Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JANUARY 5-11
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 17-20
“Zimene Zidzachitikire Amene Akutilanda Zinthu”
“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”
Kunena zoona anthuwa anachita bwino kwambiri kusintha chonchi. Paja Baibulo limayerekezera anthu m’dzikoli ndi nyanja yowinduka yomwe ikukanika kukhala bata. (Yes. 17:12; 57:20, 21; Chiv. 13:1) Nkhani zandale zimagawanitsa anthu ndiponso zimayambitsa chiwawa koma ifeyo timapitiriza kukhala mwamtendere komanso mogwirizana. Popeza anthu ndi ogawikana m’dzikoli, Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri akamaona mgwirizano wa anthu ake.—Werengani Zefaniya 3:17.
Musakhale Mbali ya Dzikoli
Mwina panopa m’dziko lathu anthu satikakamiza kuchita ndale. Koma tiyenera kudziwa kuti pamene mapeto akuyandikira, tikhoza kukumana ndi mayesero pa nkhaniyi. M’dzikoli, anthu ambiri ndi “osafuna kugwirizana ndi anzawo” komanso “osamva za ena.” Choncho m’posavuta kuti anthu akhale ogawanika. (2 Tim. 3:3, 4) M’mayiko ena, zinthu zikasintha chifukwa cha ndale, abale ndi alongo amakumana ndi mavuto osayembekezereka. Choncho tiyenera kukonzekera panopa kuti tisakhale mbali ya dzikoli. Tikutero chifukwa chakuti tikangokhala mpaka pamene mayeserowo afika, tikhoza kupezeka tagonja. Tiyeni tsopano tikambirane mfundo 4 zimene zingatithandize pokonzekera kuti tisalowerere ndale.
ip-1 198 ¶20
Uphungu wa Yehova Wotsutsa Amitundu
Zotsatira zake? Yesaya akuti: “Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanache [“usanafike m’mawa,” NW], iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu.” (Yesaya 17:14) Ambiri akulanda zinthu anthu a Yehova, kuwachitira nkhanza ndi kusawalemekeza. Chifukwa choti sali, ndipo safuna kukhala mbali ya zipembedzo zikuluzikulu za padziko lapansi, otsutsa atsankho ndi otengeka maganizowa, amaona kuti Akhristu oona ndi osavuta kuwambwandira. Koma anthu a Mulungu amakhulupilira kuti “m’mawa” ukuyandikira kwambiri, pamene masautso awo adzatha.—2 Atesalonika 1:6-9; 1 Petro 5:6-11.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 1
20:2-5—Kodi Yesaya anayendadi ali maliseche kwa zaka zitatu? N’kutheka kuti Yesaya anangochotsa chovala chake chapamwamba n’kumayenda ali ndi zovala zochepa chabe.—1 Samueli 19:24, mawu am’munsi.
JANUARY 12-18
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 21-23
Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Zimene Zinachitikira Sebina?
Mulungu Amatilangiza Chifukwa Chotikonda
Kuti timvetse ubwino wa chilango tiyeni tsopano tikambirane za anthu awiri amene Yehova anawapatsa chilango. Woyamba ndi Sebina, yemwe anakhalapo pa nthawi ya Mfumu Hezekiya, ndipo wachiwiri ndi Graham, yemwe ndi m’bale wamasiku ano. Sebina anali ndi udindo waukulu chifukwa Baibulo limanena kuti anali “kapitawo woyang’anira nyumba ya mfumu” ndipo mfumu yake iyenera kuti inali Hezekiya. (Yes. 22:15) Koma chomvetsa chisoni n’chakuti anayamba kudzikuza ndipo ankafuna kuti anthu azimutama. Anafika mpaka podzipangira manda apamwamba ochita kugoba komanso ankayenda pa “magaleta ankhondo aulemerero.”—Yes. 22:16-18.
Mulungu ataona kuti Sebina ali ndi mtima wofuna kutamandidwa, ‘anamuchotsa pa udindo wake’ ndipo m’malomwake anaikapo Eliyakimu. (Yes. 22:19-21) Kusinthaku kunachitika pa nthawi imene Mfumu Senakeribu ankafuna kuwononga Yerusalemu. Patapita nthawi, mfumuyi inatuma akuluakulu a boma limodzi ndi asilikali ambiri kuti akaopseze Ayuda komanso akachititse Hezekiya kungonena kuti wagonja. (2 Maf. 18:17-25) Ndiyeno Eliyakimu ndi amene anatumidwa kuti akalankhule ndi anthuwo. Koma anapita ndi anthu ena awiri ndipo mmodzi mwa iwo anali Sebina, yemwe pa nthawiyo anali mlembi. Izitu zikusonyeza kuti Sebina sanakwiye koma anadzichepetsa n’kuvomera udindo wotsikirapo. Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhaniyi? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene tikuphunzirapo.
Choyamba, Sebina anachotsedwa pa udindo wake. Izi zikutsimikizira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.” (Miy. 16:18) Ngati muli ndi udindo woonekera mumpingo, kodi mudzayesetsa kukhala odzichepetsa? Kodi muzilemekeza Yehova chifukwa cha zabwino zimene muli nazo kapena zimene mwachita? (1 Akor. 4:7) Paja mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.”—Aroma 12:3.
Mulungu Amatilangiza Chifukwa Chotikonda
Chachiwiri n’chakuti zimene Mulungu anachitira Sebina sizinkasonyeza kuti Sebinayo ndi wokanika. (Miy. 3:11, 12) Mfundo imeneyi ndi yothandiza kwa anthu amene aimitsidwa pa udindo masiku ano. M’malo mokwiya, ndi bwino kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse pa nthawi imeneyi n’kumaona kuti chilango chimene apatsidwacho ndi umboni wakuti Yehova amawakonda. Tisaiwale kuti Yehova sationa kuti ndife okanika ngati tili ndi mtima wodzichepetsa. (Werengani 1 Petulo 5:6, 7.) Nthawi zina Yehova amaumba anthu powapatsa chilango. Choncho tiyeni tizikhala ngati dongo loumbika m’manja mwake.
