NKHANI YOPHUNZIRA 34
‘Pitirizani Kuyenda M’choonadi’
‘[Pitirizani] kuyendabe m’choonadi.’—3 YOH. 4.
NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi kukambirana mmene tinayambira “choonadi” kumatithandiza bwanji?
“KODI munayamba bwanji choonadi?” N’zosakayikitsa kuti mwakhala mukufunsidwa funso limeneli kambirimbiri. Limeneli ndi limodzi mwa mafunso amene Mkhristu mnzathu angatifunse tikamafuna kudziwana. Timafuna kudziwa mmene abale ndi alongo athu anayambira kudziwa komanso kukonda Yehova ndipo ifenso timasangalala kuwafotokozera mmene timasangalalira chifukwa chodziwa choonadi. (Aroma 1:11) Kukambirana zimenezi kumatithandiza kupitiriza kumaona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali. Ndipo zikatere timakhala otsimikiza mtima kuti tipitirize ‘kuyendabe m’choonadi,’ zomwe zikutanthauza kupitirizabe kuchita zinthu zimene zingachititse kuti Yehova azisangalala nafe komanso kutidalitsa.—3 Yoh. 4.
2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Munkhaniyi, tikambirana zifukwa zina zomwe zimatichititsa kuti tizikonda choonadi. Kenako tikambirana zimene tingachite kuti tipitirize kusonyeza kuti timakonda mphatso yamtengo wapataliyi. N’zosakayikitsa kuti kukambirana zimenezi kutithandiza kuti tiziyamikira kwambiri zomwe Yehova anachita potithandiza kudziwa choonadi. (Yoh. 6:44) Kutilimbikitsanso kuti tizifunitsitsa kuuza ena choonadichi.
CHIFUKWA CHAKE TIMAKONDA “CHOONADI”
3. Kodi chifukwa chachikulu chomwe chimatichititsa kukonda choonadi ndi chiti?
3 Pali zifukwa zambiri zimene zimatichititsa kukonda choonadi. Chifukwa chachikulu ndi chakuti timakonda Yehova Mulungu, yemwe ndi mwiniwake wa choonadicho. Kudzera m’Mawu ake Baibulo, tinafika pomudziwa monga Atate wathu wakumwamba yemwe amatisamalira mwachikondi, osati kungomudziwa monga Mlengi wamphamvuyonse yemwe analenga kumwamba ndi dziko lapansi. (1 Pet. 5:7) Timadziwa kuti Mulungu wathu ndi “wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.” (Eks. 34:6) Yehova amakonda chilungamo. (Yes. 61:8) Zimamupweteka akamationa tikuvutika ndipo ndi wokonzeka komanso wofunitsitsa kudzathetsa mavuto onse pa nthawi yoyenera. (Yer. 29:11) Zimenezitu ndi zosangalatsa. Mpake kuti timakonda kwambiri Yehova.
Choonadi cha M’Baibulo Chili Ngati . . . Nangula
Mofanana ndi nangula yemwe amathandiza kuti boti lisamayendeyende, chiyembekezo chathu chimatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika tikamakumana ndi mayesero. Choonadi cha m’Baibulo chimatithandizanso kuti tiziuza ena chiyembekezo chathu cham’tsogolo (Onani ndime 4-7)
4-5. N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo anayerekezera chiyembekezo chathu ndi nangula?
4 Kodi n’chifukwa chinanso chiti chomwe chimatichititsa kukonda choonadi? Choonadi chimatithandiza m’njira zambiri. Tiyeni tiganizire chitsanzo. Choonadi cha m’Baibulo chimaphatikizapo chiyembekezo chathu cham’tsogolo. Pofuna kusonyeza kufunika kwa chiyembekezo chimenechi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Chiyembekezo chimene tili nachochi chili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika.” (Aheb. 6:19) Monga mmene nangula amachititsira kuti boti lisayendeyende, chiyembekezo chathu chingatithandize kuti tikhalebe olimba tikakumana ndi mayesero.
5 Pamenepa Paulo ankafotokoza za chiyembekezo chopita kumwamba chomwe Akhristu odzozedwa ali nacho. Koma zimene ananenazi zikukhudzanso anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala m’paradaiso padzikoli. (Yoh. 3:16) Kunena zoona, kuphunzira za chiyembekezo cha moyo wosatha kwatithandiza kuti tikhale ndi moyo watanthauzo.
6-7. Kodi kudziwa choonadi chonena zam’tsogolo kunathandiza bwanji Yvonne?
6 Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Yvonne. Iye sanakulire m’banja la Mboni ndipo ali mwana ankaopa imfa. Iye amakumbukirabe mawu ena amene anawerenga omwe ankamusowetsa mtendere akuti: “Tsiku lina sitidzaonanso mawa.” Yvonne anati: “Mawu amenewa ankachititsa kuti ndizikanika kugona usiku n’kumangoganizira zam’tsogolo. Ndinkaganizira kuti, ‘Umu si m’mene moyo uyenera kukhalira. N’chifukwa chiyani ndili ndi moyo?’ Ndinkaganiza zimenezi chifukwa sindinkafuna kufa.”
7 Kenako asanakwanitse zaka za m’ma 20, Yvonne anakumana ndi a Mboni za Yehova. Iye anati: “Ndinayamba kukhulupirira kuti ndili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli.” Kodi kuphunzira choonadi kunamuthandiza bwanji mlongo wathuyu? Iye anawonjezera kuti: “Sindimalepheranso kugona chifukwa chodera nkhawa zam’tsogolo kapena imfa.” N’zoonekeratu kuti Yvonne amaona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali ndipo amasangalala kuuza ena chiyembekezo chimene ali nacho.—1 Tim. 4:16.
Choonadi cha M’Baibulo Chili Ngati . . . Chuma
Kutumikira Yehova panopa komanso kukhala ndi chiyembekezo chodzachita zimenezo mpaka kalekale mu Ufumu wake kuli ngati chuma. N’kofunika kwambiri kuposa zilizonse zomwe tingasiye (Onani ndime 8-11)
8-9. (a) Kodi munthu wina wam’fanizo la Yesu, ankaona bwanji chuma chomwe anapeza? (b) Kodi inuyo mumaona bwanji choonadi?
8 Choonadi cha m’Baibulo chimaphatikizaponso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yesu anayerekezera choonadi cha Ufumuwo ndi chuma chobisika. Pa Mateyu 13:44, iye anati: “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m’munda, chimene munthu anachipeza n’kuchibisa. Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.” Onani kuti munthu wotchulidwa palembali sikuti ankafunafuna chumacho. Koma atachipeza analolera kusiya zinthu zambiri kuti akhale nacho. Ndipotu anagulitsa chilichonse chimene anali nacho. Chifukwa chiyani? Ankadziwa kuti chumacho chinali chamtengo wapatali kwambiri kuposa chilichonse chomwe anasiya.
9 Kodi umu ndi mmene inunso mumaonera choonadi? Sitikukayikira kuti ndi mmene mumaonera. Timadziwa kuti palibe chimene dzikoli lingatipatse, chomwe tingayerekezere ndi chimwemwe chimene timapeza chifukwa chotumikira Yehova panopa poyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu. Mwayi wokhala naye pa ubwenzi ndi wamtengo wapatali kuposa chilichonse chomwe tingafunike kusiya. Timasangalala kwambiri ‘tikamamukondweretsa pa chilichonse.’—Akol. 1:10.
10-11. Kodi n’chiyani chinathandiza Michael kuti asinthe moyo wake?
10 Ambirife tinasintha zinthu zambiri kuti tizisangalatsa Yehova. Ena anasiya ntchito zapamwamba m’dzikoli. Enanso anasiya kufunafuna chuma. Palinso ena omwe ataphunzira za Yehova anasinthiratu moyo wawo. Izi ndi zomwe Michael anachita. Iye sanakulire m’banja la Mboni ndipo ali wachinyamata anaphunzira karati. Michael anati: “Ndinkasangalala kuti ndizioneka kuti ndine munthu wamphamvu ndipo nthawi zina ndinkaona kuti palibe amene angandigonjetse.” Koma atayamba kuphunzira Baibulo, Michael anadziwa mmene Yehova amaonera zachiwawa. (Sal. 11:5) Ponena za banja limene linkamuphunzitsa Baibulo, iye anati: “Iwo sanandiuzepo kuti ndisiye karati. Ankangopitiriza kundiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo.”
