizo a mmene makolo angalerere ana mwachikondi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) N’zosangalatsa kudziwa kuti tingadalire miyezo ya Yehova; siidzasintha!

Mfundo Zothandiza

w06 6/1 11 ¶8

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachiwiri cha Masalimo

62:11. Mulungu sadalira mphamvu zochokera kwina kwake. Iye mwini ndi gwero la mphamvu. ‘Mphamvu ndi yake ya iye.’

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w22.02 4-5 ¶7-10

Kodi Mumakhulupirira Kuti Yehova Amachita Zinthu M’njira Yoyenera?

7 Timakhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene Yehova amachita nthawi zonse zimakhala zoyenera. Komabe mwina tingamavutike kukhulupirira anthu amene iye akuwagwiritsa ntchito. Tingamakayikire ngati anthu amene ali ndi udindo m’gulu la Yehova akuchita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yehovayo kapena maganizo awo. N’kutheka kuti anthu enanso akale ankaganiza choncho. Taganizirani zitsanzo zomwe zatchulidwa mundime 3. Mwina wachibale wa munthu yemwe anaphwanya lamulo la Sabata ankakayikira ngati Mose anafunsa kaye Yehova asanaweruze kuti munthuyo aphedwe. Ndipo mnzake wa Uriya Mhiti, yemwe mkazi wake anachita chigololo ndi Davide akanaona kuti Davide anagwiritsa ntchito udindo wake monga mfumu pothawa chilango chomwe ankayenera kupatsidwa. Mfundo yosatsutsika ndi yakuti sitinganene kuti timakhulupirira Yehova pamene sitikhulupirira anthu omwe iye amawakhulupirira ndipo amawagwiritsa ntchito.

8 Masiku ano Yehova amatsogolera mbali yapadziko lapansi ya gulu lake pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Mofanana ndi bungwe lolamulira la munthawi ya atumwi, kapoloyu amatsogolera anthu a Mulungu padziko lonse ndipo amapereka malangizo kwa akulu. (Werengani Machitidwe 16:4, 5.) Akulu nawonso amagwiritsa ntchito malangizowo m’mipingo. Timasonyeza kuti timakhulupirira mmene Yehova amachitira zinthu potsatira malangizo ochokera kugulu lake komanso kwa akulu.

9 Nthawi zina zingativute kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene akulu asankha. Mwachitsanzo, m’zaka zaposachedwapa mipingo ndi madera ambiri zakonzedwanso. Nthawi zina, akulu amapempha ofalitsa ena kuti asamukire kumipingo ina n’cholinga choti mipando m’Nyumba ya Ufumu izigwiritsidwa ntchito mokwanira. Ngati atatipempha kusamukira mumpingo wina, mwina tingaone kuti n’zovuta kusiyana ndi anzathu komanso achibale. Kodi akulu amauzidwa mwanjira inayake ndi Mulungu kuti asamutsire ofalitsa mumpingo winawake? Ayi. Choncho izi zingachititse kuti zizitivuta kuti titsatire malangizo omwe tapatsidwa. Koma Yehova amakhulupirira kuti akulu asankha bwino pa nkhani zimenezi ndipo ifenso tiyenera kuwakhulupirira.

10 N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene akulu asankha, ngakhale kuti zimene asankhazo si zimene tikanakonda? Chifukwa tikamachita zimenezi, timathandiza kuti anthu a Mulungu apitirize kukhala ogwirizana. (Aef. 4:2, 3) Zinthu zimayenda bwino mumpingo, anthu onse akamatsatira modzichepetsa zimene bungwe la akulu lasankha. (Werengani Aheberi 13:17.) Koma chofunika kwambiri n’chakuti timamusonyeza Yehova kuti timamukhulupirira tikamachita zinthu mogwirizana ndi anthu omwe wawapatsa udindo wotisamalira.​—Mac. 20:28.

JULY 15-21

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 63-65

“Chikondi Chanu Chokhulupirika N’chabwino Kuposa Moyo”

w01 10/15 15-16 ¶17-18

Ndani Adzatisiyanitsa ndi Chikondi cha Mulungu?

17 Kodi chikondi cha Mulungu n’chofunika motani kwa inu? Kodi mumaganiza mmene anachitira Davide amene analemba kuti: “Pakuti chifundo [“kukoma mtima,” NW] chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani. Potero ndidzakuyamikani m’moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m’dzina lanu.” (Salimo 63:3, 4) Ndithudi, kodi pali china chilichonse chimene moyo m’dziko lapansi lino ungatipatse chomwe n’chabwino kuposa kuti Mulungu atikonde ndi kukhala naye paubale wokhulupirika? Mwachitsanzo, kodi kufunafuna ntchito yapamwamba kuli bwino kusiyana ndi kukhala ndi mtendere wamaganizo ndi chimwemwe zimene zimabwera chifukwa cha kukhala paubale weniweni ndi Mulungu? (Luka 12:15) Akhristu ena auzidwa kusankha kusiya kumvera Yehova kapena kuphedwa. Zimenezo zinachitikira Mboni za Yehova zambiri ku misasa ya ukaidi ya Nazi m’nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Abale athu achikhristu ambiri anasankha kukhalabe m’chikondi cha Mulungu ndipo analolera kuphedwa ngati kunafunikira kutero. Amene amakhalabe m’chikondi cha Mulungu mokhulupirika angakhale otsimikiza kuti iye adzawapatsa tsogolo losatha, chinthu chimene dziko lapansi silingapereke. (Marko 8:34-36) Komatu pali zambiri kuposa moyo wosatha wokha.

