Yehova
Dzina lake
Dzina lakuti Yehova limatanthauza “Amachititsa Kukhala”
Kodi Yehova amakhala chiyani, kapena amachita chiyani kuti asamalire atumiki ake?
N’chifukwa chiyani kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi nkhani yofunika kwambiri?
N’chifukwa chiyani aliyense ayenera kumvera Yehova monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse?
Mayina ena audindo a Yehova
Wamphamvuyonse—Ge 17:1; Chv 19:6
Atate—Mt 6:9; Yoh 5:21
Mlangizi Wamkulu—Yes 30:20
Yehova wa magulu ankhondo—1Sa 1:11
Mfumu yamuyaya—1Ti 1:17; Chv 15:3
Wolemekezeka—Ahe 1:3; 8:1
Wam’mwambamwamba—Ge 14:18-22; Sl 7:17
Thanthwe—De 32:4; Yes 26:4
Ambuye Wamkulu Koposa—Yes 25:8; Amo 3:7
Makhalidwe a Yehova ochititsa chidwi
Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi woyera? Nanga kudziwa zimenezi kuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?
Eks 28:36; Le 19:2; 2Ak 7:1; 1Pe 1:13-16
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yes 6:1-8—Mneneri Yesaya ataona masomphenya osonyeza kuti Yehova ndi woyera, anayamba kudziona kuti ndi wochimwa kwambiri. Kenako mngelo anamukumbutsa kuti n’zotheka anthu ochimwa kukhala oyera pamaso pa Mulungu
Aro 6:12-23; 12:1, 2—Mtumwi Paulo anafotokoza zimene tingachite kuti tilimbane ndi zilakolako za uchimo n’kuyamba kubala “zipatso za chiyero”
Kodi mphamvu za Yehova ndi zazikulu bwanji? Nanga amazigwiritsa ntchito m’njira ziti?
Eks 15:3-6; 2Mb 16:9; Yes 40:22, 25, 26, 28-31
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
De 8:12-18—Mneneri Mose anakumbutsa Aisiraeli kuti anali ndi zinthu zabwino zambiri chifukwa choti Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu zake powadalitsa
1Mf 19:9-14—Yehova analimbikitsa mneneri Eliya pomusonyeza mphamvu zake zazikulu
N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti chilungamo cha Yehova ndi chapamwamba kuposa chilichonse?
De 32:4; Yob 34:10; 37:23; Sl 37:28; Yes 33:22
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
De 24:16-22—Chilamulo cha Mose chimasonyeza kuti chilungamo cha Yehova nthawi zonse chimayendera limodzi ndi chikondi komanso chifundo chake
2Mb 19:4-7—Mfumu Yehosafati anakumbutsa oweruza kuti ayenera kumaweruza mogwirizana ndi chilungamo cha Yehova osati kutengera maganizo a anthu
N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ali ndi nzeru zapamwamba kuposa wina aliyense?
Sl 104:24; Miy 2:1-8; Yer 10:12; Aro 11:33; 16:27
Onaninso Sl 139:14; Yer 17:10
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Mf 4:29-34—Yehova anadalitsa Mfumu Solomo pomupatsa nzeru zochuluka kuposa munthu wina aliyense yemwe anakhalapo pa nthawiyo
Lu 11:31; Yoh 7:14-18—Yesu anali ndi nzeru zambiri zoposa Solomo, koma modzichepetsa anasonyeza kuti zinali zochokera kwa Yehova
Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti chikondi ndi khalidwe lake lalikulu?
Yoh 3:16; Aro 8:32; 1Yo 4:8-10, 19
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 10:29-31—Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha mpheta pofuna kusonyeza kuti Yehova amatikonda kwambiri komanso amaona kuti munthu wina aliyense ndi wofunika
Mko 1:9-11—Yehova anauza Yesu kuti amamukonda komanso amasangalala naye. Makolo ayenera kutengera chitsanzo cha Yehova posonyeza chikondi kwa ana awo komanso kuwayamikira
Kodi ndi zifukwa zinanso ziti zimene zimatichititsa kukonda Yehova? Baibulo limanena kuti Yehova ali ndi makhalidwe enanso abwino kwambiri monga . . .
Amaona zonse—2Mb 16:9; Miy 15:3
Sasintha; ndi wodalirika—Mki 3:6; Yak 1:17
Wachifundo chachikulu—Yes 49:15; 63:9; Zek 2:8
Wamuyaya; wopanda chiyambi kapena mapeto—Sl 90:2; 93:2
Wowolowa manja—Sl 104:13-15; 145:16
Waulemerero—Chv 4:1-6
Wosangalala—1Ti 1:11
Wodzichepetsa—Sl 18:35
Wokoma mtima—Lu 6:35; Aro 2:4
Wokhulupirika—Chv 15:4
Wapamwamba—Sl 8:1; 148:13
Wachifundo—Eks 34:6
Woleza mtima—Yes 30:18; 2Pe 3:9
Wamtendere—Afi 4:9
Wolungama—Sl 7:9
Kodi chimachitika n’chiyani tikamudziwa bwino Yehova Mulungu?
Kodi tingatumikire bwanji Yehova?
N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova samayembekezera kuti atumiki ake azichita zinthu zoposa zomwe angakwanitse?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
De 30:11-14—Lamulo limene Yehova anapereka kudzera mwa mneneri Mose silinali lovuta kwambiri kulitsatira
Mt 11:28-30—Yesu yemwe ankachita zinthu ngati Atate wake, anatsimikizira otsatira ake kuti iye ndi Mbuye wotsitsimutsa
N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kutamandidwa?
Onaninso Yer 20:9; Lu 6:45; Mac 4:19, 20
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Sl 104:1, 2, 10-20, 33, 34—Wamasalimo anatamanda Yehova chifukwa cha zinthu zimene analenga
Sl 148:1-14—Zinthu zonse zimene Yehova analenga kuphatikizapo angelo, zimatamanda Yehova ndipo nafenso tiyenera kuchita chimodzimodzi
Kodi zochita zathu zingachititse bwanji anthu ena kuti azitamanda Yehova?
Kodi tingatani kuti tikhale anzake a Yehova?
Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kukhala anzake a Yehova?
Kodi kuwerenga Baibulo komanso kuganizira mozama zomwe tikuwerengazo kungatithandize bwanji kukhala anzake a Yehova?
N’chifukwa chiyani m’pofunika kuti tizichita zimene timaphunzira zokhudza Yehova?
N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyesa ngakhale pang’ono kubisira zinazake Yehova?
Yob 34:22; Miy 28:13; Yer 23:24; 1Ti 5:24, 25
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mf 5:20-27—Gehazi anayesa kubisa tchimo lake, koma Yehova anathandiza mneneri wake Elisa kudziwa zoona zake
Mac 5:1-11—Zimene Hananiya ndi Safira anachita zinaululika ndipo analangidwa chifukwa chonamiza mzimu woyera