Mulungu Amatilangiza Chifukwa Chotikonda
Chachitatu, zimene Yehova anachitira Sebina n’zothandiza kwa anthu amene ali ndi udindo wopereka chilango monga makolo ndi akulu. Tikutero chifukwa chakuti chilango cha Yehova chimasonyeza kuti amadana ndi zoipa koma pa nthawi imodzimodziyo chimasonyeza kuti amaganizira munthu amene walakwitsa zinthuyo. Choncho ngati ndinu makolo kapena mkulu, muyenera kutsanzira Yehova. Mukamapereka chilango muzisonyeza kuti mumadana ndi zoipa koma mumaona zabwino zimene mwana wanu kapena Mkhristu mnzanu amachita—Yuda 22, 23.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 1
21:1—Ndi dera liti lomwe likutchedwa kuti “chipululu chimene chili ngati nyanja”? Ngakhale kuti Babulo sanali kufupi ndi nyanja ina iliyonse, ndiye amene akutchulidwa m’njira imeneyi. Akutchedwa choncho chifukwa choti madzi a m’mitsinje ya Firate ndi Tigirisi ankasefukira m’deralo chaka ndi chaka n’kumapanga malo alowe ooneka ngati “kunyanja.”
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwyp nkhani Na. 71
Kodi Ndingasankhe Bwanji Munthu Wabwino Woti Ndizimutsanzira?
Kodi mungasankhe bwanji?
Pali njira ziwiri zomwe mungagwiritse ntchito posankha munthu womutsanzira.
1. Mungasankhe khalidwe linalake lomwe mumafuna mutakhala nalo, kenako pezani munthu amene mumasirira yemwe ali ndi khalidwelo.
2. Mungasankhe munthu yemwe mumamusirira kenako mungasankhe khalidwe labwino linalake lomwe ali nalo limene mukufuna mutakhala nalo.
Gawo la zoti muchite lomwe lili m’nkhani ino lingakuthandizeni kuchita zimenezi.
Anthu omwe mungawatsanzire angakhale:
Achinyamata anzanu: “Ndinasankha munthu yemwe ndikufuna kutengera makhalidwe ake kuti akhale mnzanga wapamtima. Iye amapeza nthawi yosamalira anthu ena. Ndi wamng’ono kwa ine koma ali ndi makhalidwe abwino amene ineyo ndilibe, ndipo zimenezi zimandichititsa kuti ndiyesetse kumutsanzira.”—Miriam.
Akuluakulu. Angakhale makolo anu kapenanso Akhristu anzanu. “Kunena zoona makolo anga ndi zitsanzo zabwino. Ali ndi makhalidwe abwino. Ngakhale kuti ndimaona zolakwa zawo, koma ndimadziwanso kuti ndi okhulupirika. Ndikukhulupirira kuti nanenso ndikadzakhala ndi ana nawonso adzaona kuti ndine chitsanzo chawo chabwino.”—Annette.
Anthu otchulidwa m’Baibulo. Ndinasankha anthu amakhalidwe abwino angapo kuchokera m’Baibulo monga Timoteyo, Rute, Yobu, Petulo ndi kamtsikana ka Chiisiraeli pa zifukwa zosiyanasiyana. Ndikamaphunzira zambiri zokhudza anthu otchulidwa m’Baibulo m’pamene ndimaona kuti ndi enieni. Kuphunzira nkhani za m’buku lakuti Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo, kwandithandiza kwambiri. Komanso gawo lakuti ‘Zitsanzo Zabwino,’ lomwe lili m’mabuku akuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa landithandizanso kwambiri.”—Melinda.
Zimene Zingakuthandizeni: Musangokhala ndi munthu mmodzi yemwe mukufuna kumutsanzira. Mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Muzionetsetsa amene akuyenda mogwirizana ndi chitsanzo chimene tinakupatsani.”—Afilipi 3:17.
Kodi mukudziwa? Inunso mukhoza kukhala chitsanzo chabwino cha munthu wina. Baibulo limati: “Ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.”—1 Timoteyo 4:12.
“Ngakhale kuti nanu mumafunika kusintha zinthu zina koma mukhozabe kuthandiza ena kutengera makhalidwe anu abwino. Simungadziwe kuti ndi anthu angati amene amaona makhalidwe anuwo ndiponso kuti zimene mungayankhule zingathandize bwanji munthu wina.”—Kiana.
JANUARY 19-25
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 24-27
“Uyu Ndi Mulungu Wathu”
“Taonani! Uyu Ndi Mulungu Wathu”
Kodi munaonapo mwana akulozera anzake bambo ake ndiyeno mosangalala ndiponso monyadira n’kunena kuti, “Bambo anga awo”? Atumiki a Mulungu ali ndi zifukwa zomveka zowachititsa kuti azimuonanso choncho Yehova. Baibulo linaneneratu za nthawi imene anthu okhulupirika adzafuule kuti: “Taonani! Uyu ndi Mulungu wathu.” (Yesaya 25:8, 9) Tikadziwa zambiri zokhudza makhalidwe a Yehova, m’pamenenso timayamba kumuona kuti ndi Bambo wathu wabwino kwambiri.
Yesu Anapereka Chakudya Modabwitsa
Pamene Yesu anatiuza kuti tizipempherera “chakudya chimene tikufunikira lero,” anatiuzanso kuti tizipemphera kuti zofuna za Mulungu “zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.” (Mat. 6:9-11) Kodi n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamva zimenezi? Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amafuna kuti padziko lapansi padzakhale chakudya chabwino. Lemba la Yesaya 25:6-8 limasonyeza kuti mu Ufumu wa Mulungu, padzikoli padzakhala chakudya chochuluka komanso chabwino. Lemba la Salimo 72:16 limanena kuti: “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.” Kodi mumadziyerekezera mukugwiritsa ntchito tiriguyu kuphika chakudya chimene mumachikonda kapena kuyesa kuphika zakudya zina zomwe simunaphikepo? Kuwonjezera pamenepo, mungadzalime minda yanuyanu ya mpesa n’kumadya zipatso zake. (Yes. 65:21, 22) Ndipo aliyense padzikoli adzakhala ndi zinthu ngati zimenezi.
Madalitso Amene Timapeza Chifukwa cha Chikondi cha Yehova
Taganizirani mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso. Simudzadanso nkhawa chifukwa cha matenda kapena imfa. (Yes. 25:8; 33:24) Yehova adzakupatsani zinthu zonse zoyenera zimene mumalakalaka. Kodi inuyo mudzafuna kuphunzira zinthu ziti? Za sayansi, nyimbo kapena zojambula? N’zoonekeratu kuti padzafunika akatswiri oona za mapulani ndi zomangamanga komanso a zaulimi. Padzafunikanso anthu ogwira ntchito zina monga kukonza zoonongeka, kuphika, kupanga zipangizo zogwirira ntchito komanso kudzala maluwa. (Yes. 35:1; 65:21) Popeza kuti tidzakhala ndi moyo wosatha, tidzatha kuphunzira luso lililonse lomwe tingadzafune.
Zidzakhalatu zosangalatsa kulandira anthu amene adzaukitsidwe. (Mac. 24:15) Tidzasangalalanso kuphunzira zambiri zokhudza Yehova kudzera m’zinthu zimene analenga. (Sal. 104:24; Yes. 11:9) Chosangalatsa kwambiri n’chakuti tizidzalambira Yehova popanda kudziimba mlandu chifukwa chakuti talakwitsa zinazake. Kodi mungalolere kutaya zonsezi chifukwa chongofuna ‘kusangalala kwa nthawi yochepa pochita machimo’? (Aheb. 11:25) Simungafune kuchita zimenezo. Tingalolere kutaya chilichonse panopa kuti tidzapeze madalitso amenewa. Kumbukirani kuti zimene tikuyembekezera m’Paradaiso tsiku lina zidzachitikadi. Tizidzatere tili m’Paradaiso. Zimenezi sizikanatheka Yehova akanapanda kutikonda n’kupereka mphatso ya Mwana wake.
Mfundo Zothandiza
Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Lomwe Linatuluka mu 2013
Nkhani zina zinalembedwa ngati ndakatulo. Anthu amene analemba Baibulo, nkhani zambiri anazilemba ngati ndakatulo. M’zilankhulo zambiri, ndakatulo zimakhala ndi mawu omveka mofanana. Koma ndakatulo zachiheberi zimakhala ndi mawu otsutsana kapena mfundo zofanana. Ndipo ndakatulozi zimadziwika chifukwa cha mmene asanjira mfundo zake.
Poyamba mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi, buku la Yobu ndi la Masalimo linalembedwa mosonyeza kuti ndi ndakatulo kapena nyimbo. Kalembedwe kameneko kankathandiza kuti munthu aziona mosavuta mfundo zikuluzikulu komanso kuti azitha kuzikumbukira. M’Baibulo lokonzedwansoli, mabuku a Miyambo, Nyimbo ya Solomo komanso machaputala ena a m’mabuku aulosi, anawalembanso ngati ndakatulo. Anachita zimenezi chifukwa ndi zogwirizana ndi mmene olemba Baibulo analembera mabukuwa. Chitsanzo ndi pa Yesaya 24:2, pamene mzera uliwonse uli ndi mawu awiri otsutsana. Yesaya analemba chonchi pofuna kutsindika mfundo yakuti palibe angathawe chiweruzo cha Mulungu. Choncho mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso analemba mavesi ngati amenewa mwandakatulo pofuna kuthandiza owerenga kuona kuti cholinga cha wolembayo sichinali kungobwereza mawu, koma ankafuna kutsindika uthenga wake.
M’Chiheberi ndi zovuta kusiyanitsa ngati nkhani yalembedwa ngati ndakatulo kapena ayi ndipo omasulira Mabaibulo amasiyana maganizo pa nkhaniyi. Choncho mavesi amasindikizidwa ngati ndakatulo kapena ayi potengera zimene omasulirawo asankha. Mavesi ena omwe sanalembedwe mwandakatulo amakhalanso ndi mawu ngati andakatulo, mawu ophiphiritsa komanso zinthu zina zothandiza kutsindika mfundo yofunika.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwbq nkhani Na. 160
N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu?
Yankho la m’Baibulo
Nthawi zambiri Baibulo limatchula Yesu kuti ndi “Mwana wa Mulungu.” (Yohane 1:49) Mawu akuti “Mwana wa Mulungu,” akusonyeza kuti Mulungu ndiye Mlengi, Kasupe wa zamoyo zonse kuphatikizaponso Yesu. (Salimo 36:9; Chivumbulutso 4:11) Baibulo silinena kuti Mulungu anaberekadi mwana ngati mmene zimakhalira ndi anthu.
Baibulo limatchulanso angelo kuti ndi “ana a Mulungu woona.” (Yobu 1:6) Limanenanso kuti munthu woyambirira Adamu, anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Komabe, popeza kuti Yesu ndi woyambirira kulengedwa komanso kuti analengedwa ndi Mulungu weniweniyo, Baibulo likamanena za Yesu limati ndi Mwana wokondedwa kwambiri wa Mulungu.