18 Ngakhale kuti n’zosatheka kukhala ndi moyo kosatha popanda Yehova, tayesani kuyerekeza mmene moyo wautali kwambiri ungakhalire popanda Mlengi. Ungakhale wosasangalatsa, wopanda cholinga chenicheni. Yehova wapatsa anthu ake ntchito yokhutiritsa yoti aichite m’masiku otsiriza ano. Motero tikukhulupirira kuti Yehova, Wamkulu amene amakwaniritsa zolinga zake, akadzatipatsa moyo wosatha, padzakhala zinthu zambiri zochititsa chidwi zoti tidzaziphunzire ndi kuzichita. (Mlaliki 3:11) Kaya tidzaphunzira zochuluka motani m’zaka zikwizikwi zikubwerazo, sitidzatha kumvetsa zonse za “kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu.”​—Aroma 11:33.

w19.12 28 ¶4

“Muziyamika pa Chilichonse”

Tiyenera kuyamikira kwambiri Mulungu kuposa aliyense. N’zosachita kufunsa kuti mwaganizirapo mobwerezabwereza zinthu zambiri zimene Mulungu amapereka. (Deut. 8:17, 18; Mac. 14:17) Koma m’malo mongoganizira pang’ono zinthuzi, mungachite bwino kuganizira mozama madalitso onse amene Mulungu wakupatsani inuyo komanso anzanu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzimuyamikira. Kungakuthandizeninso kudziwa kuti amakukondani komanso kukuyamikirani.​—1 Yoh. 4:9.

w15 10/15 24 ¶7

Tiziganizira Kwambiri za Yehova

7 Tiyenera kuchita khama kuti tiziganizira kwambiri zimene tikuwerenga. Tikutero chifukwa chakuti ubongo wathu suchedwa kusokonezedwa ndi zinthu zina. Choncho tingachite bwino kuwerenga ndi kuganizira zimene tikuwerengazo pa nthawi imene sitinatope komanso pamalo opanda zinthu zosokoneza. Davide ananena kuti ankakonda kuganizira za Yehova usiku. (Sal. 63:6) Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, iye ankakonda kupita kumalo aphee kuti azikaganizira zinthu zofunika ndiponso kupemphera.​—Luka 6:12.

w09 7/15 16 ¶6

Phunzitsani Mwachikondi Ngati Yesu

6 Anthufe timamva bwino tikamalankhula za zinthu zimene timazikonda. Timalankhula mwamphamvu ndiponso mosangalala moti anthu amatha kuona kuti zikutisangalatsa. Izi zimachitika makamaka tikamalankhula za munthu amene timam’konda. Nthawi zambiri timalakalaka kuuza ena zinthu zokhudza munthuyo zimene ife tikudziwa. Timalankhula zabwino za iye, kumukweza ndiponso kumuikira kumbuyo. Timatero chifukwa chakuti timafuna kuti anthu akopeke naye ndiponso kuti akopeke ndi makhalidwe ake ngati mmene ifeyo timachitira.

Mfundo Zothandiza

w07 11/15 15 ¶6

Kodi Mumatsitsimula Ena?

Kumanga nyumba n’kovuta kwambiri, koma kuigwetsa n’kosavuta. Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pakalankhulidwe kathu. Tonsefe ndi opanda ungwiro ndipo timalakwitsa pochita zinthu. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.” (Mlaliki 7:20) N’zosavuta kuti tione zolakwa za munthu wina n’kumulankhula mawu opweteka kwambiri. (Salimo 64:2-4) Koma sizophweka kuti mawu athu akhale olimbikitsa.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwfq 51

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amabwereranso Kunyumba za Anthu Omwe Anakana Kuti Awalalikire?

A Mboni za Yehova amalalikira anthu onse uthenga wa m’Baibulo chifukwa chakuti amakonda Mulungu komanso anthu ena. Amalalikiranso ngakhale anthu omwe nthawi ina anakana kuwalalikira. (Mateyu 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatichititsa kuti tizimvera lamulo limene mwana wake anatiuza lakuti ‘tizipereka umboni wokwanira.’ (Machitidwe 10:42; 1 Yohane 5:3) Chifukwa chomvera lamulo limeneli, timalalikira anthu maulendo angapo ngatinso mmene aneneri akale a Mulungu ankachitira. (Yeremiya 25:4) Komanso chifukwa chakuti timakonda anzathu, timauza aliyense ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ Timalalikira uthenga wa chipulumutsowu ngakhale kwa anthu omwe nthawi ina anakana kuti tiwalalikire.​​—Mateyu 24:14.

Nthawi zambiri timapeza anthu achidwi pakhomo lomwe poyamba anatiuza kuti sakufuna kuti tiwalalikire. Onani zifukwa zitatu zomwe zimachititsa zimenezi.

● Anthu amasamuka.

● Anthu ena pakhomo lomwelo amatha kukhala ndi chidwi ndi uthenga wathu.

● Anthu amasintha. Zinthu zikasintha m’dzikoli komanso pamoyo wa munthu, zimachititsa munthu kuzindikira ‘zosowa zake zauzimu’ n’kufuna kuti aphunzire Baibulo. (Mateyu 5:3) Ngakhalenso anthu omwe amatitsutsa amatha kusintha ngati mmene anachitira mtumwi Paulo.​—1 Timoteyo 1:13.

Komabe sitikakamiza anthu kuti amvetsere uthenga wathu. (1 Petulo 3:15) Timaona kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha yekha zimene akufuna pa nkhani yolambira Mulungu.​​—Deuteronomo 30:19, 20.

JULY 22-28

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 66-68

Yehova Amanyamula Katundu Wathu Tsiku Lililonse

w23.05 12 ¶15

Mmene Yehova Amayankhira Mapemphero Athu

15 Si nthawi zonse pamene mapemphero athu amayankhidwa m’njira yodabwitsa. Koma mayankho amene Yehova amapereka amatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika kwa Atate wathu wakumwambayu. Choncho muzikhala tcheru kuti muone mmene Yehova akuyankhira mapemphero anu. Mlongo wina dzina lake Yoko ankaona kuti Yehova sankayankha mapemphero ake, koma kenako anayamba kumalemba m’buku lake zimene wapempha. Patapita kanthawi, iye anayang’ananso m’buku lake lija ndipo anazindikira kuti Yehova anali atayankha mapemphero ake ambiri ngakhalenso ena omwe anali atawaiwala. Nthawi ndi nthawi timafunika kumaima kaye n’kuganizira mmene Yehova akuyankhira mapemphero athu.​—Sal. 66:19, 20.

w10 12/1 23 ¶6

Muziganizira Makolo Amene Sali Pabanja

Yehova anauzira anthu ena kulemba nyimbo zapadera, kapena kuti masalimo, amene Aisiraeli ankaimba polambira. Ndiyeno taganizirani mmene amayi amasiye ndi ana amasiye ku Isiraeli ankalimbikitsidwira akamaimba nyimbo zouziridwa ndi Mulungu zimenezi. Nyimbozi zinkawakumbutsa kuti Yehova ndi “tate” ndi “woweruza “ wawo ndipo zinkawatsimikizira kuti iye ndi wokonzeka kuwathandiza. (Salimo 68:5; 146:9) Nafenso tingauze makolo amene akulera okha ana mawu olimbikitsa amene angamawakumbukirebe ngakhale patapita zaka zambiri. Ngakhale kuti papita zaka 20, Ruth amene akulera yekha ana amakumbukirabe nthawi imene bambo wina anamuuza kuti: “Mukugwira ntchito yotamandika kwambiri yosamalira ana anu awiriwa. Pitirizani, mukuchita bwino kwambiri.” Ruth ananena kuti: “Mawu amenewa anandilimbikitsa kwambiri.” Ndi zoonadi kuti “mawu abwino ndi mankhwala” ndipo angalimbikitse kholo limene likulera lokha ana kuposa mmene timayembekezera. (Miyambo 15:4, Contemporary English Version) Kodi mungaganizire za zinthu zinazake zabwino zimene kholo limene likulera lokha ana likuchita zimene mungaliyamikire?

w09 4/1 31 ¶1

Atate wa Ana Amasiye

BAIBULO limati: “Mulungu mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye.” (Salimo 68:5) Mawu ouziridwa amenewa akutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yokhudza Yehova Mulungu, yakuti iye ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu osowa. Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, chikusonyeza kuti iye amamvera chisoni ana amene makolo awo anamwalira. Tiyeni tione lemba loyamba m’Baibulo limene lili ndi mawu akuti “mwana wamasiye,” lomwe ndi Eksodo 22:22-24.

w23.01 19 ¶17

Yehova Amatithandiza Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino

17 Werengani Salimo 40:5. Munthu amene akukwera phiri cholinga chake chimakhala kukafika pamwamba penipeni pa phirilo. Komabe akafika pamalo ena amaima n’kusangalala ndi zomwe akuona. Mofanana ndi zimenezi nthawi zina muziima kaye n’kuganizira mmene Yehova akukuthandizirani kuti zinthu zikuyendereni bwino ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto. Kumapeto kwa tsiku lililonse muzidzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova wandipatsa madalitso ati lero? Ngakhale kuti ndikukumanabe ndi mayesero, kodi Yehova akundithandiza bwanji kuwapirira?’ Muzipeza ngakhale dalitso limodzi lochokera kwa Yehova lomwe lakuthandizani kuti zinthu zikuyendereni bwino.

Mfundo Zothandiza

w06 6/1 10 ¶5

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachiwiri cha Masalimo

68:18​—Kodi ndani amene anali “zaufulu mwa anthu”? Amenewa anali amuna amene anatengedwa kuchokera pa gulu la anthu amene anali akaidi, atalanda Dziko Lolonjezedwa. Kenaka amuna amenewa anapatsidwa ntchito yothandiza Alevi pa ntchito yawo.​—Ezara 8:20.

JULY 29–AUGUST 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 69

Zimene Zinachitika pa Moyo wa Yesu Zinanenedweratu mu Salimo 69

w11 8/15 11 ¶17

Anthu Ankayembekezera Mesiya

17 Mesiya adzadedwa popanda chifukwa. (Sal. 69:4) Yesu anati: “Ndikanapanda kuchita pakati [pa anthu] ntchito zimene wina aliyense sanachitepo, akanakhala opanda tchimo, koma tsopano aona ndipo adana nane, ndi kudananso ndi Atate wanga. Zili choncho kuti mawu olembedwa m’Chilamulo akwaniritsidwe. Mawu ake ndi akuti, ‘Anadana nane popanda chifukwa.’” (Yoh. 15:24, 25) Mawu akuti “Chilamulo” nthawi zambiri amatanthauza Malemba onse. (Yoh. 10:34; 12:34) Mauthenga Abwino amatsimikizira kuti Yesu ankadedwa ndi anthu ambiri, makamaka ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda. Ndipotu Yesu ananena kuti: “Dziko lilibe chifukwa chodana ndi inu, koma limadana ndi ine, chifukwa ndimachitira umboni kuti dzikoli ntchito zake ndi zoipa.”​—Yoh. 7:7.

w10 12/15 8 ¶7-8

Khalani Odzipereka pa Kulambira Koona

7 Zimene Yesu anachita nthawi ina zinasonyeza bwino kuti iye anali wodzipereka kwambiri. Anachita zimenezi chakumayambiriro kwa utumiki wake pa nyengo ya Pasika mu 30 C.E. Yesu ndi ophunzira ake atafika m’kachisi ku Yerusalemu anapeza “ogulitsa ng’ombe, nkhosa ndi nkhunda komanso osintha ndalama ali m’kachisi atakhala m’mipando yawo.” Kodi Yesu anachita chiyani ataona zimenezi, nanga ophunzira ake anamva bwanji ndi zimene Yesu anachitazi?​—Werengani Yohane 2:13-17.

8 Zimene Yesu anachita ndiponso kulankhula pa nthawi imeneyi zinakumbutsa ophunzira ake mawu aulosi opezeka mu salimo la Davide akuti: “Pakuti kudzipereka kwambiri panyumba yanu kwandidya.” (Sal. 69:9) N’chifukwa chiyani zinali choncho? Chifukwa chakuti zimene Yesu anachita zikanamuika pa ngozi. Ndipotu akuluakulu a pakachisipo monga ansembe, alembi ndi anthu ena ndi amene ankalimbikitsa anthu kuchita malondawa pakachisi. Choncho zimene Yesu anachita pouza anthu poyera chinyengo cha atsogoleri achipembedzo komanso kusokoneza mapulani awo kukanachititsa kuti adane naye kwambiri. Ophunzira ake anazindikira kuti iye anachita zimenezi chifukwa chakuti anali ‘wodzipereka kwambiri panyumba ya Mulungu’ kapena kuti pa kulambira koona. Koma kodi mawu akuti kudzipereka kwambiri amatanthauza chiyani? Kodi ndi osiyana ndi mawu akuti changu?

g95 10/22 31 ¶4

Kodi Mungafe Chifukwa Chosweka Mtima?

Anthu ena amanena kuti Yesu anafa chifukwa choti anasweka mtima, popeza zinaloseredwa kuti: “Mtima wanga wasweka chifukwa cha kunyozedwa, ndipo bala lake ndi losachiritsika.” (Salimo 69:20) Kodi pamenepa ankatanthauza kusweka kwenikweni? N’kuthekadi kuti ankatanthauza zimenezo, chifukwa maola ochepa asanaphedwe, Yesu anamva kupweteka kwambiri m’thupi komanso mumtima. (Mateyu 27:46; Luka 22:44; Aheberi 5:7) Kuwonjezera pamenepo, n’kutheka kuti “magazi ndi madzi” amene anatuluka atamubaya ndi mkondo atangofa kumene, akusonyeza kuti anaswekadi mtima. Mtima kapena mtsempha waukulu ukaphulika, magazi amatsikira m’chifuwa kapena mu chinachake chamadzimadzi chimene chimakuta mtimawo. Zimenezi zingachititse kuti pamene paphulikapo pazituluka zinthu zooneka ngati “magazi ndi madzi.”​—Yohane 19:34.

it-2 650

Chomera Chapoizoni

Baibulo linaneneratu za Mesiya kuti adzapatsidwa “chomera chapoizoni” ngati chakudya. (Sl 69:21, mawu a m’munsi) Zimenezi zinachitika Yesu Khristu asanapachikidwe, pamene anamupatsa vinyo wosakaniza ndi zinthu zowawa zamadzimadzi koma atazilawa, anakana kumwa chifukwa ankadziwa kuti zichepetsa ululu wake. Polemba kukwaniritsidwa kwa ulosiwu, Mateyu (27:34) anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti kho·leʹ, omwenso anagwiritsidwa ntchito mu Baibulo la Chigiriki la Septuagint pa Salimo 69:21. Komabe, nkhani imene Maliko analemba imanena za mule (Mko 15:23), ndipo zimenezi zimachititsa anthu ena kuganiza kuti, “chomera chapoizoni” kapena “zinthu zowawa zamadzimadzi” zimene zinatchulidwazi zinali “mule.” Komabe zikhoza kutheka kuti mu chakumwacho, anaikamo zonse ziwiri, zinthu zowawa zamadzimadzi komanso mule.

Mfundo Zothandiza

w99 1/15 18 ¶11

Kwezani Manja Okhulupirika m’Pemphero

11 Anthu ambiri amangopemphera akamafuna chinachake, koma ife timayamikira komanso kutamanda Yehova Mulungu chifukwa chomukonda, ndipo timachita zimenezi kaya tikupemphera pagulu kapena kwatokha. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musamade nkhawa ndi chinthu chilichonse. M’malomwake, nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu, muzimuchonderera kuti azikutsogolerani pa chilichonse ndipo nthawi zonse muzimuthokoza. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu pamene mukutsatira Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Kuwonjezera pa kupemphera kwa Mulungu ndi kumuchonderera, tiyenera kumamuthokoza chifukwa cha zinthu za uzimu zomwe amatipatsa komanso chifukwa choti amatithandiza. (Miyambo 10:22) Wolemba masalimo anaimba kuti: “Yamikani Mulungu kuti ikhale ngati nsembe imene mukupereka kwa iye, ndipo perekani kwa Wam’mwambamwamba zimene mwalonjeza.” (Salimo 50:14) Ndipo Davide m’pemphero lake anatchula mawu awa okhudza mtima: “Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Mulungu, ndipo ndidzamulemekeza komanso kumuyamikira.” (Salimo 69:30) Kodi sitiyenera kuchita zomwezi tikamapemphera pagulu komanso kwatokha?

AUGUST 5-11

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 70-72

‘Uzani M’badwo Wotsatira’ za Mphamvu za Mulungu

w99 9/1 18 ¶17

Achinyamata​—Muzigwiritsa Ntchito Luso Lanu la Kuganiza

17 Kupewa misampha ya Satana kumafuna kuti muzikhala tcheru nthawi zonse, ndipo nthawi zina, kumafuna kulimba mtima kwambiri. Nthawi zina mungazindikire kuti ndinu wosiyana osati ndi anzanu okha, koma ndi dziko lonse. Wolemba masalimo Davide anapemphera kuti: “Chifukwa chiyembekezo changa ndi inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Ndakhala ndikudalira inu kuyambira ndili mnyamata. Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ndili mnyamata, ndipo mpaka pano ndikupitiriza kulengeza ntchito zanu zodabwitsa.” (Salimo 71:5, 17) Davide amadziwika chifukwa cha kulimba mtima kwake. Koma kodi anayamba liti kukhala wolimba mtima? Pamene anali mnyamata. Ngakhale asanagonjetse Goliati, chochitika chimene anatchuka nacho kwambiri, Davide anali atasonyezapo kale kulimba mtima kwake poteteza nkhosa za bambo ake pamene anapha mkango komanso chimbalangondo. (1 Samueli 17:34-37) Komabe, Davide anapereka ulemu wonse kwa Yehova chifukwa chomuthandiza kukhala wolimba mtima, ndipo anamuuza kuti “Ndakhala ndikudalira inu kuyambira ndili mnyamata.” Davide anakwanitsa kugonjetsa mayesero alionse omwe anakumana nawo chifukwa choti ankadalira Yehova. Inunso mudzaona kuti ngati mumadalira Yehova, adzakupatsani kulimba mtima ndi mphamvu kuti mukwanitse ‘kugonjetsa dziko.’​—1 Yohane 5:4.

g04 10/8 17 ¶3

Kodi Anthu Okalamba Tiyenera Kuwachitira Zinthu Motani?

Wamasalimo anapemphera kuti: “Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.” (Salimo 71:9) Mulungu ‘sataya’ atumiki ake okhulupirika, ngakhale iwowo aziona ngati atha ntchito. Wamasalimo sanaone ngati Yehova anamutaya, m’malo mwake, anazindikira kuti afunika kudalira Mlengi wake, makamaka pamene anali kukalamba. Yehova akaona munthu wokhulupirika, kapena kuti wachifundo woteroyo, amamuthandiza moyo wake wonse. (Salimo 18:25) Nthawi zambiri chithandizo chimenecho chimachokera kwa Akhristu anzathu.

w14 1/15 23 ¶4-5

Tumikirani Yehova Masiku Oipa Asanafike

4 Ngati ndinu wachikulire ndipo mwachita zambiri pa moyo wanu, mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndizichita chiyani panopa, ndidakali ndi mphamvu?’ Popeza kuti ndinu Mkhristu wachikulire, muli ndi mwayi umene anthu ena alibe. Mungaphunzitse achinyamata zimene mwaphunzira kuchokera kwa Yehova. Mungalimbikitse anthu ena powauza zinthu zosangalatsa zimene mwakumana nazo potumikira Mulungu. Mfumu Davide anapemphera kuti akhale ndi mwayi wochita zimenezi. Iye analemba kuti: “Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira pa unyamata wanga . . . Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye, kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira, kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.”​—Sal. 71:17, 18.