11 Pamene ankaphunzira zambiri zokhudza Yehova, m’pamenenso anayamba kumukonda kwambiri. Iye anakhudzidwa kwambiri ndi mmene Yehova amachitira zinthu mwachifundo ndi atumiki ake. Patapita nthawi, Michael anazindikira kuti ankafunika kusintha zinthu pa moyo wake. Iye anati: “Ndinkadziwa kuti zikhala zovuta kwambiri kuti ndisiye karati. Koma ndinkadziwanso kuti kuchita zimenezi kusangalatsa Yehova ndipo sindinkakayikira kuti kutumikira Yehova ndi kofunika kwambiri kuposa chilichonse chimene ndingasiye.” Michael amayamikira choonadi chamtengo wapatali chomwe anapeza ndipo zimenezi ndi zomwe zinamuchititsa kusintha kwambiri moyo wake.—Yak. 1:25.
Choonadi cha M’Baibulo Chili Ngati . . . Nyale
Nyale imatithandiza kuti tizitha kuona kumene tikupita mumdima. Mofanana ndi zimenezi, Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tizidziwa zoyenera kuchita m’dziko lam’dimali lomwe wolamulira wake ndi Satana (Onani ndime 12-13)
12-13. Kodi choonadi cha m’Baibulo chinathandiza bwanji Mayli?
12 Pofuna kusonyeza kuti choonadi ndi chamtengo wapatali, Baibulo limachiyerekezera ndi nyale yomwe imaunikira mumdima. (Sal. 119:105; Aef. 5:8) Mayli, wa ku Azerbaijan, amayamikira kwambiri chifukwa cha mmene Mawu a Mulungu amuthandizira. Iye anakulira m’banja limene makolo ake anali m’zipembedzo zosiyana. Bambo ake anali a Chisilamu ndipo mayi ake anali a Chiyuda. Iye anati: “Ngakhale kuti sindinkakayikira kuti Mulungu alipo, panali nkhani zina zomwe sindinkazimvetsa. Ndinkadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu analenga anthu? Komanso pali phindu lanji kuti munthu azunzike kwa moyo wake wonse kenako n’kukawotchedwanso kumoto mpaka kalekale?’ Popeza anthu amanena kuti chilichonse chomwe chimachitika ndi chifuniro cha Mulungu, ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu amasangalala kumangoonerera anthu akuvutika?’”
13 Mayli anapitiriza kufufuza mayankho a mafunso amene anali nawo. Patapita nthawi, iye anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndipo anakhala wa Mboni za Yehova. Iye anati: “Kuona mmene Baibulo linkafotokozera zinthu momveka bwino kunandithandiza kuti ndiyambe kusangalala. Kuphunzira mfundo zodalirika zopezeka m’Mawu a Mulungu kumandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wamumtima.” Mofanana ndi Mayli, timatamanda Yehova ‘amene anatiitana kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.’—1 Pet. 2:9.
14. Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri choonadi? (Onaninso bokosi lakuti, “Zinthu Zinanso Zomwe Zimayerekezeredwa Ndi Choonadi.”)
14 Zimenezi ndi zitsanzo zochepa chabe zosonyeza kuti choonadi ndi chamtengo wapatali. Sitikukayikira kuti pali zitsanzo zinanso zimene inu mukuzidziwa. Bwanji osakonza zoti mukamaphunzira panokha mufufuze zifukwa zina zomwe zimatichititsa kuti tizikonda choonadi? Tikamakonda kwambiri choonadi, m’pamenenso tingafufuze njira zina zosonyezera kuti timachikonda.
MMENE TIMASONYEZERA KUTI TIMAKONDA CHOONADI
15. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe tingasonyezere kuti timakonda choonadi?
15 Tingasonyeze kuti timakonda choonadi pophunzira Baibulo nthawi zonse komanso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Ndipotu kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yaitali bwanji, nthawi zonse pamakhala zambiri zoti tiphunzire. Nsanja ya Olonda yoyambirira inanena kuti: “Mofanana ndi kaduwa komwe kali kokhakokha m’chipululu, m’dzikoli muli mfundo zambiri zabodza zomwe zimachititsa kuti kukhale kovuta kuzindikira choonadi. Kuti munthu achipeze, afunika kufufuza mosamala. . . . Kuti akhale nacho, afunika kuchita khama. Munthu sayenera kungokhutira ndi duwa la choonadi limodzi lomwe wapeza. . . . Amafunika kupitiriza kufufuza kuti apeze mfundo zambiri za choonadi.” Kuphunzira kumafuna khama, koma n’kothandiza kwambiri.
16. Kodi ndi njira iti imene mumaona kuti imakuthandizani mukamaphunzira? (Miyambo 2:4-6)
16 Si tonse amene timakonda kuwerenga ndi kuphunzira. Koma Yehova amatilimbikitsa kuti ‘tizifunafuna’ komanso “kufufuza” kuti timvetse bwino mfundo zozama za choonadi. (Werengani Miyambo 2:4-6.) Tikamachita zimenezi, nthawi zonse timapindula. Pofotokoza zimene amachita akamawerenga Baibulo, Corey ananena kuti amaganizira zimene zili pavesi lililonse palokha. Iye anafotokoza kuti: “Ndimawerenga mawu a m’munsi aliwonse komanso kufufuza mavesi ena ofotokoza mfundo yofanana ndi ya vesilo ndiponso zinthu zina zowonjezereka. . . . Kugwiritsa ntchito njira imeneyi kumandithandiza kuti ndiphunzire zambiri.” Kaya timagwiritsa ntchito njira imeneyi kapena ina, timasonyeza kuti timakonda choonadi tikamapatula nthawi yathu komanso kuchita khama kuti tichiphunzire.—Sal. 1:1-3.
17. Kodi kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi kumatanthauza chiyani? (Yakobo 1:25)
17 Komabe timadziwa kuti kungophunzira choonadi si kokwanira. Kuti tipindule mokwanira, tiyenera kumachita zinthu mogwirizana ndi choonadicho, kapena kuti kugwiritsa ntchito mfundo zake pa moyo wathu. Tikamachita zimenezo m’pamene timapeza chimwemwe chenicheni. (Werengani Yakobo 1:25.) Kodi tingadziwe bwanji kuti timachita zinthu mogwirizana ndi choonadi? M’bale wina anafotokoza kuti tingachite zimenezo podzifufuza n’kuona mbali zimene tikuchita bwino komanso zimene tiyenera kusintha. Mtumwi Paulo anafotokoza mfundoyi motere: “Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenera m’njira yomweyo.”—Afil. 3:16.
18. N’chifukwa chiyani timayesetsa kuti ‘tipitirize kuyendabe m’choonadi’?
18 Tangoganizirani madalitso omwe timapeza chifukwa choyesetsa kuti ‘tipitirize kuyendabe m’choonadi.’ Sikuti choonadi chimangotithandiza kukhala ndi moyo wabwino koma chimatithandizanso kuti tizisangalatsa Yehova ndi Akhristu anzathu. (Miy. 27:11; 3 Yoh. 4) Kunena zoona, zimenezi ndi zifukwa zabwino zotichititsa kuti tizikonda choonadi komanso kumachita zinthu mogwirizana ndi choonadicho.
NYIMBO NA. 144 Yang’ananibe Pamphoto
a Nthawi zambiri tikamanena za “choonadi” timatanthauza zimene timakhulupirira kapenanso zimene timachita pa moyo wathu monga Akhristu. Kaya tangophunzira kumene choonadi kapena tinayamba kalekale, tingapindule kwambiri ngati titaganizira chifukwa chake timakonda choonadicho. Tikamachita zimenezi, tidzakhala otsimikiza mtima kuti tizisangalatsa Yehova.