NYIMBO 120
Tikhale Ofatsa Ngati Khristu
Losindikizidwa
1. Yesu anali munthu wapadera
Koma sanadzikuze, sananyade.
Anali ndi udindo wapamwamba
Komatu anali wodzichepetsa.
2. Kwa anthu omwe ali ndi mavuto,
Yesu walonjeza kuwathandiza.
Akamaika Ufumu poyamba
Iye aziwachitira chifundo.
3. Yesu anati: ‘Tonse ndi abale.’
Timamumvera monga Mutu wathu.
Ofatsa ndi ofunika kwa M’lungu,
Adzalandira dziko latsopano.
(Onaninso Miy. 3:34; Mat. 5:5; 23:8; Aroma 12:16.)