5 Kodi mungaphunzitse bwanji anthu ena zinthu zimene mwaphunzira pa zaka zonse zimene mwakhala ndi moyo? Mukhoza kuitana Akhristu achinyamata kuti abwere kunyumba kwanu kudzacheza. Kapena mungawapemphe kuti ayende nanu mu utumiki kuti aone mmene mukusangalalira potumikira Yehova. M’nthawi ya Yobu, Elihu anati: “Masiku alankhule. Zaka zambiri n’zimene ziyenera kudziwitsa anthu nzeru.” (Yobu 32:7) Mtumwi Paulo analimbikitsa akazi achikulire kuti azilimbikitsa ena ndi mawu awo komanso chitsanzo chawo. Iye analemba kuti: “Akazi achikulire . . . akhale aphunzitsi a zinthu zabwino.”​—Tito 2:3.

Mfundo Zothandiza

it-1 768

Firate

Malire a Dziko la Isiraeli. Mulungu analonjeza Abulahamu kuti adzapereka dziko kwa mbewu yake “kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.” (Ge 15:18) Lonjezoli linabwerezedwanso kwa mtundu wa Isiraeli. (Eks 23:31; De 1:7, 8; 11:24; Yos 1:4) Lemba la 1 Mbiri 5:9 limanena kuti Davide asanayambe kulamulira, ana ena a Rubeni anakulitsa malire a dera limene ankakhala kukafika “mpaka kum’mawa poyambira chipululu pamtsinje wa Firate.” Koma popeza kuti mtsinje wa Firate unali pa mtunda wa makilomita 800 kuchokera kum’mawa kwa Giliyadi (1Mb 5:10), zimenezi zikutanthauza kuti Arubeni anakulitsa dera lawo kum’mawa kwa Giliyadi kukafika m’malire a Chipululu cha Siriya, chomwe chimafika kumtsinje wa Firate. (Mabaibulo ena amati “mpaka polowera kuchipululu kuyambira mtsinje wa Firate.”) Zikuoneka kuti lonjezo la Yehovali linakwaniritsidwa koyamba mu ulamuliro wa Mfumu Davide ndi Solomo pamene malire a Isiraeli anakafika ku ufumu wa Zoba wa Chiaramu mpaka m’mphepete mwa mtsinje wa Firate, umene umadutsa kumpoto kwa Siriya. (2Sa 8:3; 1Mf 4:21; 1Mb 18:3-8; 2Mb 9:26) Chifukwa chakuti unali wodziwika bwino, nthawi zambiri unkangotchulidwa kuti “Mtsinje.”​—Yos 24:2, 15; Sl 72:8.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwfq 49

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Anasintha Zinthu Zina Zomwe Ankakhulupirira?

Zonse zimene timakhulupirira zimachokera m’Baibulo. Choncho tinasintha zinthu zina zomwe tinkakhulupirira chifukwa chomvetsa bwino mfundo za m’Malemba.

Zimenezi n’zogwirizana kwambiri ndi mfundo ya pa Miyambo 4:18, yomwe imati: “Koma njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” Dzuwa likamatuluka limayamba kuwala pang’onopang’ono ndipo timayamba kuona bwino zinthu, mofanana ndi zimenezi Mulungu amatithandiza kumvetsa bwino mfundo za m’Mawu ake pang’onopang’ono komanso pa nthawi yake. (1 Petulo 1:10-12) Ndipo monga mmene Baibulo linaneneratu, Yehova wathandiza anthu kuti azimvetsa Mawu ake mofulumira kwambiri “nthawi yamapeto” ino.​—Danieli 12:4.

Choncho, tisamadabwe kapena kukhumudwa zinthu zimene timakhulupirira zikasintha. Tikutero chifukwa chakuti atumiki a Mulungu akale nawo ankafunikanso kusintha zinthu zina zomwe poyamba ankazikhulupirira komanso kuziyembekezera.

● Mose ali ndi zaka 40 ankafuna kupulumutsa mtundu wa Isiraeli koma nthawi yoti Mulungu achite zimenezi inali isanakwane.​—Machitidwe 7:23-25, 30, 35.

● Atumwi sanamvetse ulosi womwe unkanena za kuphedwa kwa Mesiya komanso kuukitsidwa kwake.​—Yesaya 53:8-12; Mateyu 16:21-23.

● Akhristu ena akale anali ndi maganizo olakwika okhudza nthawi imene“tsiku la Yehova” lidzafike.​—2 Atesalonika 2:1, 2.

Komabe patapita nthawi, Mulungu anawathandiza kumvetsa zinthu zimene sankazimvetsa. Ifenso timapempha Mulungu kuti apitirize kutithandiza kumvetsa bwino Mawu ake.​—Yakobo 1:5.

AUGUST 12-18

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 73-74

Kodi Ndimachitira Nsanje Anthu Amene Satumikira Mulungu?

w20.12 19 ¶14

Yehova Amapulumutsa Anthu a Mtima Wosweka

14 Munthu amene analemba Salimo 73 anali Mlevi. Choncho anali ndi mwayi wapadera wotumikira pamalo olambirira Yehova. Ngakhale zili choncho, pa nthawi ina iye anafooka. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti iye afooke? Iye anayamba kusirira anthu oipa ndi odzitukumula, osati chifukwa choti ankafuna kuchita zoipa koma ankaona ngati anthu amenewo zinthu zinkawayendera bwino. (Sal. 73:2-9, 11-14) Ankaoneka ngati anali ndi chilichonse, chuma, moyo wabwino komanso analibe nkhawa. Mleviyo ataona zimenezi anakhumudwa kwambiri moti ananena kuti: “Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe, ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.” Zimenezi zikanachititsa kuti asiye kutumikira Yehova.

w20.12 19-20 ¶15-16

Yehova Amapulumutsa Anthu a Mtima Wosweka

15 Werengani Salimo 73:16-19, 22-25. Mleviyu ‘analowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.’ Mmenemo, ali pakati pa okhulupirira anzake, anayamba kuganizira mofatsa mmene zinthu zinalili pa moyo wake komanso kupemphera. Zimenezi zinamuthandiza kuti adziwe kuti maganizo ake sanali anzeru ndipo akanatha kumuchititsa kuti asakhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. Iye anazindikiranso kuti anthu oipa anali “pamalo oterera” ndiponso kuti “afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa.” Mleviyu anafunika kumaona zinthu monga mmene Yehova amazionera kuti asafooke komanso asiye kusirira anthu oipa. Atachita zimenezi anakhalanso ndi mtendere ndipo ankasangalala. Iye anati: “Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha [Yehova].”

16 Zimene tikuphunzirapo. Tisamasirire anthu oipa omwe akuoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino. Chimwemwe chawo ndi chakanthawi ndipo sadzakhala ndi moyo wosatha. (Mlal. 8:12, 13) Tikamawasirira tingathe kufooka ndiponso tingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho mukayamba kuona kuti mwayamba kusirira anthu oipa, muzichita zimene Mleviyu anachita. Muzimvera malamulo a Mulungu komanso muzikhala pafupi ndi anthu amene amachita zimene Yehova amafuna. Ndipotu mungakhale osangalala kwambiri mukamakonda Yehova kuposa china chilichonse. Komanso mungapitirizebe kuyenda panjira ya ‘kumoyo weniweniwo.’​—1 Tim. 6:19.

w14 4/15 4 ¶5

Tsanzirani Chikhulupiriro cha Mose

5 Kodi mungakane bwanji “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo”? Musaiwale kuti zosangalatsa zauchimo ndi zakanthawi. Chikhulupiriro chanu chingakuthandizeni kuona kuti “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.” (1 Yoh. 2:15-17) Muziganizira zimene zidzachitikire anthu osalapa. Iwo ali “pamalo oterera . . . kuti awonongeke.” (Sal. 73:18, 19) Tikamayesedwa kuti tichite zoipa, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘kodi ndikufuna kuti tsogolo langa lidzakhale lotani?’

w13 2/15 25-26 ¶3-5

Musalole Chilichonse Kukulepheretsani Kupeza Ulemerero

3 Wamasalimo ankakhulupirira kuti Yehova adzagwira dzanja lake lamanja n’kumutsogolera ku ulemerero. (Werengani Salimo 73:23, 24.) Kodi Yehova amapatsa bwanji anthu ulemerero? Iye amatsogolera anthu ake odzichepetsa ku ulemerero powadalitsa m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amawathandiza kumvetsa cholinga chake. (1 Akor. 2:7) Iye amalolanso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi anthu amene amamumvera.​—Yak. 4:8.

4 Yehova amalemekezanso atumiki ake powapatsa mwayi wolalikira uthenga wabwino. (2 Akor. 4:1, 7) Utumiki umenewu umatipatsa ulemerero. Anthu amene amachita utumikiwu n’cholinga choti alemekeze Yehova ndiponso kuthandiza anthu ena, akulonjezedwa kuti: “Amene akundilemekeza ndiwalemekeza.” (1 Sam. 2:30) Anthu oterewa amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo nthawi zambiri amalemekezedwa ndi atumiki anzawo.​—Miy. 11:16; 22:1.

5 Kodi tsogolo la anthu amene ‘amayembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake’ ndi lotani? Baibulo limawalonjeza kuti: “[Yehova] adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi. Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.” (Sal. 37:34) Iwo amayembekezera kuti Mulungu adzawapatsa moyo wosatha.​—Sal. 37:29.

Mfundo Zothandiza

it-2 240

Leviyatani

Salimo 74 limafotokoza mmene Mulungu anapulumutsira anthu ake, ndipo vesi 13 ndi 14 limafotokoza mophiphiritsira mmene anapulumutsira Aisiraeli m’manja mwa Aiguputo. Palembali, mawu akuti “zilombo zam’nyanja [Chihe., than·ni·nimʹ, chimodzi tan·ninʹ]” anagwiritsidwa ntchito mofanana ndi mawu akuti “Leviyatani” ndipo kuphwanyidwa mutu kwa Leviyatani kukuimira kugonjetsedwa kwa Farao ndi asilikali ake pamene Aisiraeli ankachoka ku Iguputo. Palembali, ma Targum a Chiaramu anagwiritsa ntchito mawu akuti ‘anthu amphamvu a Farao’ m’malo mwa mawu akuti “mitu ya Leviyatani.” (Yerekezerani ndi Eze 29:3-5, pomwe Farao anayerekezeredwa ndi “chilombo chachikulu cham’nyanja” chogona m’ngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo; onaninso Eze 32:2.) Lemba la Yesaya 27:1 limasonyeza kuti Leviyatani ndi chizindikiro cha ufumu kapena bungwe lina lapadziko lonse lomwe wolamulira wake wamkulu ndi amene Baibulo limamutchula kuti ‘chinjoka’ komanso “njoka yakale ija.” (Chv 12:9) Ulosiwu unkakhudza kubwezeretsedwa kwa Isiraeli, choncho pamene Yehova ankanena kuti ‘alanga’ Leviyatani ankatanthauza kuti aphatikizanso Babulo. Komabe, vesi 12 ndi 13 limanenanso za Asuri ndi Iguputo. Choncho pamenepa zikuoneka kuti mawu akuti Leviyatani amaimira bungwe kapena ufumu wapadziko lonse omwe umatsutsa Yehova komanso anthu amene amamulambira.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwbq 89

Kodi Zipembedzo Zonse N’zofanana Ndipo Zimathandizadi Anthu Kudziwa Mulungu?

Yankho la m’Baibulo

Ayi, zipembedzo zonse sizofanana. M’Baibulo muli zitsanzo za zipembedzo zimene sizisangalatsa Mulungu. Zipembedzozi zilipo magulu awiri.

