Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 12/1 tsamba 29-31
  • “Kumbukirani Masiku Apitawo”—Chifukwa Ninji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kumbukirani Masiku Apitawo”—Chifukwa Ninji?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chisonkhezero ndi Chilimbikitso
  • Kuphunzira pa Zophophonya Zakale
  • Kudzichepetsa ndi Kuyamikira
  • Musaiwale Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Mukhoza Kunola Luso Lanu Lokumbukira Zinthu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Musaleme Kuthamanga Makani a Moyo!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Phunzirani Njira za Yehova
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 12/1 tsamba 29-31

“Kumbukirani Masiku Apitawo”​—Chifukwa Ninji?

“KUMBUKIRANI masiku apitawo.” Uphungu umenewu wa mtumwi Paulo, wolembedwa cha ku ma 61 C.E., unaperekedwa kwa Akristu achihebri ku Yudeya. (Ahebri 10:32, The New English Bible) Kodi nchiyani chinachititsa mawu ameneŵa kulankhulidwa? Kodi nchifukwa ninji alambiri a Yehova a m’zaka za zana loyamba amenewo sanafunikire kuiŵala zakale? Kodi tingapindule mwa kulabadira chikumbutso chimodzimodzicho lerolino?

M’zaka mazana onsewo, olemba Baibulo mobwerezabwereza anachenjeza za kunyalanyaza kapena kusalingalira zakale. Nthaŵi ndi zochitika zakale zinayenera kukumbukiridwa ndi kulingaliridwa. Ngakhale Yehova anati: “Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi ine.” (Yesaya 46:9) Tiyeni tisanthule zifukwa zitatu zamphamvu zolabadirira uphunguwu.

Chisonkhezero ndi Chilimbikitso

Choyamba, ungakhale wosonkhezera ndi wolimbikitsa kwambiri. Pamene Paulo analemba kalata yake yopita ku mpingo wachihebri, anali kulembera Akristu anzake amene chikhulupiriro chawo chinali kuyesedwa masiku onse chifukwa cha chitsutso cha Ayuda. Pozindikira kuti anafunikira kulimbitsa chipiriro, Paulo anati: “Tadzikumbutsani masiku akale, m’menemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zoŵaŵa.” (Ahebri 10:32) Kukumbukira kwawo zochita zakale za kukhulupirika m’nkhondo yauzimu kunali kudzawapatsa kulimba mtima kofunikira kuti atsirize makaniwo. Mofananamo, mneneri Yesaya analemba kuti: “Kumbukirani ichi, nimuchirimike.” (Yesaya 46:8) Yesu Kristu anali kulingaliranso za chotulukapo chokhumbika chimenechi pamene anauza mpingo wa ku Efeso kuti: “Potero kumbukira kumene wagwerako [“wagwako,” NW], [chikondi chako choyamba], nulape, nuchite ntchito zoyamba.”​—Chivumbulutso 2:4, 5.

Uphungu wakuti ‘akumbukire masiku akale, kuzindikira zaka za mibadwo yambiri’ unali mfundo yobwerezedwa m’nkhani zimene Mose anapereka kwa Israyeli, pamene anali kulimbikitsa mtunduwo kukhala wokhulupirika kwa Yehova mopanda mantha. (Deuteronomo 32:7) Taonani mawu ake, olembedwa pa Deuteronomo 7:18 akuti: “Musamawaopa [Akanani]; mukumbukire bwino chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Farao, ndi Aigupto wonse.” Kukumbukira zochita zopulumutsa za Yehova zimene anachitira anthu ake kunayenera kuwasonkhezera kuti apitirize kutsatira malamulo a Mulungu mokhulupirika.​—Deuteronomo 5:15; 15:15.

Mwachisoni, Aisrayeli nthaŵi zambiri anagonjera ku tchimo la kuiŵala. Ndi chotulukapo chotani? “Anabwerera m’mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israyeli. Sanakumbukira dzanja lake, tsikuli anawaombola kwa msautsi.” (Salmo 78:41, 42) M’kupita kwa nthaŵi, kuiŵala kwawo malamulo a Yehova kunachititsa kuti awakane.​—Mateyu 21:42, 43.

Chitsanzo chabwino chinaperekedwa ndi wamasalmo amene analemba kuti: “Ndidzakumbukira zimene adazichita Ambuye; inde, ndidzakumbukira zodabwiza zanu zoyambira kale. Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita inu.” (Salmo 77:11, 12) Kukumbukira kosinkhasinkha kotero kwa utumiki wokhulupirika wakale ndi zochita za Yehova zachikondi kudzatipatsa chisonkhezero chofunikira, chilimbikitso, ndi chiyamikiro. Ndiponso, ‘kudzikumbutsa masiku akale’ kungathetse kutopa ndipo kungatisonkhezere kuchita zonse zimene tingathe ndi kupirira mokhulupirika.