JANUARY 26–FEBRUARY 1
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 28-29
Muzilemekeza Yehova ndi Milomo Yanu Komanso Mtima Wanu
ip-1 299 ¶23
Yesaya Akulosera ‘Ntchito Yachilendo’ ya Yehova
Atsogoleri achipembedzo a Yuda amanena kuti ndi ozindikira mwauzimu, koma iwo asiya kudalira Yehova. M’malo mwake akuphunzitsa maganizo awoawo opotozeka pa nkhani ya chabwino ndi choipa, kuti alungamitse zochita zawo zopanda chikhulupiriro ndi zonyansa komanso kuchititsa kuti anthu asakondedwe ndi Mulungu. Kudzera mu “ntchito yodabwitsa”—“ntchito yake yachilendo”—Yehova adzawafunsa kuti ayankhepo pa chinyengo chawo. Akuti: “Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m’kamwa mwawo, koma mtima wawo uli kutali ndi Ine, ndi mantha awo akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira; chifukwa chake, taonani, ndidzachitanso mwa anthu awa ntchito yodabwitsa, ngakhale ntchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu awo anzeru idzatha, ndi luntha la anthu awo ozindikira lidzabisika.” (Yesaya 29:13, 14) Zimene Yuda amati ndizo nzeru komanso kuzindikira zidzatha pamene Yehova adzathetseretu dongosolo lachiyuda lonse la chipembedzo champatuko pogwiritsa ntchito Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Babulo. Zimenezi zinachitikanso mu zaka 100 zoyambirira pamene atsogoleri achiyuda amene ankadzitchula kuti ndi anzeru anasocheretsa mtunduwo. Zofanana ndi zimenezi zidzachitikanso m’masiku athu ano pa Matchalitchi Achikhristu.—Mateyu 15:8, 9; Aroma 11:8.
Okonda Chilungamo Palibe Chowakhumudwitsa
Yesu ankadzudzula molimba mtima zochita zachinyengo za atsogoleri achipembedzo. Mwachitsanzo, iye anadzudzula chinyengo cha Afarisi omwe ankaona kuti kusamba m’manja n’kofunika kwambiri kuposa kusamalira makolo awo. (Mat. 15:1-11) N’kutheka kuti ophunzira ake anadabwa ndi zimene iye ananena. Choncho, iwo anamufunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti Afarisi akhumudwa ndi zimene mwanena zija?” Yesu anawayankha kuti: “Mbewu iliyonse imene sinabzalidwe ndi Atate wanga wakumwamba idzazulidwa. Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.” (Mat. 15:12-14) Ngakhale kuti zomwe Yesu ananena zinakwiyitsa atsogoleri achipembedzo, zimenezi sizinamulepheretse kulankhula choonadi.
Pitirizani Kukhala Alendo a Yehova Mpaka Kalekale
Anthu amene ‘amalankhula zoona mumtima mwawo,’ samayerekezera kukhala omvera akakhala pagulu n’kumaphwanya malamulo a Mulungu akakhala kwaokha. (Yes. 29:13) Amapewa kuchita zinthu mwachiphamaso. Munthu wachiphamaso amayamba kukayikira ngati malamulo a Yehova alidi anzeru. (Yak. 1:5-8) Munthu wotereyo samvera Yehova pa zinthu zimene iyeyo amaziona kuti ndi zing’onozing’ono. Akaona kuti sanakumane ndi mavuto chifukwa cha kusamverako, amalimba mtima n’kumapitirizabe kuphwanya malamulo a Mulungu ndipo kulambira kwake kumakhala kwachinyengo. (Mlal. 8:11) Koma ife timafuna kukhala oona mtima pa zinthu zonse.
Mfundo Zothandiza
it “Arieli” ¶1; it “Arieli” Na. 3
Arieli
(Arieli) [Malo Osonkhapo Moto a Paguwa Lansembe la Mulungu; kapena kuti, Mkango wa Mulungu].
3. Dzina lodabwitsali linagwiritsidwa ntchito ponena za Yerusalemu pa Yesaya 29:1, 2, 7. Ku Yerusalemu n’kumene kunali malo omwe panali kachisi wa Mulungu ndipo m’kachisimo munali guwa lansembe. Choncho tingati mzindawu unali malo osonkhapo moto a paguwa lansembe la Mulungu. Mzindawu unkafunikanso kukhala likulu la kulambira koyera kwa Yehova. Komabe, uthenga umene uli pa Yesaya 29:1-4 ndi woopsa ndipo ukusonyeza kuti Yerusalemu adzawonongedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E., pamene mzindawu udzakhale “malo osonkhapo moto a paguwa lansembe” m’njira yosiyana ndi yoyambayi: unali ngati mzinda umene munkayenda magazi a anthu ophedwa, umene ukuyaka komanso wodzadza ndi mitembo ya anthu ophedwa ndi motowo. Zimene zinachititsa mavutowa zatchulidwa pa vesi 9 mpaka 16. Komabe pa Yesaya 29:7, 8, pakusonyeza kuti mitundu yonse imene ikuchita nkhondo ndi Yerusalemu idzalephera kukwaniritsa cholinga chawo.
FEBRUARY 2-8
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 30-32
Pezani Chitetezo M’mapiko a Yehova
Yehova Ndiye Pothawirapo Pathu
Popeza Yehova ndiye pothawirapo pathu, timalimbikitsidwa ndi mawu akuti: “Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza [ndi linga, NW].” (Salmo 91:4) Mulungu amatiteteza monga mmene mbalame imachitira kuuluka motchingira ana ake kuwateteza. (Yesaya 31:5) ‘Amatifungatira ndi nthenga zake.’ Nthawi zambiri, “nthenga” za mbalame zimaimira mapiko ake. Imazigwiritsa ntchito kufungatira ana ake, kuwateteza ku zinthu zimene zingawawononge. Mofanana ndi ana a mbalame, ndife otetezeka kunsi kwa nthenga zophiphiritsa za Yehova chifukwa tathawira ku gulu lake loona lachikristu.—Rute 2:12; Salmo 5:1,11.
Yehova Adzakuthandizani pa Nthawi Yovuta
Zimene tiyenera kuchita. Muzipewa mtima wosafuna kucheza ndi anthu. Nthawi zambiri munthu akakhala payekha saganiza bwino chifukwa amangoganizira za iyeyo ndi mavuto amene akukumana nawo. Kaganizidwe kameneka kangachititse kuti asasankhe bwino zochita. (Miy. 18:1) N’zoona tonsefe timafunika kukhala patokha makamaka tikakumana ndi mavuto aakulu. Komabe tikakhala kwatokha kwa nthawi yaitali, timatalikirana ndi anthu amene Yehova angawagwiritse ntchito kuti atithandize. Choncho muzilola kuti anthu a m’banja lanu, anzanu komanso akulu akuthandizeni ngakhale kuti nthawi zina zimenezi zimakhala zovuta tikakumana ndi mavuto. Muziona kuti anthu amenewa ndi njira imene Yehova angagwiritse ntchito kuti akuthandizeni.—Miy. 17:17; Yes. 32:1,2.
Yehova “Adzakulimbitsani”
Kodi mungatani kuti chiyembekezo chanu chikhale champhamvu? Mwachitsanzo, ngati mukuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi, muziwerenga ndiponso kuganizira zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Paradaiso. (Yes. 25:8; 32:16-18) Muziganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Muziyerekezera muli m’dzikolo. Kodi mukuonamo ndani? Nanga mukumva zinthu zotani? Mumtima mwanu mukumva bwanji? Kuti mukhale ndi zinthu zambiri zoziganizira, muziyang’ana zithunzi zam’mabuku athu zosonyeza Paradaiso kapena kuonera mavidiyo a nyimbo monga zakuti, Dziko Latsopano Lomwe Likubwera, Dziko Latsopano Lili Pafupi kapena Ganizirani Nthawiyo. Tikamaganizira kwambiri za chiyembekezo chathu cha dziko latsopano, mavuto athu adzaoneka kuti ndi “akanthawi ndipo ndi opepuka.” (2 Akor. 4:17) Chiyembekezo chimene Yehova wakupatsani chingakuthandizeni kuti mupirire mayesero.
Mfundo Zothandiza
it “Chakudya” ¶6
Chakudya
Tanthauzo Lophiphiritsa. M’Baibulo mawu akuti “chakudya” amagwiritsidwa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Yoswa ndi Kalebe anauza Aisiraeli amene anasonkhana kuti Akanani “ali ngati chakudya kwa ife,” kutanthauza kuti anali osavuta kuwagonjetsa ndipo zimenezi zikanapatsa mphamvu Aisiraeliwo. (Nu 14:9) Mawuwa angagwiritsidwenso ntchito ponena za chisoni chachikulu chobwera chifukwa choti Yehova sakusangalala ndi munthu kapena anthu. Zimenezi zikuonekera bwino pa Salimo 80:5, lomwe ponena za m’Busa wa Aisiraeli Yehova, limati: “Mwawapatsa misozi kuti ikhale chakudya chawo.” Baibulo limanenanso kuti Yehova akupatsa anthu ake “mavuto kuti akhale chakudya chawo ndi kuponderezedwa kuti kukhale madzi awo akumwa,” zomwe zikuimira mavuto omwe adzakumane nawo akadzazunguliridwa ndi adani awo, ndipo mavutowo adzangokhala ngati chakudya komanso madzi.—Yes 30:20.
FEBRUARY 9-15
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 33-35
“Mʼmasiku Anu, Iye Adzachititsa Kuti Muzimva Kuti Ndinu Otetezeka”
Yehova Adzakuthandizani pa Nthawi Yovuta
Vuto limene tingakumane nalo. Tikakumana ndi mavuto aakulu timamva kupweteka mumtima, maganizo athu amasokonezeka ndipo sitingachite zinthu ngati mmene timachitira nthawi zonse. Tingakhale ngati sitima yomwe ikukankhidwira uku ndi uku ndi mphepo yamphamvu. Ana yemwe tamutchula kale uja ananena kuti Luis atamwalira ankaganiza zambiri. Iye anati: “Nthawi zina ndinkangodziona ngati wachabechabe ndipo ndinkangodzimvera chisoni. Koma kenako ndinkakwiya kwambiri ndikaganizira zoti wapita.” Kuwonjezera pamenepo, Ana ankangodziona kuti ali yekhayekha komanso ankakhala wokhumudwa chifukwa ankafunika kusankha zochita pa nkhani zimene Luis sankavutika nazo. Nthawi zina ankangodzimva ngati ali panyanja pomwe pali chimphepo chamkuntho. Kodi Yehova amatithandiza bwanji tikamamva chonchi?
Zimene Yehova amachita. Iye amatitsimikizira kuti adzatithandiza kuti tisagwedezeke. (Werengani Yesaya 33:6.) Sitima ikakumana ndi mphepo yamphamvu panyanja, imayamba kukankhidwira uku ndi uku ndipo zimakhala zoopsa. Koma sitima zina zimakhala ndi zinthu zina m’mbali mwake zomwe zimathandiza kuti sitima ikhazikike pamadzi. Zinthu zimenezi zimathandiza kuti sitimayo isamatengeketengeke, zomwe zimachititsa kuti anthu omwe akwera akhale otetezeka. Koma zinthu zambiri zomwe zimathandiza kuti sitima isamagwedezeke zimagwira bwino ntchito sitimayo ikamayenda. Mofanana ndi zimenezi, Yehova adzatithandiza kuti tisagwedezeke ngati tikupitirizabe kumutumikira mokhulupirika pamene tikukumana ndi mavuto.
Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Tikakumana ndi Mayesero
Zimene tingachite: Tizipempha Yehova kuti atipatse nzeru. Kuti tikwanitse kupirira mayesero athu mosangalala, choyamba tiyenera kupemphera kwa Yehova kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kusankha bwino zochita. (Werengani Yakobo 1:5.) Ndiye kodi tiyenera kutani ngati tikuona kuti sanayankhe pemphero lathu mwamsanga? Yakobo ananena kuti tiyenera ‘kumapemphabe’ kwa Mulungu. Yehova sakwiya nazo tikamapitirizabe kumupempha kuti atipatse nzeru ndipo samatinyoza. M’malomwake Atate wathu wakumwamba amatipatsa “mowolowa manja” tikamapempha kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kuti tipirire mayesero. (Sal. 25:12, 13) Yehova amaona mayesero amene tikukumana nawo, amakhudzidwa tikamavutika komanso ndi wokonzeka kutithandiza. Zimenezitu zimatithandiza kukhala osangalala. Koma kodi Yehova amatipatsa bwanji nzeru?
Yehova amatipatsa nzeru kudzera m’Mawu ake. (Miy. 2:6) Kuti tipeze nzeru zimenezi, tiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu komanso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Koma kuphunzira kokha sikokwanira, tiyenera kugwiritsira ntchito nzeru za Mulungu pa moyo wathu potsatira malangizo ake. Yakobo analemba kuti: “Muzichita zimene mawu amanena, osati kungomva chabe.” (Yak. 1:22) Tikamatsatira malangizo a Mulungu timakhala anthu amtendere, ololera komanso achifundo. (Yak. 3:17) Makhalidwe amenewa amatithandiza kuti tizipirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo koma n’kumakhalabe osangalala.
ip-1 352-355 ¶21-22
“Wokhalamo Sadzanena, Ine Ndidwala”
Komabe, ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwanso masiku ano. Anthu a Yehova akusangalalanso ndi kuchiritsidwa kwauzimu. Amasulidwa ku ziphunzitso zonyenga monga zakuti mzimu wa munthu sumafa, Utatu komanso moto wa helo. Amalandira malangizo owathandiza kukhala ndi makhalidwe abwino, owateteza ku chiwerewere ndiponso owathandiza kusankha zinthu mwanzeru. Ndipo chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu Khristu, ndi oyera pamaso pa Mulungu komanso akusangalala pokhala ndi chikumbumtima choyera. (Akolose 1:13, 14; 1 Petro 2:24; 1 Yohane 4:10) Kuchiritsidwa mwauzimu kumeneku kulinso ndi mapindu akuthupi. Mwachitsanzo, kupewa chiwerewere ndi kusuta fodya kumateteza Akhristu ku matenda opatsirana pogonana komanso mitundu ina ya khansa.—1 Akorinto 6:18; 2 Akorinto 7:1.
Padzakhalanso kukwaniritsidwa kwakukulu kwa mawu a pa Yesaya 33:24 pambuyo pa Armagedo, m’dziko latsopano la Mulungu. Mu ulamuliro wa Ufumu Waumesiya, anthu adzachiritsidwa mwakuthupi komanso mwauzimu pamlingo waukulu. (Chivumbulutso 21:3, 4) Posakhalitsa, dongosolo la zinthu la Satanali litawonongedwa, mosakayikira zozizwitsa ngati zija zimene Yesu anachita pamene anali padziko lapansi zidzachitika kuzungulira dziko lonse lapansi. Akhungu adzaona, ogontha adzamva, opunduka adzayenda! (Yesaya 35:5, 6) Zimenezi zidzatheketsa opulumuka chisautso chachikulu kutenga nawo mbali m’ntchito yaikulu yobwezeretsa dziko lapansi kukhala paradaiso.
Mfundo Zothandiza
Pitirizani Kuyenda pa “Msewu wa Chiyero”
Ena angaganize kuti, ‘Zimenezitu n’zochititsa chidwi. Koma kodi zomwe zinachitikira Ayuda kalekalezi zikutikhudza bwanji?’ Tinganene kuti zimatikhudza chifukwa nafenso tikuyenda pa “Msewu wa Chiyero.” Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tiyenera kupitiriza kuyenda pa “Msewu wa Chiyero” chifukwa umatithandiza kukhalabe m’Paradaiso wauzimu komanso udzatithandiza kupeza madalitso amene Ufumu udzabweretse m’tsogolo. (Yoh. 10:16) Kungoyambira mu 1919 C.E., amuna, akazi komanso ana mamiliyoni akhala akutuluka mu Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, ndipo ayamba kuyenda pamsewu wophiphiritsawu. N’zosakayikitsa kuti inuyo muli m’gulu limeneli. Ngakhale kuti anthu anayamba kuyenda pamsewu umenewu zaka pafupifupi 100 zapitazo, ntchito youkonza inayamba zaka zambiri m’mbuyo mwake.
FEBRUARY 16-22
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 36-37
“Usachite Mantha Chifukwa cha Mawu Amene Wamva”
it “Hezekiya” Na. 1 ¶14
Hezekiya
Senakeribu Analephera Kugonjetsa Yerusalemu. Mogwirizana ndi zimene Hezekiya ankayembekezera, Senakeribu ankafunitsitsa kugonjetsa Yerusalemu. Pamene Senakeribu ndi asilikali ake ankagonjetsa mzinda wa Lakisi womwe unali ndi mpanda wolimba kwambiri, anatumiza asilikali ena limodzi ndi akuluakulu a asilikaliwo kuti akauze anthu a ku Yerusalemu kuti angogonja. Rabisake (limene silinali dzina lake lenileni, koma la udindo wake monga msilikali), yemwe ankalankhula bwino Chiheberi, ndi amene ankalankhula m’malo mwa gulu la asilikalilo. Iye ankakuwa n’kumanena mawu onyoza Hezekiya komanso kunenera zachipongwe Yehova, kwinaku akudzitamanda kuti Yehova sangapulumutse Yerusalemu ngati mmene milungu ina inalepherera kupulumutsa anthu awo m’manja mwa mfumu ya Asuri.—2Mf 18:13-35; 2Mb 32:9-15; Yes 36:2-20.
ip-1 387 ¶10
Chikhulupiriro cha Mfumu Chifupidwa
Kenako kazembeyo akukumbutsa Ayudawo kuti pankhani ya nkhondo akuperewera momvetsa chisoni. Ndiyeno akuwalankhula mwamwano kuti: “Ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.” (Yesaya 36:8) Komabe, kodi zili n’kanthu kuti okwera pakavalo odziwa nkhondo a Yuda ndi ambiri kapena ochepa? Ayi, chifukwa chipulumutso cha Yuda sichidalira mphamvu yapamwamba ya anthu yomenya nkhondo. Lemba la Miyambo 21:31 limalongosola nkhaniyi motere: “Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo; koma wopulumutsa ndiye Yehova.” Pamenepo kazembeyo akuti Yehova akudalitsa Asuri, osati Ayuda. Chifukwa si bwenzi Asuri atalowa mpaka m’kati mwenimweni mwa dziko la Yuda, akutero kazembeyo.—Yesaya 36:9, 10.