Gulu loyamba: Zipembedzo zolambira milungu yonyenga

Baibulo limanena kuti kulambira milungu yonyenga ndi ‘kopanda pake,’ ‘kwachabechabe’ ndiponso ‘kosapindulitsa.’ (Yeremiya 10:3-5; 16:19, 20) Yehova Mulungu analamula mtundu wa Aisiraeli kuti: “Usakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.” (Ekisodo 20:3, 23; 23:24) Pamene Aisiraeli anayamba kulambira milungu yonyenga, “mkwiyo wa Yehova unawayakira.”​—Numeri 25:3; Levitiko 20:2; Oweruza 2:13, 14.

Masiku anonso Yehova amakwiya ndi anthu olambira “milungu” yonyenga. (1 Akorinto 8:5, 6; Agalatiya 4:8) Iye amalamula anthu amene akufuna kumulambira kuti ayenera kutuluka m’chipembedzo chonyenga, ndipo amati: “Tulukani pakati pawo, lekanani nawo.” (2 Akorinto 6:14-17) Zikanakhala kuti zipembedzo zonse n’zofanana ndipo zimathandizadi anthu kudziwa Mulungu, ndiye n’chifukwa chiyani Mulungu anapereka lamulo limeneli?

Gulu lachiwiri: Zipembedzo zolambira Mulungu woona m’njira yosavomerezeka

Nthawi zina Aisiraeli ankalambira Mulungu pogwiritsa ntchito zikhulupiriro ndiponso miyambo yochokera kwa anthu amene ankalambira milungu yonyenga. Koma Yehova ankadana ndi zoti anthu aziphatikiza kulambira koona ndi konyenga. (Ekisodo 32:8; Deuteronomo 12:2-4) Yesu anadzudzula atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake chifukwa cha zimene ankachita polambira Mulungu. Iwo ankadzionetsera kuti amalambira Mulungu koma zoona zake n’zakuti anali achinyengo chifukwa ‘ankanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.’​—Mateyu 23:23.

Masiku anonso chipembedzo chokhacho chimene chimaphunzitsa zoona n’chimene chingathandize anthu kudziwa Mulungu. Zinthu zoona zokhudza Mulungu zimapezeka m’Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17; 2 Timoteyo 3:16, 17) Zipembedzo zimene zimaphunzitsa zinthu zosemphana ndi zimene zili m’Baibulo sizingathandize anthu mpang’ono pomwe kudziwa Mulungu. Ziphunzitso zambiri zimene anthu amaganiza kuti ndi za m’Baibulo monga zakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi, munthu ali ndi mzimu wosafa ndiponso zoti anthu oipa amakazunzidwa kumoto, zinachokera kwa anthu amene ankalambira milungu yonyenga. Zipembedzo zimene zimaphunzitsa zimenezi n’zosathandiza chifukwa zimaphunzitsa miyambo ya anthu m’malo mophunzitsa zimene Mulungu amafuna.​—Maliko 7:7, 8.

Mulungu amadana ndi kumulambira mwachinyengo. (Tito 1:16) Chipembedzo choona chiyenera kuthandiza anthu kukhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu osati chizingokhala ndi miyambo inayake kapenanso kuti anthu azingopemphera mwamwambo chabe. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake. Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo, ndi kukhala wopanda banga la dzikoli.” (Yakobo 1:26, 27) Baibulo la King James Version, limagwiritsa ntchito mawu akuti “chipembedzo chosadetsedwa” ponena za kulambira Mulungu mopanda chinyengo.

AUGUST 19-25

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 75-77

N’chifukwa Chiyani Sitiyenera Kudzitukumula?

w18.01 28 ¶4-5

Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoli

4 Paulo atanena kuti anthu ambiri adzakhala odzikonda komanso okonda ndalama, analembanso kuti anthu adzakhala odzimva, odzikweza, odzitukumula ndiponso onyada. Munthu amasonyeza makhalidwe amenewa chifukwa choganiza kuti ndi wapamwamba kuposa ena potengera luso lake, maonekedwe ake, chuma chake kapena udindo wake. Anthu amakhalidwe amenewa amalakalaka kuti ena aziwatama kapena kuwasirira. Katswiri wina analemba kuti munthu wonyada kwambiri amadziona kuti ndi wapadera moti tingati amadzilambira yekha. Anthu ena amanena kuti khalidwe lonyada ndi lonyansa kwambiri moti ngakhale anthu onyadawo amanyansidwa ndi anthu ena amene ali ndi khalidweli.

5 Yehova amadana ndi khalidwe la kunyada. Paja Baibulo limanena kuti iye amanyansidwa ndi “maso odzikweza.” (Miy. 6:16, 17) Munthu wonyada sangakhale pa ubwenzi ndi Mulungu. (Sal. 10:4) Mdyerekezi ndi wonyada. (1 Tim. 3:6) Koma n’zomvetsa chisoni kuti ngakhale atumiki ena a Yehova anayamba kusonyeza khalidweli. Mwachitsanzo Uziya, yemwe anali mfumu ya ku Yuda, anakhala wokhulupirika kwa zaka zambiri, koma Baibulo limanena kuti: “Atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa. Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.” Pa nthawi ina, nayenso Mfumu Hezekiya anayamba mtima wonyada koma kenako anasiya.​—2 Mbiri 26:16; 32:25, 26.

w06 7/15 11 ¶3

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachitatu ndi Chachinayi cha Masalimo

75:4, 5, 10​—Kodi mawu akuti “nyanga” amaimira chiyani? Nyanga za nyama ndi chida champhamvu. Motero, mawu akuti “nyanga” mophiphiritsa amaimira mphamvu kapena nyonga. Yehova amanyamula nyanga za anthu ake, kuwaika pokwezeka, koma ‘amatseteka nyanga zonse za oipa.’ Tikuchenjezedwa kuti ‘tisamakwezetse nyanga yathu kuti tisakhale onyada kapena odzikweza. Popeza Yehova ndiye amakweza anthu, tiyenera kuona udindo pampingo kuti umachokera kwa iye.​—Salimo 75:7.

Mfundo Zothandiza

w06 7/15 11 ¶4

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachitatu ndi Chachinayi cha Masalimo

76:10​—Kodi “kuzaza kwake kwa munthu” kungalemekeze bwanji Yehova? Mulungu akamalola anthu kutikwiyira chifukwa choti ndife atumiki ake, pangakhale zotsatirapo zabwino. Vuto lililonse limene tingakumane nalo lingatipatse phunziro linalake. Yehova amalola kuvutika n’cholinga choti kuvutikako kutiphunzitse kanthu kena. (1 Petro 5:10) ‘Chotsalira cha kuzaza kwa munthu, Mulungu adzachiletsa.’ Bwanji ngati tivutika mpaka kumwalira? Izinso zingalemekeze Yehova chifukwa anthu omwe ankationa tikupirira mokhulupirika iwonso angayambe kupembedza Mulungu.