Kuphunzira pa Zophophonya Zakale

Chachiŵiri, kusaiŵala kungakhale njira yophunzirira pa zophophonya zakale ndi zotulukapo zake. Akumaganizira zimenezi, Mose anapatsa Aisrayeli uphungu wakuti: “Kumbukirani, musamaiŵala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m’chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m’dziko la Aigupto, kufikira munaloŵa m’malo muno munapikisana ndi Yehova.” (Deuteronomo 9:7) Chotulukapo cha kusamvera kwa Aisrayeli kumeneku chinali chakuti, monga momwe Mose anasonyezera, ‘Yehova Mulungu wawo anawayendetsa m’chipululu zaka makumi anayi.’ Kodi nchifukwa ninji analimbikitsidwa kukumbukira zimenezi? Kuti awachepetse ndi kuwawongolera njira zawo zachipanduko kotero kuti ‘azisunga malamulo a Yehova Mulungu [wawo], kuyenda m’njira zake, ndi kumuwopa.’ (Deuteronomo 8:2-6) Anayenera kuphunzira m’lingaliro la kusabwereza zophophonya zawo zakale.

Wolemba wina anati: “Munthu wochenjera apindula ndi zokumana nazo za iye mwini, wanzeru ndi zokumana nazo za ena.” Pamene kuli kwakuti Mose analimbikitsa anthu a Israyeli kupindula mwa kulingalira za zophophonya zawo zakale, mtumwi Paulo analimbikitsa ena​—mpingo wa ku Korinto wa m’zaka za zana loyamba ndiponso, m’lingaliro lalikulu, ifeyo​—kutengapo phunziro pa cholembedwa cha mbiri chimodzimodzicho. Iye analemba kuti: ‘Koma izi zinachitika kwa iwowa [Aisrayeli] monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife.’ (1 Akorinto 10:11) Yesu Kristu ankaganizira chochitika chinanso cha m’Baibulo ndi kufunikira kwa kutengapo phunziro pamene anati: “Kumbukirani mkazi wa Loti.” (Luka 17:32; Genesis 19:1-26) Wandakatulo ndi wafilosofi wachingelezi Samuel Taylor Coleridge analemba kuti: “Ngati anthu anali kuphunzira pa zochitika zakale, zikanatiphunzitsa maphunziro abwino chotani nanga!”

Kudzichepetsa ndi Kuyamikira

Chachitatu, kukumbukira kungatichititse kukhala ndi mikhalidwe yomwe imakondweretsa Mulungu ya kudzichepetsa ndi kuyamikira. Pamene tisangalala ndi mbali zambiri za paradaiso wathu wauzimu wa padziko lonse, tisaiŵaletu kuti maziko ake ndi njerwa zomangira zakutizakuti. Zimenezi zimaphatikizapo kukhulupirika, chikondi, kudzimana, kulimba mtima poyang’anizana ndi nsautso, kupirira, kuleza mtima, ndi chikhulupiriro​—mikhalidwe imene inasonyezedwa ndi abale ndi alongo athu achikristu amene zaka makumi ambiri zapitazo anatsegulira ntchitoyi m’maiko osiyanasiyana. Potsiriza lipoti lake la mbiri ya anthu a Mulungu amakono ku Mexico, 1995 Yearbook of Jehovah’s Witnesses inati: “Kwa anthu amene anayamba kugwirizana ndi Mboni za Yehova posachedwa, ziyeso zimene zinagwera amene anagaŵanamo kutsegulira ntchitoyi ku Mexico zingakhale zodabwitsa. Iwo azoloŵera paradaiso wauzimu mmene muli chakudya chauzimu chochuluka, mmene muli zikwi mazana ambiri za anzawo owopa Mulungu, ndi mmene utumiki wa Mulungu ukuchitidwa m’njira yolinganizidwa bwino kwambiri.”

Nthaŵi zambiri otsegulira ntchito oyamba amenewo ankagwira ntchito ali okha kapena m’timagulu tokhala kwatokha. Iwo anayang’anizana ndi kusungulumwa, kusoŵeka kwa zinthu zofunikira, ndi ziyeso zina zazikulu za kusunga umphumphu pamene analimbikira kulengeza uthenga wa Ufumu. Ngakhale kuti ambiri a atumiki akale ameneŵa anamwalira, nkotonthoza kwambiri chotani nanga kudziŵa kuti Yehova amakumbukira utumiki wawo wokhulupirika! Mtumwi Paulo anatsimikiza zimenezi, pamene analemba kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Ngati Yehova amakumbukira moyamikira, kodi ifeyo sitiyenera kuchita mofananamo mumzimu wachiyamikiro?

Awo amene anayamba choonadi posachedwa angapeze chidziŵitso cha mbiri chimenechi m’chofalitsa chakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom.a Ndiponso, ngati tili ndi mwaŵi wa kukhala m’banja kapena mumpingo wachikristu umene ziŵalo zake zikuphatikizapo abale ndi alongo achikulire amene atumikira kwa nthaŵi yaitali, tikulimbikitsidwa mumzimu wa Deuteronomo 32:7 kuti “kumbukirani masiku akale, zindikirani zaka za mibadwo yambiri; funsani atate wanu, adzakufotokozerani; akulu anu, adzakuuzani.”

Inde, kukumbukira zochita zakale za kudzipereka kwaumulungu kungatisonkhezere kupitiriza kupirira mwachimwemwe mu utumiki wathu wachikristu. Ndiponso, mbiri ili ndi maphunziro amene tifunikira kuphunzira. Ndipo kusinkhasinkha ponena za paradaiso wathu wauzimu wodalitsidwa ndi Mulungu kumakulitsa mikhalidwe yoyenera ya kudzichepetsa ndi kuyamikira. Zoonadi, “kumbukirani masiku apitawo.”

[Mawu a M’munsi]

a Chofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena