-
Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 1: Tanthauzo la KubatizidwaZimene Achinyamata Amafunsa
-
-
ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 1: Tanthauzo la Kubatizidwa
Chaka chilichonse, achinyamata ambiri amene akukulira m’banja la Mboni za Yehova amabatizidwa. Kodi inuyo mukuganizira zobatizidwa? Ngati zili choncho, poyamba muyenera kumvetsa tanthauzo la kudzipereka kwa Mulungu komanso kubatizidwa.
Kodi kubatizidwa kumatanthauza chiyani?
Mawu oti kubatizidwa omwe amapezeka m’Baibulo amatanthauza kumizidwa thupi lonse m’madzi osati kungowazidwa ndi madzi basi. Mawuwa amakhalanso ndi tanthauzo lophiphiritsa.
Kumizidwa m’madzi mukabatizidwa kumasonyeza kuti mwasiya kumangochita zimene zimakusangalatsani inuyo.
Kutulutsidwa m’madzi kumasonyeza kuti mwayamba moyo watsopano wochita zimene zimasangalatsa Mulungu.
Mukabatizidwa mumasonyeza pa gulu kuti Yehova ali ndi ulamuliro wosankha zoyenera ndi zosayenera komanso kuti mwalonjeza kuchita zimene iye amafuna.
Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani mungafune kusonyeza pa gulu kuti mwalonjeza kumvera Yehova? Onani 1 Yohane 4:19 ndi Chivumbulutso 4:11.
Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza chiyani?
Musanabatizidwe muyenera kudzipereka kwa Yehova muli nokha. Kodi mungachite bwanji zimenezi?
Muyenera kupemphera kwa Yehova muli nokha n’kumamuuza kuti mwalonjeza kudzamutumikira mpaka kalekale. Muyenera kumuuzanso kuti muzidzachita zimene iye amafuna zivute zitani mosatengera zimene anthu ena angasankhe kuchita.
Mukabatizidwa mumasonyeza pa gulu zimene munachita panokha podzipereka kwa Mulungu. Mumasonyeza kwa anthu ena kuti mwasankha kuchita zimene Yehova amafuna m’malo mochita zofuna zanu.—Mateyu 16:24.
Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani moyo wanu umakhala wabwino kwambiri mukayamba kuchita zimene Yehova amafuna? Onani Yesaya 48:17, 18 ndi Aheberi 11:6.
N’chifukwa chiyani kubatizidwa n’kofunika?
Yesu ananena kuti ophunzira ake ayenera kubatizidwa. (Mateyu 28:19, 20) Choncho masiku anonso, Akhristu ayenera kubatizidwa. Baibulo limanena kuti munthu ayenera kubatizidwa kuti adzapulumuke.—1 Petulo 3:21.
Koma muyenera kubatizidwa chifukwa chokonda Yehova ndi kuyamikira zimene iye amachita. Muyenera kukhala ndi mtima umene wolemba masalimo unali nawo polemba kuti: “Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira? . . . Ndidzaitana pa dzina la Yehova. Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova.”—Salimo 116:12-14.
Zoti muganizire: Kodi Yehova wakuchitirani zinthu zotani, nanga mungamubwezere bwanji? Onani Deuteronomo 10:12, 13 ndi Aroma 12:1.
-
-
Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 2: Kukonzekera KubatizidwaZimene Achinyamata Amafunsa
-
-
ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 2: Kukonzekera Kubatizidwa
Ngati mukutsatira mfundo za m’Baibulo komanso mukuyesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu, muyenera kuti mukuganiza zobatizidwa. Koma kodi mungadziwe bwanji ngati mwakonzeka kuchita zimenezi?a
Zimene zili m’nkhaniyi
Kodi ndiyenera kudziwa zochuluka bwanji?
Ngati mukukonzekera kubatizidwa simuyenera kuloweza pamtima zinthu zambiri ngati mmene mungachitire pokonzekera mayeso akusukulu. Koma muyenera kugwiritsa ntchito mphamvu zanu za kuganiza kuti mudzitsimikizire zoti Baibulo limaphunzitsa mfundo zoona. (Aroma 12:1) Mwachitsanzo:
Kodi mumakhulupirira ndi mtima wonse kuti kuli Mulungu komanso ndi woyenera kumulambira?
Baibulo limati: “Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”—Aheberi 11:6.
Dzifunseni kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndimakhulupirira kuti kuli Mulungu?’ (Aheberi 3:4) ‘N’chifukwa chiyani ndiyenera kumulambira?’—Chivumbulutso 4:11.
Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 1: N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Kuti Kuli Mulungu?”
Kodi mumakhulupirira ndi mtima wonse kuti mfundo za m’Baibulo ndi zochokera kwa Mulungu?
Baibulo limati: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.”—2 Timoteyo 3:16.
Dzifunseni kuti: ‘N’chifukwa chiyani sindikhulupirira kuti m’Baibulo muli maganizo a anthu basi?’—Yesaya 46:10; 1 Atesalonika 2:13.
Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 1: Kuganizira Mozama Mfundo za M’Baibulo”
Kodi mumakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova akugwiritsa ntchito mpingo wa Chikhristu pokwaniritsa cholinga chake?
Baibulo limati: “Kwa [Mulungu] kukhale ulemerero kudzera mwa mpingo ndi mwa Khristu Yesu, ku mibadwo yonse kwamuyaya.”—Aefeso 3:21.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimaona kuti zimene ndimaphunzira kumisonkhano zimachokera kwa anthu kapena kwa Yehova?’ (Mateyu 24:45) ‘Kodi ndimapezeka pamisonkhano ngakhale pamene makolo anga sangathe (ngati amakulolani kupezeka)?’—Aheberi 10:24, 25.
Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupezeka Pamisonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu?”
Kodi ndiyenera kuchita zotani?
Simuyenera kukhala munthu wangwiro kuti mubatizidwe. Komabe, muyenera kusonyeza kuti mumafunitsitsa ‘kupatuka pa zinthu zoipa ndi kuchita zabwino.’ (Salimo 34:14) Mwachitsanzo:
Kodi mumatsatira mfundo za Yehova pa moyo wanu?
Baibulo limati: “Khalani ndi chikumbumtima chabwino.”—1 Petulo 3:16.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimasonyeza bwanji kuti ndaphunzitsa “mphamvu zanga za kuzindikira kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera”?’ (Aheberi 5:14) ‘Kodi pali nthawi zina pamene ndakana kuchita zinthu zoipa zimene anzanga ankafuna? Kodi ndimasankha kucheza ndi anthu amene amandilimbikitsa kuchita zabwino?’—Miyambo 13:20.
Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “Kodi Ndingaphunzitse Bwanji Chikumbumtima Changa?”
Kodi mumazindikira kuti muyenera kuyankha mlandu pa zimene mumachita?
Baibulo limati: “Aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.”—Aroma 14:12.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndine woona mtima podzifufuza komanso pochita zinthu ndi anthu ena?’ (Aheberi 13:18) ‘Kodi ndimavomereza ndikalakwitsa zinthu kapena ndimakonda kuzibisa, apo ayi kuloza chala anthu ena?’—Miyambo 28:13.
Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?”
Kodi muli pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?
Baibulo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuchita zotani kuti ndilimbitse ubwenzi wanga ndi Yehova?’ Mwachitsanzo, ‘Kodi ndimawerenga Baibulo pafupipafupi?’ (Salimo 1:1, 2) ‘Kodi ndimakonda kupemphera?’ (1 Atesalonika 5:17) ‘Nanga kodi ndimanena zinthu zimene zili mumtima mwanga ndikamapemphera? Kodi anzanga ndi amene ndi anzakenso a Yehova?’—Salimo 15:1, 4.
Kodi mukufuna thandizo? Onani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 2: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikusangalatsani.”
ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Kuti mukonzekere kubatizidwa, werengani chaputala 37 m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. Makamaka, onani zimene mungalembe patsamba 308 ndi 309.
a Werengani nkhani yakuti “Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 1,” yomwe ikufotokoza tanthauzo ndiponso kufunika kwa kudzipereka kwa Mulungu komanso kubatizidwa.
-