ip-1 388 ¶13-14
Chikhulupiriro cha Mfumu Chifupidwa
Kuchokera m’thumba lake la zida za mfundo, titero kunena kwake, kazembeyo akusololanso chida china cha mawu. Akuchenjeza Ayudawo kuti asakhulupirire Hezekiya ngati anena kuti: “Yehova adzatipulumutsa ife.” Kazembeyo akukumbutsa Ayudawo kuti milungu ya Samariya sinathe kuteteza mafuko 10 kwa Asuri. Ndiponso bwanji za milungu ya mitundu ina imene Asuri agonjetsa? Iye akufunsanso kuti: “Ili kuti milungu ya Hamati, ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya m’manja mwanga?”—Yesaya 36:18-20.
Zoona, kazembeyo, pokhala wolambira milungu yonyenga, sakuzindikira kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa Samariya wampatukoyo ndi Yerusalemu wotsogoleredwa ndi Hezekiya. Milungu yonyenga ya Samariya inalibe mphamvu yopulumutsa ufumu wa mafuko khumiwo. (2 Mafumu 17:7, 17, 18) Mosiyana ndi zimenezo, Yerusalemu wolamuliridwa ndi Hezekiya wafulatira milungu yonyenga ndi kuyambanso kutumikira Yehova. Komabe, nthumwi zitatu zachiyudazo sizikuyesa kufotokoza zimenezi kwa kazembeyo. “Iwo anakhala chete, osamuyankha mawu, pakuti mfumu inawalamulira kuti, Musamuyankhe.” (Yesaya 36:21) Eliakimu, Sebina, ndi Yoaki akubwerera kwa Hezekiya kukapereka lipoti pamawu a kazembeyo.—Yesaya 36:22.
Mfundo Zothandiza
it “Zingwe” ¶4
Zingwe
Yehova anauza Senakeribu mfumu ya Asuri kuti: “Ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako. Kenako ndidzakukoka nʼkukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.” (2Mf 19:28; Yes 37:29) Chifukwa cha mphamvu ya Yehova, osati mwakufuna kwake, Senakeribu anakakamizika kusiya kuukira mzinda wa Yerusalemu n’kubwerera ku Nineve komwe pambuyo pake anakaphedwa ndi ana ake. (2Mf 19:32-37; Yes 37:33-38) Zimene Yehova anachita pomanga pakamwa pa adani ake zikusonyeza kuti anthuwo anali opanda mphamvu ngati nyama zomwe zamangidwa pakamwa.—Yes 30:28.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwbq nkhani Na. 110 ¶1-4
Kodi Ubatizo Umatanthauza Chiyani?
Yankho la m’Baibulo
Ubatizo ndi kuviika munthu m’madzi kenako n’kumuvuula. Baibulo limafotokoza za anthu ambiri amene anabatizidwa. (Machitidwe 2:41) Yesu ndi mmodzi mwa iwo ndipo iye anabatizidwa mumtsinje wa Yorodano. (Mateyu 3:13, 16) Patadutsa zaka zingapo, munthu wina wa ku Itiyopiya anabatizidwa pamene panali “madzi ambiri” pafupi ndi msewu womwe ankadutsa.—Machitidwe 8:36-40.
Yesu ananena kuti anthu amene amamutsatira ayenera kubatizidwa. (Mateyu 28:19, 20) Mtumwi Petulo nayenso anafotokoza bwino mfundo imeneyi.—1 Petulo 3:21.
Ubatizo ndi chizindikiro chakuti munthu yemwe akubatizidwayo analapa machimo ake ndiponso analonjeza Mulungu kuti kwa moyo wake wonse, azichita zomwe Mulunguyo akufuna. Zimenezi zikuphatikizapo kumvera Mulungu ndi Yesu nthawi zonse. Anthu akabatizidwa amayamba kuchita zimene Mulungu amafuna n’cholinga choti adzakhale ndi moyo kwamuyaya.
Munthu akamizidwa m’madzi chimakhala chizindikiro chakuti wasintha moyo wake. Kodi zimatheka bwanji zimenezi? Baibulo limayerekezera ubatizo ndi kuika munthu wakufa m’manda. (Aroma 6:4; Akolose 2:12) Choncho munthu akabatizidwa m’madzi amakhala ngati wafa ku moyo wake wakale. Akavuuka m’madzi amakhala ngati wayamba moyo watsopano monga Mkhristu wodzipereka.
FEBRUARY 23–MARCH 1
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 38-40
“Iye Adzasamalira Gulu la Nkhosa Zake Ngati Mʼbusa”
Zimene Baibulo Limatiuza Zokhudza Mlembi Wake
Werengani Yesaya 40:8. Kwa zaka zambiri, Mawu a Mulungu akhala akupereka malangizo abwino kwa amuna ndi akazi okhulupirika. Kodi zimenezi zatheka bwanji? Funso limenelitu ndi labwino chifukwa Malembawa analembedwa kalekale pa zinthu zoti zitha kuwonongeka. Choncho masiku ano zolemba zoyambirira sizipezekanso. Koma Yehova anaonetsetsa kuti anthu akopera Malemba opatulika. Ngakhale kuti okoperawa sanali angwiro, anayesetsa kuchita zinthu mosamala kwambiri. Mwachitsanzo, ponena za Malemba a Chiheberi katswiri wina analemba kuti: “Tinganene motsimikiza kuti palibe buku lina lakale lomwe linakoperedwa molondola kwambiri ngati Malembawa.” Choncho ngakhale kuti zinthu zomwe analembapo zinali zoti zimawonongeka, okopera ake sanali angwiro komanso kuti padutsa nthawi yaitali, tingakhalebe otsimikiza kuti zimene timawerenga m’Baibulo masiku ano ndi maganizo a Mlembi wake, Yehova.
Yehova ndi amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yak. 1:17) Baibulo ndi imodzi mwa mphatso zabwino kwambiri zimene iye anatipatsa. Mphatso imatiuza zambiri zokhudza woperekayo kuti amatidziwa bwino komanso amadziwa zimene timafunikira. Ndi mmenenso zilili ndi Mulungu yemwe anatipatsa Baibulo. Timaphunzira zambiri zokhudza Yehova kudzera mu mphatsoyi. Timaphunziramonso kuti iye amatidziwa bwino kwambiri komanso amadziwa zimene timafunikira. Munkhaniyi, tikambirana mmene Baibulo limasonyezera atatu mwa makhalidwe a Yehova omwe ndi nzeru, chilungamo komanso chikondi. Choyamba, tiyeni tikambirane mmene Baibulo limasonyezera nzeru za Mulungu.
Mphamvu Zoteteza—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”
Podziyerekezera ndi m’busa, Yehova amatitsimikizira kuti ndi wofunitsitsa kutiteteza. (Ezekieli 34:11-16) Kumbukirani zimene lemba la Yesaya 40:11 limafotokoza zokhudza Yehova. Lembali linafotokozedwa m’Mutu 2 wa bukuli ndipo limati: “Iye adzasamalira gulu la nkhosa zake ngati m’busa. Ndi dzanja lake, adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” Kodi zimatheka bwanji kuti kamwana kankhosa kakhale “pachifuwa” cha m’busa, kapena kuti pachovala chake chakumtunda chomwe wachipinda? Kamwanako kangafike pamene pali m’busayo, mwinanso n’kumakhudza mwendo wake. Komabe m’busayo ndi amene amayenera kuwerama n’kukanyamula ndiponso kukaika mosamala pachifuwa chake pomwe kangakhale motetezeka. Zimenezitu zikusonyeza bwino kuti M’busa wathu wamkulu amafunitsitsa kutiteteza.
“Iye Amapereka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”
Werengani Yesaya 40:26. Palibe munthu amene angakwanitse kuwerenga nyenyezi zonse m’chilengedwechi. Asayansi amaona kuti mumlalang’amba wathu wokha muli nyenyezi pafupifupi 400 biliyoni. Ngakhale zili choncho, Yehova amatha kutchula dzina la nyenyezi iliyonse. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngati Yehova amachita chidwi ndi zinthu zopanda moyo zimene analenga, kuli bwanji inuyo? Mumamutumikira chifukwa choti mumamukonda, osati chifukwa chakuti munalengedwa m’njira yoti muzingochita zimenezo. (Sal. 19:1, 3, 14) Atate wathu wakumwamba amadziwa chilichonse chokhudza ifeyo. Paja Baibulo limanena kuti ngakhale ‘tsitsi lenilenilo la m’mutu mwathu amaliwerenga.’ (Mat. 10:30) Wolemba masalimo amatitsimikiziranso kuti: “Yehova amadziwa za moyo wa anthu osalakwa.” (Sal. 37:18) Iye amaona mavuto amene tikukumana nawo ndipo amatha kutipatsa mphamvu kuti tipirire.
Werengani Yesaya 40:28. Yehova ali ndi mphamvu zambiri. Tangoganizirani za mphamvu zimene Mulungu anaika m’dzuwa. Wasayansi wina dzina lake David Bodanis anati: “Pa sekondi iliyonse, dzuwa limatulutsa mphamvu yofanana ndi mphamvu ya mabomba [anyukiliya okwana mabiliyoni ambiri].” Wasayansi winanso ananena kuti ‘mphamvu zimene zimachokera kudzuwa pa sekondi iliyonse, zikhoza kukhala zokwanira kuthandiza anthu kwa zaka 200,000.’ Ndiye ngati Mulungu amapatsa dzuwa mphamvu zochuluka chonchi, kodi angalephere kutipatsanso mphamvu zoti tipirire mavuto athu?
Werengani Yesaya 40:29. Kutumikira Yehova n’kosangalatsa kwambiri. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Senzani goli langa.” Koma anawonjezera kuti: “Mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Mfundo imeneyi ndi yoona. Nthawi zina timakhala otopa kwambiri tikamanyamuka kupita kumisonkhano kapena mu utumiki. Koma kodi timamva bwanji tikamabwerera kunyumba? Timamva bwino ndipo zimatithandiza kupirira mavuto athu. Izi zikusonyeza kuti goli la Yesu ndi lofewadi.
Mfundo Zothandiza
ip-1 400 ¶7
‘Mutonthoze Anthu Anga’
Kubwezeretsedwa komwe kunachitika m’ma 500 B.C.E. sikunali kukwaniritsidwa kokhako kwa ulosiwu. Ulosiwu unakwaniritsidwanso m’zaka 100 zoyambirira. Yohane Mbatizi anali mawu a winawake “wofuula m’chipululu,” pokwaniritsa Yesaya 40:3. (Luka 3:1-6) Mouziridwa, Yohane ananena kuti mawu a Yesaya ankanena za iyeyo. (Yohane 1:19-23) Kuyambira mu 29 C.E., Yohane anayamba kukonzera njira Yesu Khristu. Zimene Yohane ankalengeza zinachititsa chidwi anthu kuti ayembekezere Mesiya wolonjezedwayo kotero kuti, iwonso, adzamumvetsere n’kumamutsatira. (Luka 1:13-17, 76) Kudzera mwa Yesu, Yehova adzatsogolera olapawo kuti adzakhale pa ufulu umene Ufumu wa Mulungu wokhawo ndiwo ungapereke—ufulu womasuka ku uchimo ndi imfa. (Yohane 1:29; 8:32) Mawu a Yesaya anakwaniritsidwa pamlingo waukulu pamene otsalira a Isiraeli wauzimu anamasulidwa kwa Babulo Wamkulu mu 1919 ndi kubwezeretsedwa pa kulambira koona.