AUGUST 26–SEPTEMBER 1

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 78

Kusakhulupirika kwa Aisiraeli Ndi Chitsanzo Chotichenjeza

w96 12/1 29-30

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kumakumbukira Masiku Akale’?

N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri Aisiraeli ankakonda kuiwala. Kodi zotsatirapo zake zinkakhala zotani? “Ankayesa Mulungu mobwerezabwereza, ndipo ankachititsa kuti Woyera wa Isiraeli amve chisoni. Iwo sanakumbukire mphamvu za Mulungu, tsiku limene anawapulumutsa kwa mdani wawo.” (Salimo 78:41, 42) Patapita nthawi, kuiwala kwawo malamulo a Yehova kunachititsa kuti awakane.​—Mateyu 21:42, 43.

Chitsanzo chabwino chinaperekedwa ndi wolemba masalimo amene analemba kuti: “Ndidzakumbukira ntchito za Ya, ndidzakumbukira zochita zanu zodabwitsa zakale. Ndidzaganizira mozama za ntchito zanu zonse, ndipo ndiziganizira mwakuya zochita zanu.” (Salimo 77:11, 12) Kuganizira mozama zimene Yehova anachita m’mbuyomu komanso chikondi chomwe anasonyeza, kungatilimbikitse komanso kutithandiza kuti tizimuyamikira kwambiri. “Kukumbukira masiku akale” kungatithandize kuti tisakhale aulesi komanso kungatilimbikitse kuti tipitirize kuchita zonse zomwe tingathe ndiponso kuti tipitirizebe kupirira mokhulupirika.

w06 7/15 17 ¶16

Pewani Kudandaula

16 Munthu akamang’ung’udza amangoganizira za iye yekha ndi mavuto ake ndipo amanyalanyaza madalitso amene tili nawo monga Mboni za Yehova. Ngati tili ndi chizolowezi chodandaula ndipo tikufuna kuchithetsa, tifunikira kumakumbukira madalitso amenewa. Mwachitsanzo, aliyense wa ife ali ndi mwayi wosangalatsa wodziwika ndi dzina la Yehova. (Yesaya 43:10) Tingakhale ndi ubwenzi wolimba ndi iye, ndipo timatha kulankhula ndi “Wakumva pemphero” ameneyu panthawi iliyonse. (Salimo 65:2; Yakobo 4:8) Moyo wathu umakhala n’cholinga chifukwa chakuti timamvetsa nkhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse ndipo timakumbukira kuti ndi mwayi wathu kukhala okhulupirika kwa Mulungu. (Miyambo 27:11) Tingatenge nawo mbali kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu nthawi zonse. (Mateyu 24:14) Kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Khristu kumatithandiza kukhala ndi chikumbumtima choyera. (Yohane 3:16) Amenewa ndi madalitso omwe timakhala nawo kaya tifunikira kupirira zinthu zotani.

w11 7/1 10 ¶3-4

Kodi Yehova Amasangalala Kapena Kukhumudwa Ndi Zochita Zathu?

Wamasalimo ananena kuti: “Iwo analitu kumupandukira kawirikawiri m’chipululu.” (Vesi 40) Vesi lotsatira limanena kuti: “Mobwerezabwereza, anali kumuyesa Mulungu.” (Vesi 41) Kodi mwaona kuti salimo limeneli likusonyeza kuti zimenezi zinkachitika mobwerezabwereza? Aisiraeli anayamba kusalemekeza Mulungu komanso kumupandukira ali m’chipululu, pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Mulungu anawapulumutsa ku Iguputo. Iwo anayamba kung’ung’udza komanso kukayikira ngati Mulungu angathe kuwasamalira komanso ngati ankafunadi kuwasamalira. (Numeri 14:1-4) Buku lina lothandiza anthu omasulira Baibulo limanena kuti mawu akuti ‘anali kumupandukira’ angamasuliridwenso kuti ‘anaumitsa mitima yawo kuti asamvere Mulungu’ kapena ‘anauza Mulungu kuti, “sitikufuna kuti mukhale Mulungu wathu.”’ Komabe, popeza Yehova ndi Mulungu wachifundo, iye ankakhululukira anthu akewa akalapa. Koma zikatero iwo ankayambiranso kuchita zinthu zoipa ndipo ankamupandukiranso. Akalapa, Yehova ankawakhululukiranso ndipo izi zinkachitika mobwerezabwereza.​—Salimo 78:10-19, 38.

Kodi Yehova ankamva bwanji Aisiraeli osamverawa akamupandukira? Vesi 40 limanena kuti: “Anali kumukhumudwitsa.” Baibulo lina linamasulira mawu amenewa kuti, “ankachititsa kuti Mulungu amve chisoni.” Buku lina lofotokoza nkhani za m’Baibulo limati: “Mawu amenewa akutanthauza kuti zimene Ayuda ankachita zinkamupweteketsa mtima Yehova ngati mmene makolo amamvera, mwana wawo akamawachitira mwano komanso akawapandukira.” Mofanana ndi mmene mwana wosamvera amapweteketsera kwambiri mtima makolo ake, Aisiraeli “anali kumvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli.”​—Vesi 41.

Mfundo Zothandiza

w06 7/15 11 ¶5

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachitatu ndi Chachinayi cha Masalimo

78:24, 25​—N’chifukwa chiyani mana amatchedwa “tirigu wa kumwamba” ndiponso “mkate wa omveka” kapena kuti angelo? Mawu onsewa satanthauza kuti mana chinali chakudya cha angelo. Mana anali “tirigu wa kumwamba” chifukwa chakuti ankachokera kumwamba. (Salimo 105:40) Popeza angelo, kapena kuti “omveka,” amakhala kumwamba, mawu akuti “mkate wa omveka” angatanthauze kuti mana anaperekedwa ndi Mulungu, amene amakhala kumwamba. (Salimo 11:4) Yehova angakhale kuti analinso kugwiritsa ntchito angelo kupereka mana kwa Aisiraeli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena