NYIMBO 39
Tipange Mbiri Yabwino Kwa Mulungu
Losindikizidwa
1. Tsiku ndi tsiku tiziyesetsabe
Kupanga mbiri yabwino kwa M’lungu.
Tikachita zomwe M’lungu amafuna
Adzatikonda nthawi zonse.
2. Kufunitsitsa kutchuka m’dzikoli
Cholinga choti anthu atikonde,
Ndi kopanda phindu chifukwa Yehova
Sangatikonde tikatero.
3. Tikufunadi kulembedwa dzina
Kuti likhale mu buku la moyo.
Choncho tizikhala ndi mbiri yabwino
Kwa M’lungu wathu mpaka kale.
(Onaninso Gen. 11:4; Miy. 22:1; Mal. 3:16; Chiv. 20:15.)